NYIMBO 54
“Njila ni Iyi”
(Yesaya 30:20, 21)
1. Pali njila,
Njila ija
Yamtendele.
Ni njila imene
Munaiphunzila;
Ni ‘mene Yesu
Anakuphunzitsani;
Imapezeka mu Mau a Yehova.
(KOLASI)
Nayi njila, njila yakumoyo.
M’saceuke; inu m’sapatuke!
Yehova M’lungu aitana:
‘Nayi njila, njila ni ‘meneyi’.
2. Pali njila,
Njila ija
Yacikondi.
Inde, njila yosacita
Kusakila.
Mu njilayi
Timamudziŵa Yehova.
Ni Mulungu wa cikondi cazoona.
(KOLASI)
Nayi njila, njila yakumoyo.
M’saceuke; inu m’sapatuke!
Yehova M’lungu aitana:
‘Nayi njila, njila ni ‘meneyi’.
3. Pali njila,
Njila yopezela moyo.
M’njila iyi
Yehova watilonjeza:
“Mudzapeza
Madalitso amuyaya.”
Tim’tamande
Yehova Mulungu wathu.
(KOLASI)
Nayi njila, njila yakumoyo.
M’saceuke; inu m’sapatuke!
Yehova M’lungu aitana:
‘Nayi njila, njila ni ‘meneyi’.
(Onaninso Sal. 32:8; 139:24; Miy. 6:23.)