LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g18 na. 1 masa. 8-9
  • Cikondi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cikondi
  • Galamuka!—2018
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “CIMAGWILIZANITSA ANTHU [OKWATILANA] MWAMPHAMVU KWAMBILI KUPOSA CINTHU CINA CILICONSE”
  • Cikondi Khalidwe Lamtengo Wapatali
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Kodi ‘Mumakonda Anzanu Mmene Mumadzikondela’?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Galamuka!—2018
g18 na. 1 masa. 8-9
Banja lacimwemwe

NJILA YOPEZELA CIMWEMWE

Cikondi

ANTHU AMAFUNA-FUNA CIKONDI. Cikondi n’cofunika kwambili m’banja komanso pakati pa mabwenzi. Cimathandizanso kuti munthu akhale na mtendele wa m’maganizo na umoyo wacimwemwe. Kodi cimeneci ni “cikondi” ca bwanji?

N’zoona kuti cikondi ca pakati pa mwamuna na mkazi n’cofunika, koma cikondi cimene tikamba si cimeneci. Cikondi cimene tikamba ni capamwamba kwambili ndipo cimapangitsa munthu kukomela mtima ena, na kuika patsogolo zofuna za ena. Cikondi cimeneci cimayendela mfundo za m’Baibo komanso cimaphatikizapo ubwenzi na cifundo.

Baibo imafotokoza cikondi momveka bwino kuti: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima. Cikondi sicicita nsanje, sicidzitama, sicidzikuza, sicicita zosayenela, sicisamala zofuna zake zokha, sicikwiya. Sicisunga zifukwa. Sicikondwela ndi zosalungama, koma cimakondwela ndi coonadi. Cimakwilila zinthu zonse, . . . cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse. Cikondi sicitha.”—1 Akorinto 13:4-8.

Cikondi cimeneci “sicitha,” kutanthauza kuti cimapitiliza kukhalapo nthawi zonse, ndipo m’kupita kwa nthawi cimakula. Cifukwa cakuti n’coleza mtima, n’cokoma mtima, komanso cimakhululuka, cikondi cimeneci “cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.” (Akolose 3:14) Conco, ngati mabwenzi ali na cikondi cimeneci onse amakhala otetezeka ndi acimwemwe, ngakhale kuti ni opanda ungwilo. Mwacitsanzo, ganizilani za mgwilizano wa mwamuna na mkazi m’banja.

“CIMAGWILIZANITSA ANTHU [OKWATILANA] MWAMPHAMVU KWAMBILI KUPOSA CINTHU CINA CILICONSE”

Yesu Khristu anaphunzitsa mfundo zofunika kwambili zokhudza banja. Mwacitsanzo, iye anati: “‘Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiliwo adzakhala thupi limodzi.’ . . . Conco cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.” (Mateyu 19:5, 6) Pa lembali tipezapo mfundo ziŵili zofunika kwambili.

“AWILIWO ADZAKHALA THUPI LIMODZI.” Banja ni mgwilizano wamphamvu kuposa mgwilizano uliwonse umene munthu angakhale nawo. Ndipo cikondi ndiye cingateteze banja kuti lisaipitsidwe, popewa kukhala “thupi limodzi” na munthu amene si mwamuna kapena mkazi wake. (1 Akorinto 6:16; Aheberi 13:4) Kusakhulupilika kumacititsa okwatilana kusadalilana ndipo banja lingayambe kugwedezeka. Ngati m’banja muli ana, iwo angayambe kuvutika maganizo, kukhumudwa, na kudzimva kuti ni osatetezeka komanso osoŵa cikondi.

“CIMENE MULUNGU WACIMANGA PAMODZI.” Cikwati ni mgwilizano wopatulika. Mwamuna na mkazi amene amalemekeza mfundo imeneyi amayesetsa kulimbitsa cikwati cawo. Iwo akakumana na mavuto safuna-funa njila zothetsela cikwati cawo. Cikondi cawo cimakhala colimba ndipo amapilila. Cikondi monga cimeneci “cimapilila zinthu zonse” m’lingalilo lakuti cimathandiza okwatilana kutsiliza mavuto na kupitiliza kukhala ogwilizana ndi amtendele.

Ngati makolo ali na cikondi codzimana, mwana aliyense m’banja amapindula kwambili. Mtsikana wina dzina lake Jessica anati: “Atate na amayi amakondana na kulemekezana maningi. Nikaona mmene amayi alemekezela atate, zimanilimbikitsa kutengela khalidwe lawo.”

Cikondi ndiye khalidwe lalikulu la Mulungu. Ndipo Baibo imati: “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) N’cifukwa cake m’pake kuti Yehova amachedwa “Mulungu wacimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Na ise tingakhale na umoyo wacimwemwe ngati tiyesetsa kutengela makhalidwe a Mlengi wathu, maka-maka cikondi cake. Lemba la Aefeso 5:1, 2 limati: “Muzitsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo yendanibe m’cikondi.”

MFUNDO ZOFUNIKA

‘Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima. Cimakwilila zinthu zonse. Cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse. Cikondi sicitha.’—1 Akorinto 13:4-8.

Cikondi cimabweletsa cimwemwe cifukwa . . .

  • Cimatithandiza kuonetsa kuti timafunitsitsa kuika patsogolo zofuna za ena

  • Cimakula m’kupita kwa nthawi

  • Cimapeleka mphamvu zothandiza mabwenzi na mabanja kupilila

  • Cimathandiza kuti ana akule bwino na kudzimva kuti ni otetezeka

  • Cimatithandiza kutengela makhalidwe a Mlengi wathu

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani