LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g23 na. 1 masa. 12-14
  • Mpwey

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mpwey
  • Galamuka!—2023
  • Tumitu
  • Cifukwa Cake Mpweya Uli pa Ciwopsezo
  • Dziko Lapansi Analipanga Kuti Likhalepo Kwamuyaya
  • Kodi Anthu Akucitapo Ciyani?
  • Kodi Baibo Imatipatsa Ciyembekezo Cotani pa Nkhaniyi?
Galamuka!—2023
g23 na. 1 masa. 12-14
Mkazi na mwamuna wake akuyenda pa cipale cofewa ndipo akuyang’ana nyanja yozungulilidwa na nkhalango komanso mapili.

KODI DZIKO LAPANSI LIDZAPULUMUKA?

MPWEYA

MPWEYA ni wofunika kwambili, koma sitimaufunila kupuma kokha. Mpweya umatetezanso dziko lapansi ku cheza ca dzuŵa cowononga. Ndipo popanda mpweya, dziko lonse lapansi likanakhala lozizila kwambili.

Cifukwa Cake Mpweya Uli pa Ciwopsezo

Kuwononga mpweya kumawononganso zamoyo za padziko lapansi. Malinga na zimene bungwe la Padziko Lonse Loona Zaumoyo linakamba, ni anthu ocepa cabe amene amapuma mpweya wabwino.

Kuwononga mpweya kungabweletse matenda am’cifuwa, khansa ya kumapapu, komanso matenda a mtima. Kuwononga mpweya n’kumene kumacititsa anthu pafupifupi 7,000,000 kufa msanga caka ciliconse.

Dziko Lapansi Analipanga Kuti Likhalepo Kwamuyaya

Dziko lapansi analipanga kuti lizitha kupeleka mpweya wabwino wokwanila zamoyo zonse padziko lapansi. Izi zingatheke ngati anthu acepetsako kucita zinthu zowononga dziko. Onani zitsanzo izi.

  • Tidziŵa kuti nkhalango zimatenga mpweya wa carbon dioxide. Koma mitengo yochedwa mangrove yopezeka kufupi na gombe la nyanja imacita zoposa pamenepa. Mitengoyi imatenga mpweya wa carbon dioxide nthawi zoposa 5 poyelekezela na zimene nkhalango zimacita.

  • Posacedwapa akatswili apeza kuti zomela za m’madzi zobiliwila zimacotsa carbon dioxide mu mpweya. Zomelazi zimaoneka ngati masamba ndipo zimakhala ni tumphako tomwe tumapangitsa kuti ayandame mtunda wautali pamadzi. Zomelazi zikafika kutali pa nyanjapo, tumphako tuja tumaphulika, ndipo zomelazi zokhala na mpweya wa carbon dioxide zimamila mpaka pansi pa nyanja. Zomelazi zimakhazikika pansi pa nyanjapo kwa zaka mahandiledi ambili.

  • Pa nthawi ya mlili wa COVID-19, zinaonekela bwino kuti dziko lapansi limakwanitsa kukonzanso zimene anthu awononga. Mu 2020, pamene mafikatale a padziko lonse na magalimoto anacepetsako kutulutsa zowononga mpweya, mwamsanga mpweya unayamba kukhala wabwino. Malinga na lipoti la mu 2020 la padziko lonse lokamba za mpweya, maiko ambili amene anacitila lipoti anati anakhalako na mpweya wabwino pa nthawi imene anthu sanali kucoka pa nyumba cifukwa ca mlili.

    KODI MUDZIŴA?

    Mpweya Umatha Kudziyeletsa n’Kukhala Wabwino

    Chati yoonetsa kuculuka kwa fumbi mu mphweya ku New Delhi, India. Fumbilo linatsika kucoka pa 128.1, zimene zinali zowopsa kwa anthu onse, mu January 2020, kufika mpaka pa 35.5,zinakhalako nkhasako, mu August 2020.

    Pa nthawi ya mlili wa COVID-19, mu mzinda wa New Delhi, ku India, kuwonongeka kwa mpweya cifukwa ca mafakitale na magalimoto kunacepekela mwamsanga. Fumbi loipa lopezeka mu mpweya linacepa kwambili. Fumbi limeneli silioneka, koma lingabweletse matenda am’cifuŵa komanso matenda ena aakulu. Kusintha kumeneku kunali cabe kwa kanthawi, koma kunaonetsa kuti mpweya ungathe kudziyeletsa mwamsanga ku zinthu zowononga.

    Mu mzinda wa New Delhi, ku India, kumapeto kwa caka ca 2019, kukuoneka fumbi lambili cifukwa ca kuwonongeka kwa mpweya.

    © Amit kg/Shutterstock

    Kumapeto kwa caka ca 2019

    Mu mzinda wa New Delhi, ku India, panthawi ya mlili wa COVID-19, kukuoneka bwino cifukwa mpweya wakhalako wabwino.

    © Volobotti/Shutterstock

    Pa nthawi ya mlili wa COVID-19

Kodi Anthu Akucitapo Ciyani?

Mwamuna akuika njinga yake pambuyo pocoka ku nchito.

Kuyenda pa njinga kungacepetseko kuwononga mpweya

Maboma akupitiliza kulangiza anthu kuti acepetseko kucita zinthu zowononga mpweya. Nawonso asayansi akupezabe njila zatsopano zoyeletsela mpweya umene umawonongeka. Mwacitsanzo, njila ina yoyeletsela mpweya imaseŵenzetsa tuzilombo tosaoneka tumene tumacotsa zinthu zoipa mu mpweya. Cina, akatswili amalimbikitsa anthu kuyenda pansi kapena kuyendela pa njinga m’malo mwa galimoto. Amalimbikitsanso anthu kucepetsa kugwilitsa nchito zinthu monga nkhuni na malasha.

Mzimayi wakhala pansi ndipo akuphika cakudya panyumba pake. Citofu cimene akuphikapo n’cacing’ono koma cimacotsa utsi pang’ono.

Maboma ena akupeleka masitovu amakono kwa nzika zawo kuti acepetseko kuwonongeka kwa mpweya. Koma anthu ambili samakwanitsa kupeza zinthu zimenezi

Koma monga linaonetsela lipoti la maiko onse la 2020 (2020 World Air Quality Report), kuphatikizapo locokela ku Bungwe Loona Zaumoyo Padziko Lonse (WHO) ndiponso World Bank, anthu afunikila kucita zoposa pamenepa.

Lipotilo linati mu 2020, pali anthu ambili padziko omwe amaseŵenzetsa zinthu zowononga mpweya pophika. M’madela ambili, ni anthu ocepa cabe amene amakwanitsa kugula masitovu kapena kuseŵenzetsa njila zina zophikila.

Kodi Baibo Imatipatsa Ciyembekezo Cotani pa Nkhaniyi?

“Mulungu woona Yehova, amene analenga kumwamba ndiponso . . . amene anakhazikitsa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo, amene anapeleka mpweya kwa anthu amene ali mmenemo.”—Yesaya 42:5.

Mulungu ndiye anapanga mpweya umene timapuma na njila zacilengedwe zoyeletsa mpweya. Iye ali na mphamvu zopanda malile komanso amakonda anthu. Conco, kodi m’pomveka kuganiza kuti sadzacitapo kanthu kucotsa zimene zimawononga mpweya? Onani nkhani yakuti “Mulungu Analonjeza Kuti Dziko Lapansi Lidzakhalapo Kwamuyaya.”

DZIŴANI ZAMBILI

Mmene dziko lapansi limaonekela mlengalenga.

Kodi dziko lapansi linakhalako bwanji? Tambani vidyo yakuti Kodi Kumwamba na Dziko Lapansi Zinacita Kulengedwa? pa jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani