NYIMBO 123
Gonjelani Dongosolo la Mulungu
Yopulinta
1. Anthu a Yehova polalikila
Uthenga wabwino pa dziko lonse,
Mokhulupilika amatsatila
Dongosolo lake Yehova M’lungu.
(KOLASI)
Tizigonjela Mulungu wathu,
Mokhulupilika.
Atiteteza, aticengeta,
Timukhulupilile.
2. Atate Yehova anatipatsa
Kapolo wake na mzimu woyela.
Amafuna kuti ticilimike,
Mokhulupilika tim’tumikile!
(KOLASI)
Tizigonjela Mulungu wathu,
Mokhulupilika.
Atiteteza, aticengeta,
Timukhulupilile.
(Onaninso Luka 12:42; Aheb. 13:7, 17.)