Buku Lothandiza Kwambili M’mbili Yonse Ya Anthu
Baibo ni buku imene yamasulilidwa na kufalitsidwa kuposa buku lina lililonse. Conco, nzelu zopezeka m’Baibo zafikila anthu ambili na kuŵathandiza kuposa buku lina lililonse. Onani ziŵelengelo zotsatilazi:
KUMASULILA NA KUFALITSIDWA KWA BAIBO
96.5 pelesenti ya ciŵelengelo ca anthu pa dziko lonse angakhale na Baibo
Ipezeka m’vitundu 3,350 (YATHUNTHU KAPENA MBALI YAKE)
MABAIBO 5 BILIYONI Kapena kuposapo apangidwa. M’mbili yonse ya anthu, ici n’ciŵelengelo cacikulu kuposa buku lina lililonse
DZIŴANI ZAMBILI
YENDANI PA WEBUSAITI YATHU YA JW.ORG. PA WEBUSAITI IMENEYI:
Mungaŵelenge Baibo (m’vitundu vofika m’mahandiledi)
Mungacite daunilodi Baibo
Mungapeze mayankho pa mafunso a m’Baibo
Mungaŵelenge nkhani za mmene Baibo yathandizila anthu ambili kukhala na umoyo wabwino
Mungacite maphunzilo a Baibo a pa intanetia
Mungapemphe kuti wina aziphunzila Baibo na imwe
MABAIBO AMENE AFALITSIDWA NA MBONI ZA YEHOVA
MBONI ZA YEHOVA ZAYESETSA KUMASULILA NA KUFALITSA BAIBO.
Ena mwa ma Baibo amene tafalitsa kwa zaka zambili ni awa:
American Standard Version ya mu 1901
The Bible in Living English, Byington
The Emphatic Diaglott
King James Version
Revised Standard Version
Baibo ya Tischendorf ya Cipangano Catsopano
BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO
Ili m’vitundu vopitilila 180 (YATHUNTHU KAPENA MBALI YAKE)
227 MILIYONI MABAIBO A DZIKO LATSOPANO AMENE APULINTIWA KUCOKELA MU 1950
a Palipano, maphunzilo amenewa apezeka cabe m’Cizungu na Cipwitikizi. Kutsogolo adzayamba kupezekanso m’vitundu vina.