Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
JULY 3-9
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZARA 4-6
“Musalowelele Nchito Yomanga Nyumba ya Mulungu”
Kodi Mumatha Kuona Zimene Zekariya Anaona?
13 Nchito yomanganso kacisi inali italetsedwa. Komabe, amuna oikidwa kuti atsogolele—Mkulu wa Ansembe Yesuwa (Yoswa), komanso Bwanamkubwa Zerubabele—‘anayamba kumanganso nyumba ya Mulungu.’ (Ezara 5:1, 2) Mwina Ayuda ena anaona kuti kucita zimenezo kunali kosathandiza. Nchito yomanga kacisi sikanabisika kwa adani, amene anayesetsa kucita zonse zotheka kuti ailepheletse basi. Amuna aŵiliwo apaudindo, Yoswa na Zerubabele, anayenela kukhala na citsimikizo cakuti Yehova adzawathandiza. Ndipo iwo anakhala naco. Motani?
w86 2/1 29, bokosi ¶2-3
Maso a Yehova “Anali pa Akulu”
Ayuda otsala ku Babulo atabwelela, panapita zaka 16 asanayambenso kumanga kacisi. Mneneli Hagai na mneneli Zekariya anakwanitsa kulimbikitsa Ayudawo kuti asakhale aulesi, ndipo nchito yomanganso kacisi wa Yehova inayambilanso. Koma posakhalitsa akulu-akulu a boma la Perisiya analetsa nchitoyo. Iwo anafunsa kuti “Kodi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi”?—Ezara 5:1-3.
Kuyankha funso limeneli kunali kovuta cifukwa akuluwo akanacita mantha, nchito yomanganso kacisi ikanaimila pomwepo. Komanso iwo akanakwiyitsa akulu a bomawo, nchito yomanga ikanaletsedwa. Conco akuluwo (mosakayikila motsogoleledwa na bwanamkubwa Zerubabele komanso mkulu wa ansembe Yesuwa) anayankha mosamala komanso mogwila mtima. Iwo anakumbutsa akulu-akulu a bomawo za lamulo lakale-kale la mfumu Koresi lopatsa Ayuda cilolezo copitiliza nchitoyo. Podziŵa kuti malamulo a Aperisi sanali kusinthidwa, akulu-akulu a bomawo mwanzelu sanatsutse lamulo la mfumulo. Nchitoyo inapitilizabe mpaka pamene mfumu Dariyo nayonso inapeleka lamulo lake lakuti nchitoyo isaimitsidwe!—Ezara 5:11-17; 6:6-12.
Kodi Mumatha Kuona Zimene Zekariya Anaona?
7 Kusintha kunabweletsa mpumulo kwa omanga kacisi. N’kusintha kotani? Mu 520 B.C.E., Dariyo Woyamba anakhala mfumu ya Perisiya. M’caka caciŵili ca ulamulilo wake, iye anazindikila kuti ciletso cimene cinaikidwa pa nchito yomanga kacisi n’cosagwilizana na malamulo. Conco, analamula Ayuda kuti atsilize nchito yawo. (Ezara 6:1-3) Nkhaniyo inadabwitsa aliyense. Koma mfumuyo inacita zoposa pamenepo. Inalamula kuti anthu owazungulila aleke kusokoneza nchito yomangayo, komanso kuti apeleke ndalama na zinthu zina zothandizila pa nchitoyo. (Ezara 6:7-12) Cotulukapo n’cakuti Ayuda anatsiliza kumanga kacisi mu 515 B.C.E., pambuyo pa zaka zinayi.—Ezara 6:15.
Kodi Mumatha Kuona Zimene Zekariya Anaona?
16 Yehova amapelekanso malangizo kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Nthawi zina, kapoloyo angapeleke malangizo amene sitingawamvetsetse. Mwacitsanzo, mwina tingapatsidwe malangizo acindunji otithandiza kukapulumuka ngozi yacilengedwe, imene tingaone kuti singacitike kudela lathu. Kapena mwina tingaone kuti kapolo akuumitsa kwambili zinthu pa nthawi ya mlili. Kodi tingacite ciyani tikaona kuti malangizo amene tapatsidwa ni osathandiza? Tiyenela kuganizila mmene Aisiraeli anapindulila cifukwa colabadila malangizo amene anapatsidwa kupitila mwa Yoswa na Zerubabele. Tingaganizilenso nkhani zina za m’Baibo zimene timaŵelenga. Nthawi zina, anthu a Mulungu amalandila malangizo amene mkaonedwe kathu ka umunthu angaoneke osathandiza. Koma pambuyo pake, amakhala opulumutsa moyo.—Ower. 7:7; 8:10.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w93 6/15 32 ¶3-5
Kodi Mungakhulupilile Baibulo?
Kobililo linasulidwa ku Tariso, mzinda wa kum’mwela koma cakum’maŵa kwa mbali yomwe tsopano ili ku Turkey. Kobilili linasulidwa muulamulilo wa kazembe Mazaeus wa ku Perisiya m’zaka za zana lachinayi B.C.E. Ilo limachula iye kukhala kazembe wa dera la “Tsidya la Mtsinje,” kutanthauza mtsinje wa Firate.
Koma kodi n’cifukwa ninji mawuwo ali okondweletsa? Cifukwa cakuti mudzapeza mawu ofananawo m’Baibo lanu. Lemba la Ezara 5:6–6:13 limanena za kulembelana makalata kwa pakati pa Mfumu Dariyo ya Perisiya na kazembe wochedwa Tatenai. Nkhani yake inali yonena za kumanganso kacisi wa ku Yerusalemu kwa Ayuda. Ezara anali mlembi waluntha m’Cilamulo ca Mulungu, ndipo mungamuyembekezele kukhala wacindunji, na wolondola m’zimene analemba. Mudzaona pa lemba la Ezara 5:6 ndi 6:13 kuti anacha Tatenai kukhala “kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo.”
Ezara analemba zimenezo ca m’ma 460 B.C.E., zaka pafupifupi 100 kobililo lisanasulidwe. Inde, pali anthu ena amene angaganize kuti kuchulidwa kwa nduna yaboma yamakedzanako kulibe nchito. Koma ngati mungakhulupilile olemba Baibo pankhani zazing’ono conco, kodi zimenezi siziyenela kuwonjezela cikhulupililo canu m’zinthu zinanso zimene analemba?
JULY 10-16
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZARA 7-8
“Khalidwe la Ezara Linacititsa Kuti Yehova Alemekezeke”
w00 10/1 14 ¶8
Kuphunzila—N’kothandiza Komanso Kokondweletsa
8 Inde, kukonda kwathu Mawu a Yehova kuyenela kucokela mumtima, phata la malingalilo onse. Tiyenela kumaganizilabe za ndime zina zomwe tangoziŵelenga kumene. Tiyenela kulingalila mozama mfundo zakuya zauzimu, kuziloŵetsa mumtima mwathu, na kuzisinkhasinkha. Zimenezi zimafuna kuganiza modekha ndiponso pemphelo. Monga Ezara, tifunikila kukonzekeletsa mitima yathu tisanayambe kuŵelenga na kuphunzila Mawu a Mulungu. Ponena za Ezara, Baibo imati: “Popeza Ezara anakonza mtima wake kuti aphunzile cilamulo ca Yehova ndi kucicita ndiponso kuti aphunzitse mu Isiraeli malamulo ndi cilungamo.” (Ezara 7:10) Onani zolinga zitatu zomwe Ezara anakonzekeletsela mtima wake: kuphunzila, kuzigwilitsa nchito payekha, ndi kuphunzitsa ena. Tiyenela kutsanzila citsanzo cake.
si 75 ¶5
Buku la m’Baibo la Nambala 13—1 Mbiri
5 Palibe wina amene anali woyenelela bwino kuposa Ezara kulemba mbili yoona na yolondola imeneyi, “cifukwa Ezara anakonza mtima wake kuti aphunzile cilamulo ca Yehova ndi kucicita ndiponso kuti aphunzitse mu Isiraeli malamulo ndi cilungamo” (Ezara 7:10) Yehova anam’thandiza na mzimu wake woyela. Wolamulila wamphamvu padziko lonse waciperisiya anaona nzelu yaumulungu mwa Ezara, ndipo anam’patsa ulamulilo waukulu m’cigawo ca Yuda. (Ezara 7:12-26) Popeza Ezara anali na ulamulilo wocokela kwa Mulungu komanso kwa mfumu, analemba bukuli pogwilitsa nchito zolemba zodalilika zimene zinalipo pa nthawiyo.
it-1 1158 ¶4
Kudzicepetsa
Kumathandiza Munthu Kupeza Citsogozo Coyenela. Munthu amene amadzicepetsa pamaso pa Mulungu, amatsogoleledwa na Yehova. Ezara anali na udindo waukulu wotsogolela Ayuda kucoka ku Babulo kupita ku Yerusalemu. Pa gululo panali amuna oposa 1,500 kupatulapo ansembe, Anetini komanso akazi na ana. Kuwonjezela apo, anthuwo ananyamula golide na siliva woculuka wokakongoletsela kacisi ku Yerusalemu. Iwo anafunika citetezo pa ulendowo. Koma Ezara sanafune kupempha mfumu ya Perisiya kuti imupatse gulu la asilikali owapelekeza, cifukwa kucita zimenezo kukanaonetsa kuti iye akudalila mphamvu za anthu. Komanso m’mbuyomo Ezara anali atauza mfumu kuti: “Dzanja la Mulungu wathu lili ndi onse om’funafuna kuti awacitile zabwino.” Conco Iye analamula anthu kuti asale kudya kuti adzicepetse pamaso pa Yehova. Iwo anapemphela kwa Mulungu, iye anamva ndipo anawateteza kwa adani awo m’njila moti anayenda bwino ulendo wawo wowopsawo mpaka kukafika ku Yerusalemu (Ezara 8:1-14, 21-32) Nayenso mneneli Danieli ali ku ukapolo ku Babulo anayanjidwa kwambili na Mulungu moti anam’tumizila mngelo kukamuonetsa masomphenya. Izi zinacitika cifukwa cakuti Danieli anadzicepetsa pamaso pa Mulungu, pofuna kuti amutsogolele na kum’thandiza kumvetsa zimene anali kuwelenga.—Dan. 10:12.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06 1/15 19 ¶10
Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezara
7:28–8:20—N’cifukwa ciyani Ayuda ambili ku Babulo sanafune kupita naye Ezara ku Yerusalemu? Ngakhale kuti panali patadutsa zaka 60 gulu loyamba la Ayuda litabwelela kwawo, ku Yerusalemu kunali anthu ocepa cabe. Munthu wobwelela ku Yerusalemu anayenela kukayamba moyo watsopano wokhala na zovuta ndiponso zowopsa zosiyanasiyana. Panthawi imeneyo ku Yerusalemu kunalibe moyo wapamwamba umene Ayuda omwe zinthu zinali kuwayendela bwino ku Babulo, akanaukhumbila. Komanso ulendo wake unali wowopsa. Anthu obwelela ku Yerusalemuwo anayenela kukhala na cikhulupililo colimba mwa Yehova, cangu pa kulambila koona, ndiponso anayenela kulimba mtima kuti asamuke. Ngakhale Ezara mwiniwakeyo anadzilimbikitsa cifukwa dzanja la Yehova linali naye. Ezara analimbikitsa mabanja 1,500, omwe mwina anali anthu 6,000, motelo nawonso anasamuka. Ezara anapitilizabe kulimbikitsa anthu ndipo Alevi 38 na Anetini 220 anasamukanso.
JULY 17-23
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZARA 9-10
“Zotulukapo Zowawa za Kusamvela”
w06 1/15 20 ¶1
Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezara
9:1, 2—Kodi kukwatilana na anthu a maikowa kunali kowopsa motani? Mtundu wobwezeletsedwawo unayenela kukhala cimake ca olambila Yehova mpaka Mesiya atabwela. Kukwatilana na anthu a mitundu ina kukanasokoneza kulambila koona. Popeza kuti anthu ena anali atakwatilana na a mitundu yolambila mafano, mtundu wonsewo ukanatha kutengela zocita za anthu akunjawa. Motelo, kulambila koona kukanathelatu padziko lonse. Conco kodi Mesiya akanabwela ku mtundu uti? N’cifukwa cake Ezara anakhumudwa kwambili ataona zimene zinali kucitikazo.
w09 10/1 10 ¶6
Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizicita Ciyani?
Mulungu adzatidalitsa kwambili ngati timamumvela mwakufuna kwathu. Mose analemba kuti: “Muzisunga malamulo a Yehova ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lelo, kuti zinthu zikuyendeleni bwino.” (Vesi 13) Inde, ciliconse cimene Yehova amatiuza kuti tizicita cimakhala cotikomela kapena kuti cotithandiza. Conco, sicingatilepheletse kusangalala. Baibo imati: “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) N’cifukwa cake anatipatsa malamulo amene angatithandize kuti tikhale na moyo wabwino kwambili. (Yesaya 48:17) Kucita zonse zimene Yehova amafuna kumatithandiza kupewa zokhumudwitsa zambili panopa ndipo kudzatithandiza kuti m’tsogolo, tidzapeze madalitso ambili mu ulamulilo wa Ufumu wake.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06 1/15 20 ¶2
Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezara
10:3, 44—N’cifukwa ciyani ana anawacotsa pamodzi na amayi awo? Anawo akanatsalila, akazi ocotsedwawo akanatha kudzabwelelanso mosavuta pofuna anawo. Komanso, ana aang’ono nthawi zambili amafuna cisamalilo ca mayi awo.
JULY 24-30
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 1-2
“Nthawi Yomweyo N’napemphela”
w08 2/15 3 ¶5
Ikani Yehova Patsogolo Panu Nthawi Zonse
5 Nthawi zina tingafunikile kupempha thandizo la Mulungu mwacidule. Tsiku lina, Mfumu Aritasasita ya Perisiya inaona kuti Nehemiya, yemwe anali wopelekela cikho, anali wacisoni. Mfumuyo inafunsa kuti: “Ndiye ukufuna ciyani?” Nthawi yomweyo Nehemiya anapemphela kwa Mulungu wakumwamba. Apa n’zoonekelatu kuti sizikanatheka Nehemiya kupeleka pemphelo lalitali la mumtima. Koma Mulungu anayankhabe pemphelo lake, cifukwa mfumuyo inathandiza Nehemiya kuti amange linga la Yerusalemu. (Ŵelengani Nehemiya 2:1-8.) Zoonadi, Mulungu amayankha pemphelo ngakhale litakhala lacidule na la mumtima.
be 177 ¶4
Kulankhula Kucokela mu Mtima
Ngati mwafunsidwa mosayembekezela kuti mupeleke zifukwa pankhani yokhudza cikhulupililo canu, n’ciyani cingakuthandizeni kulankhula mawu ogwila mtima? Tengelani citsanzo ca Nehemiya, amene anapemphela mu mtima asanayankhe funso locokela kwa Mfumu Aritasasita. (Neh. 2:4) Mukatelo, msangamsanga konzani autilaini ya m’maganizo. Mungatsatile masitepe ofunikila aŵa: (1) Sankhani mfundo imodzi kapena ziŵili zimene mukufuna kufotokoza (mfundozo zingakhale zimene zimapezeka m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba) (2) Sankhani malemba amene mukufuna kugwilitsa nchito ngati maziko a mfundo zanu. (3) Konzani mmene muyambile nkhani yanu mosamala kuti wofunsayo akhale na cidwi comvetsela. Pamenepo yambani kulankhula.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w86 2/15 25
Kulambila Koona Kupambana
Ayi, cifukwa kwa nthawi yaitali, Nehemiya anali kupemphela “usana ndi usiku” cifukwa ca kuwonongeka kwa Yerusalemu. (Neh. 1:4, 6) Atapatsidwa mwayi wouza mfumu Aritasasta cifuno cake comanganso mpanda wa Yerusalemu, Nehemiya anapemphelanso. Panthawiyo, iye anali kucita zinthu zimene anali atacitapo kale mobweleza-bweleza. Yehova anamva pemphelo la Nehemiya, ndipo zotulukapo zake, iye anatumidwa kuti akamangenso mpanda wa Yerusalemu.
Zimene Tiphunzilapo: Nehemiya anadalila Yehova kuti amutsogolele. Nafenso tikafuna kupanga zisankho zazikulu, tiyenela kulimbikila kupemphela na kucita zinthu mogwilizana na citsogozo ca Yehova.—Aroma 12:12.
JULY 31–AUGUST 6
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 3-4
“Kodi Mumaona Kuti Nchito Yamanja si Yokuyenelelani?”
w06 2/1 10 ¶1
Mfundo Zazikulu za M’buku la Nehemiya
3:5, 27. Tisamadzione ngati apamwamba kwambili moti sitingathe kugwila nchito zimene zimaoneka ngati zonyozeka zopititsa patsogolo kulambila koona, monga mmene anachitila Atekowa “ochuka,” kapena kuti apamwamba. M’malo mwake, titsanzile Atekowa omwe sanali ochuka amene anadzipeleka mwa kufuna kwawo.
Kodi Mudzalola Yehova Kukucititsani Kukhala Ndani?
11 Patapita zaka zambili, ana aakazi a Salumu anali pakati pa anthu amene Yehova anawaseŵenzetsa pa nchito yokonzanso mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 2:20; 3:12) Olo kuti atate awo anali kalonga, iwo anadzipeleka kucita nchito yovuta imeneyo, komanso yoika moyo pa ciopsezo. (Neh. 4:15-18) Iwo anali osiyana kwambili ndi anthu ochuka pakati pa Atekowa, amene sanadzicepetse kuti agwile nawo nchitoyo. (Neh. 3:5) Ganizilani cimwemwe cimene ana aakazi a Salumu anakhala naco, pamene nchitoyo inatha m’masiku 52 cabe! (Neh. 6:15) Masiku anonso, pali alongo amene amadzipeleka mwacimwemwe kucita utumiki wapadela, womanga na kukonzanso nyumba zolambilila zopatulidwa kwa Yehova. Thandizo la alongo odzipeleka, aluso, na okhulupilika amenewa ni lofunika kwambili pa nchitoyi.
w04 8/1 18 ¶16
Khalani na Maganizo a Khristu Pankhani ya Kukhala Wamkulu
16 Akhristu onse, ana na akulu omwe, ayenela kuyesetsa kukhala na maganizo a Khristu pankhani ya kukhala wamkulu. Mumpingo mumakhala nchito zosiyanasiyana. Tisamadane nazo tikapemphedwa kugwila nchito zimene zingaoneke ngati nchito wamba. (1 Sam. 25:41; 2 Maf. 3:11) Makolo, kodi mumalimbikitsa ana anu, ang’ono-ang’ono ndiponso acinyamata, kuti azigwila mosangalala nchito iliyonse yomwe apatsidwa, kaya ni pa Nyumba ya Ufumu, pamalo a msonkhano wadela, kapena wacigawo? Kodi amakuonani inuyo mukugwila nchito wamba? M’bale wina amene tsopano akutumikila pa likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova, amakumbukila bwino citsanzo ca makolo ake. Iye anati: “Mmene anali kugwilila nchito yoyeletsa pa Nyumba ya Ufumu kapena pamalo a msonkhano zinanionetsa kuti iwo anali kuona nchitoyo kuti ni yofunika. Nthaŵi zambili anali kudzipeleka kugwila nchito zothandiza pampingo kapena zothandiza abale athu onse, mosaganizila kuti nchitoyo ikuoneka yonyozeka motani. Mtima umenewu wanithandiza kulandila mosanyinyilika nchito iliyonse yomwe napatsidwa pa Beteli pano.”
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06 2/1 9 ¶1
Mfundo Zazikulu za M’buku la Nehemiya
4:17, 18—Kodi munthu angagwile bwanji nchito yomanga na dzanja limodzi? Zimenezi sizingakhale zovuta kwa anthu amene asenza katundu. Akaika katundu pamutu kapena paphewa, anali kugwila katunduyo na dzanja limodzi ndipo “kudzanja lina anali kunyamula mkondo.” Womanga amene anafunikila kugwilitsa nchito manja onse aŵili, ‘anamangilila lupanga lake m’ciuno pamene anali kumanga mpandawo.’ Anali okonzeka kudziteteza adani atawaukila.
AUGUST 7-13
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 5-7
“Nehemiya Anali Kufuna Kutumikila Ena, Osati Kutumikilidwa”
w02 11/1 27 ¶3
Anthu Othandiza Kulambila Koona Akale ndi Amasiku Ano
Nehemiya anathandizila m’zinthu zambili kuwonjezela pa kugwilitsa nchito nthaŵi yake na luso lake lolinganiza zinthu. Anagwilitsilanso nchito cuma cake pothandizila kulambila koona. Anagwilitsila nchito ndalama zake kugula abale ake aciyuda ku ukapolo. Anakongoletsa ndalama zake popanda ciwongola dzanja. Iye ‘sanalemetse’ Ayuda mwa kuwauza kuti azimulipila monga kazembe, zomwe anayenelela kucita. M’malo mwake, iye kunyumba kwake anali kulandila na kudyetsa “amuna okwana 150, pamodzi ndi anthu obwela kwa ife kucokela ku mitundu yotizungulila.” Tsiku lililonse anali kupeleka “ng’ombe imodzi yamphongo, nkhosa zosankhidwa mwapadela 6 ndi mbalame” kwa alendo ake. Kuwonjezela pamenepo, kamodzi pa masiku khumi alionse, iye ankawapatsa “vinyo woculuka wamtundu uliwonse,” zonsezi ankatelo pogwilitsila nchito ndalama za m’thumba mwake.—Neh. 5:8, 10, 14-18.
“Manja Anu Asakhale Olefuka”
16 Yehova analimbitsa dzanja la Nehemiya na anzake kuti agwile nchito yomanga. Anamanga mpanda wa Yerusalemu m’masiku 52 cabe. (Neh. 2:18; 6:15, 16) Nehemiya sanali kungoyang’anila cabe nchito. Iye anagwila nawo nchito yomanganso mpandawo. (Neh. 5:16) Masiku ano, akulu acikondi amatengela citsanzo ca Nehemiya. Ambili amagwila nawo nchito zomanga-manga, kapena kuyeletsa na kukonzanso Nyumba ya Ufumu imene amasonkhanamo. Kuwonjezela apo, akulu amalimbikitsanso manja amene ali lende na onse amene ali na nkhawa mwa kulalikila nawo na kucita maulendo aubusa.—Ŵelengani Yesaya 35:3, 4.
w00 2/1 32
Kodi Yehova Adzakukumbukilani Motani?
Nthaŵi zonse, Baibo limasonyeza kuti kwa Mulungu, ‘kukumbukila’ kumatanthauza kucitapo kanthu motsimikiza. Mwacitsanzo, dziko lapansi litamizidwa na cigumula kwa masiku 150, “Mulungu anakumbukila Nowa . . . , anacititsa cimphepo kuwomba padziko lapansi, ndipo madzi anayamba kucepa.” (Gen. 8:1) Patapita zaka mahandiledi, Samsoni, atacititsidwa khungu komanso kumangidwa na Afilisti, anapemphela kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, conde, ndikumbukileni ndi kundipatsa mphamvu kamodzi kokhaka.” Yehova anam’kumbukila Samsoni mwa kum’patsa mphamvu zoposa zacibadwa kotelo kuti athe kubwezela yekha cilango pa adani a Mulungu. (Ower. 16:28-30) Ponena za Nehemiya, Yehova anadalitsa zoyesayesa zake, ndipo kulambila koona kunabwezeletsedwa m’Yerusalemu.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w07 7/1 30 ¶15
“Pitilizani Kugonjetsa Coipa mwa Kucita Cabwino”
15 Cacitatu, adani a Nehemiya anagwilitsa nchito Semaya, Mwisiraeli wopanduka, kuti acititse Nehemiya kuphwanya Malamulo a Mulungu. Semaya anauza Nehemiya kuti: “Tipangane nthawi kuti tikakumane kunyumba ya Mulungu woona, m’kacisi, ndi kutseka zitseko za kacisiyo, pakuti akubwela kudzakupha.” Semaya anauza Nehemiya kuti moyo wake uli pangozi koma akhoza kupulumuka mwa kubisala m’kacisi. Koma popeza Nehemiya sanali wansembe, akanacimwa ngati akanabisala m’nyumba ya Mulungu. Kodi Nehemiya anaswa Malamulo a Mulungu cifukwa cofuna kupulumutsa moyo wake? Nehemiya anayankha kuti: “Kodi munthu ngati ine angalowe m’kacisi ndi kukhala ndi moyo? Ine sindikalowamo!” N’cifukwa ciyani Nehemiya sanagwele m’msampha umene anam’chela? Cifukwa anazindikila kuti ngakhale Semaya anali Mwisiraeli mnzake, “sanatumidwe ndi Mulungu.” Ndipotu, mneneli woona sangamuuze kuti aphwanye Malamulo a Mulungu. Nehemiya sanalolenso kuti agonjetsedwe na anthu oipa amene ankam’tsutsa. Patapita nthawi yochepa anatha kunena kuti: “Nchito yomanga mpanda inatha pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli.”—Neh. 6:10-15; Num. 1:51; 18:7.
AUGUST 14-20
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 8-9
“Cimwemwe Cimene Yehova Amapeleka Ndico Malo Anu Acitetezo”
w13 10/15 21 ¶2
Zimene Tingaphunzilepo pa Pemphelo Lokonzedwa Bwino
2 Ayuda anacita msonkhano umenewu patapita mwezi umodzi kucokela pamene anamaliza kumanganso mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 6:15) Anthu a Mulungu anamaliza kugwila nchito imeneyi pambuyo pa masiku 52 cabe, ndipo atamaliza anayamba kusamalila zosoŵa zawo za kuuzimu. Pa tsiku loyamba la mwezi wotsatila wa Tishiri, iwo anasonkhana m’bwalo lalikulu kuti amvetsele pamene Ezara na Alevi ena anali kuŵelenga na kufotokozela Cilamulo ca Mulungu. (Cithunzi 1) Mabanja onse, kuphatikizapo onse “amene akanatha kumvetsela ndi kuzindikila,” anaimilila na kumvetsela “kuyambila m’mawa mpaka masana.” Cimeneci n’citsanzo cabwino kwa ife masiku ano amene timasonkhana m’Nyumba za Ufumu zabwino. Kodi nthawi zina timayamba kuganizila zinthu zina zosafunika pamene tili pamisonkhano? Ngati n’conco, kumbukilani citsanzo ca Aisiraeli akale amene anamvetsela na kusinkha-sinkha zimene anamva, ndipo anayamba kulila cifukwa cakuti mtundu wawo unalephela kumvela Cilamulo ca Mulungu.—Neh. 8:1-9.
w07 7/15 22 ¶9-10
Kodi ‘Mupitiliza Kuyenda mwa Mzimu’?
9 Mawu akuti cimwemwe amatanthauza cisangalalo cacikulu. Yehova ni “Mulungu wacimwemwe.” (1 Tim. 1:11; Sal. 104:31) Mwana wake amakondwela kucita cifunilo cha Atate wake. (Sal. 40:8; Aheb. 10:7-9) Ndipo “cimwemwe cimene Yehova amapeleka ndico malo [athu] acitetezo.”—Neh. 8:10.
10 Tikamacita cifunilo ca Mulungu, ngakhale m’nthawi ya mavuto, cisoni, kapena cizunzo, timakhala osangalala cifukwa ca cimwemwe cimene Mulungu amatipatsa. Timasangalala ‘tikamudziŵadi Mulungu.’ (Miy. 2:1-5) Timakhala pa ubale wosangalatsa na Mulungu ngati timamudziŵa bwino ndiponso ngati timamukhulupilila na kukhulupililanso nsembe ya dipo ya Yesu. (1 Yoh. 2:1, 2) Ndifenso acimwemwe cifukwa cakuti tili na ubale weniweni padziko lonse. (Zef. 3:9; Hag. 2:7) Ciyembekezo cathu ca Ufumu na nchito yolalikila uthenga wabwino zimatipatsanso cimwemwe. (Mat. 6:9, 10; 24:14) Ciyembekezo cathu ca moyo wosatha cimatipatsanso cimwemwe. (Yoh. 17:3) Popeza tili na ciyembekezo cabwino cimeneci, tiyenela “kukhala osangalala basi.”—Deut. 16:15
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 145 ¶2
Ciaramu
Zaka zingapo Ayuda atabwelako ku ukapolo wa ku Babulo, wansembe Ezara anaŵelenga buku la Cilamulo kwa Ayuda amene anasonkhana ku Yerusalemu. Ndipo Alevi anali kufotokozela anthuwo Cilamuloco. Nehemiya 8:8 stating: “Iwo anapitiliza kuŵelenga bukulo mokweza. Anapitiliza kuwelenga cilamulo ca Mulungu woona, kucifotokozela ndi kumveketsa tanthauzo lake. Iwo anapitiliza kuthandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene anali kuŵelenga.” Mwina pofotokozela kapena kumveketsa tanthauzo la Cilamulo, Aleviwo anali kumasulila mawu a Ciheberi m’Ciaramu, cifukwa n’kutheka kuti Aheberi anaphunzila Ciaramu pamene anali ku Babulo. Komanso n’zoonekelatu kuti Aleviwo anali kufotokozela zimene zinali kuŵelengedwazo n’colinga cakuti Ayuda amvetsetse bwino tanthauzo la zimene zinali kuŵelengedwa, ngakhale kuti anali kumva Ciheberi.
AUGUST 21-27
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 10-11
“Anadzimana Zinazake Cifukwa Comvela Yehova”
w98 10/15 22 ¶13
Yerusalemu Woyeneleladi Dzina Lake
13 “Pangano lokhazikika” lomwe linapangidwa m’tsiku la Nehemiya linakonzekeletsa anthu akale a Mulungu kaamba ka kupelekedwa kwa linga la Yerusalemu. Koma panali nkhani inanso yofunabe chisamalilo chamwamsanga. Tsopano atazingidwa ndi linga lalikulu lokhala ndi zipata 12, Yerusalemu anafunikila kukhala na anthu oculukilapo. Ngakhale kuti munali kukhala Aisrayeli ena, “mzindawo unali wotakasuka ndi waukulu. Mkati mwake munali anthu ocepa ndipo sanamangemo nyumba.” (Neh. 7:4) Kuti athetse vutoli, anthu “anacita maele kuti apeze munthu mmodzi mwa anthu 10 alionse woti akakhale m’Yerusalemu, mzinda woyela.” Kutsatila makonzedwe ameneŵa mofunitsitsa kunasonkhezela anthu kudalitsa “amuna onse amene anadzipeleka kukakhala m’Yerusalemu.” (Neh. 11:1, 2) Cimeneci n’citsanzo cabwino kwambili kwa olambila oona lelolino amene mikhalidwe yawo imawalola kusamukila kumene kufunika thandizo la Akhristu ofikapo!
w86 2/15 26
Kulambila Koona Kupambana
Munthu akasiya coloŵa cake n’kusamukila mumzinda wa Yerusalemu, anafunika kuwonongelapo ndalama kuti ayambenso umoyo watsopano, komanso panali zovuta zina. Kuwonjezela apo, anthu okhala mumzindawo anali pa ciwopsezo cokumana na mavuto ena. Pozindikila zimenezi, ena anawayamikila anthu amene anadzipeleka kusamukila mumzinda wa Yerusalemu, ndipo mosakayikila anapemphela kwa Yehova kuti awadalitse.
Mulungu Amakonda Anthu Okhulupilika
15 Pamene tinadzipeleka kwa Yehova, tinalonjeza kuti tidzacita cifunilo cake zivute zitani. Tinadziŵa kuti nthawi zina zidzakhala zovuta kusunga lonjezo limeneli. Koma kodi timacita ciani tikapemphedwa kucita zinthu zina zimene ifeyo sitikufuna? Ngati tikhala olimba mtima ndi kumvela Mulungu ndi mtima wonse, ndiye kuti tikusunga lonjezo lathu. Nthawi zina, tingakumane ndi mavuto cifukwa ca kudzipeleka kwathu, koma tikamvela Yehova, iye amatidalitsa kwambili. (Mal. 3:10) Nanga bwanji za mwana wa Yefita? Kodi anacita ciani ndi lonjezo la atate wake?
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06 2/1 11 ¶1
Mfundo Zazikulu za M’buku la Nehemiya
10:34—N’cifukwa ciyani anthu anali kufunika kupeleka nkhuni? M’Cilamulo ca Mose munalibe lamulo la copeleka ca nkhuni. Koma panthawiyi anayenela kutelo. Cifukwa cake n’cakuti panafunika nkhuni zambili zowochela nsembe pa guwa. Zikuoneka ngati panalibe Anetini okwanila, akapolo a pakacisi omwe sanali Aisrayeli. Conco, anacita maele otsimikiza kuti nkhuni zizipezeka nthawi zonse.
AUGUST 28–SEPTEMBER 3
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 12-13
“Khalani Okhulupilika kwa Yehova Posankha Mabwenzi”
it-1 95 ¶5
Aamoni
Tobiya atacotsedwa pa kacisi, Aisiraeli anaŵelenga na kutsatila lamulo la Mulungu la pa Deuteronomo 23:3-6 loletsa Aamoni na Amowabu kuloŵa mumpingo wa Isiraeli. (Neh. 13:1-3) Lamulo limeneli linali litaikidwa zaka 1,000 m’mbuyomo cifukwa Aamoni na Amowabu anakana kuthandiza Aisiraeli pamene anali pafupi kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Lamuloli linatanthauza kuti mwalamulo anthu a mitundu imeneyo sanaloledwe kukhala mbali ya mtundu wa Isiraeli, ndipo sakanapatsidwa mwayi na ufulu uliwonse umene Aisiraeli anali nawo. Komabe sikuti lamuloli linatanthauza kuti zivute zitani, Muamoni kapena Mmowabu aliyense sakanayanjana na Aisiraeli kapena kukhala pakati pawo na kulandila nawo madalitso ocokela kwa Mulungu. Citsanzo ni Zeleki Muamoni, mmodzi wa asilikali olimba mtima a Davide amene tamuchulapo kale, komanso Rute mkazi wacimowabu.—Ru 1:4, 16-18.
w13 8/15 4 ¶5-6
Mwapatulidwa
5 Ŵelengani Nehemiya 13:4-9. Si zopepuka kukhalabe oyela cifukwa cakuti makhalidwe oipa ali paliponse. Ganizilani za Eliyasibu ndi Tobia. Eliyasibu anali mkulu wa ansembe, Tobia anali waciamoni ndipo anali kugwila nchito mu ofesi ya mfumu ya Perisiya ku Yudeya. Tobia ndi anzake anali kufuna kulepheletsa Nehemiya kumanga mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 2:10) Aamoni anali kuletsedwa kulowa m’mabwalo a kacisi. (Deut. 23:3) Koma n’cifukwa ciani mkulu wa ansembe anakonzela Tobia malo m’cipinda codyelamo ca pakacisi?
6 Tobia anali wacibale wa Eliyasibu. Tobia ndi mwana wake wamwamuna Yehohanani anakwatila akazi aciyuda ndipo Ayuda ambili anali kutamanda kwambili Tobia. (Neh. 6:17-19) Manase mdzukulu wa Eliyasibu, anakwatila mwana wa Sanibalati amene anali Msamariya, mnzake kwambili wa Tobia. (Neh. 13:28) Mkulu wa ansembe Eliyasibu, analola Tobia munthu wosakhulupilila Mulungu ndi wotsutsa kumuuza zocita mwina cifukwa cakuti anthu amenewa anali pacibale. Koma Nehemiya anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova mwa kuponya katundu yense wa Tobia kunja kwa cipinda codyelamo.
w96 3/15 16 ¶6
Kupambana Ciyeso ca Kukhulupilika
6 Ngati tili okhulupilika kwa Yehova Mulungu, tidzapeŵa kukhala paubwenzi na onse amene ni adani ake. N’cifukwa cake wophunzila Yakobo analemba kuti: “Acigololo inu, kodi simukudziŵa kuti kucita ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu? Conco, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi la dziko akudzisandutsa mdani wa Mulungu.” (Yak. 4:4) Tifunika kukhala okhulupilika monga Mfumu Davide amene anati: “Inu Yehova, pajatu ine ndimadana ndi anthu amene amadana nanu kwambili, Ndipo anthu okupandukilani ndimanyansidwa nawo. Ndimadana nawo kwambili. Kwa ine akhala adani enieni”. (Sal. 139:21, 22) Sitifunika kumaceza na ocimwa dala alionse, pakuti tilibe nawo cocita. Kodi kukhulupilika kwathu kwa Mulungu kungatithandize bdwanji kupewa kuceza na mdani aliyense wotelo wa Yehova, kaya maso na maso kapena kupyolela pawailesi yakanema?
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 452 ¶9
Nyimbo
Kuimba kunali kofunika kwambili pa Kacisi. Malemba ambili amacitila umboni zimenezi kuti oimba “sanali kupatsidwa nchito zina” zimene Alevi ena anali kucita kuti aike maganizo pa nchito yawo na kuigwila mofikapo. (1Mbiri 9:33) Kuwonjezela apo, Baibo imawatchula paokha kuti oimba osati monga Alevi onse pa anthu amene anamasulidwa kucoka ku Babulo, poonetsa kuti linali gulu lapadela. (Ezara 2:40, 41) Ndipo ngakhale lamulo la mfumu Aritasasita (Longimanasi) linati oimbawo asamakhome “msonkho uliwonse umene munthu amakhoma, msonkho wakatundu, kapena msonkho wapanjila.” (Ezara 7:24) Pambuyo pake, Mfumuyo inalamula kuti pakhale “dongosolo loti aziwapatsa thandizo tsiku lililonse malinga ndi zofunikila za tsikulo.” Ngakhale kuti Aritasasita ndiye analamula zimenezi, zioneka kuti Ezara ndiye anapeleka lingalilo limeneli cifukwa ca mphamvu zimene anapatsidwa na Aritasasitayo (Ne 11:23; Ezr 7:18-26) Conco m’pomveka kuti, ngakhale kuti oimba onse anali Alevi Baibo imaonetsa kuti linali gulu lapadela powatchula paokha kuti “oimba ndi Alevi.”—Neh 7:1; 13:10.