LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w17 June masa. 22-26
  • Muziika Maganizo Anu pa Nkhani Yaikulu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muziika Maganizo Anu pa Nkhani Yaikulu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’CIFUKWA CIANI NI NKHANI YOFUNIKA KWAMBILI?
  • KUKWEZA ULAMULILO WA YEHOVA N’KOFUNIKA KUPOSA CIPULUMUTSO
  • CITSANZO COTITHANDIZA KUONA ZINTHU MOYENELA
  • KUIKABE MAGANIZO ATHU PA NKHANI YAIKULU
  • Muzicilikiza Ulamulilo wa Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • “Yembekezela Yehova”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
w17 June masa. 22-26
Satana pofuna kuonetsa Mulungu kuti zimene iye anakamba n’zoona, anagwetsela Yobu masoka, kum’dwalitsa matenda oopsa, ndi kum’sautsa na anthu otonthoza acinyengo

Muziika Maganizo Anu pa Nkhani Yaikulu

“Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, . . . . pa dziko lonse lapansi.”—SAL. 83:18.

NYIMBO: 46, 136

KODI MWAPHUNZILA CIANI?

  • N’cifukwa ciani kucilikiza ulamulilo wa Yehova ni nkhani yaikulu yokhudza anthu onse?

  • Kodi kukhulupilika kwa Yobu poyesedwa kunakweza bwanji ulamulilo wa Yehova? Nanga n’ciani cimene Yobu analakwitsa?

  • Ni zinthu zina ziti zofunika zimene tingacite zoonetsa kuti timacilikiza ulamulilo wa Yehova?

1, 2. (a) Ni nkhani yaikulu iti imene ikhudza anthu onse? (b) N’cifukwa ciani tifunika kuiona kukhala yofunika kwambili?

ANTHU ambili masiku ano amaona kuti ndalama ndiye nkhani yaikulu. Iwo amaika maganizo awo onse pa kudziunjikila cuma kapena kuciteteza. Ena amaona kuti cofunika ngako ni banja lawo, thanzi, kapena zinthu zina zimene afuna kucita paumoyo.

2 Komabe, nkhani yaikulu kwambili imene ikhudza anthu onse ni kucilikiza ucifumu wa Yehova. Tifunika kukhala osamala kuti tisaleke kuona nkhaniyi kukhala yofunika kwambili. N’ciani cingatilepheletsa kuiona conco? Tingayambe kutangwanika ngako na zocitika za paumoyo. Kapena tingakhale na nkhawa kwambili ndi mavuto amene tikumana nawo cakuti tingalephele kuika maganizo athu pa nkhani yaikulu imeneyi. Koma ngati timaona kuti kucilikiza ucifumu wa Yehova n’kofunika, cidzakhala cosavuta kupilila mavuto amene timakumana nawo tsiku na tsiku. Komanso ubwenzi wathu ndi Yehova udzalimba ngako.

N’CIFUKWA CIANI NI NKHANI YOFUNIKA KWAMBILI?

3. Kodi Satana anakamba ciani ponena za ulamulilo wa Mulungu?

3 Zimene Satana Mdyelekezi anacita zinayambitsa cikayikilo cakuti kaya Yehova ni woyeneladi kulamulila kapena ayi. Iye anakamba kuti ulamulilo wa Mulungu ni woipa ndi kuti Yehova amamana zabwino anthu ake. Malinga n’zokamba zake, Mdyelekezi anaonetsa kuti anthu angakhale acimwemwe ngako ngati adzilamulila okha. (Gen. 3:1-5) Cinanso, iye anaonetsa kuti palibe munthu amene ni wokhulupilika kwa Mulungu ndi mtima wonse, ndi kuti aliyense angakane ulamulilo wa Yehova ngati atakumana ndi mavuto aakulu. (Yobu 2:4, 5) Cifukwa ca zimene Mdyelekezi anakamba, Yehova walola kuti anthu adzilamulile n’colinga cakuti adzionele okha kuti kudzilamulila kumabweletsa mavuto aakulu.

4. N’cifukwa ciani nkhani yokhudza ulamulilo wa Mulungu iyenela kuthetsedwa?

4 Yehova amadziŵa kuti zimene Mdyelekezi anakamba n’zabodza. Nanga n’cifukwa ciani iye walola kuti nkhaniyi ipitilizebe mwa kupatsa Satana nthawi yotsimikizila kuti zokamba zake n’zoona? N’cifukwa cakuti nkhaniyi ikhudza anthu onse kuphatikizapo angelo. (Ŵelengani Masalimo 83:18.) Kumbukilani kuti anthu aŵili oyambilila anakana ulamulilo wa Yehova, ndipo kuyambila nthawiyo, anthu enanso ambili aukana. Izi zingapangitse ena kuganiza kuti mwina zimene Mdyelekezi anakamba zokhudza ulamulilo wa Mulungu n’zoona. Ngati anthu ndi angelo sangadziŵe zoona pankhaniyi, n’zosatheka padziko lapansi kukhala mgwilizano ndi mtendele weni-weni. Koma zikadzadziŵika kuti ucifumu wa Yehova ndiwo wabwino, onse adzagonjela ulamulilo wake wolungama kwamuyaya. Ndipo m’cilengedwe conse mudzakhala mtendele.—Aef. 1:9, 10.

5. Kodi tingam’cilikize bwanji Yehova pankhani ya ulamulilo?

5 Panthawi yake, ulamulilo wa Mulungu udzadziŵika kuti ndiwo woyenela, koma ulamulilo wa Satana ndi anthu udzalephela ndipo udzathetsedwa. Ndiyeno, Mulungu adzayamba kulamulila kupitila mu Ufumu wa Mesiya. Panthawiyo, anthu okhulupilika adzakhala atapeleka umboni wakuti anthu akhoza kucilikiza ulamulilo wa Mulungu molimba mtima. (Yes. 45:23, 24) Kodi mufuna kukhala mmodzi wa anthu ocilikiza ulamulilo wa Yehova mokhulupilika? Mwacionekele mufuna. Komabe, kuti tikhale okhulupilika, tifunika kuikabe maganizo athu pa nkhani yaikulu imeneyi ndi kumvetsetsa kufunika kwake.

KUKWEZA ULAMULILO WA YEHOVA N’KOFUNIKA KUPOSA CIPULUMUTSO

6. Kodi kucilikiza ulamulilo wa Yehova n’kofunika bwanji?

6 Monga takambila kale, kucilikiza ulamulilo wa Yehova ndiyo nkhani yaikulu yokhudza anthu onse. Ni yofunika ngako kuposa cinthu ciliconse cokondweletsa cimene anthufe tingapeze. Kodi izi zitanthauza kuti kupulumutsidwa kwa anthu n’kosafunika kweni-kweni ndi kuti Yehova satinganizila? Iyayi. N’cifukwa ciani takamba conco?

7, 8. Pokweza ucifumu wake, n’cifukwa ciani tinganene kuti Mulungu adzaonetsetsa kuti wakwanilitsa malonjezo ake?

7 Yehova amatikonda kwambili ise anthu ndipo amationa kuti ndise ofunika ngako. Iye analolela kugwilitsila nchito magazi a Mwana wake kuti tidzakhale na moyo wosatha. (Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:9) Ngati Yehova sangacite zimene analonjeza, Mdyelekezi angapeze cifukwa conenela Mulungu kuti ni wabodza, amamana anthu ake zabwino, ndi kuti salamulila mwacilungamo. Komanso zingapangitse kuti zokamba za anthu onyoza zioneke monga zoona. Iwo amati: “Kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti? Taonani, kucokela tsiku limene makolo athu anamwalila, zinthu zonse zikupitililabe cimodzimodzi ngati mmene zakhalila kuyambila pa ciyambi ca cilengedwe.” (2 Pet. 3:3, 4) Conco, pokweza ucifumu wake, Yehova adzaonetsetsa kuti wapulumutsanso anthu onse omvela. (Ŵelengani Yesaya 55:10, 11.) Kuwonjezela apo, Yehova amalamulila mwacikondi nthawi zonse. Cotelo, tingakhale otsimikiza kuti sadzaleka kukonda atumiki ake okhulupilika, kuwaona kukhala ofunika, ndi kuwayamikila pa zimene amacita.—Eks. 34:6.

8 Nkhani ya ulamulilo wa Yehova tiyenela kuiona kukhala yofunika kwambili kuposa cipulumutso cathu. Kucita izi sikutanthauza kuti timaona cipulumutso cathu kukhala cosafunika, kapena kuti timadziona ngati osafunika pamaso pa Mulungu. Koma kumatanthauza kuti nkhani ziŵilizi, ya ulamulilo wa Mulungu ndi ya cipulumutso, timaziona moyenelela. Kuona zinthu moyenelela n’kofunika ngako kuti tipitilize kuika maganizo athu pa nkhani yaikulu, ndi kucilikiza ulamulilo wa Yehova.

CITSANZO COTITHANDIZA KUONA ZINTHU MOYENELA

9. Kodi Satana anam’neneza ciani Yobu? (Onani pikica kuciyambi.)

9 Buku la Yobu limaonetsa kuti kuona zinthu moyenela n’kofunika ngako. Buku limeneli ni limodzi mwa mabuku a m’Baibo oyambilila kulembedwa. Bukuli limafotokoza zimene Satana anakamba zakuti Yobu angakane Mulungu ngati angakumane na mavuto aakulu. Satana anapempha Mulungu kuti agwetsele Yobu masoka. Yehova sanacite zimenezo, koma analola Satana kuyesa Yobu. Anamuuza kuti: “Ciliconse cimene ali naco cikhale m’manja mwako.” (Ŵelengani Yobu 1:7-12.) M’kanthawi kocepa cabe, Yobu anatayikilidwa anchito ake, katundu, ndi ana ake 10. Satana anacita izi m’njila yakuti zioneke ngati kuti Mulungu ndiye anacititsa mavuto a Yobu. (Yobu 1:13-19) Kenako Satana anacititsa Yobu kudwala matenda opweteka ndi onyansa. (Yobu 2:7) Mavuto ake anawonjezeka cifukwa ca mau opweteka ndi ofooketsa a mkazi wake ndi a anzake atatu acinyengo.—Yobu 2:9; 3:11; 16:2.

10. (a) Kodi Yobu anacita ciani cimene cinaonetsa kuti anali wokhulupilika kwa Mulungu? (b) Nanga n’ciani cimene analakwitsa?

10 Kodi zotulukapo zake zinali zotani? Zokamba za Satana zinadziŵika kuti zinali bodza lamkunkhuniza. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto oopsa, Yobu sanamusiye Mulungu. (Yobu 27:5) Komabe, kwa kanthawi, Yobu analeka kuona zinthu moyenela. Anali kungokamba zinthu zodzilungamitsa, ndipo anafika popempha Mulungu kuti amuuze cifukwa cake anali kuvutika. (Yobu 7:20; 13:24) Mwina tingaganize kuti pamenepa Yobu sanalakwitse cifukwa anali atakumana ndi mavuto ambili. Koma Mulungu anaona kuti afunika kum’thandiza Yobu kuwongolela maganizo ake. Kodi Yehova anamuuza ciani?

11, 12. Kodi Yehova anathandiza Yobu kuzindikila ciani? Nanga Yobu anacitapo ciani?

11 Mau amene Mulungu anakamba kwa Yobu amakwana macaputa anayi m’buku la Yobu—caputa 38 mpaka 41. M’macaputa onsewa, Mulungu sanam’fotokozela mwacindunji Yobu cifukwa cake anali kuvutika. Cacikulu cimene Yehova anali kufuna pokamba na Yobu si kumufotokozela cifukwa cake anali kuvutika, ngati kuti Mulunguyo ndiye anacititsa mavuto ake, ndipo afuna kudzilungamitsa. Koma anali kufuna kumuthandiza kuzindikila kucepa kwake poyelekezela ndi Mulungu, amene ni wamkulu kwambili. Anathandizanso Yobu kuzindikila kuti pali nkhani zina zofunika kwambili zimene anafunika kuziganizila kuposa mavuto ake. (Ŵelengani Yobu 38:18-21.) Malangizo amenewo anam’thandiza kuyambanso kuona zinthu moyenela.

12 Kodi Yehova anacita nkhanza mwa kupatsa Yobu uphungu wamphamvu pambuyo pakuti wapilila ciyeso cacikulu? Iyayi, sanacite nkhanza, ndipo Yobu nayenso sanaganize conco. Ngakhale kuti anali pa mavuto aakulu, Yobu anayamikila malangizo amene Mulungu anam’patsa. Anafika pokamba kuti: “Ndikubweza mau anga, ndipo ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.” Umu ni mmene uphungu wamphamvu ndi wolimbikitsa wa Yehova unam’khudzila Yobu. (Yobu 42:1-6) Asanapatsidwe uphungu na Mulungu, Yobu anali atalandilapo kale uphungu wina wopelekedwa na Elihu. (Yobu 32:5-10) Yobu atalandila uphungu wa Mulungu ndi kusintha maganizo ake, Yehova anauza anzake a Yobu mau omuyamikila cifukwa ca kukhulupilika kwake pa ciyeso.—Yobu 42:7, 8.

13. Kodi uphungu umene Yehova anapatsa Yobu uyenela kuti unam’thandiza bwanji mavuto ake atatha?

13 Uphungu umene Yehova anapatsa Yobu unam’thandiza ngakhale pamene mavuto ake anatha. Kodi unam’thandiza bwanji? Malemba amati, “Yehova anadalitsa kwambili mapeto a Yobu kuposa ciyambi cake,” ndipo pambuyo pake “anakhalanso ndi ana aamuna 7 ndi ana aakazi atatu.” Ngakhale n’conco, payenela kuti panatenga nthawi yaitali ndithu kuti Yobu aiŵale mavuto ake. (Yobu 42:12-14) Mosakayikila, Yobu anali kuyewabe ana ake a poyamba amene anaphedwa na Satana. Kwa nthawi yaitali ndithu, iye ayenela kuti anali kuona zithunzi m’maganizo ake za mavuto amene anakumana nawo. Ngakhale kuti mwina m’kupita kwa nthawi Yobu anadziŵa cimene cinacititsa mavuto ake, nthawi zina ayenela kuti sanali kumvetsa cifukwa cake Mulungu analola kuti akumane na mavuto aakulu conco. Yobu akakhala na nkhawa cifukwa coganizila mavuto ake akale, mwacionekele anali kukumbukila uphungu umene Mulungu anam’patsa. Kucita izi kuyenela kuti kunali kum’thandiza kuonabe zinthu moyenela ndiponso kunam’tonthoza.—Sal. 94:19.

Mlongo alalikila atagona pabedi kucipatala; m’bale wagwila sinapu; mayi wanyamula mwana wake wamkazi panthawi ya tsoka la zacilengedwe

Kodi mumayesetsa kuganizila nkhani yaikulu, m’malo mongoganizila za mavuto anu? (Onani palagilafu 14)

14. Kodi tingaphunzilepo ciani pa zimene zinacitikila Yobu?

14 Nkhani ya Yobu ingatithandize kukhala na maganizo oyenela ndi kutitonthoza. Ndipo Yehova anaonetsetsa kuti nkhaniyi yalembedwa ‘kuti itilangize ndi kutipatsa ciyembekezo cifukwa malemba amatithandiza kupilila ndiponso amatilimbikitsa.’ (Aroma 15:4) Kodi tiphunzilapo ciani pankhaniyi? Mfundo yaikulu ni yakuti, sitiyenela kumangoganizila zocitika za pa umoyo wathu mpaka kufika poiŵala nkhani yofunika kwambili, imene ndi kucilikiza ulamulilo wa Yehova. Ndipo tizikumbukila kuti tingathandize kukweza ucifumu wa Mulungu mwa kukhalabe okhulupilika ngati Yobu tikakumana ndi mavuto aakulu.

15. Kodi kukhala okhulupilika pa mayeselo kuli na phindu lanji?

15 Kodi kuganizila phindu la kukhala wokhulupilika kumatithandiza bwanji? Kumatithandiza kudziŵa kuti ngati takumana ndi mavuto, si ndiye kuti Yehova watikwiyila, koma zimatipatsa mwayi woonetsa kuti timacilikiza ucifumu wa Mulungu. (Miy. 27:11) Kupilila mavuto kumatithandiza kukhala “ovomelezeka” komanso kumatipatsa ciyembekezo. (Ŵelengani Aroma 5:3-5.) Nkhani ya Yobu imapeleka umboni wakuti “Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo.” (Yak. 5:11) Conco, sitiyenela kukayikila kuti iye adzatidalitsa ifeyo ndi ena onse amene amacilikiza ulamulilo wake. Kukumbukila mfundo imeneyi kumatithandiza “kupilila zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso acimwemwe.”—Akol. 1:11.

KUIKABE MAGANIZO ATHU PA NKHANI YAIKULU

16. N’cifukwa ciani tifunika kumaganizila za kufunika kocilikiza ulamulilo wa Yehova?

16 Kuikabe maganizo athu pa nkhani yaikulu ya ulamulilo wa Yehova kungakhale kovuta. Nthawi zina, tingakhale na nkhawa kwambili cifukwa ca mavuto amene takumana nawo. Ngakhale mavuto aang’ono, angaoneke aakulu ngati timangokhalila kuwaganizila. Conco, nthawi zonse tikakumana ndi mavuto, ni bwino kumaganizila za kufunika kocilikiza ulamulilo wa Mulungu.

17. Kodi kugwila nchito ya Yehova nthawi zonse kungatithandize bwanji kuikabe maganizo athu pa nkhani yaikulu?

17 Kugwila nchito ya Yehova nthawi zonse, kumatithandiza kuikabe maganizo athu pa nkhani yaikulu yokhudza ucifumu wa Mulungu. Mwacitsanzo, mlongo wina dzina lake Renee, anadwala matenda a sitroko komanso anali na khansa, ndipo anali kuvutika na ululu nthawi zonse. Pamene anali m’cipatala, anali kulalikila madokota, odwala, ndi alendo okaona odwala. Nthawi ina pamene anali m’cipatala, analalikila kwa maola 80, m’mawiki yaŵili na hafu cabe. Ngakhale pamene anatsala pang’ono kumwalila, Renee sanaleke kuika maganizo ake pa nkhani ya ulamulilo wa Yehova. Kucita zimenezi kunali kum’thandiza kucepetsako nkhawa.

18. Kodi zimene zinacitikila mlongo wina zionetsa bwanji phindu locilikiza ulamulilo wa Yehova?

18 Timafunikanso kucilikiza ulamulilo wa Yehova ngakhale pamene tikumana ndi mavuto ang’ono-ang’ono. Mwacitsanzo, mlongo Jennifer anakhala pa eyapoti kwa masiku atatu kuyembekezela ndeke yopita kwawo. Kangapo konse, ndeke zopita kwawo sizinapite cifukwa ca zovuta zina. Mlongoyu anatopa, ndipo anayamba kusungulumwa. Zimenezi zikanacititsa kuti azingokhala n’kumadandaula. Komabe, iye anapemphela kuti adziŵe mmene angathandizile anzake amene anakhudzidwa na vutoli. Kodi zotulukapo zake zinali zotani? Analalikila anthu ambili ndi kugaŵila zofalitsa zoculuka. Iye anati: “N’naona kuti Yehova ananidalitsa panthawi yovuta imeneyo, ndipo ananipatsa mphamvu kuti nikwanitse kucita zinthu zimene zinacititsa kuti dzina lake litamandidwe.” Inde, mlongoyu anaika maganizo ake pa kucita cifunilo ca Yehova.

19. Kodi anthu a Yehova amaiona bwanji nkhani ya ulamulilo wake?

19 Mosiyana ndi cipembedzo conama, cipembedzo coona cimaona kuti ulamulilo wa Yehova ni wofunika kwambili. Kuyambila kale-kale, anthu a Mulungu akhala akucilikiza ucifumu wake. Conco, monga olambila oona, aliyense wa ise ayenela kuyesetsa kucilikiza ulamulilo wa Mulungu.

20. Kodi Yehova amamvela bwanji ngati muyesetsa kucilikiza ulamulilo wake?

20 Dziŵani kuti Yehova amayamikila kwambili zimene mumacita pocilikiza ulamulilo wake mwa kum’tumikila mokhulupilika ndi kupilila ziyeso. (Sal. 18:25) Nkhani yotsatila idzafotokoza zifukwa zina zimene mufunika kucilikizila ulamulilo wa Yehova na mtima wonse komanso mmene mungacitile zimenezi.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani