LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g22 na. 1 masa. 4-6
  • 1 | Tetezani Thanzi Lanu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 1 | Tetezani Thanzi Lanu
  • Galamuka!—2022
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIFUKWA CAKE KUCITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA
  • Zimene Muyenela Kudziŵa
  • Zimene Mungacite Pali Pano
  • Thanzi Labwino
    Galamuka!—2019
  • Zimene Mungacite kuti Muthane na Nkhawa
    Galamuka!—2020
  • Yamikilani Mphatso ya Mulungu ya Moyo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Galamuka!—2022
g22 na. 1 masa. 4-6
Pa tebulo pali zakudya zosiyanasiyana zopatsa thanzi.

DZIKOLI LILI PA MAVUTO AAKULU

1 | Tetezani Thanzi Lanu

CIFUKWA CAKE KUCITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA

Mavuto akhoza kuwononga thanzi lathu m’njila zambili.

  • Tikakumana na mavuto aakulu timapanikizika. Ndipo kupanikizika maganizo kwa nthawi yaitali kukhoza kutidwalitsa.

  • Pakagwa matsoka kapena pakacitika mavuto ena aakulu, cimakhala covuta acipatala kupeleka cithandizo cofunikila cifukwa odwala amaculuka ndipo mankhwala akhoza kucepa.

  • Matsoka amabweletsa mavuto a zacuma. Pa cifukwa cimeneci, anthu amalephela kugula zinthu zofunikila monga cakudya copatsa thanzi komanso mankhwala.

Zimene Muyenela Kudziŵa

  • Matenda aakulu komanso kupanikizika maganizo zingacititse kuti mupange zisankho zolakwika. Ndipo zimenezi zingakulepheletseni kusamalila thanzi lanu. Zotulukapo zake, matenda anu akhoza kukulilakulila.

  • Kusasamalila thanzi lanu kungapangitse kuti mudwale kwambili, ndipo zimenezi zingaike moyo wanu paciopsezo.

  • Mukakhala athanzi, m’pamenenso mumakhala okonzeka kupanga zisankho zabwino mukakumana na mavuto.

  • Kaya ndinu olemela kapena osauka, pali zimene mungacite kuti muteteze thanzi lanu.

Zimene Mungacite Pali Pano

Nthawi zonse munthu wanzelu, amaonelatu zimene zingacititse ngozi na kucita zonse zotheka kuti apewe ngoziyo. Mfundo imeneyi igwilanso pa nkhani ya thanzi lathu. Ngati timakhala aukhondo nthawi zonse, tingacepetseko kufalikila kwa matenda. Paja amati kupewa kumaposa kuciza.

“Tikakhala aukhondo komanso tikamasunga malo athu okhala ali aukhondo, timacepetsako ndalama zolipilila ku cipatala komanso zogulila mankhwala.”—Andreas.a

a Maina ena mu Galamuka! ino asinthidwa.

ZIMENE MUNGACITE​—Mfundo Zothandiza

Pa nthawi ya mavuto aakulu, tetezani thanzi lanu mwa kucita izi

KHALANI AUKHONDO

Munthu ali panja ndipo akusamba m’manja na sopo.

Khalani Aukhondo

Baibo imati: “Wocenjela ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Ganizilani zinthu zimene zingawononge thanzi lanu na kuzipewa.

  • Muzisamba kumanja na sopo kaŵili-kaŵili maka-maka musanagwile cakudya komanso mukacoka kucimbudzi.

  • Nthawi zonse muziyeletsa m’nyumba mwanu na kupaka mankhwala opha tulombo toyambitsa matenda, makamaka pamalo kapena pa zinthu zimene zimagwilidwa kaŵili-kaŵili.

  • Ngati n’kotheka, pewani kukhala pafupi na munthu amene ali na matenda oyambukila.

MUZIDYA ZAKUDYA ZOPATSA THANZI

Pa tebulo pali zakudya zosiyanasiyana zopatsa thanzi.

Muzidya zakudya zopatsa thanzi

Baibo imati: “Pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” (Aefeso 5:29) Timaonetsa kuti timakonda thupi lathu mwa kusamala na zimene timadya na kumwa.

  • Muzimwa madzi ambili.

  • Muzidya zipatso zosiyanasiyana komanso ndiwo zamasamba.

  • Cepetsani kudya zakudya za mafuta kwambili, mcele wambili, komanso shuga wambili.

  • Musamasute fodya, kugwilitsa nchito mankhwala osokoneza bongo, kapena kumwa moŵa kwambili.

“Kuti tipewe matenda, timayesetsa kudya zakudya zopatsa thanzi nthawi zonse. Apo ayi, sembe tiwononga kandalama kocepa kamene timapeza pogula mankhwala na kulipilila kucipatala. Conco, timaona kuti n’canzelu kugwilitsa nchito ndalama zathu kugula zakudya zopatsa thanzi.”—Carlos.

MUZICITA ZINTHU ZOLIMBITSA THUPI NA KUGONA MOKWANILA

Munthu akuthamanga mumsewu wafumbi.

Muzicita zinthu zolimbitsa thupi

Baibo imati: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwila nchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” (Mlaliki 4:6) Tiyenela kugaŵa bwino nthawi yogwila nchito komanso yopumula.

  • Muzicita zinthu zolimbitsa thupi. Mungayambe mwa kumapita kokayenda. Kucita zinthu zolimbitsa thupi kungakuthandizeni kukhalako athanzi ngakhale kuti ndinu acikulile, aulemali, kapena mukudwala matenda osathelapo.

  • Mayi wacitsikana akugona.

    Uzigona mokwanila

    Muzigona mokwanila. Kusagona mokwanila ngakhale kwa masiku oŵelengeka kungapangitse kuti muzikhala opanikizika komanso kuti muzilephela kuganiza bwino. M’kupita kwanthawi, kungapangitse kuti mudwale matenda aakulu.

  • Dziikileni nthawi yabwino yogona komanso youka. Ndipo tsiku lililonse muziitsatila.

  • Pewani kuonelela TV kapena kuseŵenzetsa foni, tabuleti, kapena kompyuta panthawi yogona.

  • Pewani kudya kwambili, kudya zakudya zopangitsa munthu kusoŵa tulo (caffeine), komanso kumwa moŵa mukatsala pang’ono kugona.

“Nimaona kuti kuculuka kwa nthawi imene nagona kumakhudza thanzi langa m’mbali zambili. Ngati sin’nagone mokwanila, nthawi zina mimamvela mutu kuŵaŵa komanso thupi kuphwanya. Koma nikagona mokwanila, nimakwanitsa kucita zilizonse zimene ningafunike kucita. Nimakhala wamphamvu kwambili ndipo sinidwala-dwala.”—Justin.

Cithunzi ca mu vidiyo yakuti “Kufalikila Kwa Tulombo Twa Matenda—Zoyenela Kucita.” Mzimayi akutsegulila citseko kalombo koyambitsa matenda.

KUTI MUDZIŴE ZAMBILI, onelelani vidiyo yakuti Kufalikila kwa Tulombo twa Matenda—Zoyenela Kucita. Fufuzani mutu wa vidiyo iyi, komanso ŵelengani nkhani yakuti “Zimene Mungacite Kuti Mukhale na Umoyo Wathanzi” pa jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani