LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lv nkhani 212-nkhani 215
  • Kucitila Saliyuti Mbendela, Kuvota ndi Kugwila Nchito Imene Si Yausilikali

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kucitila Saliyuti Mbendela, Kuvota ndi Kugwila Nchito Imene Si Yausilikali
  • “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Nkhani Zofanana
  • N’cifukwa Ciyani a Mboni za Yehova Satengako Mbali pa Zikondwelelo Zonyadila Dziko Lawo?
    Mafunso Ofunsidwa Kaŵili-kaŵili pa Mboni za Yehova
“Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
lv nkhani 212-nkhani 215

ZAKUMAPETO

Kucitila Saliyuti Mbendela, Kuvota ndi Kugwila Nchito Imene Si Yausilikali

Kucitila saliyuti mbendela. Mboni za Yehova zimakhulupilila kuti kuwelamila kapena kucitila saliyuti mbendela, kumene nthawi zambili kumacitika poimba nyimbo ya fuko, ndi kupembedza. Kupembedza kumeneku kumaonetsa kuti amene angapulumutse anthu ndi boma kapena atsogoleli ake osati Mulungu. (Yesaya 43:11; 1 Akorinto 10:14; 1 Yohane 5:21) Mmodzi mwa atsogoleli amene anali kufuna kulambilidwa anali Mfumu Nebukadinezara wa ku Babulo. Kuti aonetse anthu ulemelelo wake ndi cangu cake pa kulambila, mtsogoleli wamphamvu ameneyu anapanga fano lalikulu. Ndipo analamula anthu onse kuti aligwadile pamene nyimbo yokhala ngati ya fuko inali kulila. Koma Aheberi atatu, Sadirake, Mesake ndi Abedinego, anakana kugwadila fano limenelo, ngakhale kuti kucita zimenezo kukanapangitsa kuti aphedwe.—Danieli, caputa 3.

Katswili wa mbili yakale, dzina lake Carlton Hayes, analemba kuti masiku ano, “anthu okweza dziko lao amakhulupilila ndi kulambila mbendela yao. Amuna amavula zisoti akafika pali mbendela, ndipo olakatula ndakatulo amatamanda mbendela, naonso ana amaimba nyimbo zotamanda mbendela.” Katswiliyo anakambanso kuti poonetsa kukonda dziko lao maboma anakhazikitsa “masiku a holide,” monga tsiku lokondwelela ufulu wodzilamulila. Iwo anakhazikitsa masiku okumbukila ndi kulemekeza anthu amene anamenyela ufulu wa dziko lao ndipo amawaona ngati “oyela mtima”. Ndiponso ali ndi malo kumene amapita pofuna kulemekeza mbendela. Pa cikondwelelo ca dziko ku Brazil, nduna ya gulu la asilikali inati: “Timalemekeza mbendela ndi kuilambila . . . monga mmene timalambilila dziko.” Buku la Encyclopedia Americana linati: “Mbendela ndi yopatulika monga mmene mtanda ulili wopatulika.”

Buku limene tachula pamwambapa limanena kuti nyimbo za fuko “zimaonetsa mmene munthu amakondela dziko lake, ndipo nthawi zambili zimakhala pemphelo lakuti Mulungu atsogolele ndi kuteteza anthu ndi atsogoleli ao.” Ndiye cifukwa cake atumiki a Yehova amaona kuti kucita zikondwelelo za dziko zimene zimaphatikizapo kucitila saliyuti mbendela ndi kuimba nyimbo ya fuko ndi kupembedza. Ndiponso, pothilila ndemanga pa cifukwa cimene ana a Mboni za Yehova sawelamila mbendela kapena kulumbila m’masukulu a ku United States, buku lina linati: “Pambuyo poweluza nkhani zosiyanasiyana, Khoti Lalikulu linavomeleza mfundo yakuti kucita miyambo imeneyi ndi kupembedza.”—The American Character.

Ngakhale kuti anthu a Yehova sacitako miyambo imene amaona kuti ndi yosemphana ndi Malemba, io saletsa anthu kucita miyamboyo. Iwo amalemekeza mbendela monga cizindikilo ca dziko, ndipo amadziŵa kuti maboma amenewa ndi “olamulila akuluakulu,” komanso ndi “mtumiki wa Mulungu.” (Aroma 13:1-4) Conco, Mboni za Yehova zimamvela lamulo lakuti azipemphelela ‘mafumu ndi anthu onse apamwamba.’ Koma colinga cathu n’cakuti “tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendele, ndiponso kuti tikhale odzipeleka kwa Mulungu mokwanila ndi oganiza bwino.”—1 Timoteyo 2:2.

Kuvota pa masankho a ndale. Akristu oona saletsa ena kuvota. Iwo sacita zionetselo zosavomeleza mmene masankho ayendela, ndipo amagonjela ulamulilo umene wasankhidwa. Komabe, io sakhala kumbali iliyonse pa nkhani yokhudza ndale za dziko. (Mateyu 22:21; 1 Petulo 3:16) Nanga Mkristu angacite ciani ngati lamulo m’dziko lake ndi lakuti aliyense ayenela kuvota, kapena ngati anthu aukila anthu amene sapita kukavota? Kumbukilani kuti Sadirake, Mesake ndi Abedinego anapita ku cigwa ca Dura. Mkristu amene ali mumkhalidwe wofananawo, angapite ku malo ovotela ngati cikumbumtima cake cimulola. Komabe, sayenela kutenga mbali m’ndale. Iye ayenela kuganizila mfundo 6 izi:

  1. Otsatila a Yesu “sali mbali ya dzikoli.”—Yohane 15:19.

  2. Akristu amaimila Kristu ndi Ufumu wake.—Yohane 18:36; 2 Akorinto 5:20.

  3. Mpingo wacikristu umakhulupilila zofanana, ndipo anthu ake amagwilizana cifukwa amakondana ngati mmene Kristu anawakondela.—1 Akorinto 1:10; Akolose 3:14.

  4. Anthu amene amasankha munthu wina kukhala mtsogoleli wao, amakhudzidwa ndi mlandu ulionse umene mtsogoleli ameneyo angacite.—Onani mfundo zimene zili pa 1 Samueli 8:5, 10-18 ndi 1 Timoteyo 5:22.

  5. Pamene Aisiraeli anafuna munthu wina kukhala mtsogoleli wao, Yehova anaona kuti io akana kuti iye aziwalamulila.—1 Samueli 8:7.

  6. Akristu afunika kukhala ndi ufulu wa kulankhula pokamba ndi anthu a cipani ciliconse za boma la Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 24:14; 28:19, 20; Aheberi 10:35.

Nchito imene si yausilikali. M’maiko ena, Boma limafuna kuti onse amene akana kugwila nchito yausilikali agwile nchito yosakhala yausilikali kwa kanthawi. Tisanapange cosankha pa nkhani imeneyi, tiyenela kupemphela, kapena kukambilana ndi Mkristu mnzathu wofikapo kuuzimu. Ndiyeno, tingagwilitsile nchito cikumbumtima cathu kupanga cosankha mogwilizana ndi zimene tafufuza pa nkhaniyo.—Miyambo 2:1-5; Afilipi 4:5.

Mau a Mulungu amatiuza kuti “tizimvela maboma ndiponso olamulila. Komanso tikhale okonzekela nchito iliyonse yabwino, . . . tikhale ofatsa kwa anthu onse.” (Tito 3:1, 2) Tili ndi zimenezo m’maganizo, tingadzifunse mafunso awa: ‘Kodi kugwila nchito imeneyi kudzandipangitsa kutenga mbali m’ndale kapena kucita zinthu zogwilizana ndi cipembedzo conama?’ (Mika 4:3, 5; 2 Akorinto 6:16,17) ‘Kodi kugwila nchitoyi kungapangitse kuti ndizivutika kukwanilitsa maudindo anga acikristu, kapena kulephelelatu kukwanilitsa maudindo amenewo?’ (Mateyu 28:19, 20; Aefeso 6:4; Aheberi 10:24, 25) ‘Komanso, kodi kugwila nchitoyi kudzandipatsa mpata wocita zambili kuuzimu, monga kucita upainiya wa nthawi zonse?’—Aheberi 6:11, 12.

Ngati cikumbumtima ca Mkristu cimulola kugwila nchito imene si yausilikali m’malo mopita kundende, Akristu ena ayenela kulemekeza cosankha cake. (Aroma 14:10) Koma ngati Mkristuyo waona kuti sangagwile nchitoyo, ena ayenelanso kulemekeza cosankha cakeco.—1 Akorinto 10:29; 2 Akorinto 1:24.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani