LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g19 na. 2 masa. 8-9
  • Mmene Angakhalile Olimbikila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Angakhalile Olimbikila
  • Galamuka!—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KODI KULIMBIKILA KUMATANTHAUZA CIANI?
  • N’CIFUKWA CIANI KULIMBIKILA N’KOFUNIKA?
  • MMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA KULIMBIKILA
  • Makolo—Thandizani Ana Anu Kulimbitsa Cikhulupililo Cawo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Galamuka!—2019
g19 na. 2 masa. 8-9
Alimbikitsa mwana wawo amene wakhumudwa, cifukwa keke imene wapanga sinaoneke bwino

PHUNZILO 3

Mmene Angakhalile Olimbikila

KODI KULIMBIKILA KUMATANTHAUZA CIANI?

Munthu wolimbikila sabwelela m’mbuyo akakumana na zopinga, kapena zofooketsa. Koma pamatenga nthawi kuti munthu akhale na khalidwe limeneli. Nthawi zina, mwana amagwa pophunzila kuyenda, koma amalimbikila. Mofananamo, mwana kuti aphunzile mmene angakhalile na umoyo waphindu, afunika kulimbikila olo akumane na mavuto.

N’CIFUKWA CIANI KULIMBIKILA N’KOFUNIKA?

Ana ena amagwa mphwayi akalephela kukwanilitsa zinazake, akakumana na vuto, kapena akapatsidwa uphungu. Ndipo ena salimbikila olo pang’ono. Komabe, ana afunika kudziŵa mfundo izi:

  • Si nthawi zonse pamene zinthu zidzatiyendela bwino.—Yakobo 3:2.

  • Mavuto amagwela aliyense. —Mlaliki 9:11.

  • Uphungu umathandiza munthu kuti awongolele. —Miyambo 9:9.

Kulimbikila kudzathandiza mwana wanu kulimbana na mavuto mu umoyo.

MMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA KULIMBIKILA

Mwana wanu akalephela zina zake.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.”—Miyambo 24:16.

Thandizani mwana wanu kuti aziona zinthu moyenela. Mwacitsanzo, kodi angacite ciani akafeluka mayeso ku sukulu? Mwina angacite ulesi na kukamba kuti: “Ine ndine wolephela!”

Conco, kuti mwana wanu akhale wolimbikila, mufunika kum’thandiza mmene angacitile bwino ulendo wotsatila. Mwanjila imeneyi, iye adzagonjetsa vuto imeneyo m’malo molola vutolo kum’gonjetsa.

Koma pewani kum’thetsela vuto mwana wanu. M’malo mwake, m’thandizeni kupeza njila yake yothetsela vuto imeneyo. Mwina mungam’funse kuti, “Kodi ungacite ciani kuti uziimvetsetsa sabujekiti imene imakuvuta?”

Pakagwa mavuto.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.”—Yakobo 4:14.

Za kutsogolo sizidziŵika. Munthu amene ni wolemela lelo, mailo angakhale wosauka. Amene ali na thanzi labwino-bwino lelo, mailo angapezeke kuti wadwala. Baibo imakamba kuti: “Anthu othamanga kwambili sapambana pampikisano, amphamvu sapambana pankhondo . . . cifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka zimagwela onsewo.”—Mlaliki 9:11.

Monga kholo, mumayesetsa kucita zilizonse zimene mungathe kuti muteteze mwana wanu ku zoopsa. Koma n’zosatheka kum’teteza ku mavuto onse a mu umoyo.

N’zoona kuti mwana wanu sangamvetsetse mmene zimakhalila munthu akacotsedwa nchito, kapena mavuto a zandalama. Komabe, mungam’thandize kulimbana na mavuto ena. Monga ubwenzi na mnzake ukasokonezeka, kapena wa m’banja akamwalila.a

Mwana wanu akapatsidwa uphungu.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Mvela uphungu . . . kuti udzakhale wanzelu m’tsogolo.”—Miyambo 19:20.

Sikuti munthu akapatsa mwana wanu uphungu, ndiye kuti amuvutitsa. M’malo mwake afuna kum’thandiza kuti awongolele pa zimene wacita kapena pa khalidwe lake.

Ngati mwaphunzitsa mwana wanu kulandila uphungu, inu monga kholo, komanso mwana wanu mudzapindula. Tate wina dzina lake John anati: “Ngati nthawi zonse ana sawongoleledwa akalakwitsa, iwo sadzaphunzila ciliconse. Adzapitiliza kubweletsa mavuto, ndipo imwe mudzaloŵa nchito yothetsa mavutowo mpaka kalekale. Izi zingapangitse umoyo wa makolo komanso wa mwana kukhala wovuta.”

Kodi mungam’thandize bwanji mwana wanu kupindula na uphungu? Kaya mwana wanu wapatsidwa uphungu kusukulu, kapena kwina kulikonse, pewani kumuuza kuti uphunguwo ni wosayenela. M’malo mwake mungam’funse kuti:

  • “Uganiza n’cifukwa ciani akupatsa uphungu umenewo?”

  • “Nanga ungacite ciani kuti uwongolele?”

  • “Kodi udzacita ciani ukadzakumananso na vuto imeneyi kutsogolo?”

Dziŵani kuti uphungu udzathandiza mwana wanu kukhala na umoyo wabwino lomba, komanso kutsogolo akadzakula.

a Onani nkhani yakuti “Kuthandiza Mwana Wanu Panthawi Yachisoni,” mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2008.

Alimbikitsa mwana wawo amene wakhumudwa, cifukwa keke imene wapanga sinaoneke bwino

APHUNZITSENI AKALI AANG’ONO

Mwana amene amalimbikila akalakwitsa kapena akakumana na zofooketsa, akakula amakhala wolimbikila pophunzila maluso, ndipo amakhala katswili pa malusowo

Aphunzitseni mwa Citsanzo Canu

  • Kodi nimavomeleza zolakwa zanga, kapena nimakonda kukankhila ena mlandu?

  • Kodi nimaŵauza ana anga zimene n’nalakwitsapo kumbuyoko, na zimene n’naphunzilapo?

  • Kodi nimaseka ena pa zolakwa zawo?

Zimene Makolo Ena Anacita . . .

“Sitinali kuteteza ana athu pa kavuto kena kalikonse. Pamene ine n’nali mwana, kupilila mavuto ena kunanithandiza kuti nikule bwino. Nawonso ana athu aŵili anakula bwino cifukwa sitinawapusitse.”—Jeff.

“Ngati ine na mkazi wanga tawalakwila ana athu, tinali kuwapepetsa. Inde, makolo akalakwa, kukhumudwa, kapena kucita zinthu mosazindikila, ni bwino kuwauza ana awo. Zimawathandiza kudziŵa kuti ni mmene umoyo ulili.”—James.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani