PHUNZILO 5
Baibo ni Uthenga wa Mulungu kwa Ife
Yehova anatipatsa Baibo monga mphatso yapadela kwambili. Inapangidwa mwa kusanja pamodzi mabuku ang’ono-ang’ono okwana 66. Koma mungafunse kuti: ‘Kodi Baibo inapelekedwa motani kwa anthu? Nanga ni mawu a ndani kwenikweni?’ Kuti tiyankhe mafunso aya, tiyeni tikambilane mmene uthenga wa Mulungu wa m’Baibo unafikila kwa ife.
1. Ngati anthu ni amene analemba Baibo, n’cifukwa ciyani timanena kuti ni Mawu a Mulungu?
Anthu okwana ngati 40 ndiwo analemba Baibo. Inatenga zaka pafupifupi 1,600, kucokela mu 1513 B.C.E. mpaka m’ma 98 C.E. Ndipo olemba ake anali a zikhalidwe zosiyana-siyana, monga abusa, asodzi, komanso mafumu. Ngakhale n’telo, mbali zonse za Baibo zimavomelezana. Koma kodi n’zotheka bwanji? Cifukwa Baibo ni mawu a Mulungu. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:13.) Olemba Baibo sanalembemo maganizo awo. M’malo mwake, iwo “analankhula mawu ocokela kwa Mulungu motsogoleledwa ndi mzimu woyela.”a (2 Petulo 1:21) Mulungu anaseŵenzetsa mzimu wake woyela kutsogolela anthu amenewo kulemba maganizo ake.—2 Timoteyo 3:16.
2. Kodi ndani angapindule nayo Baibo?
Anthu a ‘dziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse’ angapindule na uthenga wabwino wa m’Baibo. (Ŵelengani Chivumbulutso 14:6.) Mulungu anaonetsetsa kuti Baibo ipezeke mu zinenelo zambili kuposa buku lina lililonse m’mbili ya anthu. Ndipo anthu ambili masiku ano, kulikonse kumene angakhale, kaya amakamba citundu canji, akhoza kumva uthenga wa m’Baibo.
3. Kodi Yehova waiteteza bwanji Baibo?
Baibo inalembedwa pa zinthu zimene zimawonongeka m’kupita kwa nthawi, monga cikumba komanso gumbwa. Koma anthu okonda Baibo anali kuikopolola mobweleza-bweleza pamanja. Ngakhale kuti anthu amphamvu anayesetsa kuti aiwononge Baibo, panali anthu ena amene anaika miyoyo yawo paciswe kuti aiteteze. Yehova sanalole munthu aliyense, kapena cinthu ciliconse, kutsekeleza uthenga wake kuti usatifike. Baibo imati: “Mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.”—Yesaya 40:8.
KUMBANI MOZAMILAPO
Dziŵani zambili za mmene Mulungu anauzila anthu kulemba Baibo, mmene anaitetezela, komanso zimene wacita kuti anthu ambili akhale nayo.
4. Baibo imatiululila Mwiniwake
Tambani VIDIYO. Pambuyo pake ŵelengani 2 Timoteyo 3:16, na kukambilana mafunso aya.
Ngati anthu ni amene analemba Baibo, n’cifukwa ciyani imachedwa Mawu a Mulungu?
Kodi mukhulupilila kuti zinacitikadi kuti Mulungu anaika maganizo ake mwa anthu olemba Baibo?
Kalembela amalemba kalata, koma uthenga wa kalatayo umacokela kwa womuuza zolemba. Mofananamo, anthu analemba Baibo, koma uthenga wake unacokela kwa Mulungu
5. Baibo inapulumuka kwa anthu ofuna kuiwononga
Cifukwa Baibo inacokela kwa Mulungu, mpake kuti waiteteza mpaka lelo. M’mbili yonse ya anthu, anthu amphamvu akhala akuyesa-yesa kuti aiwononge Baibo. Nawonso atsogoleli acipembedzo ayesa kuibisa kwa anthu. Koma anthu ambili anaikabe miyoyo yawo paciswe kuti ateteze Baibo, ngakhale kuti panali owatsutsa komanso oopseza kuwapha. Kuti mumveko za mmodzi wa anthu amenewo tambani VIDIYO, na kukambilana mafunso aya.
Poona mmene anthu anaikila miyoyo yawo paciswe kuti aiteteze Baibo, kodi sindinu wofunitsitsa tsopano kumaiŵelenga?
Ŵelengani Salimo 119:97, na kukambilana funso ili:
N’ciyani cinapangitsa anthu ambili kulolela kuika miyoyo yawo paciopsezo kuti amasulile Baibo na kuigaŵila kwa anthu?
6. Buku la anthu onse
M’mbili yonse ya anthu, Baibo ndilo buku limene lamasulidwa na kugaŵilidwa kwambili kuposa mabuku onse. Ŵelengani Machitidwe 10:34, 35, na kukambilana mafunso aya:
N’cifukwa ciyani Mulungu amafuna kuti Mawu ake amasulidwe na kufalitsidwa kwambili?
N’ciyani cimakucititsani cidwi na Baibo?
Pafupifupi
Anthu Onse
padziko
angathe kuŵelenga Baibo m’citundu cimene amamva
Imapezeka m’zinenelo zoposa
3,000
Baibo yathunthu kapena mbali yake cabe
5,000,000,000
Ciŵelengelo coyelekezela ca ma Baibo ofalitsidwa,
coposa buku lina lililonse
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Baibo ni buku lakale-kale lolembedwa na ŵanthu cabe.”
Nanga inu muganiza bwanji?
Kodi pali umboni wanji woonetsa kuti Baibo ni Mawu a Mulungu?
CIDULE CAKE
Baibo ni Mawu a Mulungu, ndipo iye wacita zotheka kuti anthu onse athe kukhala nayo.
Mafunso Obweleza
Kodi timatanthauza ciyani tikati Mulungu anauzila anthu kulemba Baibo?
Pa zimene mwadziŵa m’phunzilo lino, kodi n’ciyani cakucitsani cidwi ponena za Baibo?
Popeza lomba mwadziŵa zazikulu zimene Mulungu wacita kuti uthenga wake ukufikeni, kodi mukumva bwanji?
FUFUZANI
Ŵelengani mbili ya Baibo—kuyambila ku mipukutu yamakedzana mpaka ku ma Baibo amakono.
Dziŵani mmene Baibo yapulumukila ziopsezo zikulu-zikulu zitatu zofuna kuiwononga.
Onani mmene anthu ena anaikila miyoyo yawo paciopsezo kuti amasulile Baibo.
Baibo anaikopolola na kuimasulila nthawi zambili-mbili. Kodi mungatsimikize bwanji kuti uthenga wake sunasinthidwe?
“Kodi Baibo Anaisintha Kapena Anangoisinthako Zina?” (Nkhani ya pawebusaiti)
a Phunzilo 07 idzafotokoza bwino kuti mzimu woyela ni mphamvu ya Mulungu yogwila nchito.