LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 1/15 masa. 23-27
  • Lolani Yehova Kulimbitsa ndi Kuteteza Cikwati Canu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Lolani Yehova Kulimbitsa ndi Kuteteza Cikwati Canu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • TETEZANI MTIMA WANU
  • KHALANIBE PAUBWENZI NDI MULUNGU
  • VALANI UMUNTHU WATSOPANO
  • MUZILANKHULANA BWINO
  • MUZIPELEKA MANGAWA A MUCIKWATI
  • PITILIZANI KUTETEZA CIKWATI CANU
  • Kupangitsa Cikwati Cacikhiristu Kukhala Cacimwemwe
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Pambuyo Pa Tsiku La Cikwati
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Khalani ndi Banja Lolimba ndi Lacimwemwe
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • ‘Cikwati Cikhale Colemekezeka’
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 1/15 masa. 23-27
1. Okwatilana akusekelelana; 2. Okwatilana amodzimodziwo akukumana ndi mayeselo kunchito ndipo akupewa mayanjano osayenela ndi anzao a kunchito amene si Mboni

Lolani Yehova Kulimbitsa ndi Kuteteza Cikwati Canu

“Yehova akapanda kulondela mzinda, alonda amakhala maso pacabe.”—SAL. 127:1b.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kuteteza mtima wathu?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu?

  • Ndi kulankhulana kotani kumene kumalimbitsa ukwati?

1, 2. (a) N’cifukwa ciani Aisiraeli 24,000 analephela kulandila madalitso? (b) N’cifukwa ciani cocitika cakale cimeneci ndi nkhani yaikulu kwa ife?

KUTANGOTSALA kanthawi kocepa kuti Aisiraeli aloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, amuna ambili aciisiraeli anacita “ciwelewele ndi akazi a ku Mowabu.” Pa cifukwa cimeneci, Yehova anaononga anthu 24,000. N’zomvetsa cisoni kuti Aisiraeli atangotsala pang’ono kuloŵa m’dzikolo, analephela kulandila coloŵa cao cimene anaciyembekezela kwa nthawi yaitali cifukwa cogonja ku ciyeso.—Num. 25:1-5, 9.

2 Nkhani yoopsa imeneyi inalembedwa kuti “iticenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikila.” (1 Akor. 10:6-11) Panopa tili ku mapeto enieni a “masiku otsiliza” ndipo pokhala atumiki a Mulungu, tatsala pang’ono kuloŵa m’dziko latsopano lolungama. (2 Tim. 3:1; 2 Pet. 3:13) N’zomvetsa cisoni kuti olambila Yehova ena aleka kukhala maso. Iwo atengeka ndi zaciwelewele, ndipo pa cifukwa cimeneci akumana ndi zowawa. Anthu otelo angalephele kulandila madalitso osatha.

3. N’cifukwa ciani okwatilana afunika citsogozo ndi citetezo ca Yehova? (Onani cithunzi cili pamwamba.)

3 Popeza kuti khalidwe laciwelewele lafala masiku ano, amuna ndi akazi afunika citsogozo ndi citetezo ca Yehova kuti akwanitse kuteteza ukwati wao. (Ŵelengani Salimo 127:1.) Tiyeni tikambilane mmene okwatilana angalimbitsile ukwati wao mwa kuteteza mtima wao, kukhalabe paubwenzi ndi Mulungu, kuvala umunthu watsopano, kulankhulana bwino, ndi kupeleka mangawa a muukwati.

TETEZANI MTIMA WANU

4. N’ciani capangitsa Akristu ena kucita chimo?

4 Zingatheke bwanji kuti Mkristu atengeke ndi khalidwe laciwelewele? Nthawi zambili munthu amayamba kucita ciwelewele cifukwa ca zimene amaona. Yesu anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wacita naye kale cigololo mumtima mwake.” (Mat. 5:27, 28; 2 Pet. 2:14) Akristu ambili agwela m’chimo cifukwa coyamba khalidwe loipa mwa kupenyelela zamalisece, kuŵelenga mabuku odzutsa cilakolako ca kugonana, kapena kuonelela zinthu zonyansa pa Intaneti. Ena amakonda kupenyelela mafilimu aciwelewele, maseŵelo oipa, kapena mapulogalamu oipa a pa TV. Ndipo ena amapita ku malo osangalalila nthaŵi ya usiku kapena ku malo kumene amasisita thupi n’colinga codzutsa cilakolako ca kugonana.

5. N’cifukwa ciani tiyenela kuteteza mtima wathu?

5 Anthu ena amagwela m’ciyeso cifukwa coceza kwambili ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wao. M’dzikoli, anthu ambili amalephela kudziletsa ndipo amasangalala ndi ciwelewele. Kuonjezela pamenepo, tingayambe kukonda munthu amene si mwamuna kapena mkazi wathu cifukwa cakuti ndife opanda ungwilo ndipo mtima wathu ndi wonyenga. (Ŵelengani Yeremiya 17:9, 10.) Yesu anakamba kuti, mumtima mumacokela “maganizo oipa, za kupha anthu, za cigololo, za dama.”—Mat. 15:19.

6, 7. (a) Kodi mtima wonyenga ungapangitse munthu kucita ciani? (b) Tingapewe bwanji kucimwila Yehova?

6 Maganizo oipa akazika midzu mumitima ya anthu aŵili amene akhala akukopana, io angayambe kukambilana nkhani zimene ayenela kukambilana ndi mwamuna kapena mkazi wao cabe. Posapita nthawi, amayamba kupeza njila zoti akumane. Amayamba kukumana kaŵilikaŵili ndi kumanamizila kuti amangokumana mwangozi. Cikondi cao cikamalimba, kumakhala kosavuta kucita chimo, ndipo kumakhalanso kovuta kuthetsa ubwenzi wao ngakhale amadziŵa kuti zimene akucitazo n’zoipa.—Miy. 7:21, 22.

7 Iwo amaiwala kothelatu mfundo za makhalidwe abwino a Yehova. Amasiya kuceza wamba, ndipo amayamba kugwilana manja, kupsopsonana, kusisitana, ndi kugwilanagwilana modzutsa cilakolako. N’zacisoni kuti amayamba kucita zinthu zimene ayenela kucita ndi mwamuna kapena mkazi wao cabe. Mwakutelo, ‘amakopedwa ndi kukodwa m’cilakolako cao.’ Ndiyeno cilakolako cikakula, amacita ciwelewele. (Yak. 1:14, 15) Zimenezi zimakhala zomvetsa cisoni kwambili cifukwa cakuti onse aŵili akanapewa kucimwila Yehova ngati akanamulola kuwathandiza kuona cikwati cao kukhala colemekezeka. Nanga n’ciani cimene munthu ayenela kucita kuti ayambe kuona cikwati kukhala colemekezeka?

KHALANIBE PAUBWENZI NDI MULUNGU

8. Kodi kukhala paubwenzi ndi Yehova kumatithandiza bwanji kupewa ciwelewele?

8 Ŵelengani Salimo 97:10. Kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova kungatithandize kupewa ciwelewele. Tikamaphunzila za makhalidwe ake abwino ndi kuyesa kukhala “otsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndi kuyendabe m’cikondi,” tidzakhala okonzeka kukana “dama ndi conyansa camtundu uliwonse.” (Aef. 5:1-4) Kukumbukila kuti “Mulungu adzaweluza adama ndi acigololo,” kumathandiza okwatilana kucita khama kuti cikwati cao cikhale colemekezeka ndi cosaipitsidwa.—Aheb. 13:4.

9. (a) N’ciani cinathandiza Yosefe kukana ciyeso? (b) Tikuphunzilapo ciani pa citsanzo ca Yosefe?

9 Atumiki ena okhulupilika a Mulungu, ayamba khalidwe loipa cifukwa coceza ndi anzao a ku nchito amene si Mboni za Yehova akaweluka. Akhoza kukumana ndi mayeselo ngakhale panthawi yanchito. Yosefe amene anali mnyamata wokongola kwambili anazindikila kuti mkazi wa bwana wake anali kumufuna, ndipo zimenezi zinacitikila ku nchito. Tsiku ndi tsiku anali kunyengelela Yosefe. Pomaliza pake, mkaziyo “anam’gwila malaya mnyamatayo n’kumuuza kuti: ‘Ugone nane basi!’” Koma Yosefe anakana ndipo anathawa. N’ciani cinathandiza Yosefe kukhalabe wokhulupilika atakumana ndi ciyeso cimeneco? N’cifukwa cakuti anali kufunitsitsa kuteteza ubwenzi wake ndi Mulungu. N’zoona kuti Yosefe anacotsedwa nchito ndipo anaikidwa m’ndende popanda cifukwa, koma Yehova anam’dalitsa. (Gen. 39:1-12; 41:38-43) Akristu ayenela kupewa kugwela m’chimo ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wao kaya ali kunchito kapena ku malo ena obisika.

VALANI UMUNTHU WATSOPANO

10. Kodi umunthu watsopano umathandiza bwanji kuteteza cikwati?

10 Umunthu watsopano umene umalengedwa “mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu ndipo umatsatila zofunika pa cilungamo ceniceni ndi pa kukhulupilika,” ungathandize okwatilana kupewa ciwelewele. (Aef. 4:24) Amene amavala umunthu watsopano amacititsa ziwalo za thupi lao kukhala “zakufa ku dama, zinthu zodetsa, cilakolako ca kugonana, cikhumbo coipa, ndi kusilila kwa nsanje.” (Ŵelengani Akolose 3:5, 6.) Mfundo yakuti ticititse ziwalo za thupi kukhala “zakufa” ikusonyeza kuti khama ndi lofunika kuti tipewe zikhumbo zoipa. Tidzapewa ciliconse cimene cingaticititse kukhala ndi cikhumbo cofuna kugonana ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wathu. (Yobu 31:1) Tikamacita zinthu mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu, tidzaphunzila ‘kunyansidwa ndi coipa’ ndi ‘kugwilitsitsa cabwino.”—Aroma 12:2, 9.

11. Kodi kuvala umunthu watsopano kumalimbitsa bwanji cikwati?

11 Tikavala umunthu watsopano, timayamba kutengela makhalidwe a Yehova. (Akol. 3:10) Okwatilana akavala “cifundo cacikulu, kukoma mtima, kudzicepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima,” amakhala osangalala ndipo amateteza cikwati cao. (Akol. 3:12) Iwo amagwilizananso kwambili akalola ‘mtendele wa Kristu kulamulila m’mitima yao.’ (Akol. 3:15) Kukhala ndi “cikondi ceniceni” kungathandize okwatilana “kukhala patsogolo” pankhani yosamalilana ndi kupatsana ulemu.—Aroma 12:10.

12. Ndi makhalidwe ati amene muona kuti ndi ofunika kwambili kuti anthu asangalale mu cikwati?

12 Banja lina litafunsidwa kufotokoza cimene cawathandiza kukhala osangalala mu cikwati cao, Sid anati: “Cikondi ndi khalidwe lalikulu limene takhala tikuyesetsa kukulitsa. Taphunzilanso kuti kudzicepetsa n’kofunika kwambili.” Mkazi wake Sonja anavomeleza, ndipo anaonjezela kuti: “Kukoma mtima n’kofunika kwambili. Ndipo taphunzila kusonyeza kudzicepetsa ngakhale kuti nthawi zina zimakhala zovuta.”

MUZILANKHULANA BWINO

13. N’ciani cingathandize kuti cikwati cikhale colimba? Nanga cifukwa ciani?

13 Cinthu cina cofunika cimene cingathandize cikwati kukhala colimba ndi kulankhulana mokoma mtima. Koma n’zomvetsa cisoni kuti okwatilana ena amalankhulana mopanda ulemu kuposa mmene amakambila ndi munthu amene samudziŵa kapena ndi ziweto monga galu ndi cona. “Kuwawidwa mtima konse kwa njilu, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mau acipongwe,” zimaika cikwati pangozi. (Aef. 4:31) Zoonadi, kulankhula mau osuliza ndi oipa kumaononga cikwati. Conco, okwatilana ayenela kulimbitsa cikwati cao mwa kulankhulana mokoma mtima, mwacikondi, ndi mwacifundo.—Aef. 4:32.

14. N’ciani cimene okwatilana ayenela kupewa?

14 Baibulo limakamba kuti pali “nthawi yokhala cete.” (Mlal. 3:7) Koma zimenezi sizitanthauza kuti tiyenela kusiya kulankhalana ndi mnzathu wa mucikwati cifukwa kulankhulana kumathandiza cikwati kukhala colimba. Mkazi wina wa ku Germany amene ali pa banja anati: “Mnzako wa mu cikwati amavutika mtima ngati ukana kum’lankhula.” Ndipo anaonjezelanso kuti: “N’zoona kuti munthu akakhumudwa amalankhula mosasamala, koma si bwino kulankhula mozazuka. Cifukwa cokhumudwa mungalankhule mau amene angakhumudwitse mnzanu wa mucikwati, ndipo zimenezo zingapangitse kuti mkangano ukule kwambili.” Okwatilana sangathetse mavuto mwa kulalatilana kapena kuleka kulankhulana. M’malo mwake, okwatilana amalimbitsa cikwati cao ngati amathetsa mikangano mwamsanga ndi kupewa kukulitsa nkhani.

15. Kodi kulankhulana bwino kungalimbitse bwanji cikwati?

15 Cikwati cimalimba ngati okwatilana amakonda kulankhula za kukhosi momasuka. N’kofunika kuganizila mmene timalankhulila ndi zimene timalankhula. Motelo, ngakhale mwakhumudwa, muyenela kuyesetsa kulankhula mokoma mtima. Zimenezi zingaonekele ndi mmene mukukambila ndiponso mau amene mukugwilitsila nchito. Mukamalankhula mwa njila imeneyi kumakhala kosavuta kuti mnzanu amvetsele zimene mukulankhula. (Ŵelengani Akolose 4:6.) Okwatilana angalimbitse cikwati cao mwa kulankhulana bwino ndi mau “olimbikitsa monga mmene kungafunikile, kuti asangalatse” mnzao wa mu cikwati.—Aef. 4:29.

Mwamuna ndi mkazi akukambitsilana

Okwatilana angalimbitse ukwati wao mwa kulankhulana bwino (Onani ndime 15)

MUZIPELEKA MANGAWA A MUCIKWATI

16, 17. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti okwatilana azizindikila mmene mnzao akumvelela ndiponso nkhani yokhudza kugonana?

16 Okwatilana angalimbitse ukwati wao ngati amaika zofuna za mnzao wa muukwati patsogolo pa zao. (Afil. 2:3, 4) Onse aŵili ayenela kuzindikila mmene mnzake akumvelela ndiponso pankhani yokhudza mangawa a mucikwati.—Ŵelengani 1 Akorinto 7:3, 4.

17 N’zacisoni kuti okwatilana ena amalephela kusonyezana cikondi, ndipo amuna ena amaganiza kuti koonetsa cikondi mkazi n’kumupusika. Koma Baibulo limakamba kuti: “Inunso amuna, pitilizani kukhala ndi akazi anu mowadziŵa bwino.” (1 Pet. 3:7) Amuna ayenela kudziŵa kuti mangawa a mucikwati satanthauza kugonana cabe. Kudzakhala kosavuta kwa mkazi kusangalala ndi mangawa a mucikwati ngati mwamuna wake amamusonyeza cikondi nthawi zonse osati panthawi ya kugonana cabe. Ngati onse aŵili amasonyezana cikondi, kudzakhala kosavuta kwa io kukhutilitsa zosoŵa za m’maganizo ndi za kuthupi za mnzao.

18. Kodi okwatilana angalimbitse bwanji cikwati cao?

18 N’zoona kuti kucita ciwelewele n’kulakwa. Koma kusoŵeka kwa cikondi m’banja ndi kumene kumacititsa okwatilana ena kuyamba kukondana ndi munthu wina amene si mwamuna kapena mkazi wao. (Miy. 5:18; Mlal. 9:9) Ndiye cifukwa cake Baibulo limalimbikitsa okwatilana kuti: “Musamanane, [mangawa a mucikwati] kupatulapo ngati mwagwilizana kuimitsa kaye mangawawo kwa nthawi yodziŵika.” Cifukwa ciani? “Kuopela kuti Satana angapitilize kumakuyesani mukalephela kudzigwila.” (1 Akor. 7:5) Zingakhale zomvetsa cisoni ngati okwatilana angalole Satana kugwilitsila nchito ‘kulephela kudzigwila’ kwao kuti acite cigololo. Motelo, ngati aliyense m’cikwati ‘samangodzifunila zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina,’ ndipo amapeleka mangawa a mucikwati osati mwa mwambo cabe koma mwacikondi, cikondico ndi cimene cingalimbitse cikwati cao.—1 Akor. 10:24.

PITILIZANI KUTETEZA CIKWATI CANU

19. Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciani? Ndipo n’cifukwa ciani?

19 Kwangotsala pang’ono kuti tiloŵe m’dziko latsopano lolungama. N’cifukwa cake ingakhale ngozi yaikulu kwambili ngati tingagonje ku zikhumbo zoipa monga mmene zinakhalila ndi Aisiraeli 24,000 m’cigwa ca Moabu. Pambuyo  pofotokoza zocitikazo, Baibulo limacenjeza kuti: “Amene akuyesa kuti ali cilili asamale kuti asagwe.” (1 Akor. 10:12) Ngati tifuna kulimbitsa cikwati cathu, n’kofunika kukhalabe okhulupilika kwa Yehova ndi kwa mnzathu wa mu cikwati. (Mat. 19:5, 6) Panopa, kuposa ndi kale lonse, tiyenela ‘kucita ciliconse cotheka kuti iye adzatipeze opanda banga, opanda cilema ndiponso tili mu mtendele.’—2 Pet. 3:13, 14.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani