LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr23 May masa. 1-12
  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2023
  • Tumitu
  • MAY 1-7
  • MAY 8-14
  • MAY 15-21
  • MAY 22-28
  • MAY 29–JUNE 4
  • JUNE 5-11
  • JUNE 12-18
  • JUNE 19-25
  • JUNE 26–JULY 2
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2023
mwbr23 May masa. 1-12

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Umoyo na Utumiki

© 2022 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

MAY 1-7

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 17–19

“Muziona Ena Mmene Yehova Amawaonela”

w17.03 24 ¶7

Kodi Mudzatengelapo Phunzilo pa Zimene Zinalembedwa?

Nanga bwanji za Yehosafati mwana wa Asa? Iye anali na makhalidwe ambili abwino. Kudalila Mulungu kunamuthandiza kucita zinthu zambili zabwino. Koma nayenso nthawi ina anapanga zosankha mosaganiza bwino. Mwacitsanzo, Yehosafati anacita mgwilizano wacikwati na Ahabu, Mfumu yoipa ya ufumu wa kumpoto wa Isiraeli. Ndipo ngakhale kuti mneneli Mikaya anamucenjeza, iye anapitabe na Ahabu kukamenyana na Asiriya. Ku nkhondoko, Yehosafati anapulumuka ngakhale kuti anatsala pang’ono kuphedwa. Pambuyo pake, anabwelela ku Yerusalemu. (2 Mbiri 18:1-32) Zitatelo, mneneli Yehu anafunsa Yehosafati kuti: “Kodi cithandizo ciyenela kupelekedwa kwa oipa, ndipo kodi muyenela kukonda anthu odana ndi Yehova?”—Ŵelengani 2 Mbiri 19:1-3.

w15 8/15 11-12 ¶8-9

Tiziganizila Kwambili Cikondi ca Yehova

Yehova afuna kuti tidziŵe kuti amatikonda, na kuti sayang’anitsitsa pa zolakwa zathu. Koma amayesetsa kuona zabwino mwa ife. (2 Mbiri 16:9) Mwacitsanzo, iye anaona zabwino zimene Mfumu Yehosafati ya Yuda inacita. Panthawi ina, Yehosafati anacita zinthu mopanda nzelu mwa kugwilizana na Mfumu Ahabu ya Isiraeli pankhondo yofuna kulandanso mzinda wa Ramoti-giliyadi m’manja mwa Asiriya. Ngakhale kuti aneneli onyenga 400 anatsimikizila Ahabu kuti adzapambana nkhondoyo, mneneli woona wa Yehova, Mikaya, anakambilatu kuti Ahabu adzagonjetsedwa. Ahabu anafa pa nkhondoyo, koma Yehosafati anapulumuka ngakhale kuti anatsala pang’ono kuphedwa. Yehosafati atabwelela ku Yerusalemu, Yehu mwana wa Haneni, wamasomphenya anamudzudzula cifukwa cogwilizana na Ahabu pa nkhondoyo. Ngakhale zinali conco, Yehu anauzanso Yehosafati kuti: “Pali zinthu zabwino zimene zapezeka mwa inu.”—2 Mbiri 18:4, 5, 18-22, 33, 34; 19:1-3.

Kuciyambi kwa ulamulilo wake, Yehosafati analamula akalonga, Alevi, na ansembe kuti apite m’mizinda yonse ya Yuda kukaphunzitsa anthu Cilamulo ca Yehova. Zimenezi zinathandiza kwambili cakuti anthu a m’madela onse ozungulila Yuda anayamba kuopa Yehova. (2 Mbiri 17:3-10) Ngakhale kuti Yehosafati anacita zinthu mopanda nzelu, Yehova sanaiŵale zabwino zimene anacita poyamba. Nkhani ya m’Baibo imeneyi imatikumbutsa kuti ngakhale kuti ndife opanda ungwilo, Yehova adzapitilizabe kutionetsa cikondi cake cosatha ngati timayesetsa kucita zinthu zom’kondweletsa.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w17.03 20 ¶10-11

Tizitumikila Yehova ndi Mtima Wathunthu

Yehosafati mwana wa Asa “anapitiliza kuyenda m’njila za Asa bambo ake.” (2 Mbiri 20:31, 32) Kodi Yehosafati anacita zotani? Mofanana na atate wake, Yehosafati analimbikitsa anthu kufuna-funa Yehova. Iye anakonza pulogilamu yophunzitsa anthu poseŵenzetsa “buku la cilamulo ca Yehova.” (2 Mbiri 17:7-10) Anakafika mpaka ku dela la lamapili la Efuraimu, mu ufumu wakumpoto wa Isiraeli, kuti akalimbikitse anthu ‘kubwelela kwa Yehova.’ (2 Mbiri 19:4) Mfumu Yehosafati “anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.”—2 Mbiri 22:9.

Tonsefe tili na mwayi wogwila nawo nchito yaikulu yophunzitsa anthu, imene Yehova afuna kuti icitike masiku ano. Kodi mwezi uliwonse mumayesetsa kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu na kuwalimbikitsa kuti ayambe kum’tumikila? Ngati mumayesetsa kucita zimenezi, mwa dalitso la Mulungu, mungathe kuyambitsa phunzilo la Baibo. Kodi mumapemphela kuti mupeze phunzilo la Baibo? Ngati ni conco, mungafunike kulalikila mwakhama ngakhale pa nthawi imene anthu ambili amaona kuti ni yopumula. Ndiponso mofanana na Yehosafati, amene anapita ku dela la Efuraimu kukathandiza anthu kuti ayambenso kulambila Yehova, ifenso tiyenela kuyesetsa kuthandiza anthu amene anazilala. Komanso, akulu mumpingo amapanga makonzedwe oyendela na kuthandiza anthu ocotsedwa a m’gawo la mpingo wawo, amene aoneka kuti analeka kucita macimo.

MAY 8-14

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 20-21

“Khulupililani Yehova Mulungu Wanu”

w14 12/15 23 ¶8

Tikhale Ogwilizana Pamene Mapeto a Dzikoli Ayandikila

M’masiku a Mfumu Yehosafati, anthu a Mulungu anayang’anizana na “khamu lalikulu” la adani ocokela m’madela ozungulila. (2 Mbiri 20:1, 2) N’zolimbikitsa kuti atumiki a Mulungu sanayese kulimbana na adani awo mwa mphamvu zawo zokha. Koma anadalila Yehova. (Ŵelengani 2 Mbiri 20:3, 4.) Iwo anacita zinthu mogwilizana, ndipo palibe amene anali kucita za mumtima mwake. Baibo imanena kuti: “Anthu onse a ku Yuda anali ataimilila pamaso pa Yehova, kuphatikizaponso akazi awo ndi ana awo, ngakhalenso ana awo ang’ono-ang’ono.” (2 Mbiri 20:13) Onse pamodzi, acicepele na acikulile, anakhulupilila Yehova na kutsatila malangizo ake, ndipo Yehova anawateteza kwa adani awo. (2 Mbiri 20:20-27) Ici n’citsanzo cabwino kwambili kwa ife anthu a Mulungu coonetsa zimene tiyenela kucita tikakumana na mavuto.

w21.11 16 ¶7

Inu Okwatilana Caposacedwa—Ikani Mtima Wanu pa Kutumikila Yehova

Yehova anakamba na Yehosafati kupitilila mwa Mlevi wina dzina lake Yahazieli. Yehova anati: “Khalani m’malo anu, imani cilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani.” (2 Mbiri 20:13-17) Umu si mmene anthu anali kumenyela nkhondo. Koma malangizo amenewo anacokela kwa Yehova osati kwa munthu. Yehosafati anacita zonse zimene anauzidwa cifukwa anali kukhulupilila kwambili Mulungu wake. Iye na anthu ake atapita kuti akacite nkhondo na adani awo, Yehosafati anaika kutsogolo gulu la oimba m’malo motsogoza asilikali odziŵa kumenya nkhondo. Yehova anayankha pemphelo la Yehosafati mwa kugonjetsa gulu la asilikali la adani ake.—2 Mbiri 20:18-23.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 1271 ¶1-2

Yehoramu

Cifukwa cosonkhezeledwa na mkazi wake Ataliya komanso zinthu zina, Yehoramu sanacite zolungama monga anacitila atate ake Yehosafati. (2 Maf. 8:18) Kuwonjezela pa kupha abale ake 6, komanso ena mwa akalonga a Yuda, Yehoramu anacititsanso anthu a mu ufumu wake kuleka kulambila Yehova na kuyamba kulambila mafano. (2 Mbiri 21:1-6, 11-14) Panthawi yonse ya ulamulilo wake, mu Yuda munali mavuto ocokela mkati mwa ufumuwo komanso kunja. Coyamba Aedomu anapandukila Yuda. Kenako, Libina nayenso anapanduka. (2 Maf. 8:20-22) M’kalata imene analemba, mneneli Eliya anacenjeza Yehoramu kuti: “Tamvela tsopano! Yehova adzalanga mwamphamvu anthu ako, ana ako ndi akazi ako, ndipo adzawononga katundu wako yense. [Komanso] iweyo [mfumu Yehoramu] udzakhala wodwaladwala popeza udzadwala matenda a m’matumbo, mpaka matumbo ako adzatuluka chifukwa chodwala tsiku ndi tsiku.”—2 Mbiri 21:12-15.

Zonse zinacitika monga mmene Yehova ananenela. Yehova analola Aluya komanso Afilisiti kugonjetsa ufumu wa Yuda na kugwila ukapolo akazi a Yehoramu komanso ana ake. Mulungu analola mwana wamng’ono kwambili wa Yehoramu dzina lake Yehoyahazi (wochedwanso Ahaziya) kuthaŵa. Yehova analola izi cifukwa ca pangano la ufumu limene anacita na Davide. ‘Pambuyo pa zonsezi, Yehova anamudwalitsa Yehoramu matenda a m’matumbo osacilitsika. Patapita zaka ziŵili matumbo ake anatuluka ndipo m’kupita kwa nthawi anamwalila.’ Anaikidwa “m’manda mu Mzinda wa Davide, koma osati m’manda a mafumu.” Kenako Ahaziya mwana wake anakhala mfumu.—2 Mbiri 21:7, 16-20; 22:1; 1 Mbiri 3:10, 11.

MAY 15-21

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 22-24

“Yehova Amadalitsa Anthu Ocita Zinthu Molimba Mtima”

w09 4/1 24 ¶1-2

Yoasi Anasiya Kutumikila Yehova Cifukwa Coceza ndi Anthu Ocita Zoipa

INALI nthawi yovuta kwambili ku Yerusalemu, mzinda umene kunali kacisi wa Mulungu. Panthawiyi, Mfumu Ahaziya anali atangophedwa kumene. Ndipo zimene Ataliya, yemwe anali mayi wake wa Ahaziya anacita zinali zovuta kumvetsa—Iye anapha zidzukulu zake, ana aamuna a Ahaziya. Kodi ukudziŵa cifukwa cimene anacitila zimenezi?—Iye anatelo kuti akhale wolamulila m’malo mwa zidzukulu zakezo.

Komabe Yoasi, mmodzi mwa zidzukulu za Ataliya amene panthawiyi anali wakhanda, anapulumuka ndipo agogo akewo sanadziŵe ciliconse. Kodi ukufuna kudziŵa kuti anapulumuka bwanji?— Mwanayo anali ndi azakhali ake a Yehosabati ndipo iwo anam’tenga n’kukamubisa mu kacisi wa Mulungu. Iwo anatha kukamubisa m’kacisi cifukwa amuna awo a Yehoyada anali Mkulu wa aAnsembe. Conco, aŵiliwa anaonetsetsa kuti mwanayo akutetezedwa.

w09 4/1 24 ¶3-5

Yoasi Anasiya Kutumikila Yehova Cifukwa Coceza ndi Anthu Ocita Zoipa

Yoasi anabisidwa m’kacisi kwa zaka 6, ndipo ali m’kacisimo, anaphunzitsidwa mfundo zonse zokhudza Yehova Mulungu na malamulo Ake. Kenako Yoasi atafika zaka 7, Yehoyada anacita zinthu zoti Yoasi akhale mfumu. Kodi ungakonde kudziŵa mmene Yehoyada anacitila zimenezi ndiponso zimene zinacitikila mfumukazi yoipa Ataliya, yomwe inali agogo ake a Yoasi?—

Yehoyada anaitanitsa mwamseli asilikali olondela mafumu a ku Yerusalemu. Ndipo iye anawafotokozela mmene iye ndi mkazi wake anapulumutsila Yoasi, mwana wa Mfumu Ahaziya. Kenako, Yehoyada anatenga Yoasi n’kumusonyeza kwa asilikaliwo, ndipo iwo anaona kuti iye ndiye anali woyenela kukhala mfumu. Conco, anakonza njila yoti amulonge ufumu.

Yehoyada anatulutsila Yoasi kunja, n’kumuveka korona wacifumu. Zitatelo anthu anayamba ‘kuwomba m’manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.’ Asilikali olondela mfumu aja anam’zungulila Yoasi pomuteteza. Koma Ataliya atamva anthu akufuula cifukwa ca cisangalalo, anathamanga kuti akawaletse. Ndipo Yehoyada analamula kuti Ataliya aphedwe, ndipo asilikaliwo anamuphadi.—2 Mafumu 11:1-16.

it-1 379 ¶5

Kuika m’Manda, Manda

Mkulu wa Ansembe wolungama Yehoyada, anapatsidwa ulemu mwa kuikidwa m’manda a mafumu mu “Mzinda wa Davide.” Pa anthu amene sanali mu mzela wa mafumu, ni iye yekha amene anapatsidwa ulemu wotelo.—2 Mbiri 24:15, 16.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2 1223 ¶13

Zekariya

12. Mwana wa Mkulu wa Ansembe Yehoyada. Yehoyada atamwalila, Mfumu Yehoasi anapatuka pa kulambila koona, cifukwa comvela uphungu wolakwika m’malo momvela aneneli a Yehova. Zekariya, msuweni wake wa Yehoasi (2 Mbiri 22:11) anacenjeza a Yuda mwamphamvu pa nkhani imeneyi, koma m’malo molapa, iwo anamuponya miyala m’bwalo la kacisi. Zekariya pa kufa ananena kuti: “Yehova aone zimene mwacitazi ndi kubwezela.” M’kupita kwa nthawi, Yehova anayankha pemphelo limeneli la Zekariya. Asiriya anawononga zinthu zambili mu Yuda komanso Yehoasi anaphedwa na atumiki ake aŵili “cifukwa ca magazi a ana a wansembe Yehoyada.” Baibo ya Cigiriki ya Septuagint komanso ya Cilatin yocedwa Vulgate, onse amakamba kuti Yehoasi anaphedwa pobwezela magazi a “mwana” wa Yehoyada. Komabe, Baibo ya Cisiriya yocedwa Peshitta, na zolemba za Amasoreti zimagwilitsa nchito mawu oculukitsa akuti “ana.” Izi zinalembedwa conco mwina pofuna kuonetsa ulemu cifukwa mwana wa Yehoyada, Zekariya, anali mneneli komanso wansembe.—2 Mbiri 24:17-22, 25.

MAY 22-28

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 25-27

“Yehova Akhoza Kukupatsani Zambili Kuposa Pamenepa”

it-1 1266 ¶6

Yehoasi

Komanso Yehoasi analola asilikali ake 100,000, kulembedwa ganyu na mfumu ya Yuda kuti akaithandize polimbana na Aedomu. Komabe, cifukwa ca malangizo a “munthu wa Mulungu woona,” asilikaliwo anabwezedwa. Ngakhale kuti anali atawalipila kale ndalama za siliva zokwana matalente 100 ($660,600), anakhumudwa atawabweza kunyumba, mwina poona kuti ataya mwayi wotengako zofunkha. Atabwelela kwawo ku ufumu wa kumpoto, anayamba kuukila mizinda ya ufumu wa kumwela, kuyambila ku Samariya (mwina kumene amacokela) mpaka ku Beti-horoni.—2 Mbiri 25:6-10, 13.

w21.08 30 ¶16

Laŵani’ Ubwino wa Yehova—Motani?

Khalani odzimana kaamba ka Yehova. Sitiyenela kucita kudzimana zinthu zonse kuti tikondweletse Yehova. (Mlal. 5:19, 20) Komabe, ngati tizengeleza kucita zambili potumikila Mulungu cabe cifukwa cosafuna kudzimana zinthu zina, tingacite zinthu mofanana na munthu wa m’fanizo la Yesu amene anadziunjikila cuma cambili koma n’kunyalanyaza Mulungu. (Ŵelengani Luka 12:16-21.) M’bale Christian wa ku France anati: “Sin’nali kupatsa Yehova komanso banja langa nthawi yokwanila.” Iye na mkazi wake anaganiza zocita upainiya. Koma kuti akwanilitse colinga cawo, anayenela kusiya nchito zawo. Kuti azipeza zofunikila pa umoyo, iwo anayamba bizinesi yawo-yawo yoyeletsa, ndipo anaphunzila kukhala okhutila na ndalama zocepa zimene anali kupeza. Kodi kudzimana kwawo kunawapindulila bwanji? M’bale Christian anati: “Tsopano tikucita zambili mu utumiki wathu kuposa kale, ndipo ndife acimwemwe pokhala na maphunzilo a Baibo komanso maulendo obwelelako.”

Kufufuza Cuma Cauzimu

w07 12/15 10 ¶1-2

Kodi Muli ndi Mlangizi pa Zauzimu?

UZIYA anakhala mfumu ya ufumu wa kum’mwela wa Yuda ali na zaka 16 zokha. Analamulila kwa zaka zoposa 50, kuyambila mu 829 B.C.E. mpaka mu 778 B.C.E. Kuyambila ali mwana, Uziya ‘anacita zoongoka pamaso pa Yehova.’ Kodi n’ciyani cinam’thandiza kucita zinthu zoyenela? Nkhani ya m’Baibo imati: “Uziya anali kufunafuna Mulungu m’masiku a Zekariya yemwe anali kumulangiza kuti aziopa Mulungu woona. M’masiku amene iye anafunafuna Yehova, Mulungu woonayo anacititsa kuti zinthu zizimuyendela bwino.”—2 Mbiri 26:1, 4, 5.

Ni nkhani yokhayi m’Baibo imene imafotokoza za Zekariya yemwe anali mlangizi wa mfumu. Komabe, Zekariya yemwe anali ‘kulangiza Mfumu Uziya kuti aziopa Mulungu woona,’ anathandiza kwambili mfumu yacinyamatayo kucita zoyenela pamaso pa Yehova Mulungu. Buku lina lofotokoza Baibo (lotchedwa Expositor’s Bible) limati, n’zodziŵikilatu kuti Zekariya “anali munthu wodziŵa bwino malemba ndiponso zinthu zauzimu komanso wodziŵa kuphunzitsa zimene ankadziŵazo.” Katswili wina wa Baibo anafika ponena za Zekariya kuti: “Ankadziŵa kwambili maulosi ndiponso . . . anali wanzelu, wodzipeleka, munthu wabwino, ndipo zikuoneka kuti iyeyu ni amene anathandiza kwambili Uziya.”

MAY 29–JUNE 4

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 28-29

“Mungamutumikile Yehova Ngakhale Kuti Makolo Anu Sanapeleke Citsanzo Cabwino”

w16.02 14 ¶8

Tsanzilani Anthu Amene Anali pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova

Mosiyana na Rute, Hezekiya anabadwila mu mtundu wa Aisiraeli omwe anadzipeleka kwa Yehova. Koma si Aisiraeli onse amene anali kumvela Mulungu. Mwacitsanzo Mfumu Ahazi, yemwe anali bambo ake a Hezekiya, anali mfumu yoipa kwambili. Iye anacititsa kuti anthu a ku Yuda ayambe kulambila mafano ndipo sanali kulemekeza kacisi wa Yehova wa ku Yerusalemu. Ahazi anafika mpaka powotcha ana ake ena ali moyo n’kuwapeleka nsembe kwa mulungu wonyenga. Conco Hezekiya ali mwana, anaona bambo ake akucita zinthu zambili zoipa.—2 Maf. 16:2-4, 10-17; 2 Mbiri 28:1-3.

w16.02 14 ¶9-11

Tsanzilani Anthu Amene Anali pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova

Zinthu zoipa zimene Hezekiya anaona bambo ake akucita, zikanamukhumudwitsa kwambili moti akanatha kukwiyila Yehova. Masiku ano, anthu ena amene anakumanapo na mavuto amaona kuti ali na zifukwa zomveka zoti ‘azikwiyila Yehova’ kapena gulu lake. (Miy. 19:3) Amacita zimenezi ngakhale kuti mavuto awo sakhala aakulu ngati a Hezekiya. Enanso amacita zinthu zoipa poganiza kuti sangacitile mwina cifukwa anakulila m’banja limene munali kucitika zinthu zoipa. (Ezek. 18:2, 3) Koma kodi zimenezi n’zoona?

Citsanzo ca Hezekiya cimasonyeza kuti zimenezi si zoona. Palibe cifukwa comveka coticititsa kukwiyila Yehova popeza iye si amene amacititsa zinthu zoipa zimene timakumana nazo. (Yobu 34:10) N’zoona kuti zocita za makolo, zikhoza kucititsa kuti ana awo azicita zabwino kapena zoipa. (Miy. 22:6; Akol. 3:21) Koma izi sizikutanthauza kuti munthu amene anakulila m’banja limene munali kucitika zinthu zoipa sangakhale wabwino. Tikutelo cifukwa cakuti Yehova anatipatsa ufulu wosankha kucita zabwino kapena zoipa. (Deut. 30:19) Kodi Hezekiya anagwilitsa nchito bwanji ufulu umenewu?

Ngakhale kuti Hezekiya anali mwana wa mfumu yoipa kwambili, atakula anakhala mfumu yabwino. (Ŵelengani 2 Mafumu 18:5, 6.) Iye anasankha kutsatila citsanzo ca anthu abwino osati ca bambo ake. Anali kutsatila citsanzo ca anthu monga Yesaya, Mika na Hoseya omwe anali aneneli a Yehova. Hezekiya anali kumvela zimene aneneliwo anali kunena ndipo zinamuthandiza kuti akonze zinthu zoipa zimene bambo ake analakwitsa. Anayeletsa kacisi, kucotsa mafano m’dziko lonse ndiponso kupempha Yehova kuti akhululukile anthu macimo awo. (2 Mbiri 29:1-11, 18-24; 31:1) Pamene Senakeribu mfumu ya Asuri anaopseza kuti aukila mzinda wa Yerusalemu, Hezekiya anacita zinthu molimba mtima ndipo anaonetsa kuti anali kukhulupilila Yehova. Iye anadalila Yehova ndipo analimbikitsa anthu ake kucita cimodzimodzi. (2 Mbiri 32:7, 8) Pa nthawi ina, Hezekiya anayamba mtima wodzikuza koma Yehova atamudzudzula, anadzicepetsa n’kusintha. (2 Mbiri 32:24-26) Iye n’citsanzo cabwino kwa tonsefe cifukwa sanalole kuti citsanzo coipa ca bambo ake cimulepheletse kukhala munthu wabwino. M’malomwake, anacita zinthu zimene zinamuthandiza kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w12 2/15 24-25

Natani—Anali Wokhulupilika Ndipo Ankalimbikitsa Kulambila Koona

Popeza Natani anali kulambila Yehova mokhulupilika, analimbikitsa Davide kuti amange nyumba yoyamba yoti azilambililamo Mulungu padziko lapansi. Koma zikuoneka kuti pa nthawiyi, Natani anangonena maganizo ake m’malo monena zinthu m’dzina la Yehova. Ndiyeno usiku womwewo Mulungu anauza mneneliyu kuti akanene kwa mfumuyo uthenga wosiyana na umene ananena poyamba. Anakamuuza kuti samanga kacisi wa Yehova. Munthu woti adzamange kacisiyu anali mwana wa Davide. Koma Natani ananenanso kuti Mulungu akucita pangano ndi Davide lakuti mpando wake wacifumu “udzakhazikika mpaka kalekale.”—2 Sam. 7:4-16.

Maganizo a Mulungu anasiyana na zimene Natani ananena zokhudza kumanga kacisi. Izi zitacitika, mneneli wodzicepetsayu sananyinyilike, m’malomwake anagonjela na kucita zinthu mogwilizana na colinga ca Yehova. Apatu anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca zimene tiyenela kucita ngati Mulungu akutiwongolela pa nkhani inayake. Zimene Natani anacita pambuyo pa nkhani imeneyi zikuonetsa kuti ubwenzi wake na Mulungu unali wabwinobe. Ndipotu zikuoneka kuti Yehova anauzila Natani na Gadi, yemwe anali wamasomphenya, kuti alimbikitse Davide kukhazikitsa anthu 4,000 oti azidzaimbila Yehova pakacisi.—1 Mbiri 23:1-5; 2 Mbiri 29:25.

JUNE 5-11

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 30-31

“Kusonkhana Pamodzi Kumatipindulila”

it-1 1103 ¶2

Hezekiya

Cangu Cake pa Kulambila Koona. Hezekiya anaonetsa cangu cake pa kulambila Yehova atangoikidwa pa mpando wacifumu ali na zaka 25. Cinthu coyamba cimene anacita ni kutsegulanso kacisi na kumukonza. Kenako, anaitana ansembe na Alevi na kuwauza kuti: “Ineyo ndikufunitsitsa mumtima mwanga kucita pangano ndi Yehova Mulungu wa Isiraeli.” Limeneli linali pangano la kukhulupilika. Ngakhale kuti pangano la Cilamulo linalipo kale, Ayuda sanali kulitsatila. Conco, mwa kucita pangano limeneli la kukhulupilika, zinali ngati kuti pangano la Cilamulo layambanso kugwila nchito mu Yuda. Na mphamvu zake zonse, Hezekiya anaika Alevi m’mautumiki awo, anakhazikitsanso dongosolo la zida zoimbila na oimba nyimbo zotamanda Mulungu. Panali pa Nisani mwezi wa cikondwelelo ca Pasika, koma kacisi, ansembe komanso Alevi anali odetsedwa. Pa Nisani 16, kacisi anayeletsedwa komanso ziwiya zake zinabwezeletsedwa. Ndiyeno panacitika mwambo wapadela wophimba macimo a Aisiraeli onse. Coyamba, akalonga anabweletsa zopeleka kuti azipeleke monga nsembe ya macimo a ufumuwo, ya malo opatulika, komanso ya anthu. Pambuyo pake, anthu anabweletsa nsembe zambili zopseleza.—2 Mbiri 29:1-36.

it-1 1103 ¶3

Hezekiya

Popeza kuti kudetsedwa kwa anthu kunawalepheletsa kucita mwambo wa Pasika panthawi yoikika, Hezekiya anapezelapo mwayi pa lamulo lolola kuti anthu odetsedwa azidziyeletsa na kucita mwambo wa Pasika mwezi wotsatila. Iye anaitana Ayuda onse komanso Aisiraeli mwa kutumiza makalata m’dziko lonselo, kucokela ku Beere-seba mpaka ku Dani, pogwilitsa nchito asilikali othamanga. Othamangawo anatonzedwa na anthu ambili, koma anthu ena, makamaka a fuko la Aseri, Manase na Zebuloni anadzicepetsa n’kubwela ku Yerusalemu. Enanso a fuko la Efuraimu na Isakara anapezekapo. Kuwonjezela apo, anthu ambili amene sanali Aisiraeli koma anali kulambila Yehova analipo. Ziyenela kuti zinali zovuta kwa anthu a mu ufumu wa kumpoto amene anali kulambila Yehova kupezekapo. Monga zinalili na othamanga otumidwa aja, nawonso anthu a mu ufumu wa kumpoto anakumana na citsutso, komanso anatonzedwa cifukwa anthu mu ufumuwo anali na makhalidwe oipa, analowelela mu kulambila konyenga, komanso anali kuwopsezedwa na Asuri.—2 Mbiri 30:1-20; Num. 9:10-13.

it-1 1103 ¶4-5

Hezekiya

Pasika itatha, anacita Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Cofufumitsa kwa masiku 7 mosangalala kwambili. Cifukwa cosangalala, anthuwo anagwilizana zakuti awonjezele masiku ena 7 a cikondweleloco. Ngakhale panthawi yovuta imeneyi, Yehova anawadalitsa kwambili anthu ake moti “munali cikondwelelo cacikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambila m’masiku a Solomo mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli, kunali kusanacitike cikondwelelo ngati cimeneci ku Yerusalemu.”—2 Mbiri 30:21-27.

Ici sicinalli cabe cikondwelelo ca kanthawi, koma cinalidi ciyambi ca kubwezeletsa kulambila koona. Cimene cionetsa zimenezi, ni zimene zinacitika cikondweleloco citatha. Asanabwelele ku nyumba zawo, ocita cikondwelelowo anapita kukaphwanya zipilala zopatulika, kukadula mizati yopatulika, na kukagwetsa malo okwezeka na maguwa ansembe m’Yuda yense, m’Benjamini, m’Efraimu, na m’Manase. (2 Mbiri 31:1) Hezekiya anapeleka citsanzo cabwino mwa kuphwanya-phwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga, cifukwa Aisiraeli anaipanga kukhala fano ndipo anali kuifukizila nsembe yautsi. (2 Maf. 18:4) Cikondweleloco citatha, Hezekiya anaonetsetsa kuti kulambila koona kupitilizabe mwa kupanga makonzedwe akuti Aisiraeli azithandiza otumikila pakacisi. Iye analimbikitsa Aisiraeliwo kuti azipeleka cakhumi komanso zipatso zoyambilila kwa Alevi na ansembe, monga mmene cilamulo cinanenela. Ndipo anthuwo anacita zimenezi na mtima wonse.—2 Mbiri 31:2-12.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w18.09 6 ¶14-15

“Ngati Zimenezi Mukuzidziŵa, Ndinu Odala Mukamazicita”

Njila inanso imene tingaonetsele kuti ndise odzicepetsadi ni kukhala okonzeka kumvetsela ena akamakamba nase. Yakobo 1:19 imakamba kuti tiyenela kukhala “ofulumila kumva.” Yehova amapeleka citsanzo cabwino ngako pa mbaliyi. (Gen. 18:32; Yos. 10:14) Ganizilani makambilano amene anali pakati pa Mose na Yehova, malinga n’zimene zinalembedwa pa Ekisodo 32:11-14. (Ŵelengani.) Olo kuti Yehova anali kudziŵa kale zocita, anapatsa Mose mpata wofotokozako maganizo ake. Kodi imwe mungamvetsele moleza mtima kwa munthu amene amacita zinthu mosaganiza bwino, kenako n’kutsatila malingalilo amene angapeleke? Zaconco n’zimene Yehova amacita. Iye amamvetsela moleza mtima zokamba za anthu onse amene amapemphela kwa iye ali na cikhulupililo.

Aliyense wa ife angacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Ngati Yehova amadzicepetsa mpaka kumvetsela zokamba za anthu, monga anacitila kwa Abulahamu, Rakele, Mose, Yoswa, Manowa, Eliya, na Hezekiya, kodi ine siniyenela kucita zoposa pamenepo? Kodi sinifunika kulemekeza kwambili abale anga, kumvetsela malingalilo awo, komanso ngakhale kucita zinthu mogwilizana na malingalilo awo abwino? Kodi pali pano mu mpingo mwathu kapena m’banja lathu muli wina wake amene afunika thandizo langa? Kodi ningamuthandize bwanji?’—Gen. 30:6; Ower. 13:9; 1 Maf. 17:22; 2 Mbiri 30:20.

JUNE 12-18

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 32-33

“Muzilimbikitsa Ena pa Nthawi Zovuta”

it-1 204 ¶5

Asuri

Senakeribu. Senakeribu, mwana wa Sarigoni Waciŵili anaukila ufumu wa Yuda m’caka ca 14 ca ulamulilo wa Hezekiya mu (732 B.C.E.). (2 Maf. 18:13; Yes. 36:1) Hezekiya anapandukila ulamulilo wopondeleza wa Asuri umene unabwela cifukwa ca zocita za atate ake, Ahazi. (2 Maf. 18:7) Zimenezi zinakwiitsa Senakeribu cakuti analoŵa mu Yuda na kulanda mizinda 46. (Yelekezelani na Yesaya 36:1, 2) Kenako, kucokela ku msasa wake ku Lakisi, iye analamula kuti Hezekiya apeleke msonkho wa matalente a golide 30 (c. $11,560,000) komanso matalente a siliva 300 (c. $1,982,000). (2 Maf. 18:14-16; 2 Mbiri 32:1; yelekezelani na Yes. 8:5-8.) Ngakhale pambuyo popeleka ndalama zimenezi, Senakeribu anatumiza atumiki ake kuti akalamule Hezekiya kupeleka mzinda wa Yerusalemu popanda kumenya nkhondo. (2 Maf. 18:17–19:34; 2 Mbiri 32:2-20) Yehova atapha asilikali a Senakeribu okwana 185,000 mu usiku umodzi, Senakeribu anakakamizika kuleka nkhondoyo na kubwelela ku Nineve. (2 Maf. 19:35, 36) Kumeneko, anaphedwa na ana ake aŵili, ndipo analowedwa m’malo na mwana wake wina, dzina lake Esari-hadoni. (2 Maf. 19:37; 2 Mbiri 32:21, 22; Yes. 37:36-38) Zocitika zimenezi, kupatulapo za kuphedwa kwa asilikali a Asuri, zinalembedwanso pa phale la Senakeribu komanso la Esari-hadoni.—ZITHUNZI, Vol. 1, tsa. 957.

w13 11/1 20 ¶12

Kodi Abusa 7 Ndi Atsogoleli 8 Ndani Masiku Ano?

Tikakhala pa mavuto, Yehova nthawi zonse amafunitsitsa kutithandiza. Koma iye amafunanso kuti ife ticite zimene tingathe kuti tithetse vutolo. Hezekiya anafunsila uphungu kwa “akalonga ake ndi amuna ake amphamvu” ndipo iwo anagwilizana kuti “atseke akasupe a madzi amene anali kunja kwa mzindawo . . . Kuwonjezela apo, iye analimba mtima n’kumanga makoma onse a mpanda amene anali ogumuka, . . . ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina ndipo anapanga zida zambili ndi zishango.” (2 Mbiri 32:3-5) Pofuna kuteteza ndi kuweta anthu ake panthawiyo, Yehova anagwilitsila nchito amuna angapo olimba mtima. Amuna amenewa anali Hezekiya, akalonga ake na aneneli okhulupilika.

w13 11/1 20 ¶13

Kodi Abusa 7 Ndi Atsogoleli 8 Ndani Masiku Ano?

Kenako Hezekiya anacita cinthu cina cofunika kwambili kuposa kutseka akasupe a madzi na kulimbitsa mpanda wa mzinda wa Yerusalemu. Popeza kuti Hezekiya anali m’busa wacikondi, iye anasonkhanitsa anthu na kuwalimbikitsa na mawu akuti: “Musaope kapena kucita mantha ndi mfumu ya Asuri . . . , cifukwa ife tili ndi ambili kuposa amene ali ndi mfumuyo. Iyo ikudalila mphamvu za anthu, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kuti atithandize ndi kutimenyela nkhondo zathu.” Amenewa anali mawu olimbitsa cikhulupililo kwambili cifukwa cakuti Yehova anali kudzawamenyela nkhondo. Atamva zimenezi, Ayuda “anayamba kulimba mtima cifukwa ca mawu a Hezekiya mfumu ya Yuda.” Onani kuti “mawu a Hezekiya” ni amene anacititsa kuti anthuwo alimbe mtima. Hezekiya, akalonga ake, amuna ake amphamvu, mneneli Mika na mneneli Yesaya, anali abusa abwino monga mmene Yehova analoselela kudzela mwa Mika.—2 Mbiri 32:7, 8; ŵelengani Mika 5: 5, 6.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w21.10 4-5 ¶11-12

Kodi Kulapa Kwenikweni N’ciani?

M’kupita kwa nthawi, Yehova anayankha mapemphelo a Manase. Mapemphelo ake anaonetsa kuti iye anasinthadi, ndipo Yehova anaona zimenezo. Conco, iye anamubwezanso pa ufumu. Manase anacita zonse zotheka poonetsa kuti analapadi. Anacita zimene Ahabu analephela kucita. Manase anasintha khalidwe lake, anatsutsa kulambila konama, ndipo analimbikitsa anthu kulambila Yehova. (Ŵelengani 2 Mbiri 33:15, 16.) Koma kuti acite zimenezi, anafunika kukhala na cikhulupililo komanso kulimba mtima cifukwa kwa zaka zambili, anali citsanzo coipa ku banja lake, anzake, komanso kwa anthu ena. Ku ukalamba wake, iye anayesa kukonza zina zimene analakwitsa. N’kutheka kuti iye anakhala citsanzo cabwino kwa mdzukulu wake Yosiya, amene anadzakhala mfumu yabwino.—2 Maf. 22:1, 2.

Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Manase? Iye anadzicepetsa, koma sanalekele pamenepo. Anapempha Mulungu kuti am’citile cifundo, ndipo anasintha khalidwe lake. Iye anayesetsa kukonza zimene analakwitsa, komanso anacita zonse zotheka kuti alambile Yehova na kuthandiza ena kucita cimodzimodzi. Citsanzo ca Manase n’cothandiza ngakhale kwa aja amene anacita macimo aakulu. Cipeleka umboni wamphamvu wakuti Yehova Mulungu ni ‘wabwino ndipo ni wokonzeka kukhululuka.’ (Sal. 86:5) Yehova amakhululukila anthu amene alapadi zenizeni.

JUNE 19-25

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MBIRI 34-36

“Kodi Mumapindula Nawo Mofikapo Mawu a Mulungu?”

it-1 1157 ¶4

Hulida

Pamene Yosiya anamva kuŵelengedwa kwa “buku la cilamulo” limene Hilikiya mkulu wa Ansembe analipeza pokonzanso kacisi, anatumiza anthu kukafunsila kwa Yehova. Iwo anapita kwa Hulida amene anawauza mawu a Yehova oonetsa kuti matsoka onse olembedwa ‘m’bukulo’ adzagwela mtundu wopandukawo. Hulida anawonjezela kuti, cifukwa cakuti Yosiya anadzicepetsa pamaso pa Yehova, sanali kudzaona tsoka koma anali kudzaikidwa m’manda pamodzi na makolo ake mumtendele.—2 Maf. 22:8-20; 2 Mbiri 34:14-28.

w09 6/15 10 ¶20

Khalani Acangu pa Nyumba ya Yehova

Mfumu Yosiya anauza anthu kuti akonzenso kacisi. Pa nchito imeneyi, Hilikiya yemwe anali Mkulu wa Ansembe, “anapeza buku la cilamulo ca Yehova lopelekedwa ndi dzanja la Mose.” Iye anapeleka bukulo kwa Safani yemwe anali mlembi ndipo Safaniyo anamuŵelengela Yosiya bukulo. (Ŵelengani 2 Mbiri 34:14-18.) Ndiye kodi mfumu Yosiya anatani? Nthawi yomweyo iye anang’amba zovala zake cifukwa ca cisoni ndipo anauza anthu kuti apemphele kwa Yehova. Kudzela mwa mneneli wamkazi, dzina lake Hulida, Mulungu anapeleka uthenga wodzudzula miyambo ya cipembedzo imene inali kucitika mu Yuda. Ngakhale kuti Yehova analosela za tsoka limene mtundu wonsewo unadzakumana nalo, Iye anaona ndiponso anayamikila khama limene Yosiya anaonetsa pocotsa kulambila mafano. (2 Mbiri 34:19-28) Kodi tikuphunzilapo ciyani pamenepa? Tiyenela kukhala ndi mtima umene Yosiya anali nawo. Tikamva malangizo a Yehova tiyenela kuwatsatila mwamsanga. Tiyenelanso kukumbukila zimene zingacitike ngati mwapang’onopang’ono tikuyamba kucita za mpatuko kapena zosakhulupilika. Tikamatelo sitikayika ngakhale pang’ono kuti Yehova akuona ndipo akuyamikila khama limene tikusonyeza pa kulambila koona, ngati mmene anacitila na Yosiya.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w17.03 27 ¶15-17

Kodi Mudzatengelapo Phunzilo pa Zimene Zinalembedwa?

Ni cenjezo lanji limene tingatengepo pa zimene zinacitikila Mfumu yabwino Yosiya? Ganizilani zimene zinacititsa kuti iye agonjetsedwe na kuphedwa. (Ŵelengani 2 Mbiri 35: 20-22.) Yosiya “anapita kukakumana” na Mfumu Neko ya Iguputo, ngakhale kuti mfumuyo inamuuza kuti siinali kufuna kumenyana na iye. Baibo imakamba kuti mawu a Neko anali “ocokela pakamwa pa Mulungu.” Nanga n’cifukwa ciani Yosiya anapita kukamenyana naye? Baibo siikambapo ciliconse.

Koma kodi Yosiya akanadziŵa bwanji kuti mawu a Neko anali ocokela kwa Yehova? Iye akanafunsa Yeremiya, mmodzi wa aneneli okhulupilika. (2 Mbiri 35:23, 25) Koma m’Baibo mulibe mawu oonetsa kuti anacita zimenezo. Komanso Neko anali kupita kukacita nkhondo ku Karikemisi. Iye anali kupita kukamenyana “ndi mtundu wina,” osati Yerusalemu. Kuwonjezela apo, dzina la Mulungu silinali kukhudzidwa, cifukwa Neko sanali kutonza Yehova kapena anthu ake. Conco, sicinali cinthu canzelu Yosiya kukacita nkhondo na Neko. Kodi tiphunzilapo ciani pa nkhaniyi? Tikakumana na vuto, tifunika kuganizila zimene Yehova afuna kuti ticite.

Tikakumana na vuto linalake, tifunika kuganizila mfundo za m’Baibo zokhudzana na nkhaniyo ndi kuziseŵenzetsa m’njila yoyenela. Nthawi zina tingafunike kufunsa akulu. Tingafunikenso kuganizila mfundo zina zimene tikudziŵa kale pankhaniyo, ndiponso kufufuza m’zofalitsa zathu. Komanso pangakhale mfundo zina za m’Baibo zofunika kuziganizila zimene mkulu angatiuze. Mwacitsanzo, Mkhristu aliyense amadziŵa kuti ali na udindo wolalikila uthenga wabwino. (Mac. 4:20) Ndiyeno tiyelekezele kuti mlongo, amene mwamuna wake na wosakhulupilila, wakonza zakuti apite mu ulaliki. Koma mwamuna wakeyo afuna kuti mlongoyo akhale panyumba. Mwamunayo waona kuti iye na mkazi wake sakhala na nthawi yokwanila yoceza, ndipo afuna kuti iwo acitileko pamodzi zinthu zina monga banja. Mlongoyo angaganizile mfundo zofunika za m’Baibo monga mfundo yakuti tifunika kumvela Mulungu na yakuti tifunika kupanga ophunzila. (Mat. 28:19, 20; Mac. 5:29) Koma iye afunikanso kuganizila mfundo yakuti mkazi afunika kukhala wogonjela komanso wololela. (Aef. 5:22-24; Afil. 4:5) Angafunikenso kuganizila ngati mwamuna wakeyo nthawi zonse amamuletsa kupita muulaliki, kapena ni tsiku limenelo cabe limene wam’pempha kuti asapite. Kukamba zoona, timafunika kukhala oganiza bwino pamene ticita cifunilo ca Mulungu ndiponso pamene tiyesetsa kukhala na cikumbumtima cabwino.

JUNE 26–JULY 2

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZARA 1–3

“Lolani Yehova Kuti Akugwilitseni Nchito”

w22.03 14 ¶1

Kodi Mumatha Kuona Zimene Zekariya Anaona?

AYUDA anakondwela ngako pamene Yehova “analimbikitsa mtima wa Koresi mfumu ya Perisiya,” kumasula Aisiraeli amene anali mu ukapolo ku Babulo kwa zaka zambili. Mfumuyo inalengeza kuti Ayuda abwelele kudziko la kwawo, “n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli.” (Ezara 1:1, 3) Cinali cilengezo cokondweletsa kwambili! Izi zinatanthauza kuti kulambila Mulungu woona kunali kudzabwezeletsedwa m’dziko limene iye anapatsa anthu ake.

w17.10 26 ¶2

Magaleta na Cisoti Cacifumu Zimakutetezani

Zekariya anali kudziŵa kuti Ayuda amene anacoka ku Babulo kupita ku Yerusalemu anali na cikhulupililo colimba. Amenewo ni anthu amene ‘Mulungu woona analimbikitsa mitima yawo’ kuti asiye nyumba zawo na mabizinesi awo. (Ezara 1:2, 3, 5) Iwo anacoka m’dziko limene anajaila kukhalamo n’kupita kukakhala m’dziko limene ambili a iwo anali asanalionepo. Akanakhala kuti anali kuona nchito yomanga kacisi wa Yehova monga yosafunika, sembe sanayende mtunda wautali wa makilomita pafupi-fupi 1,600, kupitila m’dziko loopsa.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w06 1/15 19 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezara

1:3-6. Monga Aisrayeli ena amene anatsalila ku Babulo, pali a Mboni za Yehova ambili amene sangathe kucita utumiki wa nthawi zonse kapena kutumikila kumadela komwe kulibe olalikila okwanila. Komabe amacilikiza na kulimbikitsa anthu amene angathe kutelo, ndipo mwa kufuna kwawo, amapeleka thandizo lopititsa patsogolo nchito yolengeza Ufumu na kupanga ophunzila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani