LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr23 September masa. 1-13
  • Malifalensi a Kabuku ka “Umoyo na Utumiki”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka “Umoyo na Utumiki”
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2023
  • Tumitu
  • SEPTEMBER 4-10
  • SEPTEMBER 11-17
  • SEPTEMBER 18-24
  • SEPTEMBER 25–OCTOBER 1
  • OCTOBER 2-8
  • OCTOBER 9-15
  • OCTOBER 16-22
  • OCTOBER 23-29
  • OCTOBER 30–NOVEMBER 5
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2023
mwbr23 September masa. 1-13

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

SEPTEMBER 4-10

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 1-2

“Yesetsani Kukhala Odziceptsa Monga Esitere”

w17.01 25 ¶11

Mukhoza Kukhalabe Wodzicepetsa Ngakhale pa Ciyeso

11 Komanso, kuyamikilidwa kapena kutamandidwa mopambanitsa kungabweletsenso ciyeso pa kudzicepetsa kwathu. Ganizilani mmene Esitere anakhalilabe wodzicepetsa pamene zinthu zinamuyendela bwino kopambana. Ngakhale kuti iye anali wokongola kale mocititsa kaso, anam’samalila ndi kum’konzekeletsa kwa caka conse. Tsiku na tsiku anali kuyanjana ndi atsikana ambili ocokela kumadela onse a ufumu wa Peresiya. Onse anali pa mpikisano wa mbeta kuti mfumu isankhepo mmodzi. Ngakhale n’conco, Esitere anakhalabe waulemu ndi wodzicepetsa. Ngakhale pamene mfumu inamusankha kukhala mfumukazi yake, iye sanadzitukumule kapena kunyadila ena ayi.—Esitere 2:​9, 12, 15, 17.

ia 130 ¶15

Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

15 Ndiyeno nthawi itakwana yoti Esitere akaonekele kwa mfumu, anapatsidwa ufulu woti anene ciliconse cimene akufuna kuti am’patse, mwina kuti awonjezele kudzikongoletsa. Modzicepetsa, iye sanapemphe ciliconse cowonjezela pa zimene Hegai anachula. (Esitere 2:15) Ayenela kuti anadziŵa kuti kukongola pakokha sikungacititse kuti mfumuyo imusankhe. Anali kudziŵa kuti cofunika kwambiri n’kukhala wodzicepetsa. Koma kodi zimenezi zinathandizadi?

w17.01 25 ¶12

Mukhoza Kukhalabe Wodzicepetsa Ngakhale pa Ciyeso

12 Kudzicepetsa kumatithandizanso kuvala mwaulemu, na kudzikonza mwacikatikati. Anthu amakopeka nafe cifukwa ca “mzimu wabata ndi wofatsa,” osati kudzitama kapena kudzionetsela iyayi. (Ŵelengani 1 Petulo 3:​3, 4; Yer. 9:​23, 24) Ngati tisunga maganizo oipa mumtima mwathu, m’kupita kwa nthawi adzaonekela m’kacitidwe kathu ka zinthu. Mwacitsanzo, kakambidwe kathu cabe ngakhale koonetsa mzimu uja wakuti ‘nili na udindo wapadela ine, nimakhalako na mwayi wodziŵa nkhani zina zacinsinsi, kapena kuti nimadziŵana ndi abale amaudindo akulu-akulu ine.’ Mwinanso timakonda kufotokoza zinthu mwa njila yakuti ciyamikilo cibwele kwambili kwa ife kuposa ena pa zimene zakwanilitsidwa, ngakhale kuti enanso anaikapo maganizo awo. Apanso Yesu anapeleka citsanzo cabwino. Yesu nthawi zambili anali kugwila mawu a m’Malemba Aciheberi. Anacita zimenezo kuti omvela aone kuti anali kukamba zocokela kwa Yehova, osati za m’nzelu zake iyayi.—Yoh. 8:28.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w22.11 31 ¶3-6

Kodi Mudziŵa?

Ocita kafuku-fuku anapeza phale lokhala na dzina la Ciperisiya lakuti Marduka (m’Cinyanja Moredekai). Cioneka kuti iye anali woyang’anila cuma ku Susani. Arthur Ungnad katswili wa mbili yakale, analemba kuti “aka kanali koyamba dzina lakuti Moredekai” kuchulidwa m’zolemba zimene si mbali ya Baibo.

Kucokela pamene Ungnad analemba lipoti lake, akatswili ena a Baibo amasulila mapale masauzande okhala na mawu aciperisiya. Amodzi mwa mapale amenewo ni miyala ya mumzinda wa Persepolis, imene anaipeza pa matongwe a malo osungilako cuma pafupi na mpanda wa mzindawo. Miyala imeneyo inakhalako mu ulamulilo wa Sasita Woyamba. Mawu olembedwa pa miyalayo ali m’cinenelo ca Aelamu, ndipo pakupezeka maina ambili ochulidwa m’buku la Esitere.

Mapale ambili a ku Persepolis amachula munthu wochedwa Marduka, amene anali mlembi pa nyumba yacifumu ku Susani panthawi ya ulamulilo wa Sasita Woyamba. Phale lina linafotokoza kuti Marduka anali womasulila. Izi n’zogwilizana kwambili na zimene Baibo imakamba zokhudza Moredekai. Iye anali nduna imene inali kutumikila m’bwalo la Mfumu Ahasiwero (Sasita Woyamba), ndipo anali kukamba zinenelo ziŵili. Nthawi zonse Moredekai anali kukhala pa cipata ca nyumba yacifumu ku Susani. (Esitere 2:​19, 21; 3:3) Cipata cimeneci cinali cacikulu kwambili moti nduna za panyumba ya mfumu zinali kugwilila nchito pomwepo.

Pali kufanana kwakukulu pakati pa Marduka wochulidwa pa mapalewo, komanso Moredekai wochulidwa m’Baibo. Iwo anakhalako panthawi zofanana komanso pamalo amodzi, ndipo onse anali nduna za mfumu pa malo amodzi. Umboni wonsewu uonetsa kuti Marduka, komanso Moredekai wochulidwa m’buku la Esitere anali munthu mmodzi.

SEPTEMBER 11-17

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 3-5

“Thandizani Ena Kucita Zonse Zimene Angathe Potumikila Yehova”

it-2 431 ¶7

Moredekai

Akana Kugwadila Hamani. Pambuyo pake Mfumu Ahaswero anaika Hamani mu Agagi kukhala nduna yaikulu ndipo analamula kuti onse a pacipata ca mfumu azimugwadila Hamani amene anali atangoikidwa kumene pa udindo wake wapamwamba. Molimba mtima Moredekai anakana kucita zimenezi ndipo anapeleka cifukwa cakuti anali Myuda. (Esitere 3:​1-4) Popeza kuti Moredekai anakana kucita izi pacifukwa cimeneci, zionetsa kuti zinali kukhudza ubale wake na Yehova monga Myuda wodzipatulila. Iye anazindikila kuti kuŵelamila Hamani kunaphatikizapo zambili kuposa cabe kulemekeza munthu cifukwa ca udindo wake waukulu, monga mmene Aisiraeli anacitila kumbuyoko poonetsa ulemu kwa wolamulila wapamwamba. (2 Sam. 14:4; 18:28; 1 Maf. 1:16) Pali cifukwa comveka cimene Moredekai anakanila kuŵelamila Hamani. Zioneka kuti Hamani anali Mwamaleki ndipo Yehova anali atafotokoza momveka bwino kuti adzamenya nkhondo na Aamaleki “kumibadwomibandwo.” (Eks 17:16) Moredekai anacita zimenezi pofuna kukhala wokhulupilika kwa Mulungu osati pofuna kupikisana na olamulila.

it-2 431 ¶9

Moredekai

Anagwilitsidwa Nchito Kupulumutsa Mtundu wa Israeli. Pamene lamulo linapelekedwa lakuti Ayuda onse mu ufumuwo awonongedwe, Moredekai anaonetsa kuti anali kukhulupilila kuti Esitere anaikidwa kukhala Mfumukazi kuti akapulumutse Ayuda panthawi imeneyi. Iye anathandiza Esitere kuzindikila udindo wake waukulu ndipo anamuuza kuti akacondelele mfumu kuti iwakomele mtima Ayuda na kuwathandiza. Ngakhale kuti kucita zimenezo kunaika moyo wake paciopsezo, Esitere anavomela kucita zimene anauzidwa.—Esitere 4:7–5:2.

ia 133 ¶22-23

Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

22 Esitere ayenela kuti anacita mantha kwambili atamva uthengawo. Pamenepa cikhulupililo cake cinayesedwa kwambili. Zimene Esitere anayankha Moredekai zinasonyeza kuti anali na mantha kwambili. Iye anakumbutsa Moredekai za lamulo loletsa kukaonekela kwa mfumu usanaitanidwe lija. Munthu akaphwanya lamulo limeneli anali kuphedwa. Anali kupulumuka pokhapokha ngati mfumu yamuloza ndi ndodo yake yagolide. Ndipo akaganizila zimene zinacitikila Vasiti atakana kukaonekela kwa mfumuyo, Esitere anali kuona kuti ngakhale kuti ni mkazi wa mfumu, n’kutheka kuti mfumuyi singamucitile cifundo. Esitere anauza Moredekai kuti panali patatha masiku 30 asanaitanidwe kuti akaonekele kwa mfumu. Zimenezi ziyenela kuti zinacititsa Esitere kuyamba kukayikila ngati mfumuyi, yomwe sinali kucedwa kupsa mtima, inali kumukondabe.—Esitere 4:​9-11.

23 Moredekai anayankhanso Esitere na mawu amphamvu kuti cikhulupililo cake cilimbe. Anamutsimikizila kuti ngati sangacitepo kanthu, cipulumutso ca Ayuda cicokela kwina. Koma kodi Esitere akanapulumuka ngati lamulo loti Ayuda aphedwe likanayamba kugwila nchito? Apa Moredekai anasonyeza kuti anali kukhulupilila kwambili Yehova, yemwe sangalole kuti anthu ake onse awonongedwe kapena kulola kuti malonjezo ake asakwanilitsidwe. (Yos. 23:14) Kenako Moredekai anafunsa Esitere kuti: “Ndani akudziwa? Mwina iwe wakhala mfumukazi kuti uthandize pa nthawi ngati imeneyi.” (Esitere 4:​12-14) Moredekai anali kukhulupilila Yehova Mulungu na mtima wonse. Kodi ifenso timatelo?—Miy. 3:​5, 6.

Spiritual Gems

kr 160 ¶14

Kumenyela Ufulu wa Kulambila

14 Monga mmene Esitere na Moredekai anacitila, anthu a Yehova masiku ano amamenyela ufulu wawo wolambila Yehova m’njila imene iye amafuna. (Esitere 4:​13-16) Kodi inuyo mungathandize bwanji pa nchito yomenyela ufulu imeneyi? Mungathandize mwa kupemphelela abale na alongo athu nthawi zonse amene akukumana na mavuto cifukwa ca malamulo opondeleza amene ali m’dziko lawo. Mapemphelo otelo angathandize kwambili abale na alongo athu amene akuzunzidwa kapena kukumana na mavuto osiyanasiyana. (Ŵelengani Yakobo 5:16.) Kodi Yehova amayankha mapemphelo otelo? Milandu yosiyanasiyana imene tapambana kukhoti ni umboni wakuti amatelo.—Aheb. 13:​18, 19.

SEPTEMBER 18-24

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 6-8

“Citsanzo Cimene Tingatengele Pankhani ya Kulankhulana Bwino”

ia 140 ¶15-16

Anacita Zinthu Mwanzelu, Molimba Mtima Ndiponso Moganizila Ena

15 Cifukwa cakuti Esitere anadikilanso tsiku lina asanauze mfumuyo pempho lake, zinacititsa kuti Hamani acite zinthu zomwe zinamubweletsela yekha mavuto. N’kutheka kuti Yehova Mulungu ni amene anacititsa kuti mfumuyo isoŵe tulo. (Miy. 21:1) N’cifukwa cake Mawu a Mulungu amatilimbikitsa ‘kuyembekezela moleza mtima.’ (Ŵelengani Mika 7:7.) Tikamayembekezela kuti Mulungu atithandize pa mavuto athu, tidzaona kuti iye amapeza njila yabwino yothetsela mavuto yoposa imene ifeyo tikanatsatila.

Analankhula Molimba Mtima

16 Esitere anaona kuti si bwino kuti mfumuyo izingodikilabe kuti aiuza zotani. Conco, paphwando lotsatila, iye anaona kuti ayenela kufotokoza zonse. Koma kodi akanayambila pati? Mwamwayi, mfumuyo inamufunsanso kuti afotokoze pempho lake. (Esitere 7:2) Esitere anaona kuti tsopano imeneyi ni “nthawi yolankhula.”

ia 140 ¶17

Anacita Zinthu Mwanzelu, Molimba Mtima Ndiponso Moganizila Ena

17 N’kutheka kuti Esitere anapemphela camumtima kwa Mulungu wake asanauze mfumu mawu awa: “Ngati mungandikomele mtima mfumu, ndipo ngati zingakukomeleni, ndikupempha kuti mupulumutse moyo wanga komanso kuti musawononge anthu a mtundu wanga.” (Esitere 7:3) Onani kuti iye anasonyeza kuti anali kulemekeza zimene mfumuyo ingalamule malinga na zomwe iyoyo yaona kuti n’zoyenela. Zimene Esitere anacitazi zinasonyeza kuti anali wosiyana kwambili na Vasiti, mkazi wakale wa mfumuyi, amene anacititsa manyazi mfumuyi mwadala. (Esitere 1:1012) Komanso, Esitere sananyoze mfumuyi cifukwa cokhulupilila zinthu zabodza zimene Hamani anaiuza. M’malomwake, anapempha mfumuyo kuti imuteteze kuti asaphedwe.

ia 141 ¶18-19

Anacita Zinthu Mwanzelu, Molimba Mtima Ndiponso Moganizila Ena

18 Pempho limeneli linadabwitsa kwambili mfumuyo komanso inaona kuti iyeneladi kucitapo kanthu. Ndipotu palibe mwamuna amene angalekelele kuti mkazi wake aphedwe. Esitere anapitiliza kufotokoza kuti: “Ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti tiwonongedwe, tiphedwe ndi kufafanizidwa. Ngati tikanagulitsidwa kukhala akapolo aamuna ndi akapolo aakazi ndikanakhala cete. Koma musalole kuti tsoka limeneli licitike cifukwa liwonongetsa zinthu zambili za mfumu.” (Esitere 7:4) Onani kuti Esitere anafotokoza zokhudza ciwembuco momveka bwino koma ananenanso kuti zikanakhala kuti iwo anangokhala akapolo cabe, iye sakanadandaula ciliconse. Komano popeza kuti kupha mtundu wonse kukanakhudzanso kwambili mfumuyo, iye anaona kuti si bwino kungokhala cete.

19 Citsanzo ca Esitere cikutiphunzitsa njila yabwino yofotokozela maganizo athu mogwila mtima. Ngati mukufuna kufotokoza vuto linalake kwa munthu amene mumam’konda kapena kwa munthu waudindo, kucita zinthu moleza mtima, mwaulemu, komanso kuchula vutolo mosapita m’mbali, kungakuthandizeni kwambili.—Miy. 16:​21, 23.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w06 3/1 11 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Esitere

7:4—Kodi kuwonongedwa kwa Ayuda kukanawonongetsa bwanji “zinthu zambiri za mfumu”? Mwa kufotokoza mwanzelu kuti iye sakanavutika Ayuda akanagulitsidwa kukhala akapolo, Esitere anatsindika mmene kuwonongedwa kwawo kukanapwetekela mfumu. Ndalama za siliva 10,000 zimene Hamani anali atalonjeza sizinali zaphindu pa cuma ca mfumu kuyelekeza na cuma cimene cikanapezeka Hamani akanakhala kuti anakonza ciwembu cogulitsa Ayuda kukhala akapolo. Ciwembu ca Hamani cikanatheka, mfumu ikanataya mkazi wake.

SEPTEMBER 25–OCTOBER 1

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 9-10

“Anagwilitsa Nchito Udindo Wake pothandiza Ena”

it-2 432 ¶2

Moredekai

Tsopano Moredekai analoŵa m’malo Hamani monga nduna yaikulu ndipo anapatsidwa mphete yodindila ya mfumu kuti azidindila makalata a boma. Esitere anaika Moredekai kukhala woyang’anila nyumba ya Hamani imene mfumu inapatsa Esitere. Kenako Moredekai atavomelezedwa na mfumu anapeleka lamulo lolola Ayuda kudziteteza. Lamulo limeneli linapatsa Ayuda ciyembekezo ca cipulumutso nacisangalalo. Anthu ambili mu ufumu wa Perisiya anakhala kumbali ya Ayuda, ndipo pamene tsiku la Adara 13 linafika, tsiku limene linaikidwa kuti malamulowo ayambe kugwila nchito, Ayuda anali okonzeka kudziteteza.Ayudawo anali na citetezo ca mfumu cifukwa cakuti Moredekai anali na udindo waukulu. Ku Susani nkhondo inapitilila mpaka tsiku lotsatila. Adani a Ayuda oposa 75,000 mu ufumu wa Perisiya anaphedwa kuphatikizapo ana 10 a Hamani. (Esitere 8:1–9:18) Mogwilizana na Esitere, Moredekai analamula kuti pakhale tsiku la madyelelo caka ciliconse pa tsiku la 14 na 15 m’mwezi wa Adara, masiku a Purimu, kuti azikondwela, kucita phwando na kupatsana mphatso wina na mnzake komanso kwa osauka. Ayuda anavomeleza zimenezi ndipo anauza ana awo komanso anthu ena amene anadziphatika kuciyunda kuti azicita cikondwelelo cimeneci. Monga waciwili kwa mfumu, Moredekai anali kulemekezedwa na anthu odzipatulila a Mulungu, Ayuda, ndipo anapitilizabe kuwathandiza.—Eks. 9:​19-22, 27-32; 10:​2, 3.

it-2 716 ¶5

Purimu

Colinga cake. Anthu ena othilila ndemanga pa Baibo amakamba kuti Madyelelo a Purimu amene Ayuda masiku ano amacita sakhudza kwambili zacipembedzo koma za m’dziko, ndipo nthawi zina amacita zinthu mopambanitsa. Komabe, umu si mmene anali kucitila cikondweleloci pa nthawi imene cinakhazikitsidwa. Onse aŵili, Moredekai na Esitere anali atumiki a Mulungu woona Yehova. Conco, anakhazikitsa phwandolo kuti azimulemekeza. Tingakambe kuti Yehova ndiye anapulumutsa Ayuda pa nthawiyo cifukwa nkhaniyi inayamba pamene Moredekai anaonetsa kukhulupilika kwake pa kulambila Yehova yekha. Zioneka kuti Hamani anali Mwamaleki, mtundu umene Yehova anautembelela mwacindunji na kuuweluza kuti uwonongedwe. Moredekai anamvela lamulo la Mulungu, ndipo anakana kugwadila Hamani. (Eks. 3:​2, 5; Eks. 17:​14-16) Komanso zimene Moredekai anauza Esitere (Eks. 4:14) zionetsa kuti iye anali kudalila mphamvu ya Mulungu kuti ipulumutse Ayuda. Nayenso Esitere anaonetsa kuti anali kudalila Mulungu mwa kusala kudya asanapite kukaonekela pamaso pa mfumu kukaipempha kuti ibwele ku phwando.—Eks. 4:16.

cl 101-102 ¶12-13

‘Khalani Otsanzila Mulungu’ Pamene Mukugwilitsa Nchito Mphamvu

12 Yehova wapeleka oyang’anila kuti azitsogolela mu mpingo wacikhristu. (Aheberi 13:17) Amuna okhoza kutsogolela amenewa amayenela kugwilitsa nchito udindo womwe Mulungu wawapatsa pothandiza gulu la nkhosa na kucititsa nkhosazo kukhala na moyo wabwino. Kodi udindo wawowo umapatsa akulu ufulu wocita umbuye pa okhulupilila anzawo? M’pang’onong’ono pomwe! Akulu afunika kuona nchito imene ali nayo mu mpingo mosamala bwino komanso modzicepetsa. (1 Petulo 5:​2, 3) Baibulo limauza oyang’anila kuti: “Muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.” (Machitidwe 20:28) Cimenecitu ni cifukwa camphamvu kwabasi cocitila zinthu mokoma mtima na nkhosa iliyonse m’gululo.

13 Tingacitile fanizo motele. Bwenzi lanu lapamtima lakupemphani kuti mulisungile katundu wamtengo wapatali. Inu mukudziŵa kuti bwenzi lanu linalipila ndalama zambili pogula katunduyo. Kodi simungamugwile mosamala kwambili kuti asawonongeke? Mofananamo, Mulungu wapatsa akulu udindo wosamalila katundu wamtengo wapatali zedi: mpingo, womwe anthu ake amafanizidwa na nkhosa. (Yohane 21:​16, 17) Yehova amazikonda nkhosa zake; amazikondatu kwambili moti anazigula na magazi amtengo wapatali a Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Khristu. Panalibenso mtengo wina wokwela kuposa pamenepa umene Yehova akanalipilila nkhosa zake. Akulu odzicepetsa amakumbukila zimenezi ndipo amasamalila nkhosa za Yehova moyenelela.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w06 3/1 11 ¶4

Mfundo Zazikulu za M’buku la Esitere

9:​10, 15, 16— Ngakhale kuti lamulo linalola kulanda zofunkha, n’cifukwa ciyani Ayuda sanacite zimenezo? Kusacita kwawo zimenezo unali umboni wakuti colinga cawo cinali kuteteza mtundu wawo osati kudzilemeletsa ayi.

OCTOBER 2-8

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 1-3

“Pitilizani Kuonetsa Kukula kwa Cikondi Canu pa Yehova”

w18.02 6 ¶16-17

Tengelani Cikhulupililo na Kumvela kwa Nowa, Danieli, na Yobu

16 Mavuto amene Yobu anakumana nawo. Panthawi inayake, zinthu zinasintha kwambili mu umoyo wa Yobu. Asanayambe kuvutika, iye anali “munthu wolemekezeka kwambili pa anthu onse a Kum’mawa.” (Yobu 1:3) Anali wolemela, wochuka, ndipo anthu ambili anali kum’patsa ulemu. (Yobu 29:​7-16) Ngakhale zinali conco, iye sanayambe kudzikweza, kapena kuleka kudalila Mulungu. Mpake kuti Yehova anamucha “mtumiki” wake. Kuwonjezela apo anakamba kuti: “Iyetu ndi munthu wopanda colakwa ndi wowongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.”—Yobu 1:8.

17 Koma m’kanthawi kocepa cabe, zinthu zinasinthilatu mu umoyo wa Yobu. Anakhala munthu wosauka kwambili komanso wovutika. Tidziŵa kuti amene anacititsa zimenezi ni Satana Mdyelekezi. Iye ananeneza Yobu kuti anali kulambila Mulungu cifukwa ca dyela. (Ŵelengani Yobu 1:​9, 10.) Yehova sananyalanyaze bodza limeneli. M’malomwake, anapatsa Yobu mpata woonetsa kukhulupilika kwake, kuti zidziŵike kuti sanali kulambila Mulungu cifukwa ca dyela koma cifukwa com’konda na mtima wonse.

w19.02 5 ¶10

Khalanibe na Mtima Wamphumphu!

10 Kodi nkhani imene Satana anayambitsa ponena za Yobu imatikhudza bwanji ife? Satana amakamba kuti cikondi canu pa Yehova Mulungu n’caciphamaso, cakuti ngati mwakumana na mavuto, mungaleke kum’tumikila. Amati simungathe kukhala na mtima wamphumphu. (Yobu 2:​4, 5; Chiv. 12:10) Ndithudi, zimenezi n’zopweteka mtima ngako. Koma Yehova amatidalila kwambili. Ndipo watipatsa mwayi wamtengo wapatali wothandiza kutsimikizila kuti Mdyelekezi ni wabodza. Wacita izi mwa kulola Satana kutiyesa. Iye amakhulupilila kuti tingathe kukhalabe na mtima wamphumphu. Ndipo walonjeza kuti adzatithandiza kucita zimenezi. (Aheb. 13:6) Ni mwayi wamtengo wapatali cotani nanga kuti Mfumu ya cilengedwe conse imatidalila! Kodi mwaona tsopano kuti kukhala na mtima wamphumphu n’kofunika kwambili? Kumatithandiza kutsutsa mabodza a Satana, kukweza dzina loyela la Atate wathu, na kucilikiza ulamulilo wake. Nanga tingacite ciani kuti tikhalebe na mtima wamphumphu?

Kufufuza Cuma Cauzimu

w21.04 11 ¶9

Zimene Tingaphunzile pa Mawu Othela a Yesu

9 Kodi Yesu anakamba ciyani? Yesu atatsala pang’ono kumwalila anafuula kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyilanji ine?” (Mat. 27:46) Baibo siifotokoza cifukwa cake Yesu anakamba mawu amenewa. Koma tiyeni tione mfundo zimene tikupeza pa mawu amenewa. Mfundo yoyamba ni yakuti mwa kukamba mawu amenewa, Yesu anakwanilitsa ulosi wa pa Salimo 22:1. Cina, mawu amenewo anaonetselatu kuti Yehova ‘sanali kumuchinga’ Mwana wake. (Yobu 1:10) Yesu anali kudziŵa kuti Atate wake anali atam’peleka kothelatu m’manja mwa adani ake n’colinga cakuti ayesedwe mofikapo kuposa mmene munthu wina aliyense anayesedwela. Kuwonjezela apo, mawu amenewa anatsimikizila kuti iye analibe mlandu uliwonse woyenela imfa.

OCTOBER 9-15

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 4-5

“Samalani na Nkhani Zabodza”

it-1 713 ¶11

Elifazi

2. Mmodzi wa anzake atatu a Yobu. (Yobu 2:11) Elifazi anali wa ku Temani, ndipo mwacionekele anali mbadwa ya Esau, kutanthauza kuti analinso mbadwa ya Abulahamu, komanso wacibale wapatali wa Yobu. Iye ana mbadwa zake anali kudzitama cifukwa ca nzelu zawo. (Yer. 49:7) Pa “otonthoza” atatu a Yobu, Elifazi aoneka kuti ndiye anali wolemekezeka kwambili komanso wosonkhezela ena, zimene zionetsa kuti mwina ndiye anali wamkulu pa onse. Iye ndiye anali kuyamba kulankhula pa anzake atatuwo, ndipo zolankhula zake zinali kukhala zambili.

w05 9/15 26 ¶2

Pewani Maganizo Olakwika!

Pokumbukila masomphenya odabwitsa amene anaona nthawi ina, Elifazi anati: “Mzimu unadutsa kumaso kwanga, ndipo ubweya wa pathupi langa unayamba kuimilila.” (Yobu 4:15) Kodi ni mzimu wotani umene unam’sokoneza maganizo Elifazi? Mawu osalimbikitsa amene ananena pambuyo ponena zimenezi amasonyeza kuti mzimuwo sunali mzimu wocokela kwa Mulungu. (Yobu 4:​17,18) Mzimu umenewu unali ciŵanda. N’cifukwa cake Yehova anadzudzula Elifazi na anzake aŵili aja kuti ananena zabodza. (Yobu 42:7) Inde Elifazi anasokonezedwa maganizo na ziŵanda. Mawu amene ananena anasonyeza kuti maganizo ake sanali maganizo a Mulungu.

w10 2/15 19 ¶5-6

Musalole Mabodza a Satana Kukusokonezani Maganizo

Satana anagwilitsila nchito Elifazi, mmodzi wa anthu atatu amene anapita kukazonda Yobu, kunena mfundo yabodza yakuti anthu sangalimbelimbe akakumana na ziyeso za Satana. Iye ananena kuti anthu ni “okhala m’nyumba zadothi,” ndipo anauza Yobu kuti “maziko awo ali m’fumbi. Iwo amathudzulidwa mosavuta kuposa kadziwoche. Kuyambila m’mawa mpaka madzulo, amakhala akunyenyedwa. Amawonongeka kwamuyaya, popanda aliyense kukhudzika nazo.”—Yobu 4:​19, 20.

Malemba ena amayelekezela anthu na “zonyamulila zoumbidwa ndi dothi,” zomwe sizicedwa kusweka. (2 Akorr. 4:7) N’zoona kuti ucimo umene tinatengela kwa makolo athu oyambilila komanso kupanda ungwilo zimacititsa kuti tikhale ofooka. (Aroma 5:12) Patokha sitingathe kulimbana na Satana. Komabe, poti ndife Akhristu, Yehova amatithandiza. Ngakhale kuti tili na zofooka, ndife amtengo wapatali kwambili pamaso pa Mulungu. (Yes. 43:4) Komanso Yehova amapeleka mzimu woyela kwa amene am’pempha. (Luka 11:13) Mzimu wake ungathe kutipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa,” yomwe ingatithandize kulimbana na mavuto aliwonse amene Satana amatibweletsela. (2 Akor. 4:7; Afil. 4:13) Tikamayesetsa kulimbana na Mdyelekezi, n’kukhala “olimba m’cikhulupililo,” Mulungu angathe kutilimbitsa n’kukhala amphamvu. (1 Pet. 5:​8-10) Motelo sitiyenela kumuopa Satana Mdyelekezi.

mrt 32 ¶13-17

Dzitetezeni Kuti Musamapusitsidwe na Nkhani Zabodza

● Muziganizila kumene nkhaniyo yacokela komanso zimene imanena

Zimene Baibo imanena: “Tsimikizilani zinthu zonse.”—1 Atesalonika 5:21.

Musanakhulupilile nkhani inayake kapena kuitumiza, ngakhale imene ni yodziŵika kapena imene yalengezedwa pa nyuzi, mutsimikizile kaye kuti ni yoona. Kodi mungacite bwanji zimenezi?

Muziganizila ngati nkhani yacokela kwa munthu kapena kumalo odalilika. Makampani kapena mabungwe ofalitsa nkhani akhoza kusintha nkhanizo cifukwa ca maganizo awo andale kapena okhudza zinthu zina. Muziyelekezela nkhani zocokela kwa ofalitsa nkhani ena na nkhani zomwezo zocokela kwa ofalitsa nkhani anzawo. Nthawi zina, anzanu angakutumizileni mameseji abodza mosadziŵa. Conco musamakhulupilile nkhani iliyonse kusiyapo ngati mungadziŵe kumene yacokela.

Muzitsimikizilanso ngati zimene nkhani imanena n’zatsopano komanso zoona. Muziona madeti, mfundo zotsimikizilika komanso umboni wamphamvu wosonyeza kuti nkhaniyo ni yoona. Muzisamala kwambili ngati nkhani ikufotokoza zinthu zovuta m’njila yosavuta kwambili kapena ngati yalembedwa mokufikani pamtima kwambili.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w03 5/15 22 ¶5-6

Khalani Okhazikika Kuti Mudzapambane pa Mpikisano wa Moyo

Kukhala m’gulu la padziko lonse la olambila oona kungatilimbitse kwambili. Ni dalitso lalikulu kukhala pakati pa abale acikondi a padziko lonse amenewa! (1 Petulo 2:17) Ndipo ngakhale ifeyo tikhoza kulimbitsanso okhulupilila anzathu.

Taganizilani nchito zothandiza zimene munthu wolungama Yobu anali kucita. Ngakhale Elifazi, amene anali wotonthoza wabodza, anavomeleza kuti: “Aliyense wofuna kugwa, mawu ako anali kumudzutsa, ndipo mawondo olobodoka unali kuwacilikiza.” (Yobu 4:4) Kodi ife timathandiza anzathu? Aliyense wa ife ali na udindo wothandiza abale na alongo athu auzimu kuti apilile potumikila Mulungu. Tikamacita nawo zinthu, tizicita mogwilizana na mawu aŵa: “Limbitsani manja ofooka ndiponso mawondo agwedegwede.” (Yesaya 35:3) Conco, bwanji osakhala n’colinga colimbikitsa Mkhristu mnzanu mmodzi kapena aŵili nthaŵi iliyonse imene mwakumana? (Aheberi 10:​24, 25) Mawu owalimbikitsa na owayamikila cifukwa copitirizabe kusangalatsa Yehova angawathandize kuti akhale okhazikika kuti adzapambane pa mpikisano wa moyo.

OCTOBER 16-22

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 6-7

“Umoyo Ukafika Poti Simungathe Kupilila”

w06 3/15 14 ¶10

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu

7:1; 14:14—Kodi mawu oti “nchito yokakamiza” akuimila ciyani? Yobu anali atavutika kwambiri moti moyo wake anali kungouona ngati nchito yokakamiza. (Yobu 10:17) Popeza kuti munthu sakhala mu Shelo mwa kufuna kwake, kucokela panthawi imene wamwalila n’kufika panthawi imene adzaukitsidwe, Yobu anaiyelekezela na nchito yocita kukakamizidwa.

w20.12 16 ¶1

“Yehova Amapulumutsa Anthu Olefuka Mtima”

NTHAWI zina, timaganizila za mfundo yosatsutsika yakuti moyo ni waufupi, komanso ni “wodzaza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Conco, m’pomveka kuti nthawi zina timalefuka. Atumiki a Yehova ambili m’nthawi zakale anamvelapo cimodzi-modzi. Ena anali kufuna kuti afe cabe. (1 Maf. 19:​2-4; Yobu 3:​1-3, 11; 7:​15, 16) Koma mobweleza-bweleza, Yehova, Mulungu amene iwo anali kum’dalila anali kuwatonthoza na kuwalimbikitsa. Zocitika za mu umoyo wawo zinalembedwa kuti zititonthoze na kutiphunzitsa.—Aroma 15:4.

g 1/12 16-17

Kodi Mungatani Mukakhala na Maganizo Ofuna Kudzipha?

Ngakhale kuti mungamaone kuti mavuto amene mukukumana nawo ni osapililika, muzikumbukila kuti si inu nokha amene mukukumana na mavuto komanso pafupifupi aliyense akulimbana na vuto linalake. Baibo imanena kuti: “Cilengedwe conse cikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.” (Aroma 8:22) Ngakhale kuti panopa mungamaone kuti mavuto anuwo sadzatha, zoona zake n’zakuti zinthu zimasintha pakapita nthawi. Ndiyeno kodi panopa muyenela kucita ciyani?

Uzani Mnzanu Wodalilika Mavuto Amene Mukukumana Nawo. Baibo imanena kuti: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miyambo 17:17) Baibo imasonyeza kuti Yobu, yemwe anali munthu wokhulupilika, anali kufotokozela anzake mavuto ake. Pa nthawi yomwe ‘ankanyansidwa ndi moyo wake,’ iye ananena kuti: “Ndilankhula mwamphamvu za nkhawa zanga. Ndilankhula cifukwa ca kuwawa kwa moyo wanga.” (Yobu 10:1) Mukauzako anthu ena za mavuto anu, mumamvako bwino mumtima ndipo zingakuthandizeni kuti muyambe kuona mavuto anuwo mwanjila ina.

Pemphelani kwa Yehova. Anthu ena amaganiza kuti pemphelo limangothandiza anthu kuti azingomvako bwino pang’ono, koma Baibo imafotokoza zosiyana na zimenezo. Lemba la Salimo 65:2 limati Yehova Mulungu ni “Wakumva pemphelo” komanso lemba la 1 Petulo 5:7 limati: “Amakudelani nkhawa.” Baibo imanena mobwelezabweleza za kufunika kodalila Mulungu. Taonani malemba otsatilawa:

“Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukila m’njila zako zonse, ndipo iye adzawongola njila zako.”—MIYAMBO 3:​5, 6.

“Ndipo anthu amene amamuopa [Yehova] adzawacitila zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.”—SALIMO 145:19.

“Ifetu timamudalila kuti ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.”—1 YOHANE 5:14.

“Yehova amakhala kutali ndi anthu oipa, koma amamva pemphelo la anthu olungama.”—MIYAMBO 15:29.

Mukamauza Mulungu mavuto amene mukukumana nawo, iye adzakuthandizani. N’cifukwa cake Baibo imatilimbikitsa kuti: “Mukhulupilileni nthawi zonse, . . . Mukhuthulileni za mumtima mwanu.”—Salimo 62:8.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w20.04 16 ¶10

Amvetseleni, Adziŵeni Bwino, Aonetseni Cifundo

10 Tingatengele citsanzo ca Yehova mwa kuyesetsa kuwamvetsetsa abale na alongo athu. Adziŵeni bwino abale na alongo anu. Muzicezako nawo misonkhano ikalibe kuyamba komanso ikatha, muziyenda nawo mu ulaliki, ndipo ngati n’zotheka mungawaitanileko ku cakudya. Mukatelo, mungazindikile kuti mlongo uja amene mumamuona ngati si waubwenzi, kweni-kweni ni wamanyazi cabe, ndipo m’bale wa ndalama zambili uja si wokonda cuma, koma kweni-kweni ni wowoloŵa manja. Kapenanso mungazindikile kuti banja limene limakonda kubwela mocedwa ku misonkhano likukumana na citsutso. (Yobu 6:29) N’zoona kuti sitiyenela ‘kulowelela nkhani za eni.’ (1 Tim. 5:13) Komabe, ni bwino kuwadziŵa bwino abale na alongo athu, komanso kudziŵa zimene akukumana nazo. Tikatelo, tidzatha kuwamvetsetsa.

OCTOBER 23-29

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 8-10

“Cikondi ca Mulungu Cosasintha Cimatiteteza ku Mabodza a Satana”

w15 7/1 12 ¶3

Kodi Anthufe Tingasangalatsedi Mulungu?

Yobu anakumana na mavuto ambili motsatizana ndipo mavutowa anali kuoneka kuti samayenela kukumana nawo. Izi zinamucititsa kuti aganize molakwika n’kumaona kuti Mulungu analibe nazo nchito zakuti iyeyo ni munthu wokhulupilika. (Yobu 9:​20-22) Yobu anali kudziona kuti anali munthu wolungama kwambili moti anthu ena anali kuganiza kuti Yobuyo akunena kuti ndi wolungama kuposa Mulungu.—Yobu 32:​1, 2; 35:​1, 2.

w21.11 6 ¶14

Kodi Cikondi Cosasintha ca Yehova N’ciyani?

14 Cikondi cosasintha ca Mulungu cimatiteteza mwauzimu. Popemphela kwa Yehova, Davide anati: “Ndinu malo anga obisalamo, mudzanditeteza ku masautso. Mudzacititsa kuti cisangalalo cindizungulile pamene mukundipulumutsa. . . . “Wokhulupilila Yehova amazungulilidwa ndi kukoma mtima kosatha.” (Sal. 32:​7, 10) M’nthawi za m’Baibo, anthu mumzinda anali kukhala motetezeka cifukwa ca zipupa zimene zinali kuzungulila mzindawo. Mofananamo, nchito za Yehova zoonetsa cikondi cosasintha zimatizungulila, na kupeleka citetezo cauzimu ku zinthu zimene zingawononge umphumphu wathu. Cina, khalidwe limeneli la Yehova limamusonkhezela kutikokela kwa iye.—Yer. 31:3.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w10 10/15 6-7 ¶19-20

“Ndani Akudziŵa Maganizo a Yehova?”

19 Kodi taphunzila ciyani pa nkhani ya “maganizo a Yehova”? Tiyenela kulola kuti Mawu a Mulungu azitithandiza kudziŵa bwino maganizo a Yehova. Popeza kuti anthufe sitidziŵa zambili, tisamaweluze Yehova malinga ndi mfundo ndiponso maganizo amene timayendela. Yobu anati: “[Mulungu] si munthu ngati ine kuti ndimuyankhe, kapena kuti tizengane mlandu.” (Yobu 9:32) Mofanana na Yobu tikayamba kudziŵa bwino maganizo a Yehova tidzafuula kuti: “Zimenezi ndi kambali kakang’ono cabe ka zocita zake, ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake. Koma kodi mabingu ake amphamvu, angawamvetse ndani?”—Yobu 26:14.

20 Tikamawelenga Malemba, kodi tiyenela kutani ngati tapeza nkhani yovuta kuimvetsa makamaka yokhudza mmene Yehova amaganizila? Ngati tafufuza nkhaniyo koma osapeza yankho lomveka bwino, tiyenela kuona kuti umenewu ni mwayi wathu wosonyeza kuti timakhulupilila kwambili Yehova. Tisaiwale kuti mfundo zina zimatithandiza kusonyeza kuti timakhulupilila kuti Yehova ali na makhalidwe abwino. Tiyeni tikhale odzicepetsa n’kuvomeleza kuti sitingamvetse zocita zake zonse. (Mlal. 11:5) Izi zidzatithandiza kuvomeleza mawu a mtumwi Paulo akuti: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapeleka ndi oculuka kwambili. Nzelu zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambili. Ziweluzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukile njila zake? Pakuti ‘ndani akudziwa maganizo a Yehova, kapena ndani angakhale phungu wake?’ Kapenanso, ‘Ndani anayamba kumupatsa kanthu, kuti amubwezele?’ Cifukwa zinthu zonse zimacokela kwa iye ndipo iye ndi amene anazipanga ndiponso ndi zake. Ulemelelo ukhale wake kwamuyaya. Ame.”—Aroma 11:​33-36.

OCTOBER 30–NOVEMBER 5

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 11-12

“Njila Zitatu Zopezela Nzelu na Kupindula Nazo”

w09 4/15 6 ¶17

Yobu Analemekeza Dzina la Yehova

17 Kodi n’ciyani cinamuthandiza Yobu kusungabe umphumphu wake? N’zodziwikilatu kuti iye anali atalimbitsa kale ubwenzi wake na Yehova masoka asanamugwele. Ngakhale kuti tilibe umboni wosonyeza kuti Yobu ankadziŵa kuti Satana anali atatsutsa Yehova, iye anatsimikiza mtima kukhalabe wokhulupilika. Iye anati: “Mpaka ine kumwalila, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.” (Yobu 27:5) Kodi Yobu anacita ciyani kuti akhale pa ubwenzi wolimba conco na Mulungu? Mosakayikila, iye anamva zimene Mulungu anacitila Abulahamu, Isake na Yakobo omwe anali abale ake ndipo anali kuzikhulupilila. Ndiponso iye anaphunzila za makhalidwe ambili a Yehova poona cilengedwe.—Ŵelengani Yobu 12:​7-9, 13, 16.

w21.06 10 ¶10-12

Yehova Ali Namwe, Simuli Mwekha

10 Palanani ubwenzi na Akhristu okhulupilika. Palanani ubwenzi na anthu amene mungaphunzileko zina kwa iwo, ngakhale amene musiyana nawo zaka kapena cikhalidwe. Baibo imatikumbutsa kuti “okalamba . . . amakhala ndi nzelu.” (Yobu 12:12) Nawonso acikulile angaphunzile zambili kwa acicepele okhulupilika. Davide anali wamng’ono kwambili poyelekezela na Yonatani. Koma zimenezo sizinawalepheletse kukhala pa ubwenzi wolimba. (1 Sam. 18:1) Davide na Yonatani anali kuthandizana potumikila Yehova ngakhale pa mavuto aakulu. (1 Sam. 23:​16-18) Mlongo Irina amene palipano ndiye yekha Mboni m’banja mwawo, ananena kuti: “Abale na alongo athu angakhaledi makolo athu a kuuzimu, kapena azikulu athu na azing’ono athu. Yehova angawaseŵenzetse kukhala banja lathu limene tifunikila.”

11 Kupanga mabwenzi atsopano kungakhale kovuta maka-maka ngati ndimwe wamanyazi. Mlongo Ratna amene ni wamanyazi, ndipo anaphunzila coonadi ngakhale kuti anali kutsutsidwa ananena kuti: “N’nafunika kuvomeleza kuti n’nali kufunikila thandizo na cicilikizo cocokela ku banja langa lauzimu.” Cingakhale covuta kufotokoza mmene umvelela. Koma kukambilana momasuka na wina kumakhala maziko a ubwenzi wolimba. Mabwenzi anu amafuna kukulimbikitsani na kukucilikizani. Ngakhale n’conco, mufunika kucita kuwauza kuti adziŵe mmene angakuthandizileni.

12 Imodzi mwa njila zothandiza kwambili popanga mabwenzi, ni mwa kulalikila pamodzi na Akhristu anzathu. Mlongo Carol amene tam’gwila mawu kuciyambi anakamba kuti: “Napeza mabwenzi ambili abwino mwa kulalikila pamodzi na alongo, komanso kucita nawo zinthu zina zauzimu. Kwa zaka zambili, Yehova wakhala akunithandiza kupitila mwa mabwenzi amenewa. M’pake kulimbikila kupalana ubwenzi na Akhristu okhulupilika. Yehova amaseŵenzetsa mabwenzi otelo pokuthandizani kulimbana na maganizo olefula monga kusungulumwa.—Miy. 17:17.

it-2 1190 ¶2

Nzelu

Nzelu ya umulungu. Nzelu yeniyeni imapezeka kwa Yehova Mulungu, amene ni “wanzelu yekhayo.” (Aroma 16:27; Chiv. 7:12) Cidziŵitso ndico kudziŵa zenizeni, ndipo cifukwa Yehova ni Mlengi wathu amene wakhalapo “kuyambila kalekale mpaka kalekale” (Sal. 90:​1, 2), iye amadziŵa zonse zokhudza cilengedwe, mmene anacipangila, zinthu zimene zilimo, na mbili yake kufika lelo. Mulungu ndiye anakhazikitsa malamulo a m’cilengedwe, mmene zinthu zimacitikila m’cilengedwe, komanso miyezo ya m’cilengedwe, imene anthu amadalila pa kafukufuku na zopanga-panga. Popanda zimenezi, anthu paokha sakanatha kucita ciliconse. (Yobu 38:​34-38; Sal. 104:24; Miy. 3:19; Yer. 10:​12, 13) Pa cifukwa cimeneci, miyezo yake ya makhalidwe abwino ni yofunika kwambili kuti anthu akhale mwabata, azipanga zisankho zabwino, komanso kuti zinthu ziziwayendela bwino. (Deut. 32:​4-6) Palibe cimene iye sangathe kucimvetsa. (Yes. 40:​13, 14) Mulungu nthawi zina analolele zinthu zosemphana na miyezo yake yolungama kucitika, ngakhale kuwonjezeka kwa kanthawi. Komabe, tsogolo la zinthu zonse lili m’manja mwake, ndipo zinthu zonse zidzacitika ndendende mogwilizana na cifunilo cake, komanso mawu ake ‘adzakwanilitsidwa.’—Yes. 55:​8-11; 46:​9-11.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w08 8/1 11 ¶5

Kulankhulana na Acinyamata

▪ ‘Kodi nimamvetsa tanthauzo la zimene akunena?’ Lemba la Yobu 12:11 limati: “Kodi khutu si paja limasiyanitsa mawu, ngati mmene m’kamwa mumasiyanitsila kakomedwe ka cakudya?” Mosiyana na poyamba, muyenela ‘kusiyanitsa’ kapena kuti kuzindikila tanthauzo lenileni la zimene mwana wanu akunena. Acinyamata amakonda kukokomeza kwambili zinthu moti akamafotokoza vuto linalake amalankhula ngati kuti limacitika nthawi zonse. Mwacitsanzo, mwana wanu anganene kuti: “Inu nthawi zonse mumanditenga ngati kamwana.” Kapena kuti: “Simumandimvetsa kuyambila kale.” M’malo molimbana na mawu amene wanena akuti “nthawi zonse” kapena akuti “kuyambila kale,” ni bwino kudziŵa zimene mwanayo akutanthauza. Mwacitsanzo mawu akuti “Inu nthawi zonse mumanditenga ngati kamwana,” angatanthauze kuti “Ndikuona kuti simumandikhulupilila.” Ndipo mawu akuti “Simumandimvetsa kuyambila kale,” angatanthauze kuti “Ndikufuna kukuuzani mmene ndikumvela.” Yesetsani kumvetsa tanthauzo la zimene mwana wanu akunena.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani