Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Umoyo na Utumiki
NOVEMBER 7-13
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 5-6
“Ife Tili Ndi Ambili Kuposa Amene Ali Ndi Iwo”
it-1 716 ¶4
Elisa
Aisiraeli apulumutsidwa m’manja mwa Asiriya. Mu ulamulilo wa Mfumu Yehoramu ya Aisiraeli, Asiriya anafuna kuukila Aisiraeli modzidzimutsa. Kangapo konse mapulani a Benihadadi waciŵili analepheleka cifukwa ca Elisa. Elisayo anali kuulula zonse zimene Asiriya anali kufuna kucita. Poyamba, Benihadadi anali kuganiza kuti mu msasa wawo munali munthu wina amene anali kuulula mapulani awo kwa Aisiraeli. Koma atadziŵa zoona zake za nkhaniyi, iye anatuma asilikali ake okwela pa mahachi komanso magaleta ankhondo kuti akazungulile mzinda wa Dotana na kugwila Elisa. (CITHUNZI, Vol. 1, tsa. 950) Mtumiki wa Elisa atacita mantha, Elisa anapemphela kwa Mulungu kuti atsegule maso ake. Kenako, mtumikiyo anaona kuti dela lonse la mapili kuzungulila Elisa linadzadza ndi “mahachi ndi magaleta ankhondo oyaka moto.” Pamene asilikali a Asiriya anayandikila ku Dotana, Elisa anapempha Yehova kuti acite cozizwitsa cosiyana na cimene anapempha poyamba. Iye anapempha kuti: “Conde cititsani khungu mtundu uwu.” Pambuyo pake, Elisa anauza Asiriya kuti “nditsatileni,” koma powatsogolela iye sanacite kuwagwila dzanja, kuonetsa kuti anacita khungu la maganizo osati khungu la maso. Iwo sanamuzindikile Elisa munthu amene anabwela kudzamugwila. Ndipo sanazindikilenso kumene iye anali kuwapeleka.—2 Maf. 6:8-19.
w13 8/15 30 ¶2
Elisa Anaona Magaleta Oyaka Moto—Kodi Inunso Mukuwaona?
Elisa sanacite mantha pamene anazungulilidwa na adani ku Dotana. Iye sanaope cifukwa cakuti anali kukhulupilila kwambili Yehova. Ifenso tiyenela kukhulupilila Yehova na mtima wonse. Cotelo tizipempha mzimu woyela wa Mulungu kuti tikhale na cikhulupililo ndiponso makhalidwe ena amene mzimuwu umatulutsa.—Luka 11:13; Agal. 5:22, 23.
it-1 343 ¶1
Khungu
Khungu limene linakantha asilikali Asiriya limene Elisa anapemphelela, zioneka kuti linali khungu la maganizo. Cikanakhala kuti gulu lonse la asilikaliwo linakanthidwa na khungu la maso, ndiye kuti pakanafunika wina wowatsogolela mwa kuwagwila dzanja. Komabe, Baibo imangonena kuti Elisa anauza anthuwo kuti, “Njila yake si imeneyi ndipo mzinda wake si umenewu. Nditsatileni.” Ponena za cocitikaci, William James m’buku lake lakuti Principles of Psychology anati: “Mbali yocititsa cidwi kwambili ya matenda a ubongo ni khungu la maganizo. Sikuti munthu wodwala matendawa amaleka kuona, koma kungoti munthuyo samvetsa zimene akuonazo. Mwa njila ina tingakambe kuti ni kulephela kwa ubongo kupeleka tanthauzo pa zimene munthu akuona. Kapena kuti kusokonezeka kwa mgwilizano wa pakati pa maso na mbali zina za ubongo zimene zimathandiza munthu kuzindikila zimene akuona.” Mwacionekele ili ndilo khungu limene Yehova anacotsa asilikali acisiriya atafika ku Samariya. (2 Maf. 6:18-20) N’kutheka kuti anthu a ku Sodomu anavutika na mtundu umodzi-modziwo wa khungu la maganizo. Tikutelo cifukwa Baibo sionetsa kuti amunawo anali kudandaula cifukwa cakuti aleka kuona. Koma kuti anapitiliza kusakila khomo la nyumba ya Loti.—Ge 19:11.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 8/1 9 ¶2
Mfundo Zazikulu za M’buku la 2 Mafumu
5:15, 16—N’cifukwa ciyani Elisa anakana mphatso ya Namani? Elisa anakana mphatsoyo pozindikila kuti iye anacilitsa Namani mozizwitsa mwa mphamvu za Yehova, osati zake ayi. Iye sanacione ngati cinthu coyenelela kudyelelapo pa nchito imene Mulungu anam’patsa. Olambila oona masiku ano samafuna kudyelelapo pa nchito yotumikila Yehova. Iwo amamvela mawu a Yesu akuti: “Munalanala kwaulele, patsani kwaulele.”—Mateyu 10:8.
NOVEMBER 14-20
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 7-8
“Yehova Anapangitsa Zinthu Zooneka Zosatheka Kucitika”
it-1 716-717
Elisa
Komabe, patapita nthawi Benihadadi Waciŵili anaukilanso Samariya. Iye sanacite izi modzidzimutsa, koma anacita kuuzungulila mzindawo. Kuzungulilako kunabweletsa mavuto kwambili cakuti lipoti linafika kwa mfumu lakuti mayi wina wadya mwana wake. Pokhala mbadwa ya Ahabu, mfumu Yehoramu mwana wa munthu wopha anthu anacita kulumbila kuti adzapha Elisa. Ngakhale conco, lumbilo limenelo silinakwanilitsike. Atafika ku nyumba ya mneneli pamodzi na msilikali wake womuthandiza, Yehoramu ananena kuti wataya ciyembekezo cakuti Yehova akhoza kumuthandiza. Elisa anatsimikizila mfumuyo kuti tsiku lotsatila padzakhala cakudya ca mwana alilenji. Komabe, msilikali wothandiza mfumuyo anasuliza lonjezo limenelo, zimene zinapangitsa Elisa kumuuza kuti “uona zimenezi ndi maso ako, koma sudya nawo.” Tsiku lotsatila, Yehova anapangitsa Asiriya kumva phokoso lalikulu na kuyamba kuganiza kuti kukubwela cigulu ca nkhondo kudzawaukila. Zimenezi zinapangitsa kuti iwo athawe na kusiya zakudya zawo zonse m’misasa. Pamene mfumu inamva kuti Asiriya athaŵa m’misasa yawo, inaika msilikali womuthandiza kukhala mlonda pacipata ca Samariya. Ali pamenepo, iye anapondedwa-pondedwa na khamu la Aisiraeli la njala limene linali kuthamangila m’misasa kukafunkha zakudya. Iye anaciona cakudya koma sanadyeko.—2 Maf. 6:24–7:20.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 195 ¶7
Nyale
Mzela wa Mafumu a M’nyumba ya Davide. Yehova Mulungu anaika mfumu Davide pa mpando wacifumu wa Isiraeli. Motsogoleledwa na Mulungu, iye anakhala mtsogoleli wanzelu wa mtunduwo. Ndiye cifukwa cake anachedwa “nyale ya Isiraeli.” (2 Sam. 21:17) M’pangano lake la ufumu na Davide, Yehova analonjeza kuti, “Mpando wako wacifumu udzakhazikika mpaka kalekale.” (2 Sam. 7:11-16) Cotelo mzela wa mafumu a m’banja la Davide kupitila mwa mwana wake Solomo unakhala “nyale” ku mtundu wa Isiraeli.—1 Maf. 11:36; 15:4; 2 Maf. 8:19; 2 Mbiri 21:7.
NOVEMBER 21-27
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 9-10
“Anacita Zinthu Molimba Mtima, Modzipeleka, Komanso Mokangalika”
w11 11/15 3 ¶2
Yehu Anamenyela Nkhondo Kulambila Koyela
Yehu anadzozedwa kukhala mfumu ya Isiraeli pamene dzikolo linali loipa kwambili cifukwa ca munthu woipa Yezebeli. Pa nthawiyi, Ahabu, mwamuna wake, anali ataphedwa ndipo amene anali kulamulila anali mwana wake dzina lake Yehoramu. Yezebeli anali kulimbikitsa kulambila Baala m’malo molambila Yehova. Anapha aneneli a Mulungu ndiponso anasoceletsa anthu cifukwa ca “dama” lake na ‘zamatsenga.’ (2 Maf. 9:22; 1 Maf. 18:4, 13) Yehova analamula kuti anthu onse a m’nyumba ya Ahabu aphedwe, kuphatikizapo Yehoramu na Yezebeli. Mulungu anasankha Yehu kuti atsogolele ncito imeneyi.
w11 11/15 4 ¶2-3
Yehu Anamenyela Nkhondo Kulambila Koyela
Yehu anakana kuyankha ciliconse kwa anthu awili amene Yehoramu anawatuma. Kenako Mfumu Yehoramu inanyamuka limodzi na mfumu ya Yuda, Ahaziya. Aliyense ananyamuka pa galeta lake kukakumana na Yehu. Mfumu Yehoramu inamufunsa kuti: “Kodi ukubwelela zamtendele Yehu?” Ndipo Yehu anamuyankha kuti: “Mtendele ungakhalepo bwanji pali dama la Yezebeli mayi ako na amatsenga ake ambilimbili?” Yehoramu anacita mantha na yankho limeneli ndipo anayamba kuthawa. Koma mwamsangamsanga Yehu anakoka uta n’kubaya Yehoramu kumsana moti muviwo unatulukila pamtima pake. Yehoramu anagwela m’galeta lake n’kufela pamenepo. Ahaziya anathawa koma Yehu anamutsatila mpaka kumupeza n’kulamula kuti aphedwe.—2 Maf. 9:22-24, 27.
Munthu wina wa m’nyumba ya Ahabu amene anafunika kuphedwa anali Mfumukazi Yezebeli yomwe inali yoipa kwambili. Yehu ananena kuti iye anali ‘munthu wotembeleledwa.’ Yehu atafika ku Yezereeli anaona Yezebeli ataima pawindo la nyumba yacifumu akuyang’ana kunja. Nthawi yomweyo Yehu anauza nduna zina kuti zimuponye pansi kudzela pawindo. Zitamuponya, Yehu anam’pondaponda na mahaci ake munthu amene anaipitsa Isiraeliyu. Kenako Yehu anapitiliza kuwononga anthu ena a m’banja la Ahabu.—2 Maf. 9:30-34; 10:1-14.
w11 11/15 5 ¶3-4
Yehu Anamenyela Nkhondo Kulambila Koyela
N’zoona kuti Yehu anapha anthu ambili. Koma Malemba amanena kuti iye anali munthu wolimba mtima amene anamasula Aisiraeli mu ulamulilo wopondeleza wa Yezebeli na banja lake. Kuti wolamulila wa Isiraeli akwanitse kucita zimenezi, anayenela kukhala munthu wolimba mtima, wakhama komanso wosabwelela m’mbuyo. Buku lina lofotokoza Baibulo limati iye anagwila nchito ‘yovuta ndipo sanalekelele aliyense. Mwina akanacita zinthu mwacifatse sakanakwanitsa kuthetsa kulambila Baala mu Isiraeli.’
Apa tsopano mutha kuona kuti zinthu zina zimene Akhristu amakumana nazo masiku ano zimafuna kuti iwo asonyeze makhalidwe amene Yehu anali nawo. Mwacitsanzo, kodi tiyenela kutani ngati tikuyesedwa kuti ticite zinthu zimene Yehova amadana nazo? Tiyenela kukana mwamsanga, molimba mtima ndiponso mosanyengelela. Sitiyenela kulekelela zinthu pa nkhani zokhudza kudzipeleka kwathu kwa Yehova.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w11 11/15 5 ¶6-7
Yehu Anamenyela Nkhondo Kulambila Koyela
N’kutheka kuti Yehu anali kuganiza kuti popeza ufumu wa Isiraeli unali utagawikana na wa Yuda, ndiye kuti pafunika kuti asiyanenso pa nkhani ya kulambila. Ndiyeno mofanana na mafumu ena a Isiraeli, iye analimbikitsa kulambila ana a ng’ombe pofuna kuti akhalebe osiyana na ufumu wa Yuda. Apatu anasonyeza kuti sanali kukhulupilila kwambili Yehova, amene anamudzoza kuti akhale mfumu.
Yehova anayamikila Yehu cifukwa cakuti ‘anacita zoyenela pamaso pake.’ Komabe, Yehu “sanayesetse kuyenda motsatila malamulo a Yehova Mulungu wa Isiraeli na mtima wake wonse.” (2 Maf. 10:30, 31) Mukaganizila zimene anadzacita pamapeto ake poyelekezela na zonse zimene Yehu anacita kumbuyoku, mukhoza kudabwa ndiponso kumva cisoni. Koma zimene iye anacitazi zikutipatsa phunzilo. Ubwenzi wathu na Yehova sitiyenela kuuona mwacibwanabwana. Tsiku lililonse tiyenela kuyesetsa kukhala okhulupilika kwa Mulungu. Kuphunzila Baibo, kusinkhasinkha zimene taphunzila ndiponso kupemphela na mtima wonse kwa Atate wathu wakumwamba kungatithandize kucita zimenezi. Conco tiyeni tiyesetse kwambili kutsatila malamulo a Yehova na mtima wathu wonse.—1 Akor. 10:12.
NOVEMBER 28–DECEMBER 4
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 11-12
“Mayi Woipa Komanso Wofunitsitsa Ulamulilo Analangidwa”
it-1 209
Ataliya
Mofanana na mayi wake Yezebeli, Ataliya anasonkhezela mwamuna wake Yehoramu kucita zoipa pamaso pa Yehova pa zaka zonse 8 zimene analamulila. (1 Maf. 21:25; 2 Mbiri 21:4-6) Monga mayi ake, iyenso anakhetsa magazi ambili a anthu osalakwa. Pamene Ahaziya mwana wake woipa anamwalila atalamulila kwa caka cimodzi, Ataliya anapha ana onse a m’banja lacifumu, kupatulapo Yehoasi wakhanda. Iye anapulumuka pamene anakabisidwa mkati mwa nyumba ya Yehova, na mkulu wa ansembe komanso mkazi wake Yehosabati. Yehosabati anali mlongosi wake wa Ahaziya, bambo wa Yehoasi. Pambuyo pake Ataliya anadziika yekha kukhala mfumukazi, ndipo analamulila kwa zaka 6, ca m’ma 905-899 B.C.E. (2 Mbiri 22:11, 12) Ana ake anathyola nyumba ya Yehova n’kuba zinthu zopatulika na kukazipeleka kwa Abaala.—2 Mbiri 24:7.
it-1 209
Ataliya
Pamene Yehoasi anafika zaka 7, Mkulu wa Ansembe Yehoyada amene anali woopa Mulungu, anatulutsa mwanayo ku anthu na kumuika kukhala mfumu. Ataliya atamva phokoso kucokela ku kacisi, iye anathamangilako, ndipo atafika na kuona zimene zinali kucitika, anafuula kuti, “Mwandicitila ciwembu! Mwandicitila ciwembu!” Koma wansembe Yehoyada analamula kuti iye amutulutsile pabwalo pa kacisi, ndipo anapita kukamuphela pakhomo la nyumba ya mfumu lolowela mahachi. Mwacionekele, Ataliya ndiye anali wothela kuphedwa m’nyumba yoipa ya Ahabu. (2 Maf. 11:1-20; 2 Mbiri 22:1–23:21) Zoonadi, izi zinakwanilitsa mawu amene Yehova analankhula akuti: “Mawu onse a Yehova otsutsa nyumba ya Ahabu amene Yehova analankhula, adzakwanilitsidwa.”—2 Maf. 10:10, 11; 1 Maf. 21:20-24.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 1265-1266
Yehoasi
Komabe, panthawi yonse imene Mkulu wa Ansembe Yehoyada anakhala ngati tate komanso mlangizi wa Yehoasi, mfumu yacicepeleyo inacita zinthu mwanzelu. Atakwanitsa zaka 21 Yehoasi anakwatila akazi aŵili, ndipo mmodzi wa iwo anali Yehoyadani. Akaziwo anamubelekela ana aamuna na aakazi. Mwa njila imeneyi, mzele wa Davide wotsogolela kwa Mesiya umene unatsala pang’ono kuwonongedwa unakhalanso wolimba.—2 Maf. 12:1-3; 2 Mbiri 24:1-3; 25:1.
DECEMBER 5-11
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 13-15
“Kucita Zinthu na Mtima Wonse Kumabweletsa Madalitso”
w10 4/15 26 ¶11
Kodi Mukutsatila Khristu na Mtima Wonse?
11 Kuti timvetse kufunika kokhala acangu potumikila Mulungu, tiyeni tione zimene zinacitika pa moyo wa Mfumu Yehoasi ya Isiraeli. Iye anada nkhawa kuti mwina Aaramu agonjetsa Aisiraeli, conco anapita kwa Elisa akulila. Mneneliyu anamuuza kuti aponye muvi wake kumene kunali Siriya kudzela pa zenela, posonyeza kuti iwo adzagonjetsa mtunduwo mothanazidwa na Yehova. Zimenezi ziyenela kuti zinalimbikitsa mfumuyi. Kenako Elisa anauza Yehoasi kuti atenge mivi yake na kulasa pansi. Yehoasi anangolasa katatu kokha. Elisa anakwiya kwambili na zimenezi cifukwa cakuti akanalasa ka 5 kapena ka 6, ‘akanawapha Asiriya mpaka kuwatha.’ Conco, Yehoasi anangopambana katatu kokha cifukwa cakuti anacita zinthu mwaulesi. (2 Maf. 13:14-19) Kodi tikuphunzilapo ciyani pa nkhani imeneyi? Yehova adzatidalitsa kwambili ngati tigwila nchito yake mwakhama ndiponso na mtima wonse.
“Amapeleka Mphoto kwa Anthu Omufunafuna Ndi Mtima Wonse”
Kodi Yehova amapeleka mphoto kwa ndani? Paulo ananena kuti amapeleka mphoto “kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” Buku lina lomasulila Baibulo linanena kuti mawu acigiliki amene anawamasulila kuti “omufunafuna ndi mtima wonse” satanthauza ‘kungomufunafuna’ cabe, koma amatanthauza “kulambila Mulungu mwakhama.” Buku linanso limafotokoza kuti velebu lacigiliki limeneli, limanena za kucita zinthu mobweleza-bweleza kapena mwakhama. Conco, Yehova amapeleka mphoto kwa anthu amene amamulambila na mtima wonse.—Mateyu 22:37.
Kodi Yehova amapeleka bwanji mphoto kwa atumiki ake okhulupilika? Iye amawalonjeza mphoto ya mtengo wapatali imene imasonyeza kuti ni wacikondi komanso si woumila. Mphoto imeneyi ni moyo wosatha m’Paladaiso padziko lapansi. (Chivumbulutso 21:3, 4) Koma ngakhale pano, anthu amene amafunafuna Yehova na mtima wonse amadalitsidwa kwambili. Iwo amadalitsidwa na mzimu woyela komanso amakhala anzelu cifukwa cotsatila Mawu ake. Amakhalanso na moyo wabwino umene amakhutila nawo.—Salimo 144:15; Mateyu 5:3.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 8/1 11 ¶3
Mfundo Zazikulu za M’buku la 2 Mafumu
13:20, 21—Kodi cozizwitsa ca pa lembali cimasonyeza kuti kulambila zinthu zakale zopatulika sikulakwa? Ayi sicitelo. Baibo silisonyeza kuti mafupa a Elisa analambilidwapo. Mphamvu ya Mulungu ni imene inacititsa cozizwitsa cimeneci, ndipo ni imenenso inacititsa zozizwitsa zonse zimene Elisa anacita pamene anali na moyo.
DECEMBER 12-18
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 16-17
“Kuleza Mtima kwa Yehova Kuli na Malile”
it-2 908 ¶5
Salimanesere
Kupondelezedwa kwa Aisiraeli. Mu ulamulilo wa mfumu Hoshiya ya Aisiraeli (ca m’ma 758-740 B.C.E.), Salimanesere Wacisanu, anafutukula ulamulilo wake mpaka kufika ku Palestina. Zimenezi zinapangitsa kuti Hoshiya akhale pansi pa ulamulilo wake. Ndipo analamulidwa kuti azipeleka msonkho wa pacaka kwa iye. (2 Maf. 17:1-3) Komabe, patapita nthawi Hoshiya analephela kupeleka msonkhowo. Ndipo anapezeka kuti akucita ciwembu coukila mfumu Salimanesere, cifukwa cocita mgwilizano na mfumu So ya ku Iguputo. Kaamba ka izi, mfumu Salimanesere anaika Hoshiya m’ndende, ndipo anazungulila Samariya kwa zaka zitatu. Pambuyo pake, mzinda wolimba umenewo unagwa ndipo Aisiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo.—2 Maf. 17:4-6; 18:9-12; yelekezelani na Hos. 7:11; Ezek. 23:4-10.
it-1 414-415
Ukapolo
Maufumu onse aŵili a Aisiraeli, ufumu wa kumpoto wa mafuko 10, komanso ufumu wakumwela wa mafuko aŵili wa Yuda, cinacititsa kuti atengedwe kupita ku ukapolo cinali cimodzi. Onse anasiya kulambila Yehova na kuyamba kulambila milungu yonyenga. (De 28:15, 62-68; 2Ki 17:7-18; 21:10-15) Kumbali yake, Yehova anapitiliza kuwatumizila aneneli kuti akawacenjeze. Koma anthuwo sanamvele. (2Maf. 17:13) N’zomvetsa cisoni kuti pa mafumu onse amene analamulila mu ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli, palibe amene anakwanitsa kucotselatu kulambila konyenga kumene kunayambitsidwa na mfumu yoyamba ya ufumuwo, Yerobowamu. Ufumu wa kumwela wa Yuda unalephela kumvela macenjezo a Yehova osapita m’mbali, komanso anthu a mu ufumuwo sanatengepo phunzilo pa zimene zinacitikila ufumu wa kumpoto. (Yer. 3:6-10) Conco, anthu a m’maufumu onse aŵili anatengedwa kupita ku ukapolo. Sanatengedwe onse pa nthawi imodzi koma anatewatenga m’magulu-magulu pa nthawi zingapo zosiyana.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 847
Asamariya
Mawu akuti “Asamariya” amapezeka koyamba m’Malemba pambuyo pa kugonjetsedwa kwa ufumu wa mafuko 10 wa Samariya mu 740 B.C.E.; mawu amenewa anali kuwaseŵenzetsa pochula anthu amene anali kukhala mu ufumu wa kumpoto wa mafuko 10 usanagonjetsedwe, pofuna kuwasiyanitsa na anthu obwela ocokela m’mbali zosiyana-siyana za ufumu wa Asuri. (2 Maf. 17:29) N’zoonekelatu kuti Asuri sanatenge Asamariya onse kupita nawo ku ukapolo, cifukwa lemba la 2 Mbiri 34:6-9 (Yelekezelani na 2 Maf. 23:19, 20) limaonetsa kuti pamene Mfumu Yosiya anali kulamulila, ku Samariya kunali kukali Aisraeli. Patapita nthawi, mawu akuti Asamariya anayamba kugwilitsidwa nchito ponena za mbadwa za Aisiraeli a ku Samariya amene sanapite ku ukapolo, komanso aja amene anabweletsedwa na Asuri kucoka kumadela ena. Mwacionekele, ena mwa ana amenewo anabadwa pa ma ukwati amene anakhalapo pakati pa Aisiraeli na alendo. Patapita nthawi, mawu amenewa anali kugwilitsidwa nchito ponena za cipembedzo ca munthu, m’malo mwa mtundu kapena kudela kumene anali kucokela. Mawu amenewa anayamba kugwilitsidwa nchito ponena za anthu amene anali m’cipembedzo cina cake cimene cinali cofala m’dela la Sekemu na Samariya. Ndipo kalambilidwe kawo kanali kosiyana na ka Ayuda.—Yoh. 4:9.
DECEMBER 19-25
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 18-19
“Zimene Adani Athu Amacita Poyesa Kutifooketsa”
w05 8/1 11 ¶5
Mfundo Zazikulu za M’buku la 2 Mafumu
18:19-21, 25—Kodi Hezekiya anacita pangano na dziko la Igupto? Ayi. Apa kazembeyu ananena zabodza, ndipo ananamanso ponena kuti ‘analandila cilolezo ca Yehova,’ kapena kuti Yehova ndiye anamuuza kuti apite ku Yerusalemu. Hezekiya anali mfumu yokhulupilika ndipo anali kudalila Yehova yekha basi.
w10 7/15 13 ¶3
“Usaope Nidzakuthandiza”
Mocenjela, Rabisake anagwilitsa nchito mawu ocititsa anthu kukayikila. Iye anafunsa kuti, kodi Yehova sindiye amene Hezekiya “wamucotsela malo ake okwezeka na maguwa ake ansembe? . . . Yehova anati kwa ine, pita ukamenyane ndi dzikolo ndipo ukaliwononge.” (2 Maf. 18:22, 25) Apa Rabisake anali kutanthauza kuti Yehova sangamenyele nkhondo anthu ake cifukwa cakuti sakusangalala nawo. Koma izi sizinali zoona. Yehova anali kusangalala kwambili na Hezekiya ndiponso Ayuda amene anayambilanso kulambila koona.—2 Maf. 18:3-7.
w13 11/15 19 ¶14
Kodi Abusa 7 na Atsogoleli 8 Akuimila Ndani Masiku Ano?
14 Mfumu ya Asuri inamanga misasa ku Lakisi kum’mwela cakumadzulo kwa Yerusalemu. Ndiyeno inatumiza nthumwi zitatu kukauza anthu kuti angololela kuti agonja. Amene anali kulankhula anali na dzina laudindo lakuti Rabisake ndipo anayesa kuopseza Ayuda m’njila zosiyanasiyana. Iye analankhula mu Ciheberi ndipo analimbikitsa anthu kuti asiye kutsatila mfumu yawo n’kugonjela Asuri. Anawanamiza kuti adzapita nawo kudziko lina kumene anali kudzasangalala kwambili. (Welengani 2 Mafumu 18:31, 32.) Kenako Rabisake ananena kuti Yehova sadzatha kupulumutsa Ayuda kwa Asuri cifukwa milungu ina inalephela kuteteza anthu awo. Ayudawo anacita mwanzelu ndipo sanayankhe mabodzawo. Izi ni zimene atumiki a Yehova masiku ano amacitanso nthawi zambili.—Welengani 2 Mafumu 18:35, 36.
yb74 177 ¶1
Mbali 2—Germany
Nthawi zambili, asilikali acinsinsi a SS anali kuseŵenzetsa njila zamacenjela kwambili ponyengelela abale athu kuti asaine cikalata coonetsa kuti asiya kukhala a Mboni za Yehova. N’zocititsa cidwi kuti abale akasaina cikalataco, asilikaliwo anali kuwatembenukila na kuwazunza kwambili kuposa mmene anali kucitila poyamba. M’bale Karl Kirscht anatsimikizila mfundoyi pamene anati: “Pa anthu onse amene anali m’ndende zacibalo, Mboni za Yehova ndizo zinavutika kwambili na macenjela a asilikali a SS. Pocita zimenezi, asilikaliwo anali kuganiza kuti anganyengelele a Mboni za Yehova kuti asiye cikhulupililo cawo. Ndipo iwo anatipempha mobweleza-bweleza kusaina cikalataco. Ena anasaina, koma nthawi zambili anali kufunika kuyembekezela kwa nthawi yoposa caka cimodzi kuti atulutsidwe. Poyembekezela kutulutsidwa, abale amene asainawo anali kunyozedwa na asilikali a SS kuti anali acinyengo komanso amantha. Komanso asanatulutsidwe, anali kuwanyazitsa mwa kuwayendetsa pamaso pa abale ena amene sanasaine.”
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 155 ¶4
Kufukula za M’matongwe
Mwacitsanzo, Baibo imanena kuti Mfumu ya Asuri Senakeribu inaphedwa na ana ake aŵili, Adarameleki na Sarezere. Kenako mwana wake wina, Esari-hadoni, anayamba kulamulila. (2 Maf. 19:36, 37) Komabe, zolemba zacibabulo zionetsa kuti pa 20, m’mwezi wa Tebeti, pamene m’dziko la Asuri munali cipanduko, Senakeribu anaphedwa na mwana wake. Komanso, Belosusi, wansembe wacibabulo wa m’zaka za m’ma 200 B.C.E., na Nabonidasi, mfumu yacibabulo ya m’zaka za m’ma 500 B.C.E., onse aŵili anakamba kuti Senakeribu anaphedwa na mwana mmodzi cabe. Komabe, caposacedwapa ofukula za m’matongwe anafukula phale lochedwa Prism of Esar-haddon. Mu phale limenelo, Esari-Hadoni mwana amene analoŵa m’malo mwa Senakaribu ananena momveka bwino kuti abale ake anaukila na kupha atate awo, kenako anathawa. Pothilila ndemanga pa nkhani imeneyi, Philip Bibelfeld, amene analemba buku lakuti Universal Jewish History (1948, Vol. I, tsa. 27), ananena kuti: “M’zolemba zacibabulo, Nabonidasi na Belosusi, onse analakwitsa. Baibo yokha ni imene imafotokoza cocitikaci molondola. Phale la Esar-haddon linatsimikizila kuti zimene Baibo inakamba pa nkhaniyi ni zoona. Kafotokozedwe ka Baibo n’kolondola kwambili kuposa zolemba zacibabulo pa nkhani imeneyi yokhudza cocitika ca ku Asuri komanso ku Babulo. Mfundo imeneyi ni yofunika kwambili, makamaka pamene tisanthula zolembedwa zakale zimene zimasiyana na mmene Baibo imafotokozela zinthu.”
DECEMBER 26–JANUARY 1
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 20-21
“Pemphelo Linasonkhezela Yehova Kucitapo Kanthu”
ip-1 394 ¶23
Cikhulupililo ca Mfumu Cifupidwa
23 Panthaŵi imene Senakeribu akudzaukila Yuda kwa nthaŵi yoyamba, Hezekiya akudwala matenda akayakaya. Yesaya akumuuza kuti adzamwalila. (Yesaya 38:1) Mfumuyo ya zaka 39 ikusautsika mtima kwambili. Siikudela nkhaŵa moyo wake wokha koma ikudelanso nkhawa tsogolo la anthu ake. Yerusalemu na Yuda ali paciopsezo ca kugonjetsedwa na Asuri. Ngati Hezekiya amwalila, ati atsogolele nkhondoyo ndani? Panthaŵiyi, Hezekiya alibe mwana wamwamuna woti angapitilize ulamulilowo. M’pemphelo la mtima wonse, Hezekiya akucondelela Yehova kuti am’citile cifundo.—Yesaya 38:2, 3.
Tizitumikila Yehova na Mtima Wathunthu
16 Kenako Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa. Iye anacondelela Yehova kuti akumbukile zoti anali munthu wokhulupilika. (Welengani 2 Mafumu 20:1-3.) Tikudziwa kuti panopa sitingayembekezele Yehova kuticilitsa mozizwitsa kapena kutalikitsa moyo wathu. Komabe mofanana na Hezekiya tingathe kupemphela kwa Yehova kuti: ‘Kumbukilani kuti ninayenda pamaso panu mokhulupilika ndiponso na mtima wathunthu.’ Kodi inuyo mumakhulupilila kuti Yehova angathe kukuthandizani pamene mukudwala?—Sal. 41:3.
g01 7/22 13 ¶4
Kodi Pemphelo Linganithandize Bwanji?
M’nthawi zakale, Yehova anayankha mapemphelo a anthu ena ochulidwa m’Baibo mwa zozizwitsa. Mwacitsanzo, pamene Mfumu Hezekiya anadwala, anadziŵa kuti sadzacila matenda ake. Cotelo, anacondelela Mulungu kuti amucilitse. Mulungu anamuyankha kuti: “Ndamva pemphelo lako, ndipo ndaona misozi yako. Ndikucilitsa.” (2 Mafumu 20:1-6) Amuna na akazi ena oopa Mulungu, anayankhidwanso mapemphelo awo mwanjila imeneyi.—1 Samueli 1:1-20; Danieli 10:2-12; Machitidwe 4:24-31; 10:1-7.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 240 ¶1
Thabwa Lowongolela
Thabwa lowongolela lingagwilitsidwe nchito pamene munthu akumanga nyumba kuti aimange yowongoka. Lingagwilitsidwenso nchito pofuna kuona ngati nyumba imene inamangidwa kale iyenela kusungidwa kapena kuwonongedwa. Ponena za anthu osamvela a ku Yerusalemu, Yehova anati: “Ndidzayeza Yerusalemu ndi cingwe cimene ndinayezela Samariya, ndiponso ndidzamuyeza ndi thabwa lowongolela limene ndinayezela nyumba ya Ahabu.” Mulungu anali atayeza Samariya komanso nyumba ya mfumu Ahabu ndipo anawapeza kuti anali na makhalidwe oipa, zimene zinacititsa kuti iye awawononge. Mofananamo, Mulungu anali kudzaweluza Yerusalemu na olamulila ake poonetsa poyela makhalidwe awo oipa na kuwononga mzinda umenewo. Izi zinacitikadi m’caka ca 607 B.C.E. (2 Maf. 21:10-13; 10:11) Kupitila mwa mneneli Yesaya, Yehova anacenjeza olamulila odzikuza a ku Yerusalemu komanso anthu awo za tsoka limene linali kudzagwela mzinda wawo. Anawauza kuti: “Cilungamo ndidzacisandutsa cingwe ndipo ndidzacisandutsanso cipangizo cowongolela.” Miyezo ya cilungamo ceniceni inali kudzaonetsa poyela amene anali kutumikiladi Mulungu komanso amene sanali kum’tumikila. Izi n’zimene zinali kudzaonetsa anthu oyenela kupulumutsidwa kapena kuwonongedwa.—Yes. 28:14-19.