Malifalensi a Kabuku ka Umoyo
© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
NOVEMBER 6-12
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 13-14
“Munthu Akafa, Kodi Angakhalenso Ndi Moyo?”
w99 10/15 3 ¶1-3
Kufunafuna Kwathu Moyo Wautali
NGAKHALE lelolino, ni oŵelengeka cabe amene angatsutse malingalilo onena za kufupika kwa moyo, ngakhale kuti analembedwa zaka 3,500 zapitazo. Anthu sakukhutilabe na moyo wapamwamba umene amasangalala nawo kwa kanthaŵi ndipo pambuyo pake kukalamba na kumwalila. Conco, njila zoyesela kutalikitsa moyo, zafala zedi m’mbili.
M’nthaŵi ya Yobu, Aiguputo anali kudya mavalo anyama poyesayesa kuti mwina angabwelele ku unyamata, koma zinali zosaphula kanthu. Cimodzi mwa zolinga za sayansi ya zamankhwala ya m’nyengo zapakati, cinali kupanga mankhwala opangitsa moyo kukhala wautali. Akatswili ambili amene anayesayesa kutalikitsa moyo, anali kukhulupilila kuti golide wopangidwa na anthu angapangitse moyo kukhala wosafa, ndipo kudyela m’mbale zake kungatalikitse moyo. Atao a ku China wakale anali kuganiza kuti angathe kusintha makemikolo a m’thupi pogwilitsa nchito maluso monga kusinkhasinkha, maseŵelo otulutsa mpweya wambili m’kamwa, na kudya pang’ono ndipo potelo anali kukhulupilila kuti angathe kukhala na moyo wosafa.
Woyendela malo wa ku Spain, Juan Ponce de León amadziŵika cifukwa ca kufunafuna kwake kasupe wa unyamata. Dokotala wina wa m’zaka za zana la 18 analangiza m’buku lake lochedwa Hermippus Redivivus kuti anamwali ataikidwa m’kacipinda m’nyengo ya masika na kutengela m’mabotolo mpweya umene amapuma m’kacipindamo, ungagwilitsidwe nchito popanga mankhwala otalikitsa moyo. N’zacionekele kuti palibe na imodzi yomwe mwa njila zonsezo imene inapambana.
Kodi Mtengo Ukadulidwa Ungaphukenso?
MTENGO wakale wa maolivi sukhala wokongola kwenikweni tikauyelekezela na mtengo waukulu wa mkungudza wa ku Lebanoni. Koma mitengo ya maolivi imapilila kwambili ngakhale pamene kuli cilala. Pali mitengo ina ya maolivi imene anthu amanena kuti yakwanitsa zaka pafupifupi 1,000. Mtengo wa maolivi akaudula umaphukanso cifukwa cakuti mizu yake imapita pansi kwambili ndiponso imayala malo aakulu. Ngati mizu yake ikali bwino, mtengowu sulephela kuphuka.
Yobu anali kukhulupilila kuti ngakhale atafa, adzakhalanso na moyo. (Yobu 14:13-15) Iye anagwilitsa nchito citsanzo ca mtengo pofuna kuonetsa kuti anali na cikhulupililo cakuti Mulungu adzamuukitsa. Pankhaniyi, mwina iye anagwilitsila nchito citsanzo ca mtengo wa maolivi. Yobu anati: “Ngakhale mtengo umakhala ndi ciyembekezo. Ukadulidwa umaphukanso.” Mvula ikagwa pambuyo pa cilala coopsa, mizu ya citsa couma ca mtengo wa maolivi imaphuka n’kumela “nthambi ngati mtengo watsopano.”—Yobu 14:7-9.
“Mudzalakalaka Nchito ya Manja Anu”
Zimene Yobu ananena zikutiphunzitsa mfundo yofunika kwambili yokhudza Yehova. Mfundo yake ni yakuti, iye amakonda kwambili anthu amene amamudalila ngati mmene anali kucitila Yobu. Anthu amenewa amalola kuti Yehova awaumbe kukhala anthu amakhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo. (Yes. 64:8) Yehova amaona kuti atumiki ake okhulupilika ni anthu amtengo wapatali kwambili. Conco iye ‘amalakalaka’ kuonanso anthu okhulupilika amene anamwalila. Katswili wina wa Baibo ananena kuti, mawu acihebeli amene palembali anawamasulila kuti ‘kulakalaka,’ “ni amodzi mwa mawu amphamvu amene amafotokoza mmene munthu amamvela akakhala kuti akufunitsitsa cinacake.” Sikuti Yehova amangokumbukila atumiki ake, koma amalakalakanso atawaukitsa kuti akhalenso na moyo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 191
Phulusa
Phulusa linali kuimilako zinthu zopanda pake kapena zosafunika. Mwacitsanzo, Abulahamu anavomeleza pamaso pa Yehova kuti, “ndine fumbi ndi phulusa.” (Gen. 18:27; onaninso Yes. 44:20; Yobu 30:19) Ndipo Yobu anayelekezela mawu a anzake a bodza na “miyambi yopanda pake ngati phulusa.”—Yobu 13:12.
NOVEMBER 13-19
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 15-17
“Pewani Kutengela Elifazi Popeleka Citonthozo”
w05 9/15 26 ¶4-5
Pewani Maganizo Olakwika!
Pa nthawi zonse zitatu zimene analankhula, Elifazi anasonyeza kuti Mulungu ni wovuta kwambili kum’sangalatsa moti palibe ciliconse cimene atumiki ake amacita cimene iye amasangalala naco. Elifazi anamuuza Yobu kuti: “Iyetu, sakhulupilila atumiki ake; ndipo angelo ake amawapezela zifukwa.” (Yobu 4:18) Kenako Elifazi ananenanso kuti Mulungu “alibe cikhulupililo mwa angelo ake, ndipo kumwamba si koyela m’maso mwake.” (Yobu 15:15) Ndipo anafunsa kuti: “Kodi Wamphamvuyonse amasangalala kuti ndiwe wolungama?” (Yobu 22:3) Bilidadi anavomelezana nawo maganizo amenewa, cifukwa nayenso anati: “Kulitu mwezi koma si wowala. Ndipo nyenyezi si zoyela m’maso mwake [mwa Mulungu].”—Yobu 25:5.
Tiyenela kusamala kuti tisayambe kuganiza maganizo otele. Cifukwatu angatipangitse kuona kuti zimene Mulungu amafuna sizoti munthu angakwanitse. Kuganiza motele kungathe kusokoneza ubwenzi wathu weniweniwo na Yehova. Komanso, ngati titayamba kuganiza conco, kodi tingathe kumvela bwinobwino malangizo ena ake amene tikupatsidwa? M’malo momvela malangizowo, mtima wathu ungafike ‘pokwiyila Yehova’ motelo tingakhumudwe naye. (Miy. 19:3) Izitu zingatisokonezele kwambili ubwenzi wathu na Mulungu!
Khalani Wodzicepetsa Ndi Wacifundo Monga Yesu
16 Mawu athu acifundo. Kumvela ena cifundo kudzaticititsa ‘kulankhula molimbikitsa kwa amtima wacisoni.’ (1 Ates. 5:14) N’ciyani cimene tingakambe polimbikitsa anthu aconco? Tingawalimbikitse mwa kuwauza kuti timawakonda kwambili. Tingawayamikile mocokela pansi pamtima pa makhalidwe abwino na maluso amene ali nawo. Tingawakumbutse kuti Yehova anawakokela kwa Mwana wake, ndipo ni amtengo wapatali kwa iye. (Yoh. 6:44) Ndipo tingawatsimikizile kuti Yehova amawakonda kwambili atumiki ake a “mtima wosweka” kapena “odzimvela cisoni mumtima mwao.” (Sal. 34:18) Kulankhula mwa njila imeneyi kungalimbikitse aja amene akufunikila citonthozo.—Miy. 16:24.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06 3/15 14 ¶11
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu
7:9, 10; 10:21; 16:22—Kodi mawu a m’mavesi amenewa amasonyeza kuti Yobu sanali kukhulupilila za kuuka kwa akufa? Pamenepa Yobu anali kunena za panthawiyo osati za kutsogolo kwambili ayi. Ndiyeno kodi anali kutanthauza ciyani? N’kutheka kuti anali kutanthuza kuti ngati atafa, anzakewo sakanathanso kumuona. Motelo kwa iwowo, Yobuyo sakanabwelelanso kunyumba kwake kapenanso kudziwidwanso, kufikila nthawi imene Mulungu anaika. N’zothekanso kuti Yobu anali kutanthauza kuti palibe munthu amene angabweleko ku Shelo payekha. Mfundo yoti Yobu anali kukhulupilila kuti m’tsogolo akufa adzauka imaonekela pa lemba la Yobu 14:13-15.
NOVEMBER 20-26
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 18-19
“Musawasiye Konse Alambili Anzanu”
Yesu Anagwetsa Misozi—Tiphunzilapo Ciyani?
9 Muzilimbikitsa amene akulila. Yesu sanangolila pamodzi na Marita komanso Mariya, koma anawamvetsela na kuwalimbikitsa. Nafenso tizicita cimodzi-modzi kwa amene akulila. M’bale Dan, amene ni mkulu ku Australia, anati: “Mkazi wanga atamwalila, n’nali kufunikila cilimbikitso. Mabanja angapo anali kubwela usana na usiku kudzanimvetsela. Iwo anali kunilola kulila, ndipo sanacite nane manyazi. Kuwonjezela apo, anadzipeleka kugwila nchito za pakhomo monga kutsuka motoka, kugula zinthu, na kuphika, nikalephela kucita zimenezi panekha. Komanso anali kupemphela nane kaŵili-kaŵili. Iwo anaonetsa kuti ni mabwenzi azoona, komanso abale amene ‘anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.’”—Miy. 17:17.
Munthu Amene Timakonda Akasiya Yehova
16 Pitilizani kuthandiza okhulupilika m’banjalo. Iwo afunikila cikondi na cilimbikitso canu kuposa kale lonse. (Aheb. 10:24, 25) Nthawi zina, zacitikapo kuti a m’banja la munthu wocotsedwa amasalidwa monga kuti nawonso ni ocotsedwa. Koma tisalole zimenezi kucitika. Ana amene makolo awo anasiya coonadi, ndiwo afunikila kwambili kuwalimbikitsa na kuwayamikila. Maria, amene mwamuna wake anacotsedwa mu mpingo na kusiya banja lake, anati: “Ena a mabwenzi anga anali kubwela kwathu kudzatiphikila cakudya, na kunithandiza kuphunzitsa ana anga. Nawonso zinawakhudza kwambili, ndipo anali kulila nane. Anali kunikhalila kumbuyo pamene ena anali kunikambila mabodza. Iwo ananilimbikitsa ngako!”—Aroma 12:13, 15.
w90 9/1 22 ¶20
Kodi Mukukalamila?
20 Bungwe la akulu liyenela kuzindikila kuti kucotsedwa pakukhala mkulu kungacititse kupsinjika maganizo kwa amene anali woyang’anila kapena mtumiki wothandiza, ngakhale ngati angatule utumiki umenewo modzifunila. Ngati sanacotsedwe mumpingo, ndipo akulu akuwona kuti mbaleyo ali wokhwethemulidwa maganizo, iwo ayenela kupeleka thandizo lacikondi lauzimu. (1 Ates. 5:14) Iwo ayenela kum’thandiza kuzindikila kuti ali wofunika mumpingo. Ngakhale ngati uphungu wakhala wofunikila, sikungatenge nthawi yaitali kuti munthu wodzicepetsa ndi woyamikila alandilenso mwayi wowonjezeleka wakutumikila mumpingomo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w94 10/1 32
Mphamvu ya Mawu Acifundo
Komabe, pamene Yobu mwiniyo anafunikila cilimbikitso, Elifazi na anzake sananene mawu acifundo. Anaimba mlandu Yobu cifukwa ca tsoka lake, na kusonyeza kuti ayenela kukhala atacita chimo la mseli. (Yobu 4:8) The Interpreter’s Bible imati: “Cimene Yobu afunikila ndico cifundo ca mtima wa munthu. Cimene alandila ndico mpambo wa mawu acipembedzo ojeda na ndemanga za makhalidwe zimene zili ‘zoona’ na zabwinodi.” Yobu anavutika kwambili atamva zokamba za Elifazi na anzake kwakuti anakakamizika kulila kuti: “Musautsa moyo wanga mpaka liti, ndi kundilasa ndi mawu?”—Yobu 19:2.
Tisacititse konse mtumiki mnzathu wa Mulungu kulila mosautsidwa mtima cifukwa ca mawu athu opanda nzelu na opanda cifundo. (Yelekezelani na Deuteronomo 24:15.) Mwambi wa m’Baibo umacenjeza kuti: “Zimene mumakamba zingapulumutse moyo kapena kuuwononga; cotelo muyenela kulandila zotsatilapo za mawu anu.”—Miy. 18:21, TEV.
NOVEMBER 27–DECEMBER 3
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 20-21
“Cuma Sicimapangitsa Munthu Kukhala Wolungama”
w07 8/1 29 ¶12
Kodi Ndinu “Wolemela kwa Mulungu”?
12 Yesu anasiyanitsa kukhala wolemela kwa Mulungu na kudzikundikila cuma cakuthupi. Conco, Yesu anali kutanthauza kuti colinga cathu cacikulu pamoyo cisakhale kudzikundikila cuma cakuthupi n’kumasangalala naco. M’malo mwake, tiyenela kugwilitsa nchito cuma cathuco polimbikitsa ubwenzi wathu na Yehova. Kucita zimenezi kudzatithandiza kukhala olemela kwa Mulungu. Cifukwa ciyani? Cifukwa cakuti iye amatidalitsa kwambili tikamatelo. Baibo imati: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeletsa, ndipo sawonjezelapo ululu.”—Miy. 10:22
Kufufuza Cuma Cauzimu
w95 1/1 9 ¶19
Kumlaka Satana ndi Nchito Zake
19 Tifunikila kudziŵa kuti Yobu mtumiki wa Mulungu analimbana na “malingalilo osautsa” amene Satana anapeleka kupyolela mwa Elifazi na Zofari. (Yobu 4:13-18; 20:2, 3) Cotelo Yobu anavutika na “masautso,” zimene zinamucititsa kulankhula “zopanda pake” pa “zoopsa” zosautsa maganizo ake. (Yobu 6:2-4; 30:15, 16) Elihu anamvetsela kwa Yobu mwachelu na kumuthandizadi kuona njila yanzelu kwambili imene Yehova amaonelamo zinthu. Mofananamo lelolino, akulu acifundo amasonyeza kuti amasamala ovutika mwa kusawonjezela ‘zolemetsa’ pa anthu otelo. M’malo mwake, monga Elihu, iwo moleza mtima amamvetsela kwa iwo ndiyeno amagwilitsa nchito mafuta otonthoza a m’Mawu a Mulungu. (Yobu 33:1-3, 7; Yakobo 5:13-15) Cotelo aliyense amene malingalilo ake akuvutika na zopsinja maganizo, zenizeni kapena zongolingalila, kapena amene ‘akuwopsezedwa na maloto . . . komanso masomphenya’ monga Yobu, angapeze citonthozo ca m’Malemba mumpingo.—Yobu 7:14; Yak. 4:7.
DECEMBER 4-10
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 22-24
‘Kodi Munthu Angakhale Waphindu kwa Mulungu?’
w05 9/15 27 ¶1-3
Pewani Maganizo Olakwika!
Maganizo akuti Mulungu ni wovuta kumusangalatsa amayendela limodzi na maganizo akuti Mulungu saona anthu ngati kanthu. Elifazi atalankhula kacitatu anafunsa kuti: “Kodi mwamuna wamphamvu angakhale waphindu kwa Mulungu? Kodi aliyense wozindikila angakhale waphindu kwa iye?” (Yobu 22:2) Apatu Elifazi anali kutanthauza kuti munthu sanunkha kanthu kwa Mulungu. Bilidadi anakhudzaponso mfundo yomweyi ponena kuti: “Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu? Kapena kodi munthu wobadwa kwa mkazi angakhale bwanji woyela?” (Yobu 25:4) Tikatengela maganizo amenewa, tingafunse kuti kodi Yobu poti anali munthu, anali kudzivutitsilanji kuganiza kuti angathe kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?
Anthu ena masiku ano amavutika na maganizo olakwika okhudza moyo wawo. N’kutheka kuti amaganiza conco cifukwa ca mmene analeledwela, mavuto amene akumana nawo pa moyo wawo, mwinanso kusankhidwa mtundu kapena fuko. Koma Satana na ziŵanda zake amasangalalanso kwambili kuvutitsa anthu. Amadziŵa kuti akangocititsa munthu kuyamba kumva kuti palibe cimene angacite coti Mulungu Wamphamvuyonse n’kusangalala naco, m’posavuta kuti munthuyo asoŵe koloŵela. Kenako mwapang’ono-pang’ono munthuyo angathe kuyamba kutalikilana na Mulungu wamoyo mwinanso kufika polekana naye kumene.—Aheb. 2:1; 3:12.
Kukalamba ndiponso matenda amatilepheletsa kucita zinthu zina. Tingaone kuti tikulephela kucita zambili mu utumiki wa Ufumu poyelekezela na zimene tinali kucita tili aang’ono, tili athanzi, ndiponso tili amphamvu. M’pofunika kwambili kuzindikila kuti Satana na ziŵanda zake amafuna kuti tiziganiza kuti zimene tikucita panopa si zoti Mulungu n’kusangalala nazo ayi. Tiyeni tiyesetse kupewa maganizo otelewa.
w95 2/15 27 ¶6
Phunzilo pa Kusamalila Mavuto
Mabwenzi ake atatuwo anadetsanso mtima wa Yobu mwa kunena za malingalilo a iwo eni m’malo mwa nzelu yaumulungu. Elifazi anafika ponena kuti Mulungu “sakhulupilila atumiki ake,” komanso kuti zinalibe kanthu kwa Yehova kuti kaya Yobu anali wolungama kapena ayi. (Yobu 4:18; 22:2, 3) Nkovuta kulingalila za mawu ena olefula maganizo kwambili—kapena onama kwambili—kuposa amenewo! N’zosadabwitsa kuti pambuyo pake Yehova anadzudzula Elifazi na mabwenzi ake kaamba ka mwano umenewu. Iye anati: “Simunanene zoona za ine.” (Yobu 42:7) Koma cinenezo cina covulaza koposa cinalikudza.
w03 4/15 14-15 ¶10-12
Acinyamata Amene Amakondweletsa Mtima wa Yehova
10 Monga mmene zikuonekela m’nkhani ya m’Baibo imeneyi, Satana anakayikila osati kukhulupilika kwa Yobu yekha komanso kwa ena onse amene amatumikila Mulungu, kuphatikizapo inuyo. Ndipotu, pofotokoza za anthu onse, Satana anauza Yehova kuti: “Khungu kusinthanitsa ndi khungu [osati Yobu yekha koma aliyense] munthu angalolele kupeleka ciliconse cimene ali naco kuti apulumutse moyo wake.” (Yobu 2:4) Kodi mukuona mbali yanu pankhani yofunika kwambili imeneyi? Monga mmene lemba la Miyambo 27:11 lasonyezela, Yehova akunena kuti pali cinacake cimene mungapeleke kwa iye, cimene cingathandize kuti ayankhe womutonzayo, Satana. Tangoganizani! Wolamulila wa Cilengedwe conse akukupemphani kuthandiza nawo poyankha nkhani yaikulu kwambili kuposa ina iliyonse. Inde, muli na udindo ndiponso mwayi waukulu. Kodi mungacite zimene Yehova akukupemphani? Yobu anatelo. (Yobu 2:9, 10) Yesu anatelonso pamodzi na anthu ena ambili-mbili kuyambila kale mpaka pano, kuphatikizapo acinyamata ambili. (Afil. 2:8; Chiv. 6:9) Inunso mungacite cimodzimodzi. Komabe, dziŵani kuti n’zosatheka kukhala opanda mbali pankhani imeneyi. Mwa zocita zanu, mudzasonyeza kuti muli ku mbali yotonza ya Satana kapena kumbali ya yankho la Yehova. Kodi mudzasankha kukhala mbali iti?
Yehova Amakusamalilani!
11 Kodi zimene mwasankha kucita zimakhudza Yehova? Kodi anthu amene anasonyeza kale kukhulupilika si okwanila kuthandiza kumuyankha mofikapo Satana? N’zoona kuti Mdyelekezi ananena kuti palibe amene amatumikila Yehova cifukwa comukonda, kuneneza kumene kwatsimikizilidwa kale kuti kunali kwabodza. Komabe, Yehova akufuna kuti inuyo mukhale ku mbali yake pankhani ya ulamuliloyi cifukwa amakusamalilani monga munthu panokha. Yesu anati: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”—Mat. 18:14.
12 Inde, Yehova amaona zimene mwasankha kucita. Kuposanso pamenepo, zimene mwasankhazo zimamukhudza. Baibo imafotokoza momveka bwino kuti zinthu zabwino kapena zoipa zimene anthu amacita zimamukhudza kwambili. Mwacitsanzo, pamene Aisiraeli anapanduka mobwelezabweleza, “anali kumukhumudwitsa” Yehova. (Sal. 78:40, 41) Cigumula ca m’nthawi ya Nowa cisanacitike, pamene ‘kuipa kwa anthu kunaculuka,’ Yehova “anamva cisoni.” (Gen. 6:5, 6) Taganizilani tanthauzo la zimenezi. Ngati mungasankhe kucita zinthu zoipa, mudzacititsa Mlengi wanu kupwetekedwa mtima. Zimenezi sizikutanthauza kuti Mulungu ni wofooka kapena kutengeka maganizo kumamulamulila ayi. M’malo mwake, iye amakukondani ndipo amasamala za moyo wanu. Koma ngati mucita zabwino, mtima wa Yehova umakondwela. Amasangalala osati kokha cifukwa wapeza zina zomuyankha Satana, komanso cifukwa cakuti tsopano angakhale Wokubwezelani Mphoto. Ndipo iye amafuna kucita zimenezi. (Aheb. 11:6) Inde, Yehova Mulungu ni Atate wanu wacikondi!
Kufufuza Cuma Cauzimu
Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu
Taganizilani mmene Yehova analengela zinthu zonse. Ponena kuti “panali madzulo ndiponso panali m’maŵa,” Yehova anasonyeza kuti anagaŵagaŵa nyengo iliyonse yolengela zinthu. (Gen. 1:5, 8, 13, 19, 23, 31) Paciyambi pa nyengo iliyonse yolengela zinthuzo, iye anali kudziŵa bwino-bwino colinga cake, kapena kuti cimene anali kufuna kukwanilitsa pa nyengo imeneyo. Ndipo Mulungu anakwanilitsa colinga cake coti alenge zinthu. (Chiv. 4:11) Kholo lakale Yobu, anati “zimene moyo wake [Yehova] umalakalaka amazicita.” (Yobu 23:13) Yehova ayenela kuti anakondwela kwambili kuona “zonse zimene anapanga,” ndipo ananena kuti “zinali zabwino kwambili.”—Gen. 1: 31.
Kuti tikwanilitsedi zolinga zathu, nafenso tiyenela kukhala ofunitsitsa kuzikwanilitsa. Kodi n’ciyani cingatithandize kuti tikhale ofunitsitsa motelo? Ngakhale pamene dziko lapansi linali lopanda kanthu, Yehova anali kutha kuona mmene lidzakhalile akakwanilitsa colinga cake; anali kuona kuti lidzakhala ngati mwala wokongola wamtengo wapatali mumlengalengamu, ndipo lidzacititsa kuti iye alandile ulemelelo ndiponso alemekezedwe. Cimodzimodzinso ifeyo, tingakhale ofunitsitsa kukwanilitsa zolinga zathu poganizila bwino za mmene tidzapindulile tikakwanilitsa colinga cathuco. Izi n’zimene zinam’citikila Tony, yemwe ali na zaka 19. Iye sanaiŵale mmene anamvela nthaŵi yoyamba imene anakaona ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko lina la ku madzulo a ku Europe. Kucokela panthawiyi, funso limene Tony anali kungoliganizila linali lakuti, ‘Kodi ningamve bwanji nitamakhala ndiponso kutumikila pamalo aja?’ Tony anapitilizabe kuganizila zodzacita zimenezi, ndipo sanasiye kuyesayesa kukwanilitsa colinga cake. Patatha zaka zingapo iye anasangalala kwambili pamene anamuvomela kukatumikila pa nthambipo!
DECEMBER 11-17
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 25-27
“Tingakhale na Mtima Wosagaŵikana Ngakhale Ndife Opanda Ungwilo”
it-1 1210 ¶4
Mtima wosagaŵikana
Yobu. Yobu amene ayenela kuti anakhalako Yosefe atafa, komanso Mose asanakhale mtsogoleli wa Aisiraeli, amafotokozedwa kuti anali munthu wopanda colakwa (m’Ciheberi, tam) wowongoka mtima, woopa Mulungu, ndiponso wopewa zoipa. (Yobu 1:1) Kusagaŵikana mtima ni mbali ya nkhani yaikulu imene ili pakati pa Yehova Mulungu na Satana. Mfundo imeneyi, inaonekela bwino pamene Mulungu anafunsa mdani wake Satana za Yobu, panthawi imene anaonekela pa kukumana kwa angelo m’mabwalo a kumwamba. Satana anakamba zabodza ponena za colinga ca Yobu potumikila Mulungu. Iye anati Yobu sanali kutumikila Mulungu cifukwa codzipeleka na mtima wonse, koma anali kumutumikila cifukwa ca dyela. Apa iye anakayikila mtima wosagaŵikana umene Yobu anali nawo pa Mulungu. Ataloledwa kuwononga zinthu zonse za Yobu, ngakhale ana ake amene, Satana analephela kupwanya umphumphu wa Yobu. (Yobu 1:6–2:3) Kenako iye anakamba kuti, Yobu modzikonda anali wololela kutaya zinthu zake, kuphatikizapo ana ake malinga atapumulutsa moyo wake. (Yobu 2:4, 5) Ngakhale pambuyo pokanthidwa na matenda oŵaŵa komanso owononga thupi, kutsutsidwa na mkazi wake, komanso kunyozedwa na kutonzedwa na anzake amene sanali kumvetsa malamulo a Mulungu na colinga cake, (Yobu 2:6-13; 22:1, 5-11) Yobu anakambabe kuti adzapitiliza kukhala na mtima wosagaŵanika. Iye anati, “mpaka ine kumwalila sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagaŵanika. Ndagwila cilungamo canga ndipo sindicitaya. Mtima wanga sudzandinyoza masiku anga onse.” (Yobu 27:5, 6) Kukhalabe kwake na mtima wosagaŵikana, kunaonetsa kuti Mdani wa Mulungu ni wabodza.
Khalanibe na Mtima Wamphumphu!
3 Kwa atumiki a Mulungu, kukhala na mtima wamphumphu kumatanthauza kukonda Yehova na mtima wonse, komanso kudzipeleka kwathunthu kwa iye, moti pa zosankha zawo zonse, amaika Mulungu patsogolo. Tiyeni tione mmene mawuwa akuwaseŵenzetsela m’Baibo. M’Baibo, mawu akuti, “mtima wamphumphu,” kweni-kweni amatanthauza cinthu cathunthu, cabwino-bwino, kapena conse. Mwacitsanzo, Aisiraeli anali kupeleka nsembe za nyama kwa Yehova. Ndipo Cilamulo cinakamba kuti nyamazo zinafunika kukhala zopanda cilema. (Lev. 22: 21, 22) Aisiraeli sanaloledwe kupeleka nsembe nyama zodwala, zopanda mwendo umodzi, khutu, kapena diso. Yehova anali kufuna kuti nyama yopelekedwa nsembe izikhala yathunthu, komanso yabwino-bwino. (Mal. 1:6-9) Izi zionetsa kuti Yehova amafuna kuti tikhale na mtima wamphumphu kapena kuti wathunthu. Tiyelekezele motele: Tikapita ku msika, sitingagule cipatso conyemeka, buku long’ambika mapeji, kapena cipangizo cowonongeka mbali zina. Timafuna kugula cinthu cimene n’cathunthu, komanso cabwino-bwino. Yehova naye amafuna kuti tikhale okhulupilika kwathunthu kwa iye. Amafunanso kuti tizim’konda na mtima wonse.
4 Kodi izi zitanthauza kuti ife anthu opanda ungwilo sitingakwanitse kukhala na mtima wamphumphu? Iyayi. N’zoona kuti timalakwitsa nthawi zambili. Koma izi sizifunika kutigwetsa mphwayi. Cifukwa ciyani? Onani zifukwa ziŵili izi. Coyamba, Yehova sayang’ana kwambili pa zolakwa zathu. Mawu ake amati: “Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?” (Sal. 130:3) Iye amadziŵa kuti ndife opanda ungwilo, komanso ocimwa, ndipo ni wokonzeka kutikhululukila na mtima wonse. (Sal. 86:5) Caciŵili, Yehova amadziŵa zimene tingakwanitse kucita, ndipo satiyembekezela kucita zimene sitingakwanitse. (Ŵelengani Salimo 103:12-14.) Nanga zingatheke bwanji kukhala amphumphu komanso abwino-bwino pa maso pake?
5 Kwa atumiki a Yehova, cinsinsi cokhalila na mtima wamphumphu ni cikondi. Tifunika kukonda Mulungu na mtima wonse, komanso kukhala wodzipeleka kwathunthu kwa iye. Tikatelo, ndiye kuti olo tiyesedwe bwanji, tidzakhalabe okhulupilika. (1 Mbiri 28:9; Mat. 22:37) Ganizilaninso za Mboni zitatu zija zimene tachula kuciyambi kwa nkhani ino. N’cifukwa ciyani iwo anakhalabe okhulupilika? Kodi mlongo wacitsikana uja safuna kusangalala ku sukulu? Kodi m’bale wacinyamata uja amakondwela kunyozedwa mu ulaliki wa nyumba na nyumba? Nanga bwanji m’bale wina uja wapanchito? Kodi sadela nkhawa zocotsedwa nchito? Kutalitali! M’malomwake, Akhristu amenewa anadziŵa kuti mfundo za Yehova n’zolungama, ndipo anafuna kukondweletsa Atate wawo wakumwamba. Cikondi cawo pa Mulungu cinawasonkhezela kuika cifunilo cake patsogolo popanga zosankha. Mwa ici, iwo anaonetsa kuti ali na mtima wamphumphu.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Gulu Lake Ladongosolo Monga mwa Buku la Mawu Ake
3 Cilengedwe cimationetsa kuti palibe angapose Mulungu pa nkhani ya dongosolo. Baibo imakamba kuti: “Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzelu. Anakhazikitsa kumwamba mozindikila.” (Miy. 3:19) Ise timadziŵako “kambali kakang’ono cabe ka zocita zake,” ndipo “timangomva kunong’ona kwapansi-pansi kwa mawu ake.” (Yobu 26:14) Ngakhale n’conco, zocepa zimene timadziŵako za mapulaneti, nyenyezi, na milalang’amba, zimatipangitsa kuvomeleza kuti zinthu zakuthambo zinalinganizidwa mwa dongosolo lodabwitsa. (Sal. 8:3, 4) Mwacitsanzo, milalang’amba ili ndi nyenyezi mamiliyoni ambili, koma zonsezo zimayenda mwadongosolo. Mapulaneti amayenda mozungulila dzuŵa monga kuti akutsatila bwino-bwino malamulo a pa msewu. Kukamba zoona, maumboni a zakuthambo ogometsa maganizo amenewa amatithandiza kudziŵa kuti Yehova, amene “anapanga kumwamba mwanzelu” na dziko lapansi, afunika kum’tamanda, kum’lambila, na kukhala okhulupilika kwa iye.—Sal. 136:1, 5-9.
DECEMBER 18-24
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 28-29
“Kodi Mbili Yanu ili Ngati ya Yobu?”
w02 5/15 22 ¶19
Komelani Mtima Anthu Osoŵa Thandizo
19 Nkhani za m’Baibo zimene takambilana zikutsindikanso mfundo yosonyeza kukoma mtima kwa anthu osoŵa thandizo limene iwo paokha sangathe kulipeza. Abulahamu anafunika thandizo la Betuele kuti mzele wa banja lake upitilile. Yakobo anafunikila thandizo la Yosefe kuti mtembo wake akauike ku Kanani. Ndipo Naomi anafunika thandizo la Rute kuti apeze mwana woloŵa nyumba. Abulahamu, Yakobo, na Naomi sakanatha kucita zimenezo popanda thandizo. Mofananamo lelolino, tiyenela kusonyeza kukoma mtima makamaka kwa anthu osoŵa thandizo. (Miy. 19:17) Tifunika kutsanzila Yobu, kholo lakale, amene anasamala “wosautsika wopempha thandizo, ndiponso mwana wamasiye ndi aliyense amene analibe womuthandiza,” komanso “munthu amene watsala pang’ono kuwonongedwa.” Ndiponso, Yobu ‘anakondweletsa mtima wa mkazi wamasiye’ ndipo ‘anali ngati maso kwa wakhungu, komanso mapazi kwa wolumala.’—Yobu 29:12-15.
it-1 655 ¶10
Zovala
Zovala zimaimila zinthu zosiyanasiyana m’Baibo. Monga mmene yunifomu kapena covala cina capadela cimadziŵikitsila kuti munthu ali m’gulu linalake, nazonso zovala zikaseŵenzetsedwa mophiphilitsa m’Baibo, zimadziŵikitsa udindo wa munthu na zimene amacita mogwilizana na udindo umenewo, monga zinalili m’fanizo la Yesu la covala ca pa ukwati. (Mat. 22:11, 12) Pa Chivumbulutso 16:14, 15, Ambuye wathu Yesu Khristu, akuticenjeza kuti tisagone mwauzimu kuti tisavulidwe cizindikilo cake cakuti ndife Mboni zokhulupilika za Mulungu woona. Izi zingakhale zoopsa kwambili pamene tikuyandikila tsiku la “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”
w09 2/1 15 ¶3-4
Mayina Atanthauzo
Sitingasankhe tokha dzina limene timapatsidwa pobadwa. Komabe, timapanga tokha mbili imene timakhala nayo. (Miy. 20:11) Bwanji osadzifunsa kuti: ‘Ngati Yesu kapena atumwi ake akanakhala na mwayi wonipatsa dzina, kodi akananipatsa lotani? Kodi dzina labwino lofotokoza mbili yanga kapena khalidwe langa lingakhale liti?’
Funso limeneli tifunika kuliganizila mofatsa kwambili. N’cifukwa ciyani tikutelo? Mfumu yanzelu Solomo inalemba kuti: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi cuma coculuka.” (Miy. 22:1) Ndithudi, ngati tili na dzina labwino kapena mbili yabwino m’dela limene timakhala, ndiye kuti tili na cuma camtengo wapatali. Koma cofunika kwambili n’cakuti tikakhala na dzina labwino kwa Mulungu ndiye kuti tidzapeza cuma cosatha. Kodi zimenezi zingacitike motani? Mulungu akulonjeza kuti adzalemba mu “buku la cikumbutso” mayina a anthu amene amamuopa ndipo adzawapatsa moyo wosatha.—Mal. 3:16; Chiv. 3:5; 20:12-15
Kufufuza Cuma Cauzimu
g00 7/8 29 ¶3
Mwetulilani—N’zothandiza kwa Inu!
Kodi kumwetulila kumasinthadi zinthu? Cabwino, kodi mukumbukila nthawi yomwe kumwetulila kwa munthu winawake kunakupatsani mpumulo kapena kunakukhalitsani womasuka? Kapena pamene munacita mantha kapena kudzimva kukhala wokanidwa cifukwa cakuti winawake sanakumwetulileni? Inde, kumwetulila kumasinthadi zinthu. Kumakhudza onse aŵili, womwetulilayo komanso womwetulilidwa. Ponena za adani ake, munthu wa m’Baibo Yobu anati: “Ndinkawamwetulila, koma iwo sankakhulupilila, ndipo kuwala kwa pankhope panga sankakuzimitsa.” (Yobu 29:24) “Kuwala” kwa nkhope ya Yobu kuyenela kuti kunasonyeza cimwemwe cake kapena kukondwela kwake.
DECEMBER 25-31
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 30-31
“Zimene Zinathandiza Yobu kukhalabe Woyela”
w10 4/15 21 ¶8
Musamaone Zinthu Zacabe!
8 Akhristu oona nawonso amakhala na cilakolako ca maso na ca thupi. N’cifukwa cake Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kukhala odziletsa pa nkhani ya zinthu zimene timaona na zimene timakhumbila. (1 Akor. 9: 25, 27; ŵelengani 1 Yohane 2:15-17.) Munthu wolungama Yobu anazindikila kuti pali kugwilizana pakati pa kuona na kukhumbila. Iye anati: “Ndacita pangano ndi maso anga. Conco ndingayang’anitsitse bwanji namwali?” (Yobu 31:1) Yobu anakana kukhudza mkazi m’njila yaciwelewele komanso sanalole kumaganiza zinthu zotelozo m’pang’ono pomwe. Yesu anatsindika mfundo yakuti sitiyenela kuganizila zaciwelewele. Iye anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wacita naye kale cigololo mumtima mwake.”—Mat. 5:28.
w08 9/1 11 ¶4
Ganizilani “Mapeto Ake”
Musanaloŵe m’njila imeneyi, dzifunseni kuti, ‘Kodi njila iyi ikupita kuti?’ Kuyamba mwaganizila kaye pang’ono za “mapeto ake” kungakuthandizeni kupewa kucita zinthu zimene zingakuloŵetseni m’mavuto. Njila yonse ya anthu amene amanyalanyaza malangizo amenewa ni yodzaza na mavuto monga Edzi, matenda osiyanasiyana opatsilana pogonana, kutenga mimba zapathengo, kutaya mimba, kutha kwa mabanja, kapena kudana na anthu ena ndiponso kuvutika na cikumbumtima. Mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino za mapeto a njila ya anthu amene amacita zaciwelewele. Iye anati “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akor. 6:9, 10.
w10 11/15 5-6 ¶15-16
Acinyamata, Muzitsogoleledwa na Mawu a Mulungu
15 Kodi inu mumaona kuti mungayesedwe kwambili pa nkhani yokhala wokhulupilika pamaso pa Mulungu pa nthawi imene muli na anthu ena kapena mukakhala nokha? Mukakhala kusukulu kapena kunchito mosakayikila mumakhala wosamala na zinthu zimene zingawononge ubwenzi wanu na Mulungu. Koma pa nthawi imene mukupumula panokha ndiponso pamene simuli chelu kwambili m’pamene mungagonje mosavuta poyesedwa.
16 N’cifukwa ciyani muyenela kumvela Yehova ngakhale pamene muli nokha? Kumbukilani izi: Zocita zanu zingacititse kuti mukondweletse mtima wa Yehova kapena kumumvetsa cisoni. (Gen. 6:5, 6; Miy. 27:11) Zocita zanu zimakhudza Yehova cifukwa cakuti iye “amakudelani nkhawa.” (1 Pet. 5:7) Iye amafuna kuti muzimumvela n’colinga coti zinthu zikuyendeleni bwino. (Yes. 48:17, 18) Atumiki a Yehova m’nthawi ya Aisiraeli akanyalanyaza malangizo ake, Yehova anali kumva cisoni. (Sal. 78:40, 41) Koma Yehova anali kukonda kwambili mneneli Danieli moti mngelo anamuuza kuti iye anali “munthu wokondedwa kwambili.” (Dan. 10:11) N’cifukwa ciyani zinali conco? Danieli anali wokhulupilika kwa Mulungu akakhala pagulu komanso akakhala payekha.—Ŵelengani Danieli 6:10.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 11/15 11 ¶3
Luso Lomvetsela Ena Mwacikondi
Anzake a mwamuna uja Yobu anamvetsela nkhani zosacepela 10 kucokela kwa Yobu. Komabe, Yobu ananena kuti: “Ndikulakalaka ndikanakhala ndi wina wondimvetsela.” (Yobu 31:35) N’cifukwa ciyani Yobu analankhula conco? Cifukwa cakuti kumvetsela kwawo sikunali kotonthoza. Sanasamale za iye ndipo sanafune kumvetsa maganizo ake. N’zoona kuti iwo sizinawakhudze mtima ngati mmene zimakhalila na anthu acifundo. Koma mtumwi Petulo anapeleka uphungu wakuti: “Nonsenu mukhale a maganizo amodzi, omvelana cisoni, okonda abale, a cifundo cacikulu, a maganizo odzicepetsa.” (1 Pet. 3:8) Kodi tingasonyeze bwanji cifundo? Njila imodzi ndiyo kukhudzidwa na maganizo a wina na kuyesa kuwamvetsetsa. Kukamba mawu otonthoza ni njila imodzi yosonyezela kuti zikutikhudza. Mwacitsanzo tinganene kuti, “zimenezo n’zokhumudwitsadi,” kapena kuti “koma ndiye anakumvani molakwikatu.” Njila ina ndiyo kulankhula zomwe munthu akutiuzazo m’mawu athu-athu, ndipo zimenezi zimasonyeza kuti tikumvetsa zimene munthuyo akunena. Kumvetsela mwacikondi kumatanthauza kumva mosamala osati mawu okha ayi, koma ngakhalenso kuzindikila zimene munthuyo akuganiza ngakhale sanazilankhule.