LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 209-nkhani 211
  • Kodi Anthu Alidi ndi Mzimu Umene Sumafa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Anthu Alidi ndi Mzimu Umene Sumafa?
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 209-nkhani 211

ZAKUMAPETO

Kodi Anthu Alidi ndi Mzimu Umene Sumafa?

MUKAMVA liu lakuti “mzimu,” kodi mumaganizila ciani? Anthu ambili amakhulupilila kuti mzimu ndi cinthu cosaoneka cimene cimakhala mkati mwa munthu, ndipo sicimafa. Iwo amaganiza kuti munthu akafa, mbali yosaoneka ya munthu imeneyi imatuluka m’thupi mwake, ndi kupitiliza kukhala ndi moyo kwinakwake. Popeza kuti anthu ambili amakhulupilila zimenezi, amadabwa akadziŵa kuti Baibo siiphunzitsa zimenezi ngakhale pang’ono. Ndiye malinga ndi Mau a Mulungu, kodi mzimu n’ciani?

Polemba za “mzimu,” olemba Baibo anagwilitsila nchito liu la Ciheberi lakuti ruʹach, kapena liu la Cigiriki lakuti pneuʹma. Malemba amaonetsa bwino matanthauzo a mau amenewo. Mwacitsanzo, lemba la Yakobo 2:26 limanena kuti ‘thupi lopanda mzimu [pneuʹma] ndi lakufa.’ Conco pa lemba limeneli, liu lakuti “mzimu” limatanthauza cimene cimacititsa thupi kukhala lamoyo. Popanda mzimu, thupi n’lakufa. Conco, m’Baibo, liu lakuti ruʹach silinangotembenuzidwa monga “mzimu,” kapena monga “mpweya wa moyo,” kapenanso kuti mphamvu ya moyo. Mwacitsanzo, ponena za Cigumula m’masiku a Nowa, Mulungu anati: “Ine n’dzabweletsa cigumula camadzi padziko lapansi, kuti ciononge camoyo ciliconse ca pansi pa thambo, cimene cili ndi mphamvu ya moyo [ruʹach] m’thupi mwake.” (Gen. 6:17; 7:15, 22) Zimenezi zionetsa kuti “mzimu” ndi mphamvu yosaoneka (mphamvu ya moyo), imene imacititsa zolengedwa zonse zamoyo kuti zikhale ndi moyo.

A portable radio without any electrical or battery power source

Monga mmene wailesi imafunikila magetsi kuti igwile nchito, thupi nalonso limafunikila mzimu kuti likhale ndi moyo. Mwacitsanzo, ganizilani za wailesi ya mabatili. Mukaika mabatili mu wailesi ndi kutsegula, mphamvu yocokela m’mabatili imapangitsa wailesiyo kukhala yamoyo, titelo kukamba kwake, kapena kuti imayamba kugwila nchito. Koma popanda mabatili, wailesiyo imakhala yakufa, kapena kuti siimatha kugwila nchito. Izi n’zimene zimacitikanso ndi wailesi yolila ndi magetsi, mukacotsa nthambo yake ku gwelo la magetsi [pulagi]. Mofananamo, mzimu ndi mphamvu imene imapangitsa matupi athu kukhala amoyo. Mofanana ndi magetsi, mzimu naonso sumamva kalikonse ndipo sumaganiza. Ndi mphamvu cabe, osati munthu. Koma popanda mzimu umenewo, kapena kuti mphamvu ya moyo, matupi athu ‘amafa, ndipo amabwelela kufumbi,’ monga mmene wamasalimo anakambila.—Masalimo 104:29.

Ponena za imfa ya munthu, lemba la Mlaliki 12:7 limati: “Fumbi [thupi la munthu] lidzabwelela kunthaka kumene linali, ndipo mzimu udzabwelela kwa Mulungu woona amene anaupeleka.” Mzimu, kapena kuti mphamvu ya moyo, ukatuluka m’thupi, thupilo limafa ndi kubwelela kunthaka kumene linacokela. Koma mphamvu ya moyo imabwelela kwa amene anaipeleka, amene ndi Mulungu. (Yobu 34:14, 15; Masalimo 36:9) Zimenezi sizitanthauza kuti mphamvu ya moyo imakwela kumwamba m’lingalilo leni-leni iyai. Koma zimatanthauza kuti munthu akamwalila, Yehova Mulungu yekha ndiye adziŵa za tsogolo lake. Zili ngati kuti moyo wa munthuyo tsopano uli m’manja mwa Mulungu. Mulungu yekha mwa mphamvu yake, ndiye angapelekenso mzimu kwa munthuyo kuti akhalenso ndi moyo.

N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti izi n’zimene Mulungu adzacitila onse amene akugona “m’manda acikumbutso.” (Yohane 5:28, 29) Panthawi youkitsa akufa, Yehova adzapangila munthu amene akugona mu imfa thupi latsopano, ndi kulipatsa moyo mwa kuikamo mzimu, kapena kuti mphamvu ya moyo. Imeneyo idzakhala nthawi yosangalatsa kwambili!

Ngati mufuna kudziŵa zambili ponena za mmene Baibo imagwilitsila nchito liu lakuti “mzimu,” onani kabuku kakuti Njila ya Kumoyo Wamuyaya—Kodi Mwaipeza? Pamapeji 12 mpaka 14, ndi buku la Kukambitsirana za m’Malemba pamapeji 319 mpaka 323. Mabuku aŵiliwa ndi olembedwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani