LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g22 na. 1 masa. 13-15
  • 4 | Limbitsani Ciyembekezo Canu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 4 | Limbitsani Ciyembekezo Canu
  • Galamuka!—2022
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIFUKWA CAKE KUCITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA
  • Zimene Muyenela Kudziŵa
  • Zimene Mungacite Pali Pano
  • Baibo Imapeleka Ciyembekezo Codalilika
  • Baibo Imatilonjeza Moyo Wacimwemwe Kutsogolo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Baibo Imatilonjeza Moyo Wacimwemwe Kutsogolo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Oyambilapo
  • Kumene Mungapeze Ciyembekezo mu 2024—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
    Nkhani Zina
  • Kodi Ciyembekezo Codalilika Mungacipeze Kuti?
    Galamuka!—2004
Onaninso Zina
Galamuka!—2022
g22 na. 1 masa. 13-15
Baibo yotsegula ili pafupi na kapu yoikamo maluŵa.

DZIKOLI LILI PA MAVUTO AAKULU

4 | Limbitsani Ciyembekezo Canu

CIFUKWA CAKE KUCITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA

Nkhawa yobwela cifukwa ca mavuto a m’dzikoli, imakhudza anthu m’njila zosiyanasiyana. Ambili amene akumanapo na mavuto aakulu, sakhala na ciyembekezo ciliconse. Kodi zotulukapo zake zakhala zotani?

  • Ena safuna n’komwe kuganizila zakutsogolo.

  • Enanso amamwa moŵa kapena kugwilitsa nchito mankhwala osokoneza bongo kuti aiŵaleko mavuto.

  • Komanso ena amaona kuti zili bwino kufa cabe.

Zimene Muyenela Kudziŵa

  • Ena mwa mavuto amene mukukumana nawo angakhale a kanthawi kocepa, ndipo angathe mosayembekezeleka.

  • Ngakhale ngati mavuto anu sangathe palipano, pali zinthu zimene mungacite kuti mukwanitse kupilila.

  • Baibo imapeleka ciyembekezo ceniceni cakuti mavuto onse a anthu adzathelatu.

Zimene Mungacite Pali Pano

Baibo imati: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lotsatila lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.

Pewani kudela nkhawa kwambili zakutsogolo. Musalole kuti nkhawa ya zakutsogolo ikulepheletseni kucita zinthu zimene muyenela kucita palipano.

Kuganizila kwambili zinthu zoipa zimene zingacitike kapena ayi, kungawonjezele nkhawa yanu na kukutayitsani ciyembekezo ca tsogolo labwino.

ZIMENE MUNGACITE​—Mfundo Zothandiza

MUZIIKA MAGANIZO ANU PA ZINTHU ZOLIMBIKITSA

Mzimayi ali pafupi na windo, ndipo akuyang’ana panja mopanda nkhawa.

Baibo imati: “Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa, koma munthu wa mtima wosangalala amacita phwando nthawi zonse.” (Miyambo 15:15) Ngati mumangoganizila za mavuto anu, simungathe kuona kuti pali njila yothetsela mavutowo. Koma kuganizila zinthu zolimbikitsa, kungakuthandizeni kupeza njila yothetsela mavuto anu.

  • Cepetsankoni nthawi imene mumathela poonelela, kumvetsela, kapena kuŵelenga nyuzi.

  • Kumapeto kwa tsiku lililonse, muziganizilako zinthu ziŵili kapena zitatu zabwino zimene mungayamikile.

  • Lembani zinthu zimene muyenela kucita patsiku. Gaŵani nchito zikulu-zikulu m’zigawo zing’ono-zing’ono, kuti zikhale zosavuta kuona zimene mwakwanitsa kucita patsikulo.

PEMPHANI THANDIZO

Mwamuna wacikulile akulimbikitsa mwamuna wacinyamata.

Baibo imati: “Wodzipatula. . . amacita zosemphana ndi nzelu zonse zopindulitsa.” (Miyambo 18:1) Ngati mwagwela m’dzenje lozama, panokha simungakwanitse kutulukamo. Mungafunike thandizo la munthu wina.

  • Pemphani thandizo kwa a m’banja lanu kapena anzanu.

  • Inunso ganizilani mmene mungawathandizile. Kucitila ena zabwino kungakuthandizeni kuti musamangodela nkhawa za mavuto anu.

  • Ngati mulibiletu ciyembekezo ndipo muona kuti moyo ulibe phindu, mwina mungacite bwino kupita ku cipatala. Nthawi zina kuda nkhawa kwambili kumakhala cizindikilo ca matenda, monga a kuvutika maganizo. Anthu ambili anathandizidwa atapita ku cipatala.a

a Magazini ya Galamuka! siisankhila anthu thandizo la mankhwala.

Baibo Imapeleka Ciyembekezo Codalilika

Popemphela kwa Mulungu, wamasalimo wina anati: “Mawu anu ndi nyale younikila ku mapazi anga ndi kuwala kounikila njila yanga.” (Salimo 119:105) Onani mmene Baibo, Mawu a Mulungu, imatithandizila monga nyale.

Usiku pamene kuli mdima, nyale imatithandiza kudziŵa poyenela kuponda poyenda. Mofananamo, m’Baibo muli malangizo anzelu amene angatitsogolele pamene tifuna kupanga cisankho covuta.

Cina, nyale imatiunikila njila kuti tikwanitse kuona zimene zili kutsogolo. Mofanana na zimenezi, Baibo imatithandiza kudziŵa zimene zidzacitika kutsogolo.

Baibo ni buku lopatulika limene limafotokoza mbili ya anthu kucokela pa ciyambi. Koma si zokhazo, imapelekanso ciyembekezo codalilika ca zam’tsogolo. Imafotokoza:

Mmene mavuto anayambila

Baibo imati “ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.”—Aroma 5:12.

Cifukwa cake maboma alephela kuthetsa mavuto

Baibo imati “munthu amene akuyenda alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Mavuto a m’dzikoli aonetsa kuti lembali likamba zoona.

Zimene Mulungu adzacita

Baibo imaonetsa kuti “iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa siidzakhalaponso, sipadzakhalanso kulila kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

Cithunzi ca m’vidiyo yakuti “N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?” Mkazi akuuzako mwamuna wake zimene anaŵelenga m’Baibo.

KUTI MUDZIŴE ZAMBILI, onelelani vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani