LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr23 March masa. 1-10
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2023
  • Tumitu
  • MARCH 6-12
  • MARCH 13-19
  • MARCH 20-26
  • MARCH 27–APRIL 2
  • APRIL 10-16
  • APRIL 17-23
  • APRIL 24-30
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2023
mwbr23 March masa. 1-10

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

© 2022 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

MARCH 6-12

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 23-26

“Kulambila pa Kacisi Kunayamba Kucitika Mwadongosolo Kwambili”

it-2 241

Alevi

Nchito ya Alevi inayamba kucitika mwadongosolo kwambili m’nthawi ya ulamulilo wa Davide. Iye anaika oyang’anila nchito, akapitawo, oweluza, alonda a pazipata, komanso amsungacuma. Anasankhanso anthu ena ambili oti azithandiza ansembe pa kacisi, m’mabwalo a kacisi, komanso m’zipinda zodyelamo, pa nchito yopeleka nsembe, yoyeletsa zinthu zopatulika, yopima zinthu, na nchito zina za ulonda. Alevi oimba anagaŵidwa m’magulu 24, mofanana na magulu a ansembe, ndipo anali kutumikila mosinthana-sinthana. Powagaŵila nchito anali kucita maele. Nawonso magulu a alonda a pazipata anali kuwagaŵila nchito zawo mwa kucita maele.—1 Mbiri 23, 25, 26; 2 Mbiri 35:3-5, 10.

it-2 686

Wansembe

Ansembe otumikila pakacisi anagaŵidwa m’magulu-magulu, ndipo anali kuyang’anilidwa na akapitawo. Maele anali kugwilitsa nchito popatsa anthu nchito zinazake zoti azigwila. Gulu lililonse pa magulu 24 a ansembe linali kutumikila pa kacisi kwa mlungu umodzi, ndipo izi zinali kucitika kaŵili pacaka. N’zoonekelatu kuti pa nthawi ya zikondwelelo, ansembe onse anali kutumikila pakacisi cifukwa panthawiyo, anthu anali kupeleka nsembe masauzande, monga mmene anacitila pa nthawi yopatulila kacisi (1 Mbiri 24:1-18, 31; 2 Mbiri 5:11; yelekezelani na 2 Mbiri 29:31-35; 30:23-25; 35:10-19.) Wansembe anali na mwayi wokatumikila pa kacisi pa nthawi ina kuwonjezela pa nthawi yake yoikika, malinga ngati sakanasokoneza nchito za ansembe oikidwa kutumikila pa nthawiyo. Malinga na zolemba za arabi aciyuda, m’nthawi ya Yesu ansembe anali oculuka kwambili, moti nchito ya mlungu umodzi inagaŵidwa kuti izigwilidwa na mabanja osiyana-siyana a m’gulu limodzi la ansembe. Banja lililonse linali kukatumikila tsiku limodzi kapena angapo, malinga na kuculuka kwa mabanja a m’gululo.

it-2 451-452

Nyimbo

Pamene Davide anali kukonzekela kumangidwa kwa kacisi wa Yehova, anasankha alevi 4,000 kuti akhale oimba. (1 Mbiri 23:4, 5) Pa amenewa, okwana 288 anali “ophunzitsidwa kuimbila Yehova, onse akatswili.” (1 Mbiri 25:7) Gulu lonse la oimba linali kuyang’anilidwa na akatswili atatu oimba, Asafu, Hemani, na Yedutuni (mwacionekele wochedwanso Etani). Amuna amenewa anali mbadwa za ana atatu a Levi. Asafu anali mbadwa ya Gerisomu, Hemani anali mbadwa ya Kohati, ndipo Yedutuni anali mbadwa ya Merari. Conco, m’gulu la oimbalo munali anthu ocokela m’mabanja onse atatu akulu-akulu a fuko la Levi. (1 Mbiri 6:16, 31-33, 39-44; 25:1-6) Ana aamuna a Asafu, a Hemani, komanso a Yedutuni onse pamodzi analipo 24, ndipo onsewo anali m’gulu la akatswili oimba 288 amene tachula poyamba paja. Aliyense wa anawo anaikidwa kukhala mtsogoleli wa gulu limodzi la oimba mwa kucita maele. Ndipo pagulu limene anali kutsogolela, panali “akatswili” ena 11 osankhidwa pakati pa ana ake komanso Alevi ena. Conco, monga zinalili kwa ansembe, akatswili oimba 288 amenewo ([1 + 11] × 24 = 288) anagaŵidwa m’magulu 24. Tikacotsa akatswili 288 pa gulu lonse la oimba 4,000, pakutsala anthu “ophunzila” kuimba 3,712. Ngati ophunzilawo nawonso anagaŵidwa m’magulu 24, ndiye kuti pagulu lililonse la oimba, panali ophunzila 155. Izi zitanthauza kuti pa katswili mmodzi woimba, panali Alevi pafupfupi 13 oyenela kuwaphunzitsa. (1 Mbiri 25:1-31) Ciŵelengelo cimeneci ca Alevi oimba sicikuphatikizapo oimba malipenga, cifukwa oimba malipenga anali kukhala ansembe.—2 Mbiri 5:12; yelekezelani na Num. 10:8.

it-1 898

Mlonda wa pacipata

M’kacisi. Atatsala pang’ono kumwalila, Mfumu Davide analinganiza mwadongosolo kwambili nchito za Alevi na anthu ena otumikila pakacisi, kuphatikizapo alonda a pazipata, amene analipo 4,000. Alondawo anagaŵidwa m’magulu-magulu, ndipo gulu lililonse linali kutumikila masiku 7. Nchito yawo inali yolondela nyumba ya Yehova na kuonetsetsa kuti zitseko zake zikutsegulidwa na kutsekedwa pa nthawi yake. (1 Mbiri 9:23-27; 23:1-6) Kuphatikiza pa ulonda, ena anali kusamalila zopeleka zimene anthu anali kubweletsa pakacisi. (2 Maf. 12:9; 22:4) Patapita zaka, pamene Yehoyada mkulu wa ansembe anadzoza Yehoasi kukhala mfumu, alonda apadela anaikidwa pakacisi kuti ateteze Yehoasi wacicepeleyo kwa Mfumukazi Ataliya, amene anali atalanda ufumuwo. (2 Maf. 11:4-8) Komanso pamene Mfumu Yosiya anali kuthetsa kulambila mafano, alonda a pakhomo anathandiza kucotsa zinthu zogwilitsidwa nchito polambila Baala pakacisi. Kenako, zinthuzo anakazitentha kunja kwa kacisi.—2 Maf. 23:4.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w22.03 22 ¶10

Kulambila Koona Kudzawonjezela Cimwemwe Canu

10 Timalambila Yehova tikamaimba nyimbo za Ufumu. (Sal. 28:7) Aisiraeli anaona kuti kuimba nyimbo ni mbali yofunika kwambili pa kulambila kwawo. Mfumu Davide anasankha Alevi 288 kuti aziimba pa kacisi. (1 Mbiri 25:1, 6-8) Masiku ano, tingaonetse kuti timakonda Mulungu mwa kuimba nyimbo zacitamando. Kamvekedwe ka mawu athu si ndiko kofunika kwambili. Ganizilani izi: Tikamalankhula, “timapunthwa nthawi zambili.” Koma sitileka kukamba nkhani mu mpingo komanso kulalikila. (Yak. 3:2) Mofananamo, tisalole mamvekedwe a mawu athu kutilepheletsa kuimba nyimbo zotamanda Yehova.

MARCH 13-19

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 27–29

“Tate Apeleka Ulangizi Wacikondi kwa Mwana Wake”

w05 2/15 19 ¶9

Kuteteza Dzina Lathu Monga Akristu

9 Cidziŵeni bwino coonadi ca m’Baibo. Pang’ono na pang’ono tingaiwale kuti ndife atumiki a Yehova ngati utumiki wathuwo sukuyendela limodzi na kudziŵa bwino Malemba. (Afil. 1:9, 10) Mkhristu aliyense, kaya ni wacinyamata kapena wacikulile, ayenela kukhala na umboni woti iyeyo payekha azikhutila nawo woonetsa kuti zimene amakhulupilila zilidi coonadi ca m’Baibo. Paulo anapempha okhulupilila anzake kuti: “Tsimikizilani zinthu zonse. Gwilani mwamphamvu cimene cili cabwino.” (1 Ates. 5:21) Akhristu acinyamata omwe akucokela m’mabanja oopa Mulungu ayenela kuzindikila kuti iwowo sangakhale Akristu oona mwa kungodalila cikhulupililo ca makolo awo. Davide analimbikitsa Solomo, mwana wake weniweni kuti ‘am’dziŵe Mulungu wa atate wake, ndi kum’tumikila ndi mtima wangwilo.’ (1 Mbiri 28:9) Sizinali zokwanila kwa Solomo wacinyamatayo kumangoonelela mmene bambo akewo akulimbitsila cikhulupililo cawo mwa Yehova. Nayenso anafunika kum’dziŵa Yehova, ndipo anacitadi zimenezo. Iye anapempha Mulungu kuti: “Mundipatse nzelu ndi luntha lodziŵa zinthu kuti ndizitha kutsogolela anthuwa.”—2 Mbiri 1:10.

w12 4/15 16 ¶13

Pitilizani Kutumikila Yehova na Mtima Wathunthu

13 Kodi tikuphunzilapo ciyani? Zimakhala zosangalatsa tikamapezeka pa misonkhano ndiponso mu ulaliki nthawi zonse. Koma kutumikila Yehova na mtima wathunthu sikumangotanthauza zinthu zokhazo. (2 Mbiri 25:1, 2, 27) Ngati Mkhristu mumtima mwake amakondabe “zinthu za m’mbuyo,” kapena kuti zinthu zina za m’dzikoli, ubwenzi wake ndi Mulungu umakhala pa ngozi. (Luka 17:32) Tikhoza kukhala ‘oyenela ufumu wa Mulungu’ pokhapo ngati ‘timanyansidwa na coipa, n’kugwilitsitsa cabwino.’ (Aroma 12:9; Luka 9:62) Ngakhale kuti zinthu zina m’dziko la Satanali zingaoneke zothandiza kapena zosangalatsa, tiyenela kusamala kuti cinthu cina ciliconse cisatilepheletse kutumikila Yehova na mtima wonse.—2 Akor. 11:14; ŵelengani Afilipi 3:13, 14.

w17.09 32 ¶20-21

‘Limba Mtima, Ugwile Nchito Mwamphamvu’

20 Mfumu Davide anauza Solomo kuti Yehova adzakhala naye mpaka pamene adzatsiliza kugwila nchito yomanga kacisi. (1 Mbiri 28:20) Zimene atate wake anakamba zinam’limbikitsa kwambili Solomo, ndipo anakwanitsa kugwila nchitoyo ngakhale kuti anali wamng’ono komanso wosakhwima. Iye anacita zinthu molimba mtima, anagwila nchito mwamphamvu, ndipo mothandizidwa na Yehova, anatsiliza nchito yomanga kacisi waulemeleloyo m’zaka 7 na hafu.

21 Monga mmene Yehova anathandizila Solomo, nafenso akhoza kutithandiza kukhala olimba mtima komanso kugwila nchito yathu m’banja na mumpingo. (Yes. 41:10, 13) Tikamacita zinthu molimba mtima polambila Yehova, tingakhale na cidalilo cakuti tidzapeza madalitso tsopano na m’tsogolo. Conco, ‘limbani mtima, ndipo mugwile nchito mwamphamvu.’

Kufufuza Cuma Cauzimu

w17.03 29 ¶6-7

Kukhalabe Bwenzi Pakacitika Zinthu Zimene Zingasokoneze Ubwenzi

Davide analinso na anzake ena okhulupilika amene anakhala kumbali yake panthawi yovuta. Mmodzi wa anzakewo anali Husai, amene Baibo limati anali “mnzake wa Davide.” (2 Sam. 16:16; 1 Mbiri 27:33) Iye ayenela kuti anali nduna ya panyumba ya mfumu komanso mnzake wa mfumuyo. Anali kum’tumanso pa nkhani zina zacinsinsi.

Pamene Abisalomu analanda ufumu Davide bambo ake, Aisiraeli ambili anakhala kumbali ya Abisalomu. Koma Husai sanatelo. Panthawi imene Davide anali kuthaŵa, Husai anapita kwa iye. Davide anakhumudwa kwambili cifukwa ca kusakhulupilika kwa mwana wake komanso anthu ena amene anali kuwadalila. Koma Husai anakhalabe wokhulupilika ndipo anali wokonzeka kuika moyo wake paciopsezo kuti alepheletse ciwembu cimene Abisalomu anakonza. Husai sanangocita zimenezo n’colinga cakuti akwanilitse udindo wake monga nduna ya panyumba ya mfumu, koma cifukwa anali mnzake wokhulupilika wa Davide.—2 Sam. 15:13-17, 32-37; 16:15–17:16.

MARCH 20-26

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 1-4

“Mfumu Solomo Anapanga Cisankho Colakwika”

it-1 174 ¶5

Gulu lankhondo

Pamene Solomo anayamba kulamulila, gulu lankhondo la Isiraeli linasintha kwambili. Ngakhale kuti panthawi ya ulamulilo wake kunaliko mtendele, Solomo anasonkhanitsa mahosi oculuka na magaleta. Ambili mwa mahosi amenewo anali kuwagula ku Iguputo. Ndipo anamanga mizinda yosungilako zinthu zimenezo. (1 Maf. 4:26; 9:19; 10:26, 29; 2 Mbiri 1:14-17) Koma Yehova sanadalitse mapulani amenewa a Solomo, moti atamwalila komanso ufumuwo utagaŵikana, gulu lankhondo la Isiraeli linacepa. Patapita zaka, mneneli Yesaya analemba kuti: “Tsoka kwa anthu amene akupita ku Iguputo kukapempha thandizo. Iwo akudalila mahachi wamba ndi kukhulupilila magaleta ankhondo, cifukwa cakuti ndi ambili. Akudalilanso mahachi akuluakulu cifukwa cakuti ndi amphamvu kwambili, koma sanayang’ane kwa Woyela wa Isiraeli ndipo sanafunefune Yehova.”—Yes. 31:1.

it-1 427

Galeta

Solomo asanayambe kulamulila, mu Isiraeli munalibe gulu lalikulu lankhondo la amuna oyenda pa magaleta. Cacikulu cinacititsa zimenezi n’cakuti Mulungu anacenjeza mafumu a Isiraeli kuti asadziculukitsile mahosi, cifukwa citetezo ca mtunduwo sicinali kudalila mahosi. Conco Aisiraeli sanali kugwilitsa nchito kwambili magaleta, cifukwa magaleta anali kufunikila mahosi kuti ayende. (Deut. 17:16) Samueli pocenjeza Aisiraeli kuti mfumu yaumunthu idzawapondeleza, anati: “Idzatenga ana anu kuti azikayenda m’magaleta ake.” (1 Sam. 8:11) Pamene Abisalomu na Adoniya anayesa kulanda ufumu, aliyense wa iwo anadzipangila galeta na kusankha amuna 50 kuti azithamanga patsogolo pa galeta lake. (2 Sam. 15:1; 1 Maf. 1:5) Davide atagonjetsa mfumu ya ku Zoba, anasungako mahosi a magaleta 100 amene analanda.—2 Sam. 8:3, 4; 10:18.

Pokulitsa gulu lankhondo la Isiraeli, mfumu Solomo anaculukitsa magaleta mpaka anakwana 1,400. (1 Maf. 10:26, 29; 2 Mbiri 1:14, 17) Kuwonjezela pa mzinda wa Yerusalemu, matauni ena ochedwa mizinda ya magaleta anali na malo apadela osungilako na kusamalilako mahosi na magaleta ankhondo amenewo.—1 Maf. 9:19, 22; 2 Mbiri 8:6, 9; 9:25.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w05 12/1 19 ¶6

Mfundo Zazikulu za M’buku Laciŵili la Mbiri

1:11, 12. Pempho la Solomo linasonyeza Yehova kuti zimene mfumuyo inafuna kwambili mu mtima mwake ni kupeza nzelu na kudziŵa zinthu. Inde, mapemphelo athu kwa Mulungu amavumbula zimene mtima wathu umakonda. Ndiye ni bwino kuganizila mofatsa za zimene timanena m’mapemphelo athuwo.

MARCH 27–APRIL 2

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 5-7

“Mtima Wanga Udzakhala Pamenepa Nthawi Zonse”

w02 11/15 5 ¶1

Osaleka Kusonkhana Pamodzi

Pambuyo pake, Davide atakhala mfumu mu Yerusalemu, anasonyeza kuti anali wofunitsitsa na mtima wonse kumanga nyumba yoti ilemekeze Yehova. Koma popeza Davide anali munthu wankhondo, Yehova anamuuza kuti: “Sungamange nyumba ya dzina langa.” M’malo mwake, Yehova anasankha mwana wake Solomo kuti amange kacisi. (1 Mbiri 22:6-10) Solomo anapatulila kacisi ameneyu mu 1026 B.C.E., atamaliza nchito yomanga imene inatenga zaka zisanu na ziŵili na theka. Yehova anavomeleza nyumba imeneyi mwa kunena kuti: “Ndayeletsa nyumba imene wamangayi mwa kuikapo dzina langa mpaka kalekale, ndipo maso anga ndi mtima wanga adzakhala pamenepo nthawi zonse.” (1 Mafumu 9:3) Yehova akanabweletsa madalitso pa nyumba imeneyo ngati Aisrayeli akanakhalabe okhulupilika. Koma ngati akanasiya kucita zabwino, Yehova sakanayanjanso malo amenewo, ndipo nyumbayo ikanakhala bwinja.—1 Maf. 9:4-9; 2 Mbiri 7: 16, 19, 20.

it-2 1077-1078

Kacisi

Mbili yake. Kacisi ameneyu anakhalapo mpaka mu 607 B.C.E., pamene anawonongedwa na asilikali a Babulo mu ulamulilo wa mfumu Nebukadinezara. (2 Maf. 25:9; 2 Mbiri 36:19; Yer. 52:13) Cifukwa cakuti Aisiraeli anayamba kulambila mafano, Mulungu analola mitundu ina kusautsa Yuda na Yerusalemu, cakuti nthawi zina adani anali kutenga cuma ca m’kacisi. Komanso nthawi zina kacisi anali kusoŵa cisamalilo. Mfumu Sisaki ya Iguputo inatenga zinthu zamtengo wapatali za m’kacisi (mu 993 B.C.E.) m’masiku a mfumu Rehobowamu mwana wa Solomo, apa n’kuti pangopita zaka 33 kucokela pamene anapatulila kacisiyo. (1 Maf. 14:25, 26; 2 Mbiri 12:9) Mfumu Asa (977-937 B.C.E.) anali kulemekeza nyumba ya Yehova. Koma pofuna kuteteza Yerusalemu, iye anacita zinthu mopanda nzelu mwa kutenga siliva na golide wa m’kacisi na kuupeleka kwa mfumu Beni-hadadi I ya Siriya pomunyengelela kuti athetse pangano lake na Basa, mfumu ya Isiraeli.—1 Maf. 15:18, 19; 2 Mbiri 15:17, 18; 16:2, 3.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w10 12/1 11 ¶7

Iye Amadziŵa Bwino “Mtima wa Ana a Anthu”

Pemphelo la Solomo limeneli ni lolimbikitsa kwambili. Nthawi zina anthu anzathu sangamvetse ‘mlili ndi ululu wathu’ kapena kuti mmene tikumvela mumtima mwathu. (Miy. 14:10) Koma Yehova amadziŵa mitima yathu ndipo amatidela nkhawa kwambili. Kupemphela kwa iye mocokela pansi pa mtima kungatithandize kupilila mavuto amene tikukumana nawo. Baibo imati: ‘Mum’tulile nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’—1 Pet. 5:7.

APRIL 10-16

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 8-9

Anaona Nzelu Kukhala Zofunika Kwambili

w99 11/1 20 ¶4

Pamene Ambili Akhala Ooloŵa Manja

Inde, mfumu yaikazi ya ku Sheba inathelanso nthaŵi yaitali ndipo inayesetsa kwambili kuti ikacezele Solomo. Mwacionekele, Sheba anali m’dela la dziko lamakono la Republic of Yemen; cotelo mfumuyo na ngamila zake zambili anayenda ulendo wa makilomita 1,600 kupita ku Yerusalemu. Monga mmene Yesu ananenela, “imeneyi inabwela kucokela kumalekezelo a dziko lapansi.” Kodi mfumu yaikazi ya ku Sheba inadzivutilanji conco? Inangobwela “kudzamva nzelu za Solomo.”—Luka 11:31.

w99 7/1 30 ¶4-5

Ulendo Umene Unali Wopindulitsa Kwambili

Mulimonse mmene zinalili, mfumukaziyo inafika ku Yerusalemu “ndi anthu ambili oipelekeza. Inabwela ndi ngamila zitanyamula mafuta a basamu, golide wambili, ndi miyala yamtengo wapatali.” (1 Maf. 10:2a) Ena amati “anthu ambili oipelekeza” amenewo anaphatikizapo anthu onyamula zida. Izi zingakhale zomveka, popeza kuti mfumukazi inali munthu wolemekezeka kwambili ndipo inali kuyenda na katundu wamtengo wapatali wa ndalama mamiliyoni ambili zedi.

Komabe, onani kuti mfumukazi inamva mbili ya Solomo “ndi zoti anachuka cifukwa ca dzina la Yehova.” Conco uwu sunali ulendo wokacita malonda. Mwacionekele, mfumukaziyi kwenikweni inapita kuti ikamve nzelu za Solomo—mwinanso kukaphunzila zina za Mulungu wake, Yehova. Popeza iyenela kuti inali mbadwa ya Semu kapena Hamu, amene anali alambili a Yehova, iyenela kuti inali yacidwi na cipembedzo ca makolo ake.

w99 7/1 30-31

Ulendo Umene Unali Wopindulitsa Kwambili

Mfumukazi ya ku Sheba inacita cidwi na nzelu za Solomo komanso ulemelelo wa ufumu wake kotelo kuti “inazizila nkhongono.” (1 Maf. 10:4, 5) Ena amati mawu amenewa amatanthauza kuti mfumukaziyo “inabanika.” Katswili wina wa maphunzilo mpakana ananena kuti mwinamwake inakomoka! Zilizonse zimene zinacitikazo, mfumukaziyo inadabwa na zimene inaona na kumva. Inacha anyamata a Solomo kukhala odala popeza anali kumva nzelu za mfumu imeneyi, ndipo inayamika Yehova cifukwa copatsa Solomo ufumu. Kenako mfumukaziyo inapeleka kwa mfumuyo mphatso zamtengo wapamwamba, golide yekha wokwana ndalama pafupifupi $40,000,000 malinga na ndalama za masiku ano. Nayenso Solomo anapeleka mphatso, anapatsa mfumukaziyo “zofuna zake zonse zimene inapempha.”—1 Maf. 10:6-13.

it-2 990-991

Solomo

Mfumukazi ya ku Sheba itaona ulemelelo wa kacisi, wa nyumba ya Solomo, cakudya ca patebulo pake na zakumwa, mmene atumiki ake opelekela zakudya anali kucitila, zovala zawo, komanso nsembe zopseleza zimene anali kupeleka panyumba ya Yehova nthawi zonse, inazizila m’nkhongono ndipo inati, “ndaona kuti ndinangouzidwa hafu cabe ya nzelu zanu zoculuka. Mwaposa zinthu zimene ndinamva.” Kenako mfumukaziyo inakamba kuti ni odala anthu amene anali kutumikila mfumu Solomo. Mfumukaziyo itaona zonsezi inatamanda Yehova Mulungu na kum’dalitsa, cifukwa anakonda Isiraeli mwa kuika Solomo kukhala mfumu kuti azipeleka zigamulo na kucita cilungamo.—1 Maf. 10:4-9; 2 Mbiri 9:3-8.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2 1097

Mpando wacifumu

Mpando wacifumu wa Solomo ni mpando wokhawo wa mafumu a Isiraeli umene umafotokozedwa mwatsatanetsatane. (1 Maf. 10:18-20; 2 Mbiri 9:17-19) Cioneka kuti mpandowo unali kukhala “m’Bwalo la Mpando Wacifumu,” imodzi mwa nyumba zimene zinamangidwa pa Phiri la Moriya ku Yerusalemu. (1 Maf. 7:7) Unali ‘mpando waukulu wacifumu wa minyanga ya njovu, wokutidwa na golide woyengedwa bwino ndipo kuseli kwake kunali cochingila cozungulila komanso moika manja mbali zonse ziŵili.’ Ngakhale kuti minyanga ya njobu inagwilitsidwa kwambili popanga mpandowo, tikaganizila mmene zinthu zambili za pakacisi zinapangidwila, cioneka kuti mpandowo unali wamatabwa ndipo anaukuta na golide woyengedwa bwino na kuukongoletsa mwapadela poseŵenzetsa minyanga ya njovu. Conco munthu poona, anali kuona kuti mpandowo unapangidwa na minyanga ya njovu komanso golide basi. Pambuyo pofotokoza za masitepu 6 okafika ku mpando wacifumuwo, nkhaniyo imati: “M’mphepete mwake munali zifanizilo ziŵili za mikango itaimilila. Pa masitepu 6 amenewo panali zifanizilo 12 za mikango itaimilila, mbali iyi ndi iyi.” (2 Mbiri 9:17-19) Mkango ni cizindikilo coyenela coimila ulamulilo. (Gen. 49:9, 10; Chiv. 5:5) Cioneka kuti mikango 12 imeneyo inali kuimila mafuko 12 a Isiraeli, mwina pofuna kuonetsa kuti mafukowo anali kugonjela na kucilikiza mfumu yokhala pa mpandowo. Mpandowo unalinso na copondapo mapazi columikizidwa mwanjila inayake ku mpandowo. Zimene Malemba amakamba zakuti mpandowo unali wa minyanga ya njovu komanso golide, unaikidwa pa malo apamwamba, komanso kuti unali na cochingila kumbuyo kwake na zifanizilo za mikango zikulu-zikulu patsogolo pake, zionetsa kuti unali wapamwamba kuposa mipando yonse yacifumu ya panthawiyo, kaya imene ofukula za m’matongwe apeza, yojambulidwa pa zipilala, kapena yofotokozedwa m’zolemba zakale. Mpake kuti wolemba buku la 2 Mbiri anati “Panalibe ufumu wina umene unali ndi mpando wacifumu ngati umenewo.”—2 Mbiri 9:19.

APRIL 17-23

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 10-12

“Pindulani na Ulangizi Wanzelu”

w18.06 13 ¶3

Akanayanjidwa na Mulungu

Rehobowamu anaona kuti zinali zovuta kupanga cosankha pa nkhaniyi. Anadziŵa kuti akamvela anthu, iye, banja lake, ndi a m’nyumba yacifumu adzafunika kudzimana zinthu zina zimene anali kukonda, ndipo sakanakhala na ufulu wongolamula anthu zimene akufuna. Kumbali ina, anali na nkhawa yakuti anthuwo akhoza kum’pandukila akakana pempho lawo. Kodi n’ciani cimene anacita? Coyamba, anafunsila malangizo kwa amuna acikulile amene anali alangizi a Solomo, atate wake. Koma pambuyo pake, Rehobowamu anakafunsila malangizo kwa acinyamata anzake. Pomvela malangizo a anzakewo, iye anasankha kucitila nkhanza anthuwo. Anawauza kuti: “Ine ndidzakusenzetsani goli lolemela kwambili, ndipo ndidzawonjezela goli lanulo. Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu, koma ine ndidzakukwapulani ndi zikoti zaminga.”—2 Mbiri 10:6-14.

w01 9/1 28-29

Mmene Mungasankhile Mwanzelu

Yehova wapelekanso anthu okhwima maganizo mumpingo amene tingakambilane nawo zosankha zathu. (Aef. 4:11, 12) Komabe, pofunsila kwa anthu ena tisatsatile zomwe ena amacita zofunsa anthu ambili mpaka atapeza yemwe akunena zofuna zawo, ndiyeno n’kutsatila uphungu wake. Tikumbukilenso citsanzo coticenjeza ca Rehobowamu. Pamene anali kufuna kupanga cosankha cacikulu kwambili, analandila uphungu wabwino kwabasi kucokela kwa anthu acikulile amene anali kugwila nchito na abambo ake. Koma m’malo motsatila uphungu wawo, iye anakafunsila kwa anyamata anzake. Atatsatila uphungu wa anyamatawo, sanasankhe mwanzelu ndipo zotsatila zake zinali zakuti anthu m’cigawo cacikulu ca ufumu wake anam’pandukila.—1 Maf. 12:1-17.

Tikafuna kufunsila uphungu, tifunsile kwa anthu amene aona zambili m’moyo ndiponso omwe amadziŵa bwino Malemba komanso amene amaona mfundo zabwino zacikhalidwe kukhala zofunika. (Miy. 1:5; 11:14; 13:20) Ngati n’kotheka, sinkhasinkhani pa mfundo zacikhalidwe zomwe zikugwilizana na nkhaniyo ndiponso zomwe mwapeza pakufufuza kwanu. Mukayamba kuona zinthu m’kuunika kwa Mawu a Mulungu, cosankha colondola cidzaonekelatu.—Afil. 4:6, 7

it-2 768 ¶1

Rehobowamu

Cifukwa ca kudzitukumula kwa Rehobowamu, nkhanza komanso kusaganizila ena, Aisiraeli ambili analeka kucilikiza ulamulilo wake. Mafuko aŵili okha, la Yuda na la Benjamini ndiwo anapitiliza kucilikiza nyumba ya Davide. Ndipo nawonso ansembe na Alevi okhala m’maufumu onse aŵili, kuphatikizapo anthu oŵelengeka a m’mafuko 10 anali kucilikiza nyumba ya Davide.—1 Maf. 12:16, 17; 2 Mbiri 10:16, 17; 11:13, 14, 16.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 966-967

Ciwanda cooneka ngati mbuzi

Mawu a Yoswa pa Yoswa 24:14 amaonetsa kuti pamene Aisiraeli anali ku Iguputo, anatengelako mcitidwe wolambila mafano kwa anthu a kumeneko. Ndipo mawu a Ezekieli amaonetsa kuti Aisiraeli anapitiliza kucita zimenezo kwa zaka zambili atatuluka mu Iguputo. (Ezek. 23:8, 21) Akatswili ena amakhulupilila kuti pakati pa Aisiraeli panali mtundu winawake wa kulambila mbuzi, monga anali kucitila Aiguputo ambili, maka-maka okhala kumpoto kwa dzikolo. Amakhulupilila izi cifukwa ca lamulo limene Aisiraeli anapatsidwa m’cipululu, lowaletsa kupeleka “nsembe zawo ku ziwanda zooneka ngati mbuzi” (Lev. 17:1-7), komanso cifukwa ca zimene Yerobowamu anacita zoika ansembe “m’malo okwezeka kuti azitumikila ziwanda zooneka ngati mbuzi ndi mafano a ana a ng’ombe amene iye anapanga.” (2 Mbiri 11:15). Herodotus (II, 46) analemba kuti potengela mcitidwe wolambila mbuzi wa Aiguputo, Agiriki anayamba kukhulupilila milungu ya mchile ya cilakolako cosaletseka, yochedwa Pan komanso satyrs, imene pambuyo pake anali kuijambula ili na nyanga, mcila wa mbuzi, komanso miyendo ya mbuzi. Ena amati kukhulupilila milungu yotelo n’kumene kunakhala ciyambi ca mticitidwe wojambula Satana wokhala na mcila, nyanga, komanso miyendo ya ziboda zogaŵikana. Mcitidwewu unali wofala pakati pa anthu odzicha Akhristu m’zaka za m’ma 500 mpaka 1000 C.E.

Koma Baibo siifotokoza kuti “zinthu za ubweya wambili” zimenezo kapena kuti “ziwanda zooneka ngati mbuzi” (m’Ciheberi seʽi·rimʹ) zinali ciyani kwenikweni. Ena amaganiza kuti zinali mbuzi zenizeni kapena mafano ooneka ngati mbuzi. Koma cioneka kuti sizinali conco kwenikweni, komanso m’malemba mulibe umboni uliwonse wotsimikizila zimenezi. N’kutheka kuti mawu amenewa amangoonetsa kuti anthu olambila zinthuzo anali kuganiza kuti milungu yonama imeneyo inali yooneka ngati mbuzi kapena yaubweya wambili. N’kuthekanso kuti mawu akuti “mbuzi” m’mavesi amenewa ni mawu onyazitsa cabe ochulila mafano onse, monga zilili na mawu omasulidwa kuti mafano. M’mavesi ambili, mawu omasulidwa kuti mafano anacokela ku liwu limene poyamba linali kutanthauza “ndowe.” Koma izi sizitanthauza kuti mafanowo anali ndowe zenizeni.—Lev. 26:30; Deut. 29:17.

APRIL 24-30

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 13-16

“Ni Nthawi Iti Pamene Tiyenela Kudalila Yehova?”

w21.03 5 ¶12

Abale Acinyamata—Kodi Mungacite Ciyani Kuti Ena Azikudalilani?

12 Ali wacinyamata, Mfumu Asa anali wodzicepetsa komanso wolimba mtima. Mwacitsanzo, iye ataloŵa m’malo atate ake, Abiya, anayamba kugwila nchito yocotsa mafano m’dziko lake lonse. Cina, iye anauza Ayuda kuti “afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatila cilamulo.” (2 Mbiri 14:1-7) Ndipo pamene Zera Mwiitiyopiya anaukila Ayuda pamodzi na asilikali 1,000,000, Asa mwanzelu anatembenukila kwa Yehova kuti amuthandize. Iye anati: “Inu Yehova mukafuna kuthandiza, zilibe kanthu kuti anthuwo ndi ambili kapena ndi opanda mphamvu. Tithandizeni Yehova Mulungu wathu cifukwa tikudalila inu.” Mawu amenewa aonetsa kuti Asa anali na cidalilo cakuti Yehova adzamupulumutsa pamodzi na anthu ake. Asa anadalila Atate wake wakumwamba ndipo “Yehova anagonjetsa Aitiyopiyawo.”—2 Mbiri 14:8-12.

w21.03 5 ¶13

Abale Acinyamata—Kodi Mungacite Ciyani Kuti Ena Azikudalilani?

13 Mosakayikila, mungavomeleze kuti kuyang’anizana na gulu la asilikali 1,000,000 kunali koopsa kwambili. Koma cifukwa cakuti Asa anadalila Yehova, anapambana. Komabe, n’zomvetsa cisoni kuti pamene Asa anayang’anizana na gulu lankhondo locepa sanadalile Yehova. Ataopsezedwa na Baasa Mfumu yoipa ya Isiraeli, Asa anapita kwa mfumu ya Siriya kukapempha thandizo. Cosankha cimeneco cinakhala na zotulukapo zoipa. Kupitila mwa mneneli Hanani, Yehova anauza Asa kuti: “Cifukwa cakuti munadalila mfumu ya Siriya, osadalila Yehova Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya Siriya lathawa m’manja mwanu.” Kungoyambila panthawi imeneyo, anthu anali kucita naye nkhondo Asa. (2 Mbiri 16:7, 9; 1 Maf. 15:32) Kodi pali phunzilo lanji pamenepa?

w21.03 6 ¶14

Abale Acinyamata—Kodi Mungacite Ciyani Kuti Ena Azikudalilani?

14 Khalanibe odzicepetsa ndipo pitilizani kudalila Yehova. Pamene munali kubatizika, munaonetsa kuti muli na cikhulupililo cacikulu mwa Yehova ndipo mumam’dalila. Ndipo Yehova mokondwela anakupatsani mwayi wokhala m’banja lake. Koma cofunika kwambili tsopano ni kupitilizabe kudalila Yehova. Kudalila Yehova kungakhale kosavuta popanga zosankha zikulu-zikulu mu umoyo. Koma bwanji pa zosankha zina? M’pofunika kwambili kuti muzidalila Yehova popanga zosankha kuphatikizapo zija zokhudzana na zosangalatsa, nchito yakuthupi, komanso zolinga zimene mudzadziikila mu umoyo. Musadalile nzelu zanu. M’malomwake, fufuzani mfundo za m’Baibo zimene zingakuthandizeni popanga zosankha, ndipo citani zinthu mogwilizana na mfundo zimene mwapeza. (Miy. 3:5, 6) Mukacita zimenezi, mudzakondweletsa Yehova, ndipo abale na alongo mumpingo adzayamba kukulemekezani.—Ŵelengani 1 Timoteyo 4:12.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w17.03 19 ¶7

Tumikilani Yehova na Mtima Wathunthu

7 Aliyense wa ife ayenela kudzipenda kuti aone ngati ni wodzipeleka na mtima wonse kwa Mulungu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi nimayesetsa kucita zinthu zokondweletsa Yehova, kuteteza kulambila koona, na kuteteza anthu a Mulungu ku zinthu zimene zingawaononge mwauzimu?’ Ganizilani za Asa. Iye anafunika kulimba mtima kuti acotse Maaka pa udindo wokhala “mayi wa mfumu” m’dziko lake. N’zoona kuti mumpingo sitingayembekezele kupeza munthu wocita zoipa ngati Maaka. Koma nthawi zina mungafunike kucita zinthu molimba mtima ngati Asa. Mwacitsanzo, bwanji ngati wina m’banja lanu kapena mnzanu wapamtima wacita chimo, ndipo wacotsedwa mumpingo cifukwa cosalapa? Kodi mungalimbe mtima na kuleka kuceza naye? Kodi mtima wanu ungakusonkhezeleni kucita ciyani?

zeni popanga zosankha, ndipo citani zinthu mogwilizana na mfundo zimene mwapeza. (Miy. 3:5, 6) Mukacita zimenezi, mudzakondweletsa Yehova, ndipo abale na alongo mumpingo adzayamba kukulemekezani.—Ŵelengani 1 Timoteyo 4:12.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani