PHUNZILO 5
Citsogozo Ca Anthu Acikulile N’cofunikila
KODI N’NDANI AFUNIKA KUPELEKA CITSOGOZO KWA ANA?
Ana amafunikila citsogozo na malangizo ocokela kwa anthu acikulile mu umoyo wawo. Monga kholo, muli pamalo abwino kucita zimenezi, ndipo ni udindo wanu. Komabe, anthu ena acikulile angakuthandizileni kulangiza ana anu.
N’CIFUKWA CIANI CITSOGOZO CA ANTHU ACIKULILE N’COFUNIKA?
M’maiko ambili, anthu acicepele saceza kwambili na acikulile. Ganizilani izi:
Ana amathela nthawi yoculuka ku sukulu, kumene ana ndiwo amakhalako ambili kuposa matica ngakhale acikulile.
Acinyamata ena akakomboka ku sukulu, amapeza kuti makolo onse aŵili kulibe ku nyumba, mwina cifukwa cakuti onse amapita ku nchito.
Kafukufuku wina anapeza kuti ku America, ana a zaka pakati pa 8 na 12, amathela maola pafupifupi 6 tsiku lililonse, pa zosangalatsa za pa zipangizo zamakono.a
Buku lakuti Hold On to Your Kids limati: “Acicepele masiku ano amakonda kufunsila kwa . . . acicepele anzawo malangizo, citsogozo, komanso kufuna kutengela zitsanzo zawo, m’malo mofunsila kwa amayi awo, atate awo, aphunzitsi, kapena anthu ena acikulile.”
MMENE MUNGAPELEKELE CITSOGOZO KWA ANA ANU
Muzipeza nthawi yoceza nawo.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Phunzitsa mwana m’njila yomuyenelela. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”—Miyambo 22:6.
Mwacibadwa, ana amafuna citsogozo ca makolo awo. Akatswili amakamba kuti acicepele azaka pakati pa 13 na 19, amaona kuti citsogozo ca makolo awo n’cofunika ngako kuposa ca acicepele anzawo. “Makolo amakhalabe othandiza kwambili kuti ana awo akhale na maganizo, komanso makhalidwe abwino kuyambila ali aang’ono, mpaka m’zaka zaunyamata.” Izi n’zimene analemba Dr. Laurence Steinberg m’buku lakuti, You and Your Adolescent. Iye anawonjezela kuti: “Acicepele amafuna kumvela malingalilo a imwe makolo. Ndiponso amafuna kumvetsela zimene mungakambe, ngakhale kuti si nthawi zonse pamene angavomeleze poyela zimenezi, kapena kugwilizana na zonse zimene mungaŵauze.”
Mwacibadwa, ana amafuna citsogozo ca imwe makolo. Conco, athandizeni mwa kuwapatsa citsogozo canu. Pezani nthawi yoceza ndi ana anu, na kuŵauzako malingalilo anu pa nkhani zina. Mungaŵauzenso zimene mumaona kuti n’zofunika, na zimene mwapitamo mu umoyo wanu.
Apezeleni woŵathandiza.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu.”—Miyambo 13:20.
Kodi mungaganizileko munthu wina, wamakhalidwe abwino amene angakhalenso citsanzo cabwino kwa mwana wanu? Bwanji osakonza zakuti munthuyo azicezako na mwana wanu? Koma sititanthuza kuti mukam’tulile udindo wanu monga kholo ayi. Munthu wacikulile amene mumam’dalila kuti sangasokoneze mwana wanu, angakuthandizeni kupeleka citsogozo. Baibo imaonetsa kuti ngakhale pamene Timoteyo anakula, anali kupindulabe kwambili na mgwilizano umene anali nawo na mtumwi Paulo, ndipo nayenso Paulo anali kupindula.—Afilipi 2:20, 22.
Masiku ano, anthu m’mabanja ambili sakhalila pamodzi. Mwina n’cifukwa cakuti azimbuye, azimalume, anti, komanso acibale ena amakhala kwina. Ngati ni mmene zinthu zilili kwa inu, yesetsani kupezela ana anu mipata yoceza na anthu acikulile amene ali na makhalidwe abwino, amene mungakonde kuti ana anu akhale nawo.
a Kafukufuku ameneyu anapezanso kuti acicepele a zaka pakati pa 13 na 19, amathela maola pafupifupi 9 tsiku lililonse, pa zosangalatsa za pa zipangizo zamakono. Pakafukufuku ameneyo, sanaphatikizepo nthawi imene acinyamatawa amathela pa intaneti ya ku sukulu, komanso pocita homuweki.