NKHANI YA PACIKUTO | MABODZA AMENE AMALEPHELETSA ANTHU KUKONDA MULUNGU
Bodza Lakuti Mulungu Ndi Wosamvetsetseka
ZIMENE ANTHU AMBILI AMAKHULUPILILA Buku lina limanena kuti “magulu atatu [a cipembedzo cacikristu] amene ndi Roma Katolika, chalichi ca Eastern Orthodox ndi Cipulotesitanti, amakhulupilila kuti kuli Anthu atatu mwa Mulungu mmodzi. Iwo amati kuli Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu Woyela. Malinga ndi ciphunzitso cimeneci, zimenezi sizitanthauza kuti kuli milungu itatu koma kuti Anthu atatu amenewa ali mwa Mulungu mmodzi.”—The New Encyclopædia Britannica.
ZIMENE BAIBO IMANENA Yesu, Mwana wa Mulungu, sanakambepo kuti iye ndi Atate wake ndi ofanana kapena kuti iye ndiye Atate. Koma, iye anati: “Ndikupita kwa Atate wanga, cifukwa Atate ndi wamkulu kuposa ine.” (Yohane 14:28) Iye anauzanso mmodzi wa otsatila ake kuti: “Ine ndikukwela kwa Atate wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.”—Yohane 20:17.
Mzimu woyela si munthu. Akristu oyambilila “anadzazidwa ndi mzimu woyela,” ndipo Yehova anakamba kuti: “Ndidzatsanulila mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyana-siyana.” (Machitidwe 2:1-4, 17) Mzimu woyela si mbali ya Utatu koma ndi mphamvu ya Mulungu yogwila nchito.
N’CIFUKWA CIANI KUDZIŴA ZIMENEZI N’KOFUNIKA? Karl Rahner ndi Herbert Vorgrimler, amene ndi akatswili a maphunzilo acikatolika anafotokoza kuti ciphunzitso ca Utatu “ndi cosatheka kuti munthu acimvetsetse ngati Mulungu sanamuululile tanthauzo lake, ndipo ngakhale atamuululila sangacimvetsetse kothelatu.” Kodi inu mungakonde munthu amene ndi wosamvetsetseka? Ciphunzitso ca Utatu cimalepheletsa anthu kudziŵa Mulungu ndi kumukonda.
Marco, amene tachula m’nkhani yoyamba ija anaona kuti ciphunzitso ca Utatu cinali kumulepheletsa kudziŵa Mulungu. Iye anati: “Ndinali kuganiza kuti Mulungu anali kubisa umunthu wake, ndipo zimenezi zinapangitsa kuti ndiziona kuti iye ndi wosaganizila ena, wosamvetsetseka, ndi wosafikilika.” Koma “Mulungu si Mulungu wacisokonezo.” (1 Akorinto 14:33) Iye sanabise umunthu wake, ndipo amafuna kuti timudziŵe. Yesu anati: “Ife timalambila cimene tikucidziŵa.”—Yohane 4:22.
Marco anakamba kuti: “Pamene ndinaphunzila kuti Mulungu si Utatu ndinakwanitsa kukhala naye pa ubwenzi wolimba.” Ngati timaona Yehova kuti ndi weni-weni m’malo moona kuti ndi wosamvetsetseka, zidzakhala zosavuta kum’konda. Baibo imanena kuti: “Munthu wopanda cikondi sadziŵa Mulungu, cifukwa Mulungu ndiye cikondi.”—1 Yohane 4:8.