Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Umoyo na Utumiki
© 2022 Christian Congregation of Jehovah’s Witnesses
JANUARY 2-8
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 22-23
“N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kukhala Odzicepetsa?”
w00 9/15 29-30
Yosiya Wodzicepetsayo Anayanjidwa na Yehova
Kucokela m’mamaŵa, okonza kacisi ameneŵa akugwila nchito mwakhama. Ndithudi Yosiya akuthokoza Yehova kuti ogwila nchito akukonza mbali za nyumba ya Mulungu zimene makolo ake ena oipa anawononga. Nchito ili m’kati, Safani akubwela kudzamuuza zina zake. Nanga cimene wanyamulaco n’ciyani? Wanyamula mpukutu! Akufotokoza kuti Hilikiya Mkulu wa Ansembe wapeza “buku la cilamulo ca Yehova lopelekedwa ndi dzanja la Mose.” (2 Mbiri 34:12-18) Limene anapezalo mosakayikila linali buku lenileni la Cilamulo!
Yosiya akufunitsitsa kumva mawu onse a bukulo. Pamene Safani akuŵelenga, mfumuyo ikuyesetsa kuona mmene lamulo lililonse likugwilila nchito kwa iye ndi kwa anthu ake. Maka-maka akukondwela na mmene bukulo likufotokozela kwambili za kulambila koona na kunenelatu za milili na kucotsedwa m’dziko zimene zingadze ngati anthu adziloŵetsa m’cipembedzo conyenga. Podziŵa tsopano kuti malamulo ena a Mulungu sanatsatilidwe, Yosiya akung’amba covala cake nalamula Hilikiya, Safani, ndi ena kuti: ‘Mukafunse kwa Yehova zokhudza mawu a m’buku limene lapezekali, cifukwa mkwiyo wa Yehova umene watiyakila ndi waukulu, popeza makolo athu sanamvele mawu a m’buku ili.’—2 Mafumu 22:11-13; 2 Mbiri 34:19-21.
w00 9/15 30 ¶2
Yosiya Wodzicepetsayo Anayanjidwa na Yehova
Amithenga a Yosiya apita kwa Hulida mneneli wamkazi ku Yerusalemu ndipo abwelako ndi mawu. Hulida wawauza mawu a Yehova, kunena kuti masoka amene analembedwa m’buku limene langopezedwa kumenelo adzagweladi mtundu wopandukawo. Komabe, cifukwa ca kudzicepetsa kwake pamaso pa Yehova Mulungu, Yosiya sadzaona masokawo. Adzamugoneka pamodzi na makolo ake, ndipo adzaikidwa m’manda mu mtendele.—2 Mafumu 22:14-20; 2 Mbiri 34:22-28.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w01 4/15 26 ¶3-4
Mungacite Moyenela Ngakhale Sanakuleleni Bwino
Ngakhale kuti panacitika zoipa pa nthaŵi ya ubwana wake, Yosiya anacita zoyenela pamaso pa Yehova. Ulamulilo wake unali wopambana ndipo Baibo imati: “Panalibenso mfumu ina iye asanakhale mfumu imene inabwelela kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu zake zonse, mogwilizana ndi cilamulo conse ca Mose. Ngakhale pambuyo pake sipanakhalenso mfumu ina ngati iyeyo.”—2 Mafumu 23:19-25.
Zimene Yosiya anacita n’citsanzo colimbikitsa kwa amene anakumana na zoipa pa ubwana wawo. Kodi citsanzo cimeneci cingatiphunzitse ciyani? N’ciyani cinathandiza Yosiya kusankha njila yoyenela na kupitilizabe kuitsatila?
JANUARY 9-15
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 Mafumu 24–25
“Khalanibe Maso”
w01 2/15 12 ¶2
Tsiku la Yehova Lopeleka Ciweluzo Layandikila!
2 Mosakayikila, kulosela kwa Zefaniya kunacititsa Yosiya wacinyamatayo kuzindikila kwambili za kufunika kocotsa kulambila konyansa m’dziko la Yuda. Komabe, zimene mfumu inacita poyesetsa kufafaniza cipembedzo conyenga m’dzikolo sizinathetse kuipa konse pakati pa anthuwo kapena kufafaniza macimo a agogo ake aamuna, Mfumu Manase, amene “anadzaza Yerusalemu ndi magazi osalakwa.” (2 Mafumu 24:3, 4; 2 Mbiri 34:3) Cotelo, tsiku la Yehova lopeleka ciweluzo linali kudzafika ndithu.
w07 3/15 11 ¶10
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yeremiya
Caka ca 607 B.C.E., cinali caka ca 11 mu ulamulilo wa mfumu Zedekiya. Ndipo mfumu ya ku Babulo, Nebukadinezara inali itazinga Yerusalemu kwa miyezi 18 tsopano. Patsiku la 7 la mwezi wacisanu, m’caka ca 19 ca ulamulilo wa Nebukadinezara, mkulu wa asilikali oteteza mfumu dzina lake Nebuzaradani, “anabwela,” kapena kuti anafika ku Yerusalemu. (2 Mafumu 25:8) Mwina Nebuzaradani ankacokela ku misasa imene anamanga kunja kwa mpanda wa Yerusalemu, n’kumakazonda mzindawo kuti adziŵe mmene angaugonjetsele. Patangopita masiku atatu okha, patsiku la khumi la mweziwu, Nebuzaradani “anabwela,” kapena kuti analoŵa mu Yerusalemu, ndipo anatentha mzindawu na moto.—Yeremiya 52:12, 13.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 8/1 12 ¶1
Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Waciŵili
24:3, 4. Cifukwa coti Manase anali na mlandu wopha anthu, Yehova ‘sanalole kukhululukila’ Yuda. Mulungu amaona kuti mwazi wa anthu osalakwa ni ofunika. Tisamakayikile m’pang’ono pomwe kuti Yehova adzabwezela anthu okhetsa magazi wosalakwa powawononga.—Salmo 37:9-11; 145:20.
JANUARY 16-22
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 1–3
“Baibo—Buku Limene Limakamba Zenizeni Osati Nthano”
w09 9/1 14 ¶1
Kodi Adamu na Hava Anali Anthu Enieni?
Mwacitsanzo, onani ndandanda ya makolo aciyuda ochulidwa m’Baibo m’buku la 1 Mbiri caputala 1 mpaka 9, ndiponso Uthenga Wabwino wa m’buku la Luka caputala 3. Buku la 1 Mbiri limachula mwatsatanetsatane makolo a mibadwo 48 ndipo Luka amachula makolo a mibadwo 75. Buku la Luka limachula m’badwo wa makolo a Yesu Khristu, pomwe buku la 1 Mbiri limachula mibadwo ya ansembe a mtundu wa Isiraeli. Mabuku onsewa amachula maina a anthu odziŵika bwino monga Solomo, Davide, Yakobo, Isaki, Abulahamu ndi Nowa ndipo pomalizila pake amachula Adamu. Maina onse a m’mabuku amenewa ni a anthu enieni, ndipo Adamu anali munthu weniweni pa m’ndandanda uliwonse.
w08 6/1 3 ¶4
Cigumula ca Nowa, Cinacitikadi Kapena ni Nthano?
Nkhani ziŵili za m’Baibo zochula mzele wobadwila wa anthu, zimaonetsa kuti Nowa anali munthu weniweni. (1 Mbiri 1:4; Luka 3:36) Ezara na Luka, amene analemba nkhani zimenezi anali anthu odziŵa kufufuza bwino nkhani. Luka anafufuza na kupeza kuti Nowa anali m’gulu la makolo a Yesu Khristu.
w09 9/1 14-15
Kodi Adamu na Hava Anali Anthu Enieni?
Mwacitsanzo, taonani nkhani ya m’Baibo yokhudza dipo imene anthu ambili opemphela amaona kuti ni yofunika kwambili. Mawu akuti dipo amatanthauza kuti Yesu Khristu anapeleka moyo wake wangwilo monga nsembe yopulumutsa anthu ku ucimo. (Mateyo 20:28; Yohane 3:16) Monga tidziŵila, dipo ni mtengo wokwanila kuwombolela kapena kugulanso cinthu comwe cinatayika kapena kuwonongedwa. N’cifukwa cake Baibo limanena kuti Yesu ni “dipo lokwanila.” (1 Timoteyo 2:6) Koma tingafunse kuti, kodi ni dipo lolingana ni ciyani? Baibo limayankha kuti: “Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akorinto 15:22) Moyo wangwilo umene Yesu anapeleka kuti awombole anthu omvela unali wolingana na moyo wangwilo umene Adamu anataya pamene anacimwa m’munda wa Edene. (Aroma 5:12) Ndithudi, ngati Adamu sanali munthu weniweni, ndiye kuti nsembe ya dipo imene Khristu anapeleka ikanakhala yopanda tanthauzo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 911 ¶3-4
Mzele wa Mibadwo
Maina a Akazi. Nthawi zina, maina a akazi anali kulembedwa m’kaundula wa mibadwo pofuna kuti mbili isungike. Pa Genesis 11:29, 30, mwacionekele Sarai (Sara) anachulidwa cifukwa cakuti mbewu yolonjezedwa inali kudzabadwa kupitila mwa iye, osati kupitila mwa mkazi wina wa Abulahamu. Milika nayenso ayenela kuti anachulidwa pa lembali cifukwa cakuti anali ambuye ake a Rabeka, mkazi wa Isaki. Izi zinaonetsa kuti makolo a Rabeka anali pacibale na Abulahamu, cifukwa Isaki sanafunike kutenga mkazi kucokela ku mitundu ina. (Gen. 22:20-23; 24:2-4) Pa Genesis 25:1, pamachula Ketura mkazi amene Abulahamu anakwatila, Sara atamwalila. Izi zionetsa kuti Abulahamu anali akali na mphamvu zobeleka pambuyo pa zaka zoposa 40 Yehova atabwezeletsa mphamvuzo mozizwitsa. (Aroma 4:19; Gen. 24:67; 25:20) Zionetsanso ubale umene unalipo pakati pa Aisiraeli na Amidiyani komanso mitundu ina yaciarabu.
Malemba amachulanso Leya, Rakele, akazi aang’ono a Yakobo komanso ana amene anabeleka. (Gen. 35:21-26) Zimenezi zimatithandiza kumvetsa mmene Mulungu anacitila zinthu na anawo pambuyo pake. Maina a akazi enanso analembedwa m’kaundula wa mibadwo pa zifukwa zofanana na zimene tachula. N’kutheka kuti maina awo anali kulembedwa m’kaundula wa mibadwo ngati coloŵa calandilidwa kupitila mwa iwo. (Num. 26:33) Kuchulidwa kwa Tamara, Rahabi na Rute kunali kwapadela. Zocititsa cidwi pa akazi onsewa ni mmene anakhalila pa mzele wa makolo a Mesiya, Yesu Khristu. (Gen. 38; Rute 1:3-5; 4:13-15; Mat. 1:1-5) Malemba ena amene amachula akazi m’kaundula wa mibadwo ni 1 Mbiri 2:35, 48, 49; 3:1-3, 5.
JANUARY 23-29
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 4-6
“Kodi Mapemphelo Anga Amavumbula Ciyani za Ine?”
w10 10/1 23 ¶3-7
“Wakumva Pemphelo”
Yabezi anali munthu wokonda kupemphela. Iye anayamba pemphelo lake na kupempha madalitso kwa Mulungu. Kenako anapempha zinthu zitatu zimene zikusonyeza kuti iye anali na cikhulupililo colimba.
Poyamba, Yabezi anapempha Mulungu kuti: ‘Mukulitse dziko langa.’ (Vesi 10) Munthu wolemekezekayu sankalanda malo a anthu kapena kusilila zinthu za eni. N’kutheka kuti iye ankaganizila za anthu osati malo. Mwina ankapempha kuti dela lake likule mwamtendele n’colinga coti mukhale anthu ambili olambila Mulungu woona.
Caciŵili, Yabezi anapempha kuti “dzanja” la Mulungu likhale naye. Mawu ophiphilitsa akuti dzanja la Mulungu amatanthauza mphamvu zimene Mulungu amagwilitsa nchito pothandiza anthu amene amamulambila. (1 Mbiri 29:12) Kuti alandile zimene anapempha kucokela pansi pa mtima, Yabezi anadalila Mulungu yemwe dzanja lake silifupika kwa anthu amene amamukhulupilila.—Yesaya 59:1.
Cacitatu, Yabezi anapemphela kuti: ‘Munditeteze ku tsoka, kuti lisandivulaze.’ Mawu akuti, ‘kuti lisandivulaze’ akuonetsa kuti Yabezi sanapemphe kuti asakumane na tsoka koma kuti asade nkhawa kwambili na tsokalo kapena kugonja pokumana na zoipa.
Pemphelo la Yabezi limaonetsa kuti iye anali kuganizila kwambili za kulambila koona ndipo ankakhulupilila na kudalila Wakumva pemphelo. Kodi Yehova anamuyankha bwanji? Nkhani yaciduleyi imatha na mawu akuti: “Conco Mulungu anakwanilitsa zimene iye anapempha.”
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 10/1 9 ¶7
Mfundo Zazikulu za M’buku la 1 Mbiri
5:10, 18-22. M’masiku a Mfumu Sauli, mafuko amene anali kum’mawa kwa Yordano anagonjetsa Ahagala ngakhale kuti ciŵelengelo ca Ahagala cinali coculuka kuŵilikiza kaŵili pociyelekezela na ca mafukowa. Izi zinali conco cifukwa cakuti amuna amphamvu a mafuko amenewa anadalila Yehova kuwathandiza. Tiyeni tidalile Yehova na mtima wonse pamene tikupitiliza kumenya nkhondo yauzimu na adani omwe ali oculuka kutiposa.—Aefeso 6:10-17.
JANUARY 30–FEBRUARY 5
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 7-9
“Mungakwanitse Kucita Utumiki Wovuta na Thandizo la Yehova”
w05 10/1 9 ¶8
Mfundo Zazikulu za M’buku la 1 Mbiri
9:26, 27. Alevi oyang’anila zipata anali na udindo wofunika kwambili. Iwo anapatsidwa makiyi otsegulila malo opatulika osiyanasiyana a pakacisi. Anali okhulupilika potsegula zipata tsiku lililonse. Tapatsidwa udindo wofikila anthu m’gawo lathu na kuwathandiza kuyamba kupembedza Yehova. Kodi sitiyenela kukhala odalilika komanso okhulupilika monga mmene Alevi oyang’anila zipata anacitila?
w11 9/15 32 ¶7
Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi
Pinihasi anali na udindo waukulu mu Isiraeli wakale koma anathana na mavuto bwino-bwino cifukwa ca kulimba mtima, kumvetsa zinthu ndiponso kudalila Mulungu. Komanso zimene Pinihasi anacita posamalila mpingo wa Mulungu zinasangalatsa kwambili Yehova. Patapita zaka 1,000, Ezara anauzilidwa kulemba kuti: “Pinihasi mwana wa Eleazara ndiye anali mtsogoleli wawo kalekale, ndipo Yehova anali naye.” (1 Mbiri 9:20) Mawu amenewa ayenelanso kugwila nchito kwa amene amatsogolela anthu a Mulungu masiku ano komanso Akhristu onse amene amatumikila Mulungu mokhulupilika.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w10 12/15 21 ¶6
Imbilani Yehova!
6 Kudzela mwa aneneli ake, Yehova analamula kuti anthu amene amamulambila azimutamanda na nyimbo. Anthu oimba nyimbo ocokela m’fuko la ansembe sankaloledwa kugwila nchito zina zimene Alevi ena ankagwila n’colinga coti akhale na nthawi yokwanila yokonza nyimbo n’kuyesa kuziimba.—1 Mbiri 9:33.
FEBRUARY 6-12
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 10-12
“Kulitsani Cikhumbo Canu Cofuna Kucita Cifunilo ca Mulungu”
w12 11/15 6 ¶12-13
“Ndiphunzitseni Kucita Cifunilo Canu”
12 Davide anapeleka citsanzo cabwino pa nkhani yofunitsitsa kutsatila mfundo za m’Cilamulo. Mwacitsanzo, taganizilani zimene zinacitika Davide atanena kuti ankafunitsitsa kumwa “madzi a m’citsime ca ku Betelehemu.” Asilikali atatu a Davide anakaloŵa mwamphamvu mumzindawo, womwe pa nthawiyo unali utalandidwa na Afilisiti. Iwo anakatunga madzi m’citsimeco n’kubwela nawo. Koma “Davide anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapeleka kwa Yehova mwa kuwathila pansi.” N’cifukwa ciyani sanamwe? Iye anafotokoza kuti: “Sindingacite zimenezo cifukwa ndimalemekeza Mulungu wanga. Kodi ndimwe magazi a anthuwa omwe anaika moyo wawo paciswe? Iwowa akanataya moyo wawo pokatunga madziwa.”—1 Mbiri 11:15-19.
13 Davide anadziŵa kuti Cilamulo cimanena kuti magazi sayenela kudyedwa koma kupelekedwa kwa Yehova. Iye ankadziŵa kuti “moyo wa nyama [kapena munthu] uli m’magazi.” Komatu Davide anakana madzi osati magazi. Ndiye anakanilanji? Iye anakana cifukwa ankadziŵa mfundo ya m’lamulolo. Davide ankaona kuti madziwo anali amtengo wapatali ngati magazi a amuna atatuwa. Conco ankaona kuti n’kulakwa kwambili kumwa madziwo. Cotelo sanamwe koma anawathila pansi.—Lev. 17:11; Deut. 12:23, 24.
Lolani Kuti Malamulo a Mulungu Akuphunzitseni
5 Kuti tipindule na malamulo a Mulungu, tifunika kucita zambili osati cabe kuyaŵelenga kapena kuyadziŵa. Tifunika kumayakonda na kuyalemekeza. Mau a Mulungu amati: “Danani ndi coipa ndipo muzikonda cabwino.” (Amosi 5:15) Koma kodi tingacite bwanji zimenezi? Cofunika kwambili ni kuphunzila kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti imwe muli na vuto losoŵa tulo. Mutapita kucipatala, dokota wakupatsani malangizo okhudza kadyedwe, kucita maseŵela olimbitsa thupi, na kusintha zinthu zina mu umoyo wanu. Pambuyo potsatila malangizowo, mukuona kuti mwayamba kugona bwino tsopano. Mwacionekele, mungamuyamikile dokotayo cifukwa cokuthandizani kuthetsa vuto lanu.
6 Mofanana ndi zimenezi, Mlengi wathu watipatsa malamulo amene angatiteteze ku zotulukapo zoipa za ucimo na kutithandiza kukhala na umoyo wabwino. Ganizilani cabe mmene timapindulila cifukwa comvela malamulo a m’Baibo oletsa kunama, kucita cinyengo, kuba, ciwelewele, ciwawa, na zamizimu. (Ŵelengani Miyambo 6:16-19; Chiv. 21:8) Tikaona mapindu amene timapeza cifukwa comvela malamulo a Yehova, timayamba kukonda na kuyamikila kwambili Yehova na malamulo ake.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 1058 ¶5-6
Mtima
Kutumikila na “Mtima Wathunthu.” Mtima weniweni uyenela kukhala wathunthu kuti ugwile bwino nchito. Koma mtima wophiphilitsa ungakhale wogaŵanika. Davide anapemphela kuti: “Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu,” kuonetsa kuti mtima wa munthu ungakhale wogaŵanika pa zimene amakonda na kuopa. (Sal. 86:11) Munthu wotelo angakhale kuti mtima wake si wathunthu, kutanthauza kuti ni wofunda polambila Mulungu. (Sal. 119:113; Chiv. 3:16) Munthu angakhalenso na “mitima iŵili” (mawu ake eni-eni, kukhala na mtima na mtima winanso), kutanthauza kuti angamayese kutumikila ambuye aŵili kapena angamakambe zina uku akuganiza zina. (1 Mbiri 12:33; Sal. 12:2) Yesu anadzudzula mwamphamvu anthu a mitima iŵili otelo.—Mat. 15:7, 8.
Munthu amene afuna kukondweletsa Mulungu sayenela kukhala wa mitima iŵili, koma ayenela kum’tumikila na mtima wathunthu. (1 Mbiri 28:9) Kucita izi kumafuna kulimbikila cifukwa mtima ni wonyenga komanso umafuna kucita zoipa. (Yer. 17:9, 10; Gen. 8:21) Zimene zingatithandize kukhalabe na mtima wathunthu ni: kupemphela mocokela pansi pa mtima (Sal. 119:145; Maliro 3:41), kuŵelenga Mawu a Mulungu nthawi zonse (Ezara 7:10; Miy. 15:28), kulalikila uthenga wabwino mokangalika (yelekezelani na Yer. 20:9), komanso kugwilizana na anthu amene mitima yawo ni yathunthu kwa Yehova.—Yelekezelani na 2 Maf. 10:15, 16.
FEBRUARY 13-19
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 13-16
“Kutsatila Malangizo Kumacititsa Kuti Zinthu Zitiyendele Bwino”
w03 5/1 10-11
Kodi Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”
12 Likasa la cipangano litabwelela ku Israyeli ndipo litakhala zaka zambili ku Kiriyati-Yearimu, Mfumu Davide inafuna kusamutsila Likasalo ku Yerusalemu. Anakambilana na akulu amene anali kutsogolela anthu ndipo anawauza kuti Likasa lisamutsidwa ‘ngati akuona kuti ni bwino ndiponso ngati zili zovomelezeka kwa Yehova.’ Koma sanafufuze mokwanila kuti adziŵe maganizo a Yehova pankhaniyi. Akanakhala kuti anacita zimenezo, sibwenzi atanyamulila Likasalo pa galeta. Alevi Acikohati ndiwo akanalinyamula pa mapewa pawo, monga momwe Mulungu analangizila momveka bwino. Ngakhale kuti Davide nthawi zonse anali kufunsila kwa Yehova, analephela kucita zimenezo moyenela panthawi imeneyi. Zotsatila zake zinali zomvetsa cisoni zedi. Patapita nthaŵi Davide anavomeleza kuti: “Mkwiyo wa Yehova Mulungu wathu unatiphulikila, pakuti sitinatsatile malangizo ake monga mwa mwambo wathu.”—1 Mbiri 13:1-3; 15:11-13; Numeri 4:4-6, 15; 7:1-9.
w03 5/1 11 ¶13
Kodi Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”
13 Tsopano Alevi atasamutsa Likasa ku Obedi-Edomu kupita nalo ku Yerusalemu, anthu anaimba nyimbo imene Davide analemba. Ena mwa mawu a m’nyimboyo anali mawu ocokela pansi pamtima owakumbutsa, akuti: “Funafunani Yehova ndiponso mphamvu zake, funafunani nkhope yake nthawi zonse. Kumbukilani nchito zodabwitsa zimene wacita, kumbukilani zozizwitsa zake ndi zigamulo zotuluka m’kamwa mwake.”—1 Mbiri 16:11,12.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Lambilani Yehova, Mfumu Yamuyaya
14 Davide anabweletsa likasa lopatulika la pangano ku Yerusalemu. Pa cocitika capadela cimeneci, Alevi anaimba nyimbo yacitamando imene mbali yake ina timaiŵelenga pa 1 Mbiri 16:31, pamene pamati: “Anene pakati pa anthu a mitundu ina kuti: ‘Yehova wakhala mfumu!’” Koma mwina tingadzifunse kuti, ‘Kodi Yehova anakhala bwanji mfumu panthawiyo popeza kuti iye ni Mfumu yamuyaya?’ Yehova amakhala Mfumu mwa kucita zinthu zoonetsa kuti ali ndi ulamulilo kapena kugwilitsila nchito munthu wina kuti amuimile pocita zofuna zake. Kudziŵa mmene Yehova amakhalila mfumu n’kofunika kwambili. Davide asanafe, Yehova anam’lonjeza kuti ufumu wake udzakhala kosatha. Mulungu anati: “Ndidzautsa mbewu yako yobwela pambuyo pako, imene idzatuluka m’ciuno mwako. Ndipo ndidzakhazikitsadi ufumu wake.” (2 Sam. 7:12, 13) Pambuyo pa zaka zoposa 1,000, lonjezo limeneli linakwanilitsidwa pamene “mbewu” kapena kuti mwana wa Davide anaonekela. Kodi mwana ameneyu anali ndani ndipo ndi liti pamene anakhala Mfumu?
FEBRUARY 20-26
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 17-19
Khalanibe Acimwemwe Ngakhale Pamene Mwakumana na Zolefula”
w06 7/15 19 ¶1
Ganizilani za Ubwino wa Gulu la Yehova
DAVIDE wa ku Israyeli wakale ni mmodzi mwa anthu odziŵika kwambili ofotokozedwa m’Malemba Aciheberi. Munthuyu yemwe anali mbusa, woimba, mneneli ndi mfumu, ankakhulupilila kwambili Yehova Mulungu. Ubwenzi wolimba umene Davide anali nawo ndi Yehova unam’limbikitsa kukhala na cikhumbo cofuna kumangila Mulungu nyumba. Nyumba kapena kacisi ameneyu anadzakhala likulu la kulambila koona m’Israyeli. Davide ankadziŵa kuti kacisi ndiponso nchito yomwe inkacitika pakacisipo idzabweletsa cimwemwe na madalitso kwa anthu a Mulungu. Motelo, Davide anaimba kuti: “Wodala ndi munthu amene inu [Yehova] mwamusankha ndi kumuyandikizitsa kwa inu, kuti akhale m’mabwalo anu, tidzakhutila ndi zinthu zabwino za m’nyumba yanu, malo anu oyela kapena kuti kacisi wanu woyela.”—Salmo 65:4.
Muzikondwela na Mwayi Wanu wa Utumiki
11 Mofananamo, tingawonjezele cimwemwe cathu ngati tiikilapo mtima pa nchito iliyonse imene tingapatsidwe m’gulu la Yehova. Muzikhala ‘otangwanika kwambili’ na nchito yolalikila, komanso kutengako mbali mokwanila pa zocitika za pa mpingo. (Mac. 18:5; Aheb. 10:24, 25) Muzikonzekelanso bwino misonkhano kuti mukapelekepo ndemanga zolimbikitsa. Musamaione mopepuka mbali ya wophunzila imene angakupatseni pa misonkhano ya mkati mwa mlungu. Akakupemphani kugwila nchito inayake mu mpingo, osazengeleza ndipo khalani wodalilika. Musamatenge mopepuka nchito iliyonse imene mungapatsidwe, moti n’kungoicita mwa mwambo cabe. Muziyesetsa kukulitsa maluso anu. (Miy. 22:29) Mukamaikilapo mtima pa zinthu zauzimu komanso pa nchito zina, mudzapita patsogolo mofulumila, ndipo mudzakhala na cimwemwe cowilikiza. (Agal. 6:4) Cina, cidzakhala copepuka kukondwela na ena amene alandila utumiki umene inu munali kuufuna.—Aroma 12:15; Agal. 5:26.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w20.02 12, bokosi
Timam’konda Kwambili Atate Wathu Yehova
Kodi Yehova Amanionadi Kuti Ndine Wofunika?
Kodi munadzikayikilapo kuti, ‘Popeza pa dziko lapansi pali anthu mabiliyoni, kodi Yehova amanionadi kuti ndine wofunika?’ Ngati munadzikayikilapo, dziŵani kuti simuli nokha. Pali anthu ambili abwino-bwino amene amadzikayikila motelo. Mfumu Davide analemba kuti: “Inu Yehova, munthu ndani kuti mumuganizile? Kodi mwana wa munthu wocokela kufumbi ndani kuti mumuwelengele?” (Sal. 144:3) Davide sanakayikile kuti Yehova anali kum’dziŵa bwino. (1 Mbiri 17:16-18) Ndipo kupitila m’Mawu ake na gulu lake, Yehova amakutsimikizilani kuti amaona cikondi cimene mumaonetsa pom’tumikila. Onani mfundo zina za m’Mawu a Mulungu zimene zingakuthandizeni kukhulupilila zimenezi:
• Yehova anakudziŵani ngakhale musanabadwe.—Sal. 139:16.
• Yehova amadziŵa za mu mtima mwanu ndiponso zimene mumaganiza.—1 Mbiri 28:9.
• Yehova amamvetsela mapemphelo anu onse.—Sal. 65:2.
• Zimene mumacita zimam’khudza Yehova.—Miy. 27:11.
• Yehova anakukokelani kwa iye.—Yoh. 6:44.
• Yehova amakudziŵani bwino kwambili cakuti ngati mungamwalile, iye adzakwanitsa kukuukitsani. Adzapanganso thupi lanu monga mmene lilili, komanso adzabwezeletsa maganizo na umunthu wanu.—Yoh. 11:21-26, 39-44; Mac. 24:15
FEBRUARY 27–MARCH 5
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 20-22
“Thandizani Acinyamata Kuti Apambane”
‘Zimenezo Uziphunzitse kwa Amuna Okhulupilika’
8 Ŵelengani 1 Mbiri 22:5. N’kutheka kuti m’maso mwa Davide, Solomo anam’cepela kuti angayang’anile nchito yofunika kwambili imeneyo. Ndi iko komwe, kacisiyo anali “waulemelelo wosaneneka,” ndipo panthawiyo Solomo anali “wamng’ono komanso wosakhwima.” Koma kumbali ina, Davide anadziŵa kuti Yehova adzam’konzekeletsa Solomo kuti ayendetse bwino nchitoyo. Conco, Davide anaika mtima wake pa kuthandiza Solomo. Anam’thandiza kupeza zomangila zonse zofunikila.
‘Zimenezo Uziphunzitse kwa Amuna Okhulupilika’
7 Kodi Davide analeka kucilikiza nchitoyo, cifukwa cokwinyilila kuti citamando comanga kacisi sicidzabwela kwa iye? Iyai. N’zoona kuti cimangoco cinachedwa kuti kacisi wa Solomo, osati wa Davide. Ngakhale kuti mwina Davide anakhumudwa kuti sanakwanilitse cokhumba mtima wake, anacilikiza nchitoyo na mtima wonse. Iye analinganiza magulu a anchito, simbi, mkuwa, siliva, golide komanso mitengo. Kuonjezela apo, analimbikitsa Solomo kuti: “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe, ndipo zinthu zikuyendele bwino kuti umange nyumba ya Yehova Mulungu wako, monga mmene iye analankhulila za iwe.”—1 Mbiri 22:11, 14-16.
Makolo, Kodi Mukuthandiza Ana Anu Kupita Patsogolo Kuti Akabatizike?
14 Monga abusa auzimu, akulu mu mpingo angathandize makolo pa nchito yophunzitsa ana awo mwa kukamba ndi anawo za ubwino wokhala na zolinga zauzimu. Mlongo wina anafotokoza mmene mau a M’bale Charles T. Russell anam’khudzila. Pa nthawiyo, mlongoyo anali na zaka 6 cabe zakubadwa. Iye anati: “M’baleyo anakambilana nane kwa mamineti 15 pa nkhani ya zolinga zanga zauzimu.” Pambuyo pake, mlongoyo anatumikila monga mpainiya kwa zaka zoposa 70. Ndithudi, kukamba mau olimbikitsa kungakhale na zotulukapo zabwino na zokhalitsa. (Miy. 25:11) Akulu angapemphenso makolo pamodzi ndi ana awo kuti agwile nchito za pa Nyumba ya Ufumu, ndipo angapatse anawo nchito mogwilizana ndi msinkhu komanso luso lawo.
15 Abale na alongo mu mpingo angalimbikitse acicepele mwa kucita zinthu zoonetsa kuti amawaona kukhala ofunika. Izi zingaphatikizepo kukhala chelu akaona zizindikilo zakuti wacicepele akupita patsogolo mwauzimu. Kodi iye caposacedwa anapeleka ndemanga yabwino komanso yocokela pansi pa mtima? Kodi anali na mbali pa msonkhano wa mkati mwa wiki? Kodi anapilila ciyeso ca cikhulupililo cake kapena analalikila ku sukulu? Wacicepele akacita zinthu ngati zimenezi, musalephele kumuyamikila mocokela pansi pa mtima. Bwanji osakhala na colinga cakuti nthawi zonse, misonkhano isanayambe kapena ikatha, muzikambako na wacicepele mmodzi, pofuna kuonetsa kuti mumamuganizila? Ngati mucita zinthu monga zimenezi, acicepele adzayamba kudzimva kuti ali mbali ya “mpingo waukulu.”—Sal. 35:18.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 10/1 11 ¶6
Mfundo Zazikulu za M’buku La 1 Mbiri
21:13-15. Yehova analamula mngelo kuletsa mlili cifukwa cakuti Iye amakhudzidwa kwambili anthu Ake akamavutika. Ndithudi, “cifundo cake n’coculuka.”