NYIMBO 99
Abale Miyanda Miyanda
Yopulinta
(Chivumbulutso 7:9,10)
1. Abale ni myanda myanda,
Osaŵelengeka,
Aliyense ni mboni,
Yokhulupilika.
Ise ndise ambili,
Tikuwonjezeka,
Tacoka kumitundu yonse,
Titamanda M’lungu.
2. Ise tili myanda myanda,
Timalalikila
Za uthenga wabwino,
Ku mitundu yonse.
Olo tileme bwanji,
Timalalikila,
Yesu amatitsitsimula;
Timapeza mphamvu.
3. Abale ni myanda myanda,
M’lungu atikonda,
Iye afuna kuti,
Tizim’tumikila.
Mokondwa tilengeza,
Za Ufumu wake,
Tikagwila nchito na M’lungu,
Timasangalala.
(Onaninso Yes. 52:7; Mat. 11:29; Chiv. 7:15.)