LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr22 September
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2022
  • Tumitu
  • SEPTEMBER 5-11
  • SEPTEMBER 12-18
  • SEPTEMBER 19-25
  • SEPTEMBER 26–OCTOBER 2
  • OCTOBER 3-9
  • OCTOBER 10-16
  • OCTOBER 17-23
  • OCTOBER 24-30
  • OCTOBER 31–NOVEMBER 6
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2022
mwbr22 September

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Umoyo na Utumiki

SEPTEMBER 5-11

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 9-10

“Tamandani Yehova Cifukwa ca Nzelu Zake”

w99 7/1 30 ¶6

Ulendo Umene Unali Wopindulitsa Kwambili

Itakumana na Solomo, mfumukaziyo inayamba kumuyesa na “mafunso ovuta.” (1 Mafumu 10:1) Liwu laciheberi logwilitsidwa nchito pano lingatanthauze “miyambi.” Koma izi sizitanthauza kuti mfumukaziyo inali kuceza na Solomo nkhani zopanda pake. Cosangalatsa n’cakuti pa Salimo 49:4, liwu laciheberi limeneli limagwilitsidwa nchito pofotokoza za mafunso ofunika kwambili okhudza ucimo, imfa, na kumasulidwa. Conco, n’kutheka kuti mfumukazi ya ku Sheba inali kukambilana na Solomo nkhani zozama zimene zinayesa kuculuka kwa nzelu zake. Baibo imati iye ‘ananena zonse zimene zinali kumtima kwake.’ Ndipo Solomo “anaiyankha mfumukaziyo mafunso ake onse. Panalibe cimene mfumuyo inalephelela kuyankha.”—1 Mafumu 10:2b, 3.

w99 11/1 20 ¶6

Pamene Ambili Akhala Owoloŵa Manja

Podabwa na zimene inamva na kuona, mfumukaziyo inayankha kuti: “Odala atumiki anuwa amene amatumikila pamaso panu nthawi zonse, n’kumamva nzelu zanu.” (1 Mafumu 10:4-8) Sananene kuti atumiki a Solomo anali odala cifukwa cakuti mbuye wawo anali na cuma coculuka kwambili, ngakhale kuti zinalidi motelo. Mmalomwake, atumiki a Solomo anali odala cifukwa cakuti nthaŵi zonse anali kumvetsela nzelu za Solomo zimene Mulungu anam’patsa. Mfumukazi ya ku Sheba ni citsanzo cabwino kwambili kwa anthu a Yehova lelolino, amene azingidwa na nzelu za Mlengi komanso Mwana wake, Yesu Khristu!

w99 7/1 30-31

Ulendo Umene Unali Wopindulitsa Kwambili

Mfumukazi ya ku Sheba inacita cidwi na nzelu za Solomo komanso ulemelelo wa ufumu wake, cakuti “inazizila nkhongono.” (1 Mafumu 10:4, 5) Ena amati mawu ameneŵa amatanthauza kuti mfumukaziyo “inabanika.” Katswili wina wa maphunzilo anacita kukamba kuti mwina inakomoka! Kaya zinacitika n’zotani, cimene tidziŵa n’cakuti mfumukaziyo inadabwa na zimene inaona na kumva. Inacha atumiki a Solomo kukhala odala popeza anali kumva nzelu za mfumu imeneyi, ndipo inayamika Yehova cifukwa copatsa Solomo ufumu. Kenako mfumukaziyo inapeleka mphatso zamtengo wapatali kwa mfumuyo. Golide cabe anali wokwana ndalama pafupifupi $40,000,000 malinga na ndalama za masiku ano. Nayenso Solomo anapeleka mphatso. Anapatsa mfumukaziyo ‘zofuna zake zonse zimene inapempha.’—1 Mafumu 10:6-13.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w08 11/1 22 ¶4-6

Kodi Mukudziŵa?

Kodi Mfumu Solomo inali na golide woculuka bwanji?

Malemba amanena kuti Hiramu mfumu ya ku Turo, inatumiza matani anayi a golide kwa Solomo ndipo mfumukazi ya ku Sheba inapelekanso matani anayi a golide. Komanso zombo za Solomo zinali kubweletsa matani oposa 14 a golide kucokela ku Ofiri. Baibo imati: “Golide amene ankabwela kwa Solomo caka cimodzi, anali wolemela matalente 666.” Amenewa ni matani oposa 22. (1 Mafumu 9:14, 28; 10:10, 14) Kodi zimenezi ni zoona? Kodi panthawi imeneyo nkhokwe za golide za mafumu zinali zazikulu bwanji?

Zolemba zakale, zimene akatswili amati n’zodalilika, zimanena kuti Farao Thutmose III wa ku Iguputo (yemwe anakhalako zaka pafupifupi 3,500 zapitazo) anapeleka matani pafupifupi 12 a golide ku kacisi wa Amun-Ra ku Karnak. Ca m’ma 700 B.C.E., mfumu ya Asuri Tigilati Pilesere III, inalandila matani anayi a golide kucokela ku Turo ngati msonkho, ndipo Sarigoni II anapelekanso matani anayi ngati mphatso kwa milungu ya ku Babulo. Mfumu Filipo II ya ku Makedoniya (359-336 B.C.E.) akuti inali kukumba matani oposa 25 a golide caka ciliconse m’migodi ya Pangaeum ku Thrace.

Mwana wa Filipo, Alesandro Wamkulu (336-323 B.C.E.) atalanda mzinda wa ku Perisiya wochedwa Susa, akuti anatenga matani pafupifupi 1,070 a golide. Iye anatenganso matani oposa 6,000 kucokela ku Perisiya konse. Conco, tikayelekezela na zitsanzo zimenezi, zimene Baibo imanena zokhudza golide wa Mfumu Solomo si zokokomeza.

SEPTEMBER 12-18

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 11-12

“Sankhani Mwanzelu Munthu Womanga Naye Banja”

w18.07 18 ¶7

“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”

7 Tingaphunzile zambili pa nkhani ya Mfumu Solomo. Pamene anali wacicepele, Solomo anali kuyang’ana kwa Yehova kuti am’patse malangizo. Mulungu anam’patsa nzelu zambili komanso udindo womanga kacisi waulemelelo ku Yerusalemu. Koma Solomo anawononga ubwenzi wake wabwino na Yehova. (1 Maf. 3:12; 11:1, 2) M’Cilamulo ca Mulungu, munali lamulo lacindunji loletsa mfumu ya Isiraeli ‘kudziculukitsila akazi kuti mtima wake ungapatuke.’ (Deut. 17:17) Koma Solomo sanamvele lamulo limeneli, cakuti m’kupita kwa nthawi anakwatila akazi 700. Komanso anatenga akazi ena apambali 300. (1 Maf. 11:3) Akazi ake ambili sanali Aisiraeli, ndipo anali kulambila mafano. Conco pamenepa, Solomo anaphwanyanso lamulo la Mulungu loletsa kukwatila akazi a mitundu ina.—Deut. 7:3, 4

w19.01 15 ¶6

Kodi Tingauteteze Bwanji Mtima Wathu?

6 Satana ni wopanduka, amanyalanyaza miyezo ya Yehova, ndiponso ni wodzikonda. Iye amafuna kuti ife titengele zocita zake. Komabe, Satana sangatikakamize kucita zimenezi. Conco, amaseŵenzetsa njila zina pofuna kukwanilitsa colinga cake cimeneci. Mwacitsanzo, wasoceletsa anthu ambili a m’dzikoli. (1 Yoh. 5:19) Iye amafuna kuti tizigwilizana na anthu oipa amenewo, olo kuti tidziŵa kuti kucita zimenezo ‘kungawononge’ makhalidwe na maganizo athu. (1 Akor. 15:33) Mfumu Solomo anasoceletsedwa na msampha umenewu. Iye anakwatila akazi ambili acikunja, amene m’kupita kwa nthawi, “anapotoza mtima” wake na kum’sonkhezela kusiya Yehova.—1 Maf. 11:3.

w18.07 19 ¶9

“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”

9 Koma Yehova sanyalanyaza macimo. Baibo imati: “Yehova anamukwiyila kwambili Solomo cifukwa mtima wake unapatuka kwa Yehova. . . , amene anamuonekela kaŵili konse. Pa nkhani imeneyi, Mulungu anali atamulamula kuti asatsatile milungu ina, koma iye sanasunge zimene Yehova analamula.” Pamapeto pake, Mulungu analeka kumuyanja na kum’cilikiza. Komanso iye atafa, ufumu wa Isiraeli unagaŵikana moti mafumu obwela pambuyo pake anakumana na mavuto ambili kwa zaka zoculuka.—1 Maf. 11:9-13.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w18.06 14 ¶1-4

Akanayanjidwa na Mulungu

Ataona kuti Aisiraeli ena am’pandukila, Rehobowamu anasonkhanitsa asilikali ake kuti akawathile nkhondo. Koma Yehova anamuletsa kupitila mwa mneneli Semaya. Iye anati: “Musapite kukamenyana ndi abale anu, ana a Isiraeli. Aliyense abwelele kunyumba kwake, cifukwa zimene zacitikazi, zacitika mwa kufuna kwanga.”—1 Maf. 12:21-24.

Kodi muganiza kuti Rehobowamu anamvela bwanji Yehova atamuletsa kumenya nkhondo? Izi ziyenela kuti zinamuvutitsa maganizo. Pa nthawiyo, Rehobowamu anali ataopseza anthu kuti adzawalanga “ndi zikoti zaminga.” Conco, mwina anali kudzifunsa kuti, ‘Kodi anthu adzaniona bwanji nikapanda kuwalanga opandukawa?’ (Yelekezelani na 2 Mbiri 13:7.) Olo zinali conco, mfumuyo na asilikali ake “anamvela mawu a Yehova n’kubwelela kwawo malinga ndi mawu a Yehova.”

Kodi pali phunzilo lanji pamenepa? N’cinthu canzelu kumvela malamulo a Mulungu olo kuti anthu ena angatiseke. Ngati timvela Mulungu, iye adzatikonda na kutidalitsa.—Deut. 28:2.

Kodi Rehobowamu atamvela Mulungu, zotulukapo zake zinali zotani? Iye atasintha maganizo ake omenya nkhondo, anayamba kumanga mizinda m’zigawo za fuko la Yuda na Benjamini zimene anali kulamulila. Komanso analimbitsa “kwambili” citetezo m’mizinda ina. (2 Mbiri 11:5-12) Cofunika kwambili cinali cakuti, kwa kanthawi anamvela malamulo a Yehova. Pamene anthu a mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 wolamulidwa na Yerobowamu anayamba kulambila mafano, anthu ambili ocokela kumeneko ‘analimbikitsa Rehobowamu.’ Anacita izi mwa kupita ku Yerusalemu kukacilikiza kulambila koona. (2 Mbiri 11:16, 17) Conco, kumvela kwa Rehobowamu kunapangitsa kuti ufumu wake ulimbe.

SEPTEMBER 19-25

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 13-14

“N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kukhala Okhutila Komanso Odzicepetsa?”

w08 8/15 8 ¶4

Khalani Okhulupilika na Mtima Wonse

4 Ndiyeno Yerobowamu anauza munthu wa Mulunguyo kuti: “Tiyeni kunyumba mukadye cakudya, ndiponso ndikakupatseni mphatso.” (1 Maf. 13:7) Kodi pamenepa mneneliyo akanatani? Kodi akanavomela kupita ku nyumba kwa mfumuyo atapeleka uthengawo? (Sal. 119:113) Kapena kodi akanakana kupita ku nyumba kwa mfumu ngakhale kuti mfumuyo inali itazindikila kulakwa kwake? Yerobowamu anali wolemela moti akanatha kupatsa anthu mphatso zamtengo wapatali. Ngati mneneli wa Mulungu anali na kamtima kokonda cuma, mphatso zimene mfumuyo inafuna kum’patsa zikanakhala ciyeso cacikulu. Koma Yehova anali atauza mneneliyo kuti: “Usakadye cakudya kapena kumwa madzi, ndipo pobwelela usakadzele njila imene udutse popita.” Conco, mneneliyo anayankha mfumuyo mwamphamvu kuti: “Ngakhale mutandipatsa hafu ya nyumba yanu, sindingapite nanu kukadya cakudya kapena kumwa madzi kwanu kuno.” Ndipo mneneliyo atacoka ku Beteli anadzela njila ina. (1 Maf. 13:8-10) Kodi zimene mneneliyu anacita zikutiphunzitsa ciyani pankhani yokhulupilika na mtima wonse?—Aroma 15:4.

w08 8/15 11 ¶15

Khalani Okhulupilika na Mtima Wonse

15 Kodi zimene mneneli wa ku Yuda analakwitsa zikutiphunzitsanso ciyani? Lemba la Miyambo 3:5 limati: “Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu.” M’malo moti mneneliyu akhulupililebe Yehova monga anali kucitila kale, iye anayendela maganizo ake. Zimenezi zinam’phetsa komanso zinacititsa kuti asakhale na dzina labwino kwa Mulungu. Izi zikuonetselatu kuti tiyenela kukhala odzicepetsa ndiponso okhulupilika potumikila Yehova.

w08 8/15 9 ¶10

Khalani Okhulupilika na Mtima Wonse

10 Mneneli wa ku Yuda akanatha kudziŵa kuti mneneli wokalambayu amamunamiza. Iye akanadzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciyani Yehova watumiza mngelo kuuza munthu wina malangizo osiyana na amene ananiuza?’ Mneneliyu akanatha kupempha Yehova kuti am’fotokozele bwino-bwino nkhaniyo. Koma Malemba saonetsa kuti iye anacita zimenezi. Mmalomwake, “anabwelela naye [munthu wokalambayo] kuti akadye cakudya ndi kumwa madzi kunyumba kwake.” Koma Yehova sanasangalale nazo zimenezi. Mneneli amene ananamizidwayo akubwelela kwawo ku Yuda, anapezana na mkango panjila ndipo unamupha. Nchito yake ya uneneliyo inathela pomwepo.—1 Maf. 13:19-25.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w10 7/1 29 ¶5

Amaona Zabwino mwa Anthu

Cofunika kwambili n’cakuti mawu a pa 1 Mafumu 14:13 amatiphunzitsa mfundo ina yabwino kwambili yokhudza Yehova ndiponso zimene amaona mwa ife. Kumbukilani kuti cinthu cina cabwino ‘cinapezedwa mwa’ Abiya. Zikuoneka kuti Yehova anafufuza mumtima wa Abiya mpaka atapeza cinthu cabwino. Pomuyelekezela na anthu a m’banja lake, katswili wina wamaphunzilo ananena kuti Abiya anali “ngati mwala wamtengo wapatali womwe uli pamulu wamiyala wamba.” Yehova anasangalala cifukwa ca zabwino zimene Abiya anacita. Cifukwa ca zimenezi Mulungu anacitila cifundo munthu ameneyu, amene anali wabwino m’banja lawo lonse.

SEPTEMBER 26–OCTOBER 2

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 15-16

“Asa Anacita Zinthu Molimba Mtima—Kodi Inunso Mumatelo?”

w12 8/15 8 ¶4

“Mudzapeza Mphoto Cifukwa ca Nchito Yanu”

Asa anayamba kulamulila mu 977 B.C.E. Nthawi imeneyi n’kuti Isiraeli na Yuda atagaŵikana kukhala maufumu aŵili kwa zaka 20. Pa nthawiyi, kulambila konyenga kunali ponse-ponse mu Yuda. Nawonso anthu a maudindo mu ufumuwu anali kulambila milungu ya ku Kanani imene amati ni yobeleketsa. Ponena za Mfumu Asa, Baibo imati: “Anacita zabwino ndi zoyenela pamaso pa Yehova Mulungu wake.” Iye “anacotsa maguwa ansembe acilendo, anagwetsa malo okwezeka, anaphwanya zipilala zopatulika ndi kudula mizati yopatulika.” (2 Mbiri 14:2, 3) Asa anacotsanso mu Yuda monse “mahule aamuna a pakacisi” amene anali kugona na amuna anzawo polambila milungu yawo. Koma pali zinanso zimene Asa anacita. Iye analimbikitsanso anthu kuti “afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatila cilamulo” cake.—1 Maf. 15:12, 13; 2 Mbiri 14:4.

w17.03 19 ¶7

Tumikilani Yehova na Mtima Wathunthu!

7 Aliyense wa ife ayenela kudzipenda kuti aone ngati ni wodzipeleka na mtima wonse kwa Mulungu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi nimayesetsa kucita zinthu zokondweletsa Yehova, kuteteza kulambila koona, na kuteteza anthu a Mulungu ku zinthu zimene zingawaononge mwauzimu?’ Ganizilani za Asa. Iye anafunika kulimba mtima kuti acotse Maaka pa udindo wokhala “mayi wa mfumu” m’dziko lake. N’zoona kuti mumpingo sitingayembekezele kupeza munthu wocita zoipa ngati Maaka. Koma nthawi zina mungafunike kucita zinthu molimba mtima ngati Asa. Mwacitsanzo, bwanji ngati wina m’banja lanu kapena mnzanu wapamtima wacita chimo, ndipo wacotsedwa mumpingo cifukwa cosalapa? Kodi mungalimbe mtima na kuleka kuceza naye? Kodi mtima wanu ungakusonkhezeleni kucita ciani?

it-1 184-185

Asa

Nthawi zina Asa anali kucita zinthu mosaganiza bwino komanso kulephela kuona zinthu mwauzimu. Ngakhale n’conco, iye anali na makhalidwe abwino ndipo sanali kulambila mafano. Mwacidziŵikile, makhalidwe ake abwino amenewo anaposa zolakwa zake, ndipo iye amaonedwa monga mmodzi wa mafumu okhulupilika a mu mzele wa Yuda. (2 Mbiri 15:17) Asa analamulila kwa zaka 41. Iye analamulilako panthawi imodzi na mafumu 8 a Isiraeli. Mafumu amenewo ni awa: Yerobowamu, Nadabu, Basa, Ela, Zimiri, Omuri, Tibini (amene analamulila cigawo cina ca Isiraeli motsutsana na Omuri), komanso Ahabu. (1 Maf. 15:9, 25, 33; 16:8, 15, 16, 21, 23, 29) Asa atamwalila, mwana wake Yehosafati anakhala mfumu.—1 Maf. 15:24.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w98 9/15 21-22

Kodi Mulungu Ni Weniweni kwa Inu?

Mwacitsanzo, ŵelengani za ulosi wonena za cilango copelekedwa kwa munthu amene adzayesa kumanganso Yeriko, ndipo ŵelenganinso za kukwanilitsidwa kwake. Yoswa 6:26 amati: “Yoswa analumbila kuti: ‘Adzakhale wotembeleledwa pamaso pa Yehova munthu amene adzamangenso mzinda wa Yerikowu. Akadzangoyala maziko ake, mwana wake woyamba adzafe, ndipo akadzaika zitseko zake za pacipata, mwana wake wotsiliza adzafe.’” Ulosiwu unakwanilitsidwa patapita zaka pafupifupi 500, popeza timaŵelenga pa 1 Mafumu 16:34 kuti: “M’masiku ake, Hiyeli wa ku Beteli anamanga Yeriko. Atangoyala maziko ake, Abiramu mwana wake woyamba anafa, ndipo atangoika zitseko zake za pacipata, Segubu mwana wake wotsiliza anafa. Izi zinacitika mogwilizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzela mwa Yoswa mwana wa Nuni.” Mulungu woona yekha ndiye angauzile maulosi otele na kuwakwanilitsa.

OCTOBER 3-9

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 17-18

“Kodi Mukayika-kayika Mpaka Liti?”

w17.03 14 ¶6

Khalani na Cikhulupililo Ndipo Muzipanga Zosankha Mwanzelu

6 Aisiraeli atayamba kukhala m’Dziko Lolonjezedwa, anafunika kupanga cosankha cofunika kwambili. Anafunika kusankha kutumikila Yehova kapena kutumikila mulungu wina (kapena milungu ina). (Ŵelengani Yoswa 24:15.) Cosankha cimeneci cingaoneke ngati nkhani yaing’ono. Komabe, zimene akanasankha zikanawacititsa kukhala na moyo kapena kufa. M’nthawi ya Oweluza, Aisiraeli mobweleza-bweleza anali kusankha mopanda nzelu. Iwo anali kusiya Yehova na kuyamba kutumikila milungu yonama. (Ower. 2:3, 11-23) Ganizilaninso zimene zinacitika panthawi ina, pamene anthu a Mulungu anafunika kupanga cosankha. Panthawiyo, mneneli Eliya anawauza momveka bwino kuti asankhepo pakati pa kutumikila Yehova kapena kutumikila Baala, mulungu wonama. (1 Maf. 18:21) Eliya anadzudzula anthuwo cifukwa colephela kupanga cosankha. Mwina muganiza kuti cosankha cimeneci cinali cosavuta cifukwa nthawi zonse kutumikila Yehova ndiye cinthu canzelu komanso copindulitsa. Ndipo palibe munthu woganiza bwino amene anafunika kukopeka na Baala na kuyamba kum’tumikila. Ngakhale n’conco, Aisiraeli anali ‘kukayika-kayika.’ Koma Eliya anawalimbikitsa kuti asankhe kulambila Yehova, Mulungu woona.

ia 88 ¶15

Sanasunthike pa Kulambila Koona

15 Zitatelo ansembe a Baala anakhumudwa kwambili ndipo “anayamba kuitana mokuwa kwambili n’kumadziceka na mipeni na mikondo ing’onoing’ono malinga na mwambo wawo, mpaka magazi anayamba kutuluka ndi kuyendelela pamatupi awo.” Koma zonsezi sizinaphule kanthu cifukwa “sipanamveke mawu alionse. Palibe anawayankha kapena kuwamvela.” (1 Maf. 18:28, 29) Izi zinasonyeza kuti Baala anali mulungu wongopeka cabe, woti kunalibe. Satana ni amene anapangitsa anthuwo kuti aziganiza kuti kuli Baala n’colinga coti asiye kulambila Yehova. Koma zimene tiyenela kudziŵa n’zakuti, ngati tingasankhe mbuye wina osati Yehova, tidzagwilitsidwa mwala ndiponso tidzacita manyazi.—Ŵelengani Salimo 25:3; 115:4-8.

ia 90 ¶18

Sanasunthike pa Kulambila Koona

18 Eliya asanapemphele, anthuwo ayenela kuti anali kuganiza kuti Yehova nayenso sangathe kuyatsa moto. Koma zimene anthuwa anaona Eliya atangomaliza kupemphela, zinawapangitsa kuti asakayikenso. Nkhaniyi imati: “Atatelo, moto wa Yehova unatsika n’kunyeketsa nsembe yopseleza ija, nkhuni, miyala na fumbi lomwe. Unaumitsanso madzi amene anali m’ngalande muja.” (1 Maf. 18:38) Iyi inalidi yankho yotsiliza nthota. Koma kodi anthu anatani ataona zimenezi?

Kufufuza Cuma Cauzimu

w08 4/1 19, bokosi

Anali Wachelu Ndiponso Anadikila

Kodi Panadutsa Nthawi Yotalika Motani Kuti Cilala ca M’masiku a Eliya Cithe?

Eliya, mneneli wa Yehova anauza Mfumu Ahabu kuti cilala cimene cinatenga nthawi yaitali cinali citatsala pang’ono kutha. Eliya ananena zimenezi mu “caka cacitatu” kucokela panthawi imene iye analengeza kuti kudzakhala cilala. (1 Mafumu 18:1) Ndipo Yehova anavumbitsadi mvula, Eliya atangolengeza kumene kuti cilalaco citha. Conco anthu ena angaganize kuti cilalaco cinatha m’kati mwa caka cacitatu ndipo zimenezi zingaonetse kuti sicinathe zaka zitatu. Komabe, Yesu na Yakobo anati cilalaco cinatenga “zaka zitatu ndi miyezi 6.” (Luka 4:25; Yakobe 5:17) Kodi pamenepa Baibo ikudzitsutsa?

Ayi, siconco. Monga mmene mwaonela, ku Isiraeli nyengo ya dzuŵa inali yaitali ndithu mpaka miyezi 6. Mosakayikila, Eliya anafika kwa Ahabu m’nyengo ya dzuŵa kudzamuuza kuti kudzakhala cilala. Ndipo panthawiyi n’kuti cilala citayamba kale cifukwa nthawi imene nyengo ya dzuŵa inali kutha inali itapitilila. Ndipo zimenezi zikutanthauza kuti panali patapita pafupifupi miyezi 6 kucokela pamene cilalaco cinayamba. Conco, kucokela pamene Eliya analengeza kuti kudzakhala cilala kufikila nthawi imene analengeza kuti citha, panadutsa ‘zaka zitatu.’ Izi zikusonyeza kuti cilalaco cinatha zaka zitatu na hafu. Motelo, panthawi imene anthu anasonkhana ku phili la Karimeli kudzaonelela zocitika za pakati pa aneneli a Baala na Eliya, panali patadutsa “zaka zitatu ndi miyezi 6.”

Ganizilaninso nthawi yoyamba imene Eliya anapita kukaonana na Ahabu. Anthu anali kukhulupilila kuti Baala ndiye “woyendetsa mitambo,” mulungu amene anali kubweletsa mvula kuti nyengo ya dzuŵa ithe. Nyengo ya dzuŵa ikatalika kwambili, mwina anthu anali kufunsa kuti: ‘Kodi Baala ali kuti? Kodi adzabweletsa liti mvula?’ Koma zimene Eliya analengeza zoti sikudzagwa mvula ngakhale mame mpaka nthawi imene adzalengezanso kuti mvula igwe, ziyenela kuti zinakhumudwitsa kwambili anthu olambila Baala.—1 Mafumu 17:1.

OCTOBER 10-16

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 19-20

“Muziyang’ana kwa Yehova Kuti Mupeze Citonthozo”

w19.06 15 ¶5

Dalilani Yehova Pamene Muli na Nkhawa

5 Ŵelengani 1 Mafumu 19:1-4. Eliya anacita mantha pamene Mfumukazi Yezebeli anaopseza kuti adzamupha. Conco, iye anathaŵila ku Beere-seba. Eliya anavutika maganizo kwambili, cakuti “anayamba kupempha kuti afe” cabe. N’cifukwa ciani iye anataya mtima? Cifukwa cakuti anali “munthu monga ife tomwe.” (Yak. 5:17) Mwina anali na nkhawa kwambili, komanso analema ngako. Mwinanso anaganiza kuti zonse zimene anacita polimbikitsa kulambila koona, zinangopita pacabe cifukwa anthu sanasinthe. Anaganizanso kuti anangotsala yekha-yekha mtumiki wa Yehova. (1 Maf. 18:3, 4, 13; 19:10, 14) Mwina ife sitingamvetsetse kuti n’cifukwa ciani mneneli wokhulupilika ameneyu anafika pokhala na maganizo amenewa. Koma Yehova anali kudziŵa bwino mmene Eliya anali kumvelela.

ia 103 ¶13

Analimbikitsidwa na Mulungu Wake

13 Kodi muganiza kuti Yehova anamva bwanji pamene anayang’ana ali kumwambako n’kuona mneneli wake wokondedwa atagona m’cipululu pansi pa kamtengo akupempha kuti afe cabe? Kuti tidziŵe mmene Yehova anamvela, tiyeni tione zimene zinacitika. Eliya ali mtulo, Yehova anatumiza mngelo. Mngeloyo anamugwedeza Eliya pang’ono-pang’ono ndipo anamuuza kuti: “Dzuka udye.” Eliya anadzukadi ndipo anadya mkate wotentha ndiponso anamwa madzi amene mngeloyo anamubweletsela. Sitidziŵa ngati Eliya anathokoza mngeloyo cifukwa nkhaniyi imangofotokoza kuti mneneliyu anadya na kumwa kenako n’kugonanso. N’kutheka kuti Eliya sanathokoze cifukwa cakuti anali atakhumudwa kwambili moti sanafune kulankhula. Komabe patapita nthawi mngeloyo anadzutsanso Eliya ndipo mwina tsopano unali m’bandakuca. Apanso mngeloyo anauza Eliya kuti: “Dzuka udye,” ndipo anawonjezelanso kuti: “Popeza ulendowu wakukulila.”—1 Maf. 19:5-7.

ia 106 ¶21

Analimbikitsidwa na Mulungu Wake

21 Nkhaniyi imafotokoza kuti Yehova sanali mu zinthu zacilengedwe monga mphepo, civomezi ndiponso moto zimene Eliya anaona. Eliya anali kudziŵa kuti Yehova si mulungu wongoganizilidwa kuti alipo ngati mmene zinalili na Baala amene olambila ake anali kumutamanda kuti ni woyendetsa mitambo, kapena kuti wobweletsa mvula. Mphamvu zocititsa mantha zimene zili m’zinthu zosiyanasiyana zacilengedwe, zinacokela kwa Yehova. Koma iye ni wamkulu kwambili kuposa ciliconse cimene analenga. Ndipo ngakhale kumwamba kumene timaonaku, Yehova sangakwaneko. (1 Maf. 8:27) Ndiyeno kodi zimene Eliya anaonazi zinamuthandiza bwanji? Kumbukilani kuti Eliya anapezeka pamalo amenewa cifukwa cocita mantha. Popeza kuti Yehova Mulungu, yemwe ali na mphamvu zimenezi, anali kumbali ya Eliya, panalibe cifukwa cakuti iye aziopa Ahabu na Yezebeli.—Ŵelengani Salimo 118:6.

ia 106 ¶22

Analimbikitsidwa na Mulungu Wake

22 Moto uja utapita, pamalopo panakhala bata ndipo Eliya anamva “mawu acifatse apansi-pansi.” Mawuwo anali omupempha kuti anenenso zakukhosi kwake ndipo zimenezi zinacititsa kuti kaciŵilinso Eliya afotokoze zinthu zimene zinali kumudetsa nkhawa. Zimenezi ziyenela kuti zinamulimbikitsanso kwambili. Komanso mosakayikila, Eliya analimbikitsidwa kwambili na zimene “mawu acifatse apansi-pansi” aja anamuuza. Yehova anatsimikizila Eliya kuti ni munthu wofunika. Kodi anacita bwanji zimenezi? Mulungu anamuuza kuti nkhondo yothetsa kulambila Baala mu Isiraeli ipitilizabe. Ndiyetu apa n’zoonekelatu kuti nchito imene Eliya anagwila sinapite m’madzi cifukwa Mulungu anali akuyendetsabe zinthu kuti colinga cake cikwanilitsidwe. Komanso, Yehova anali kugwilitsabe nchito Eliya popeza anamupatsa malangizo omveka bwino n’kumuuza kuti abwelele akagwile nchito yomweyi.—1 Maf. 19:12-17.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w97 11/1 31 ¶2

Citsanzo ca Kudzimana na Kukhulupilika

Atumiki ambili a Mulungu lelolino amaonetsa mzimu wofananawo wodzimana. Ena asiya “minda” yawo na njila zawo zopezela ndalama, kuti akalalikile uthenga wabwino kumagawo akutali kapena kukatumikila monga mamembala a banja la Beteli. Ena apita ku maiko ena kukathandiza pa nchito yomanga ya gulu lathu. Ambili alandila zimene zingaoneke ngati nchito zapansi. Komabe, palibe kapolo wa Yehova amene akucita utumiki waung’ono. Yehova amayamikila onse amene amam’tumikila mofunitsitsa, ndipo adzadalitsa mzimu wawo wodzimana.—Maliko 10:29, 30.

OCTOBER 17-23

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MAFUMU 21-22

“Tengelani Citsanzo ca Mmene Yehova Amalamulila”

it-2 21

Yehova wa Makamu

Pamene Yoswa anaona mlendo amene anali mngelo pafupi na Yeriko na kum’funsa ngati anali kumbali ya Isiraeli kapena kumbali ya adani, mngeloyo anayankha kuti, “Iyai, koma ine pokhala kalonga wa gulu la nkhondo la Yehova, tsopano ndabwela.” (Yos. 5:13-15) Mneneli Mikaya anauza mfumu Ahabu na mfumu Yehosafati kuti, “Ndikuona Yehova atakhala pampando wake wacifumu, makamu onse akumwamba ataimilila kudzanja lake lamanja ndi kumanzele kwake.” N’zoonekelatu kuti iye anali kukamba za ana a Yehova auzimu. (1 Maf. 22:19-21) Mawu oculukitsa akuti “Yehova wa makamu” ni woyenelela, cifukwa Malemba amaonetsa kuti pali angelo osiyanasiyana, monga akerubi, aserafi, na angelo ena (Yes. 6:2, 3; Gen. 3:24; Chiv. 5:11) Malemba amaonetsanso kuti angelo ali m’magulu olinganizidwa mwadongosolo. Ndiye cifukwa cake Yesu Khristu anakamba kuti akanatha “kuitanitsa magulu ankhondo oposa 12 a angelo.” (Mat. 26:53) Pocondelela Yehova kuti amuthandize, Hezekiya anamuchula kuti “Yehova wa makamu, Mulungu wa Aisiraeli, wokhala pa akerubi.” Mwacionekele, iye anali kunena za likasa la pangano na zifanizo za akerubi, zimene zinali pa civindikilo ca likasa, zomwe zimaimila mpando wacifumu wa Yehova kumwamba. (Yes. 37:16; yelekezelani na 1 Sam. 4:4; 2 Sam. 6:2.) Pamene mtumiki wa Elisa anacita mantha poona kuti mzinda wawo wazingidwa na adani, analimbikitsidwa na masomphenya amene anaona. M’masomphenyawo, iye anaona kuti dela lonse la mapili lozungulila mzindawo, “linadzaza ndi mahachi ndi magaleta ankhondo oyaka moto,” zimene ni mbali ya gulu lankhondo la angelo a Yehova.—2 Maf. 6:15-17.

w21.02 4 ¶9

“Mutu wa Mwamuna Aliyense Ndi Khristu”

9 Kudzicepetsa. Yehova ni wanzelu kwambili kuposa wina aliyense. Ngakhale n’telo, amamvetsela malingalilo a atumiki ake. (Gen. 18: 23, 24, 32) Iye amalola amene ali pansi pa ulamulilo wake kupeleka malingalilo awo. (1 Maf. 22:19-22) Yehova ni wangwilo, koma sayembekezela kuti ife tizicita zinthu mwangwilo. M’malomwake, amathandiza anthu opanda ungwilo amene amam’tumikila kuti zinthu ziziwayendela bwino. (Sal. 113:6, 7) Ndipo Baibo imafotokoza Yehova kuti ni “mthandizi.” (Sal. 27:9; Aheb. 13:6) Mfumu Davide anazindikila kuti angakwanitse kugwila nchito yaikulu imene anapatsidwa, cabe cifukwa ca kudzicepetsa kwa Yehova.—2 Sam. 22:36.

it-2 245

Bodza

Yehova Mulungu amalola kuti anthu amene amakonda mabodza “anyengedwe” ndipo “azikhulupilila bodza,” mmalo mokhulupilila uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu. (2 Ates. 2:9-12) Citsanzo ca zimenezi ni zimene zinacitikila Mfumu Ahabu ya Isiraeli zaka mahandiledi ambili kumbuyoko. Aneneli onama anatsimikizila Ahabu kuti adzapambana pa nkhondo yolimbana na mzinda wa Ramoti-giliyadi. Koma mneneli wa Yehova Mikaya analosela za tsoka. Monga mmene Mikaya anaonela m’masomphenya, Yehova analola colengedwa cauzimu kukhala “mzimu wabodza” m’kamwa mwa aneneli a Ahabu. Izi zitanthauza kuti colengedwa cauzimu cimeneci cinagwilitsa nchito mphamvu zake pa aneneliwo kuti asalankhule zoona, koma kuti alankhule zimene iwo anafuna komanso zimene Ahabu anafuna kumva. Olo kuti anacenjezedwa, Ahabu anasankha kukhulupilila mabodza awo, ndipo anatailapo moyo wake.—1 Maf. 22:1-38; 2 Mbiri 18.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w21.10 3 ¶4-6

Kodi Kulapa Kwenikweni N’ciani?

4 Koma Yehova sanapitilize kuwalezela mtima. Anatuma Eliya kuti akauze Ahabu na Yezebeli mmene iye adzawalangila. Anati onse a m’banja lawo adzaphedwa. Mawu a Eliya amenewo anam’khudza kwambili Ahabu. Zodabwitsa n’zakuti munthu wonyada ameneyu ‘anadzicepetsa.’—1 Maf. 21:19-29.

5 Ngakhale kuti Ahabu anadzicepetsa pa nthawiyo, zimene anacita pambuyo pake zinaonetsa kuti sanalape kwenikweni. Iye sanathetse kulambila Baala mu ufumu wake. Komanso sanalimbikitse anthu kulambila Yehova. Palinso zina zimene Ahabu anacita zoonetsa kuti sanalape.

6 Patapita nthawi, Ahabu anapempha Yehosafati Mfumu yabwino ya Ayuda kuti akawathandize kukamenyana na Asiriya. Koma Yehosafati anati coyamba iwo afunsile kwa mneneli wa Yehova asanapite ku nkhondo. Poyamba, Ahabu anakana kucita zimenezo. Iye anati: “Pali munthu mmodzi amene tingathe kufunsila kwa Yehova kudzela mwa iye, koma ineyo ndimadana naye kwambili, cifukwa salosela zabwino zokhudza ine, koma zoipa.” Koma pambuyo pake, iwo anapitabe kukafunsila kwa mneneli Mikaya. Ahabu anakamba zoona, mneneliyo analoseladi zoipa zokhudza Ahabu! M’malo molapa na kupempha Yehova kuti amukhululukile, Ahabu anaponya mneneliyo m’ndende. (1 Maf. 22:7-9, 23, 27) Olo kuti mfumu yoipayi inaponya mneneli wa Yehova m’ndende, iyo sinalepheletse ulosiwo kukwanilitsika. Pankhondo yotsatila, Ahabu anaphedwa.—1 Maf. 22:34-38.

OCTOBER 24-30

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 1-2

“Citsanzo Cabwino pa Nkhani Yophunzitsa Ena”

w15 4/15 13 ¶15

Mmene Akulu Angathandizile Ena Kukhala Oyenelela Maudindo

15 Cocitika ca Elisa amene analoŵa m’malo Eliya cimaonetsanso mmene abale masiku ano angaonetsele ulemu kwa akulu amene atumikila kwa zaka zambili. Pambuyo pocezela aneneli a ku Yeriko, Eliya na Elisa anapita kumtsinje wa Yorodano. Atafika kumeneko, “Eliya anatenga covala cake cauneneli n’kucipinda. Atatelo anamenya naco madzi a mtsinjewo, ndipo pang’ono-pang’ono madzi onsewo anagaŵanika.” Atadutsa panthaka youma pakati pa mtsinje wa Yorodano, iwo anapitiliza ‘kuyenda akumalankhulana.’ N’zoonekelatu kuti Elisa sanaganize kuti tsopano wadziŵa zonse. Elisa anapitiliza kusunga zonse zimene mphunzitsi wake, Eliya, anamuuza mpaka pamene Eliyayo anacoka. Kenako Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho. Patapita nthawi, Elisa anabwelela ku mtsinje wa Yorodano ndipo anatenga covala cauneneli ca Eliya n’kumenya madzi a mtsinjewo, n’kunena kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?” Ndiyeno, madziwo anayambanso kugaŵanika.—2 Maf. 2:8-14.

w15 4/15 13 ¶16

Mmene Akulu Angathandizile Ena Kukhala Oyenelela Maudindo

16 Kodi mwaona kuti cozizwitsa comaliza cimene Eliya anacita ndiye cinali cozizwitsa coyamba cimene Elisa anacita? N’cifukwa ciani zimenezi n’zocititsa cidwi? Mwacionekele, Elisa sanadzimve kuti popeza kuti iye tsopano ndiye anali mtsogoleli anafunika kusintha zinthu mwamsanga. M’malomwake, iye anaonetsa ulemu kwa Eliya mwa kupitiliza kucita zinthu mmene Eliya anali kucitila, ndipo zimenezi zinathandiza kuti aneneli anzake ayambe kumudalila. (2 Maf. 2:15) Mkati mwa utumiki wake wa zaka 60 monga mneneli, Yehova anathandiza Elisa kucita zozizwitsa zambili kuposa zimene Eliya anacita. Kodi ophunzila masiku ano mukutengapo phunzilo lotani?

Kufufuza Cuma Cauzimu

w05 8/1 9 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Waciŵili

2:11—Kodi “kumwamba” kumene Eliya anakwela “mumphepo yamkuntho” ni kumwamba kuti? Kumeneku si kumalo kwinakwake m’miyambamu kotalikilana kwambili na dziko lapansi, ndiponso si kumalo auzimu amene Mulungu na ana ake aungelo amakhala. (Deuteronomo 4:19; Salimo 11:4; Mateyu 6:9; 18:10) “Kumwamba” kumene Eliya anapita ni mumlengalenga, osati kumwamba kwenikweni. (Salimo 78:26; Mateyu 6:26) Galeta la moto limene linatenga Eliya linayenda mumlengalenga n’kumupititsa ku mbali ina ya dziko lapansi, kumene anakakhala kwa kanthawi. Ndipotu patatha zaka zingapo, Eliya analemba kalata yopita kwa Yehoramu, mfumu ya Yuda.—2 Mbiri 21:1, 12-15.

OCTOBER 31–NOVEMBER 6

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 3-4

“Nyamulani Mwana Wanu”

w17.12 4 ¶7

“Ndidziŵa Kuti Adzauka”

7 Munthu waciŵili wochulidwa m’Malemba amene anaukitsidwa, anamuukitsa ni mneneli Elisa, amene analoŵa m’malo mwa Eliya. Mzimayi wina wodziŵika wa ku Sunemu waciisiraeli, anaceleza Elisa mwacikondi kwambili. Iye analibe mwana, koma kupitila mwa mneneli Elisa, Mulungu anadalitsa mzimayiyo na mwamuna wake wokalamba mwa kuwapatsa mwana. Koma patapita zaka, mwanayo anamwalila. Ganizilani cabe cisoni cimene mzimayiyo anakhala naco! Mwamuna wake atamulola, iye anayenda ulendo wa makilomita pafupifupi 30 kupita ku Phili la Karimeli, kumene kunali Elisa. Mneneliyo anatuma mtumiki wake Gehazi kuti atsogole kupita ku Sunemu. Gehazi analephela kuukitsa mwanayo. Ndiyeno, Elisa anafika pamodzi na amake a mwanayo.—2 Maf. 4:8-31.

w17.12 5 ¶8

“Ndidziŵa Kuti Adzauka”

8 Atafika ku Sunemu, Elisa analoŵa m’nyumba imene munali mtembowo, ndipo anakhala pa mbali pa mtembowo n’kuyamba kupemphela. Atacita izi, mwanayo anauka ndipo anam’peleka kwa amayi ake. Iwo anakondwela ngako! (Ŵelengani 2 Mafumu 4:32-37.) Mzimayiyo ayenela kuti anakumbukila pemphelo la Hana, mkazi amene poyamba anali wosabeleka. Pamene Hana anali kupeleka Samueli ku cihema kuti azitumikila Mulungu, anapemphela kuti: “Yehova . . . ndi Wotsitsila Kumanda, ndiponso Woukitsa.” (1 Sam. 2:6) Mogwilizana na mawu amenewa, Mulungu anaukitsa mnyamata wa ku Sunemu, kutsimikizila kuti alidi na mphamvu zoukitsa akufa.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2 697 ¶2

Mneneli

“Ana a Aneneli.” Monga mmene buku lakuti Gesenius’ Hebrew Grammar limafotokozela (Oxford, 1952, tsamba 418), liwu la Ciheberi lakuti ben (mwana wa) kapena benehʹ (ana a) lingatanthauze “munthu amene ali m’gulu linalake la anthu (kapena mtundu).” (Yelekezelani na Neh. 3:8, pamene mawu akuti “mmodzi wa opanga mafuta onunkhila” angamasulidwenso kuti “mwana wa opanga mafuta onunkhila.”) Conco tingati mawu akuti “ana a aneneli” amakamba za sukulu yopeleka malangizo kwa anthu amene anali kugwila nchito ya uneneli, kapena mwacidule gulu la aneneli. Baibo imakamba kuti magulu a aneneli amenewa anali kupezeka ku Beteli, ku Yeriko, na ku Giligala. (2 Maf. 2:3, 5; 4:38; yelekezelani na 1 Sam. 10:5, 10.) Samueli anali kutsogolela gulu la ku Rama (1 Sam. 19:19, 20). Ndipo cioneka kuti Elisa nayenso anakhalako pa udindo umenewu m’nthawi yake. (2 Maf. 4:38; 6:1-3; yelekezelani na 1 Maf. 18:13.) Malemba amakamba kuti ana a aneneli anali kumanga nyumba zawo-zawo, ndipo anali kugwilitsa nchito zida zina zobweleka, zimene zionetsa kuti anali kukhala umoyo wosalila zambili. Ngakhale kuti nthawi zambili anali kukhala pamodzi komanso anali kugaŵana zakudya, nthawi zina mneneli mmodzi payekha anali kutumizidwa kuti akacite nchito ya uneneli.—1 Maf. 20:35-42; 2 Maf. 4:1, 2, 39; 6:1-7; 9:1, 2.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani