LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lv nkhani 219-nkhani 221
  • Zimene Baibulo Limanena Pankhani ya Kusudzulana ndi Kupatukana

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Baibulo Limanena Pankhani ya Kusudzulana ndi Kupatukana
  • “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Nkhani Zofanana
  • Muzilemekeza “Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kupangitsa Cikwati Cacikhiristu Kukhala Cacimwemwe
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
“Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
lv nkhani 219-nkhani 221

ZAKUMAPETO

Zimene Baibulo Limanena Pankhani ya Kusudzulana ndi Kupatukana

Yehova amafuna kuti anthu okwatila azisunga lonjezo lao la cikwati. Pomanga cikwati ca mwamuna ndi mkazi woyamba, Yehova anati: ‘Mwamuna . . . adzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo io adzakhala thupi limodzi.’ Panthawi ina, Yesu Kristu anabweleza mau amenewo ndi kuonjezela kuti: “Conco cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.” (Genesis 2:24; Mateyu 19:3-6) Motelo, Yehova ndi Yesu amaona kuti cikwati ndi mgwillizano wa moyo wonse umene umatha kokha ngati mmodzi wamwalila. (1 Akorinto 7:39) Popeza kuti cikwati n’copatulika, tisaone ngati kusudzulana ndi nkhani yaing’ono. Ndipo Yehova amadana ndi kusudzulana popanda maziko a m’Malemba.—Malaki 2:15, 16.

Kodi maziko a m’Malemba ovomeleza anthu kusudzulana ndi ati? Yehova amadana ndi cigololo ndi dama. (Genesis 39:9; 2 Samueli 11:26, 27; Salimo 51:4) Ndipo amanyansidwa kwambili ndi dama cakuti amaona kuti ndi cifukwa cololela anthu kusudzulana. (Kuti mudziŵe zimene dama limaphatikizapo, onani Nkhani 9, ndime 7, imene ikufotokoza nkhani yokhudza dama.) Yehova amapeleka mwai kwa munthu wa pabanja amene ndi wokhulupilika kuti asankhe yekha kukhalabe ndi mnzake wosakhulupilika kapena kuthetsa cikwati. (Mateyu 19:9) Cotelo, ngati munthu wokhulupilika amene mnzake wa m’cikwati anacita dama wasankha kuthetsa cikwati, Yehova sakhumudwa. Ngakhale ndi conco, mpingo wacikristu sulimbikitsa munthu aliyense kuthetsa cikwati. Ndipo cifukwa ca mmene zinthu zilili, mwamuna kapena mkazi angasankhe kukhalabe ndi mnzake wosakhulupilika, makamaka ngati mnzakeyo ndi wolapadi. Komabe, munthu amene ali ndi cifukwa ca m’Malemba cothetsela cikwati afunika kusankha yekha zocita ndi kukhala okonzeka kupilila mavuto alionse amene angakumane nao cifukwa ca cosankha cakeco.—Agalatiya 6:5.

Cifukwa ca mavuto aakulu, Akristu ena asankha kupatukana kapena kuthetsa cikwati kukhoti ngakhale kuti mnzao sanacite dama. Zinthu zikakhala conco, Baibulo limapeleka malangizo akuti amene wacokayo “akhale conco wosakwatiwa. Apo ai, abwelelane ndi mwamuna wakeyo.” (1 Akorinto 7:11) Mkristu amene wacita zimenezi alibe ufulu wofunafuna munthu wina kuti akwatilane naye. (Mateyu 5:32) Tiyeni tione mavuto ena akuluakulu amene amacititsa ena kupatukana.

Kukana kusamalila banja. Nthawi zina banja lingavutike kwambili ndi umphawi ndiponso kusoŵa zinthu zofunika kwambili pa umoyo ngati mwamuna amanyalanyaza kusamalila banjalo. Baibulo limati: “Ngati munthu sasamalila, . . . a m’banja lake, wakana cikhulupililo ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupilila.” (1 Timoteyo 5:8) Ngati mwamuna wotelo safuna kusintha khalidwe lake, mkazi wake angasankhe kupatukana naye mwalamulo kuti adziteteze ndi kuteteza ana ake. Komabe, akulu ayenela kufufuza mosamala kwambili nkhani yakuti m’bale amakana kusamalila banja lake. Kukana kusamalila banja kungapangitse kuti munthu acotsedwe mumpingo.

Kucita nkhanza. Munthu angacitile nkhanza kwambili mnzake wa m’banja cakuti thanzi ngakhale moyo wa mnzakeyo zingakhale pangozi. Ngati munthu wankhanzayo ndi Mkristu, akulu mumpingo ayenela kuifufuza bwinobwino nkhaniyo. Ndeo ndiponso khalidwe laciwawa, zingakhale maziko ocotsela munthu mumpingo.—Agalatiya 5:19-21.

Kumuletselatu kucita zinthu za kuuzimu. Mwamuna kapena mkazi angayesetse kuletsa mnzake kucita zinthu za kuuzimu, ngakhale kum’kakamiza kuti aphwanye malamulo ena a Mulungu. Zikakhala conco, munthu amene akuvutikayo angasankhe kupatukana mwalamulo ndi mnzakeyo, ngati kucita zimenezo kudzasonyeza kuti ‘akumvela Mulungu monga wolamulila osati anthu.’—Machitidwe 5:29.

Pakakhala mavuto aakulu monga amene takambilana, palibe aliyense amene ayenela kukakamiza munthu wosalakwayo kucoka kapena kupitiliza kukhala m’cikwati. Ngakhale kuti Akristu okhwima kuuzimu ndiponso akulu angathandize kupeleka malangizo a m’Baibulo, io sangadziŵe zonse zimene zimacitika pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. Yehova yekha ndi amene amadziŵa zonse. Koma mkazi kapena mwamuna wacikristu angaonetse kusalemekeza Mulungu ndi makonzedwe a cikwati ngati amaonjezela nkhani zabodza ndi colinga cakuti apatukane ndi mnzake. Yehova amadziŵa colinga ciliconse colakwika cimene munthu angakhale naco kuti apatukane ndi mnzake, ngakhale munthuyo atabisa motani. Inde, “zinthu zonse zili poonekela ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenela kudzayankha pa zocita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.” (Aheberi 4:13) Koma ngati vuto lalikulu lipitiliza, palibe aliyense amene ayenela kudzudzula Mkristu amene waona kuti palibe mwina mocitila koma kupatukana ndi mnzake. Mulimonse mmene zingakhalile, “tonse tidzaimilila patsogolo pa mpando woweluzila milandu wa Mulungu.”—Aroma 14:10-12.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani