LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 46
  • N’cifukwa Ciyani Muyenela Kudzipatulila na Kubatizika?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciyani Muyenela Kudzipatulila na Kubatizika?
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Kodi Ndinu Wokonzeka Kudzipatulila kwa Yehova?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Kodi N’dzipeleke Kwa Mulungu Kuti N’kabatizike?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Ndimwe Wokonzeka Kubatizika?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Kodi Ndinu Wokonzeka Kubatizika?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 46
Phunzilo 46. Mwamunayu akupemphela payekha.

PHUNZILO 46

N’cifukwa Ciyani Muyenela Kudzipatulila na Kubatizika?

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Kodi kudzipatulila ni kucita ciyani? Ni kupeleka pemphelo lapadela kwa Yehova na kumulonjeza kuti mudzalambila iye yekha, na kuika cifunilo cake patsogolo mu umoyo wanu. (Salimo 40:8) Pambuyo pake mumabatizika. Mwa kubatizika, mumaonetsa kwa ena kuti munadzipatulila kale. Cisankho copatulila moyo wathu kwa Yehova ndiye cofunika kopambana pa umoyo wathu. Kodi n’ciyani cingakulimbikitseni kupanga cisankho cofunika kwambili cimeneci?

1. Kodi n’ciyani cimalimbikitsa munthu kupanga cisankho ca kudzipatulila?

Cikondi ndiye cimakolezela kuti tidzipatulile kwa Yehova. (1 Yohane 4:10, 19) Baibo imatilimbikitsa kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Timaonetsa kuti Mulungu timam’konda mwa zokamba zathu komanso zocita zathu. Monga mmene anthu aŵili okondana zenizeni amafika pomanga banja, cikondi cathu pa Yehova cimakolezela kuti tifike podzipatulila, pambuyo pake n’kudzabatizika.

2. Kodi Yehova amapeleka madalitso otani kwa Mboni zake zobatizika?

Mukadzabatizika mudzakhala mutalowa m’banja la Yehova lacimwemwe. Mudzaona m’njila zambili kuti iye amakukondani ndipo mudzamuyandikila kwambili kuposa pali pano. (Ŵelengani Malaki 3:16-18.) Kuwonjezela pa Yehova kukhala Tate wanu, mudzakhalanso na banja lauzimu la abale na alongo kuzungulila dziko lapansi, okonda Mulungu komanso okonda inu. (Ŵelengani Maliko 10:29, 30.) Koma musanabatizike, pali zinthu zina zimene muyenela kucita. Muyenela kuphunzila za Yehova, kufika pomukonda, na kuika cikhulupililo mwa Mwana wake. Kenako, muyenela kupeleka pemphelo lapadela lodzipatulila kwa Yehova. Mukatenga masitepe amenewa na kubatizika, mudzakhala pa njila yopita ku moyo wosatha. Mawu a Mulungu amati: “Cikupulumutsanso inuyo . . . ndico ubatizo.”—1 Petulo 3:21.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani cifukwa cake n’kofunika kuti mukadzipatulile kwa Yehova na kubatizika.

3. Tiyenela kusankha amene tifuna kum’tumikila

Pa nthawi ya Aisiraeli akale, anthu anali kuganiza kuti akhoza kulambila Yehova komanso mulungu wonama Baala. Koma Yehova anatumiza mneneli Eliya kuti akakonze maganizo olakwika amenewa. Ŵelengani 1 Mafumu 18:21, na kukambilana funso ili:

  • Kodi Aisiraeli anayenela kupanga cisankho cotani?

Monga mmene zinalili kwa Aisiraeli, ifenso tiyenela kusankha amene tikufuna kum’tumikila. Ŵelengani Luka 16:13, na kukambilana mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani n’zosatheka kulambila Yehova na munthu wina, kapena cinthu cina?

  • Kodi tingamuonetse bwanji Yehova kuti tinasankha kulambila iye?

4. Ganizilani za mmene Yehova amakukondelani

Zithunzi: Munthu uyu akuganizila pa zonse zimene Mulungu wamupatsa. 1. Citsanzo ca cikondi mmene mayi amakondela mwana wake wakhanda. 2. Citsanzo ca zakudya zokoma, zipatso zosiyana-siyana komanso zamasamba. 3. Baibo. 4. Nsembe ya dipo ya Khristu.

Yehova watipatsa mphatso zambili za mtengo wapatali. Nanga ife tingam’patse ciyani? Tambani VIDIYO.

VIDIYO: Kupeleka Mphatso kwa Mulungu (3:04)

Kodi Yehova waonetsa kuti amakukondani m’njila ziti? Ŵelengani Salimo 104:14, 15, komanso 1 Yohane 4:9, 10, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi mumayamikila mphatso ziti maka-maka zocokela kwa Yehova?

  • Kodi mumamva bwanji cifukwa ca mphatso zimenezo?

Tikalandila mphatso imene taikonda kwambili, timafuna timuyamikila munthu amene watipatsa mphatsoyo. Ŵelengani Deuteronomo 16:17, na kukambilana funso ili:

  • Mukaganizila zonse zimene Yehova wakucitilani, kodi ziyenela kukulimbikitsani kum’patsa ciyani?

5. Kudzipatulila kumabweletsa madalitso ambili

Anthu ambili amakhulupilila kuti kuchuka, nchito yabwino, kapena ndalama zambili ndizo zingawapatse cimwemwe. Kodi zimenezi n’zoona? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

VIDIYO: Bola Ndiye Inali Cakudya Canga (5:45)

Zithunzi: zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Bola Ndiye Inali Cakudya Canga.’ 1. Andrey ayambilanso kuphunzila Baibo. 2. Andrey akulalikila pamodzi na mwana wake.
  • Ngakhale kuti mnyamata wa mu vidiyo iyi, anali kukonda kwambili kuchaya bola, kodi analeka cifukwa ciyani?

  • Iye anapanga cisankho ca kudzipatulila, osati ku bola, koma kwa Yehova. Muganiza anapanga cisankho coyenela? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

Mtumwi Paulo asanakhale Mkhristu, anali na nchito yapamwamba. Iye anaphunzila malamulo aciyuda ndipo mphunzitsi wake anali wochuka kwambili. Koma Paulo anasiya zonsezo kuti akhale Mkhristu. Kodi pambuyo pake anakhala wacisoni, n’kuona kuti anataya mwayi? Ŵelengani Afilipi 3:8, na kukambilana mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani Paulo ananena kuti zimene anali kucita asanakhale Mkhristu zinali monga “mulu wa zinyalala”?

  • Kodi anapindula ciyani m’malo mwake?

  • Kodi n’ciyani cingapangitse umoyo wanu kukhala waphindu kwambili, kutumikila Yehova kapena kucita zinthu zina?

Zithunzi: 1. Saulo mfarisi wodzilungamitsa amene anadzachedwa Paulo. 2. Mtumwi wokhulupilika Paulo akulembela kalata Akhristu anzake.

Paulo atakhala Mkhristu, anapindula zoculuka kuposa zimene anasiya

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Nidziŵa kuti ici ndico coonadi, koma zakuti nikabatizike, zimenezo ine iyayi.”

  • Muganiza n’cifukwa ciyani ni cinthu canzelu kupatulila moyo wanu kwa Yehova?

CIDULE CAKE

Cikondi ndico cimakolezela kuti tidzipatulile kwa Yehova na kubatizika.

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani Yehova amafunikila kuti tizim’konda komanso kumulambila na mtima wathu wonse?

  • Kodi Yehova amazidalitsa bwanji Mboni zake zobatizika?

  • Kodi mungakonde kudzipatulila kwa Yehova?

Colinga

FUFUZANI

Onani cifukwa cake woimba nyimbo, ndiponso wocita maseŵela othamanga, anadzipatulila kwa Yehova.

Acicepele Akufunsa—Moyo Wanga Nidzauseŵenzetsa Bwanji?—Kuganizila Zakumbuyo (6:54)

Onaninso zifukwa zina zimene munthu ayenela kudzipatulila kwa Yehova.

“N’cifukwa Ciyani Muyenela Kudzipatulila Kwa Yehova?” (Nsanja ya Mlonda, January 15, 2010)

Mu vidiyo ya nyimbo iyi, onani cisangalalo ca anthu amene amadzipatulila kwa Yehova.

Nikupatsani Moyo Wanga (4:30)

Mu nkhani yakuti “Kwa Zaka Zambili N’nali Kudzifunsa Kuti, ‘Kodi Mulungu Anatilengelanji Anthufe?’” onani mmene mayi wina anaunikilanso zinthu zofunika kwenikweni paumoyo wake.

“Baibo Imasintha Anthu” (Nsanja ya Mlonda, November 1, 2012)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani