LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 7/1 tsa. 16
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Inu Makolo—Thandizani Ana Anu Kukonda Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 2
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Mmene Mungaphunzitsile Mwana Wanu
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 7/1 tsa. 16

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

N’ciani cingakuthandizeni kukhala kholo labwino?

Makolo angalele bwino ana ao ngati akukondana ndi kulemekezana. (Akolose 3:​14, 19) Makolo abwino amakonda ndi kuyamikila ana ao monga mmene Yehova Mulungu anacitila kwa mwana wake.​—Ŵelengani Mateyu 3:​17.

Atate wathu wakumwamba amamvetsela atumiki ake akamamuuza maganizo ao ndi zakukhosi kwao. Conco makolo angacite bwino kutengela citsanzo ca Mulungu pa nkhani ya kumvetsela pamene ana ao akulankhula. (Yakobo 1:​19) Iwo ayenela kuzindikila mmene ana ao akumvela, ndipo angazindikile zimenezi ngakhale kudzela m’zimene anao angalankhule.​—Ŵelengani Numeri 11:​11, 15.

Kodi mungaphunzitse bwanji ana anu kuti adzathe kudziimila paokha?

Monga kholo muli ndi udindo wopeleka malamulo kwa ana anu. (Aefeso 6:⁠1) Tengelani citsanzo ca Mulungu. Iye amaonetsa cikondi kwa ana ake mwa kufotokoza momveka bwino malamulo ndi mavuto amene angakhalepo ngati sanamvele malamulowo. (Genesis 3:⁠3) Komabe iye sakakamiza anthu kuti azimumvela, m’malo mwake amawalimbikitsa kucita zabwino kuti apindule.​—Ŵelengani Yesaya 48:​18, 19.

Khalani ndi colinga cothandiza ana anu kukonda Mulungu. Kucita zimenezi kudzawathandiza kucita zinthu mwanzelu ngakhale pamene ali kwa okha. Mofanana ndi mmene Mulungu amaphunzitsila, citsanzo canu makolo, cingathandize pophunzitsa ana anu kukonda Mulungu.⁠—Ŵelengani Deuteronomo 6:​5-7; Aefeso 4:​32; 5:⁠1.

Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 14 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Buku limeneli lipezekanso pa www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani