NKHANI 2
Baibo ndi Buku Locokela kwa Mulungu
Kodi Baibo imasiyana bwanji ndi mabuku ena onse?
Nanga ingakuthandizeni bwanji pa mavuto anu?
N’cifukwa ciani tiyenela kukhulupilila maulosi a m’Baibo?
1, 2. Kodi Baibo ndi mphatso yokondweletsa kwambili yocokela kwa Mulungu m’njila ziti?
KODI mungakumbukile pamene munalandila mphatso yocokela kwa mnzanu wapamtima? Mosakaikila, munakondwela nayo kwambili mphatso imeneyo. Mphatso imakuuzani kanthu kena ponena za munthu amene wakupatsani. Imakuuzani kuti munthu ameneyo amaona ubwenzi wanu kukhala wofunika kwambili. Mosakaikila, munamuyamikila mnzanuyo cifukwa ca mphatso imeneyo.
2 Baibo nayonso ndi mphatso yocokela kwa Mulungu, ndipo tiyenela kumuyamikila kwambili Mulungu kaamba ka mphatso imeneyi. Buku lapadela limeneli limatiuza zinthu zimene sitikanadziŵa popanda ilo. Mwacitsanzo, limatiuza za kulengedwa kwa nyenyezi zakumwamba, dziko lapansi, ndi mwamuna ndi mkazi woyamba. Baibo ili ndi mfundo zodalilika zimene zimatithandiza pa mavuto ndi nkhawa zathu. Imafotokoza mmene Mulungu adzakwanilitsila cifunilo cake ndi kubweletsa umoyo wabwino padziko lapansi. Kunena zoona, Baibo ndi mphatso yokondweletsa kwambili!
3. Kodi pamene Yehova anatipatsa Baibo zimatiuza ciani za iye? Nanga n’cifukwa ciani zimenezi zili zokondweletsa?
3 Cifukwa cina cimene Baibo ilili mphatso yokondweletsa kwambili, n’cakuti imatidziŵitsa kuti Yehova Mulungu amafuna kuti tim’dziŵe bwino kwambili. Buku limene anatipatsali ndilo umboni wa mfundo imeneyi. Zoona, Baibo ingakuthandizeni kumuyandikila Yehova.
4. Kodi n’ciani cimakucititsani cidwi ponena za kufalitsidwa kwa Baibo?
4 Ngati muli ndi Baibo, dziŵani kuti simuli nokha amene muli nayo. Baibo yonse kapena mbali yake cabe, yasindikizidwa m’zinenelo zopitilila 2,300. Zimenezi zionetsa kuti mwa anthu 100 alionse padziko lapansi 90 ali ndi Baibo. Tingakambe kuti, ma Baibo opitilila wani miliyoni amagawilidwa wiki iliyonse. Ma Baibo onse amene apangidwa, kaya athunthu kapena mbali yake cabe, afika m’mabiliyoni. Kunena zoona, palibe buku lililonse limene lingalingane ndi Baibo.
“Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika” limapezeka m’zinenelo zambili
5. Kodi Baibo ‘inauzilidwa’ bwanji ndi Mulungu?
5 Cinanso n’cakuti ‘Baibo inauzilidwa ndi Mulungu.’ (2 Timoteyo 3:16) Kodi anaiuzila bwanji? Baibo imadziyankhila yokha kuti: “Anthu analankhula mau ocokela kwa Mulungu motsogoleledwa ndi mzimu woyela.” (2 Petulo 1:21) Tiyelekezele kuti: Ambuye auza mdzukulu wao kuti awalembele kalata. Kodi tingakambe kuti maganizo ndi malangizo ali m’kalatayo ni a ndani? Mwacionekele ndi a ambuye ake. Sitingakambe kuti kalata ndi ya mdzukulu iyai, koma m’ceni-ceni ndi ya ambuye ake. N’cimodzi-modzi ndi Baibo. Uthenga umene ulimo ndi wa Mulungu, osati wa anthu amene anailemba. Mwa ici, Baibo yonse m’ceni-ceni ndi “mau a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13.
NKHANI ZAKE N’ZOGWILIZANA NDIPO N’ZOONA
6, 7. N’cifukwa ciani kugwilizana kwa nkhani za m’Baibo kuli kocititsa cidwi?
6 Baibo inalembedwa kwa zaka zopitilila 1,600. Anthu amene anailemba anakhalapo panthawi zosiyana-siyana, ndipo anakulila m’mikhalidwe yosiyana-siyana. Ena anali alimi, ena asodzi, ndi ena abusa. Panalinso aneneli, oweluza ndi mafumu. Wolemba uthenga wabwino Luka anali dokotala. Mosasamala kanthu za mikhalidwe yosiyana-siyana ya alembi a Baibo, iyo ndi yogwilizana kucokela kuciyambi mpaka kumapeto.a
7 Buku loyamba m’Baibo, limatiuza mmene mavuto a anthu anayambila. Buku lotsilizila limaonetsa mmene dziko lonse lapansi lidzakhalila paladaiso, kapena munda wokongola. Nkhani zosiyana-siyana za m’Baibo zimafotokoza zinthu zimene zinacitika kale-kale panyengo ya zaka zambili. Ndipo nkhani zonse zimenezi zimakhudza mmene Mulungu adzakwanilitsila cifunilo cake. Kugwilizana kwa nkhani za m’Baibo n’kocititsa cidwi, ndipo ndi mmene buku locokela kwa Mulungu liyenela kukhalila.
8. Pelekani zitsanzo zoonetsa kuti Baibo imakamba zoona ngakhale pa nkhani za sayansi.
8 Baibo imakambanso zoona pa nkhani za sayansi. Imakamba mfundo zimene zinali zotsogola kwambili panthawi imene inali kulembedwa. Mwacitsanzo, buku la Levitiko lili ndi malamulo a m’nthawi ya Aisiraeli, onena za kupatula munthu wodwala matenda oyambukila ndi nkhani zaukhondo, pamene mitundu ina yozungulila siinali kudziŵa zilizonse pankhani zimenezi. Ngakhale pamene anthu anali ndi maganizo olakwika ponena za mmene dziko lapansi lilili, Baibo inali itakamba kale zakuti dziko lapansi ndi lozungulila monga mpila. (Yesaya 40:22) Baibo inakambanso zoona kuti Mulungu “anakoloŵeka dziko lapansi m’malele.” (Yobu 26:7) N’zoona kuti Baibo si buku la sayansi. Koma pamene ikamba nkhani za sayansi, imakamba zoona. Kodi zimenezi sizimene timayembekezela m’buku locokela kwa Mulungu?
9. (a) Kodi Baibo imaonetsa bwanji kuti ngakhale pa nkhani za mbili yakale, ndi yoona ndipo ndi yodalilika?(b) Kodi kuona mtima kwa alembi a Baibo kumatiuza ciani za Baibo?
9 Ngakhalenso pa nkhani za mbili yakale, Baibo ndi yoona ndiponso ndi yodalilika. Pokamba zocitika za m’mbili yakale, siimakamba mwacisawawa cabe, koma molunjika. Mwacitsanzo, siimangochula maina cabe a anthu, koma imafotokozanso mibadwo ya makolo ao.b Akatswili olemba mbili yakale nthawi zambili salemba pamene mtundu wao unagonjetsedwa. Koma alembi a Baibo anali oona mtima, cakuti anali kulemba zolakwa zao ngakhalenso za mtundu wao. Mwacitsanzo, Mose, mlembi wa buku la Numeri, sanabise colakwa cake cimene Mulungu anam’dzudzula naco kwambili. (Numeri 20:2-12) Kuona mtima kumeneko sikupezeka-pezeka m’mabuku ena a mbili yakale, koma kumapezeka m’Baibo cifukwa ndi buku locokela kwa Mulungu.
BUKU LA NZELU ZOTHANDIZA
10. N’cifukwa ciani sitiyenela kudabwa kuti m’Baibo muli nzelu zothandiza?
10 Cifukwa cakuti Baibo inauzilidwa ndi Mulungu, ndi ‘yopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, ndi kuwongola zinthu.’ (2 Timoteyo 3:16) Zoona, m’Baibo muli nzelu zothandiza. Imaonetsa cibadwa ceni-ceni ca munthu. Zimenezi n’zosadabwitsa, cifukwa Mlembi wake, Yehova Mulungu, ndiye Mlengi. Iye amamvetsetsa bwino mmene timaganizila ndi mmene timamvelela kuposa ngakhale ife eni ake. Ndiponso, Yehova amadziŵa zimene timafunikila kuti tikhale acimwemwe. Amadziŵanso zinthu zimene tiyenela kupewa.
11, 12. (a) Kodi Yesu anakamba pa nkhani ziti mu Ulaliki wake wa pa Phili? (b) Kodi ndi pa nkhani zina ziti zimene Baibo imatithandizapo? Nanga n’cifukwa ciani uphungu wake ukali kugwila nchito mpaka lelo?
11 Tiyeni tione ulaliki wa Yesu wochedwa Ulaliki wa pa Phili, wopezeka pa Mateyu macaputala 5 mpaka 7. Mu ulaliki wake waluso lapamwamba umenewu, Yesu anakamba pankhani zosiyana-siyana, monga mmene tingapezele cimwemwe ceni-ceni, mmene tingathetsele mikangano, mmene tingapemphelele, ndi mmene tiyenela kuonela zinthu za kuthupi. Mau a Yesu akali amphamvu ndi othandiza kwambili ngakhale masiku ano monga mmene analili panthawi imeneyo.
12 Mfundo zina za m’Baibo zimakhudza umoyo wa m’banja, magwilidwe anchito, ndi mmene tiyenela kukhalila ndi anthu ena. Mfundo za m’Baibo zimagwila nchito kwa aliyense, ndipo uphungu wake umakhala wopindulitsa nthawi zonse. Yesaya anaonetsa kuti nzelu zopezeka m’Baibo n’zothandiza, pamene analemba zimene Mulungu anakamba. Iye anati: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula.”—Yesaya 48:17, Buku Lopatulika.
BUKU LA MAULOSI
Mlembi wina wa Baibo, Yesaya, ananenelatu za kugwa kwa Babulo
13. Kodi n’zocitika ziti zokhudza Babulo zimene Yehova anauza mneneli Yesaya kulembelatu?
13 M’Baibo muli maulosi ambili, ndipo ambili a io anakwanilitsika kale. Tiyeni tione citsanzo cimodzi. Yehova anakambilatu kuti mzinda wa Babulo udzaonongedwa. Anakambilatu zimenezi kupyolela mwa mneneli Yesaya, amene anakhalako m’zaka za m’ma 700 B.C.E. (Yesaya 13:19; 14:22, 23) Mulungu analongosola mwatsatane-tsatane mmene zimenezi zinali kudzacitikila. Anakamba kuti asilikali oukilawo adzaumitsa madzi a mu mtsinje wa Babulo ndi kuloŵa mu mzindamo popanda wina kulimbana nao. Si zimenezi cabe. Ulosi wa Yesaya unacita kuchula ngakhale dzina leni-leni la mfumu imene inali kudzaononga Babulo, kuti idzakhala Koresi.—Yesaya 44:27–45:2.
14, 15. Kodi zocitika zochulidwa mu ulosi wa Yesaya wonena za Babulo zinakwanilitsika bwanji?
14 Patapita zaka 200—usiku wa pa October 5 kucha kwa pa October 6, mu 539 B.C.E.—asilikali anazinga mzinda wa Babulo. Kodi ndani anali mtsogoleli wao wa nkhondo? Anali Koresi, mfumu ya ku Perisiya. Tsopano inali nthawi yakuti ulosi wocititsa cidwi ukwanilitsike. Koma kodi zinacitika zoona, kuti asilikali a Koresi analoŵa mu mzinda wa Babulo popanda wina kulimbana nao, ngati mmene ulosi unakambila?
15 Usiku umenewo Ababulo anali kucita madyelelo, ndipo anadzimva kukhala ochinjilizika cifukwa mpanda wa mzindawo unali wa cipupa colimba kwambili. Panthawi imeneyi, Koresi mocenjela anakumba mifolo kuti apatutse madzi a mu mtsinje umene unali kupita pakati pa mzinda. Pamenepo madzi anacepa kwambili cakuti asilikali ake anakwanitsa kuoloka mtsinjewo mpaka kukafika ku mpanda wa mzindawo. Koma kodi asilikali a Koresi akanakwanitsa bwanji kuloŵa mu mzinda wa Babulo? Pa cifukwa cosadziŵika bwino, usiku umenewo mageti a mzinda anangotsala otseguka.
16. (a) Kodi Yesaya analosela kuti cimene cidzacitika kwa Babulo n’ciani? (b) Kodi ulosi wa Yesaya wonena za kuonongedwa kwa Babulo unakwanilitsika bwanji?
16 Ulosi unakambilatu za Babulo kuti: “Simudzakhalanso anthu, ndipo iye sadzakhalaponso ku mibadwo-mibadwo. Kumeneko Mluya (Mualabu) sadzakhomako hema wake, ndipo abusa sadzagonekako ziweto zao.” (Yesaya 13:20) Ulosi umenewu sunakambe za kugwa kwa mzinda cabe. Unaonetsanso kuti mzinda wa Babulo udzakhala matongwe kunthawi zonse. Mukhoza kukauona umboni wotsimikizila kukwanilitsika kwa mau amenewa, cifukwa malo amene panali Babulo wakale akalipo mpaka lelo, ndipo sikukhala anthu. Malo amenewa ali ku Iraq, pamtunda wa makilomita 80 kum’mwela kwa Baghdad. Malo amenewo ali umboni wakuti zimene Yehova anakamba kupitila mwa Yesaya, zinakwanilitsika zoona. Iye anati: “Ndidzamusesa ndi tsache la ciwonongeko,” kapena kuti, Ndidzamupyanga ndi cipyango ca cionongeko.—Yesaya 14:22, 23.c
Matongwe a Babulo
17. Kodi kukwanilitsika kwa maulosi a m’Baibo kumalimbitsa bwanji cikhulupililo cathu?
17 Kudziŵa kuti Baibo ndi buku la maulosi odalilika kumalimbitsa cikhulupilililo cathu, si conco kodi? Zoona, ngati Yehova Mulungu anakwanilitsa malonjezo ake m’nthawi zakumbuyo, palibe cifukwa cokaikilila kuti adzakwanilitsanso lonjezo lake lobweletsa paladaiso padziko lapansi. (Numeri 23:19) Inde, tili ndi “ciyembekezo ca moyo wosatha, comwe Mulungu amene sanganame, analonjeza kalekale.”—Tito 1:2.d
“MAU A MULUNGU NDI AMOYO”
18. Kodi mtumwi Paulo anakamba ciani ponena za “mau a Mulungu”?
18 Zimene taphunzila m’nkhani ino, zaonetsa kuti zoona Baibo ndi buku lapadela kwambili. Kuonjezela pa kugwilizana kwa nkhani zake, ndi kunena kwake zoona pa nkhani za sayansi ndi mbili yakale, ndiponso kukhala buku la nzelu zothandiza, komanso la maulosi odalilika, Baibo imapindulitsanso m’njila zina. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti mau a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konse-konse. Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu, komanso mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Mau a Mulungu amathanso kuzindikila zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.”—Aheberi 4:12.
19, 20. (a) Kodi Baibo ingakuthandizeni bwanji kudzifufuza panokha? (b) Nanga mungaonetse bwanji kuti mumayamikila mphatso yapadela imeneyi, Baibo?
19 Kuŵelenga “mau” a Mulungu a m’Baibo kungasinthe umoyo wathu. Kungatithandize kuti tidzifufuze bwino kwambili kuposa kale lonse. Ife tingakambe kuti timam’konda Mulungu, koma mmene timacitila ndi zimene Mau a Mulungu amatiphunzitsa, n’zimene zimaonetsa mmene maganizo athu ndi mtima wathu ulili kweni-kweni.
20 Kunena zoona, Baibo ndi buku locokela kwa Mulungu. Ndi buku limene tiyenela kuliŵelenga, kuliphunzila, ndi kulikonda kwambili. Ngati mupitiliza kuiphunzila Baibo, mudzaonetsa kuti mumaiyamikila kwambili mphatso imeneyi yocokela kwa Mulungu. Mukacita zimenezi, mudzamvetsetsa kwambili cifunilo ca Mulungu kwa mtundu wa anthu. M’nkhani yotsatila tidzakambitsilana za cifunilo ca Mulungu cimeneco, ndi kuti adzacikwanilitsa bwanji.
a Ngakhale kuti anthu ena amakamba kuti mbali zina za Baibo zimatsutsana, zimenezo zilibe umboni. Onani mutu 7 wa buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mau a Mulungu kapena a Munthu? lolembedwa ndi Mboni za Yehova.
b Mwacitsanzo, onani mmene mbadwo wa makolo a Yesu aufotokozela mwatsatane-tsatane pa Luka 3:23-38.
c Kuti mudziŵe zambili pa maulosi a m’Baibo, onani kabuku kakuti Buku la Anthu Onse mapeji 27 mpaka 29, kolembedwa ndi Mboni za Yehova.
d Kuonongedwa kwa Babulo n’citsanzo cimodzi cabe ca maulosi a m’Baibo amene anakwanilitsika kale. Zitsanzo zina ndi za kuonongedwa kwa mzinda wa Turo ndi wa Nineve. (Ezekieli 26:1-5; Zefaniya 2:13-15) Ndiponso, ulosi wa Danieli unakambilatu za maulamulilo amphamvu a padziko amene anali kudzakhalapo motsatizana pambuyo pa ulamulilo wa Babulo. Maulamulilo amenewa anaphatikizapo maulamulilo a Amedi ndi Aperisiya, ndi wa Gilisi. (Danieli 8:5-7, 20-22) Onani Zakumapeto, pamapeji 199 mpaka 201, kuti mudziŵe maulosi ambili onena za Mesiya amene anakwanilitsika mwa Yesu Kristu.