“Ngati Kingsley Wakwanitsa, Inenso Ndingakwanitse”
KINGSLEY atangomugwila paphewa, anayamba kuŵelenga Baibulo. Iyi inali nthawi yake yoyamba kukamba nkhani mu Sukulu ya Ulaliki. Iye anachula liu lililonse molondola ndipo sanalumphe mau alionse. Koma mwina mungafunse kuti, ‘N’cifukwa ciani sanali kuyang’ana pa Baibulo lake poŵelenga?’
Kingsley ndi wakhungu ndipo amakhala ku Sri Lanka. Kuonjezela apo, iye amavutika kumva ndipo amayendela pa njinga ya olemala. Kodi Kingsley anaphunzila bwanji za Yehova, nanga zinatheka bwanji kuti alembetse m’Sukulu ya Ulaliki? Ndiloleni kuti ndikufotokozeleni.
Nthawi yoyamba pamene ndinakumana ndi Kingsley, ndinacita cidwi kuona kuti anali ndi njala ya coonadi. Iye anaphunzilapo Baibulo mobwelezabweleza ndi abale osiyanasiyana ndipo buku lake lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha la zilembo za anthu akhungu linali litaonongeka.a Iye anavomela kuti tiyambenso kuphunzila koma tinakumana ndi mavuto aŵili.
Vuto loyamba linali lakuti, Kingsley anali kukhala kunyumba zosungila okalamba ndi olemala. Cifukwa ca phokoso la anthu komanso vuto lakumva limene iye anali nalo, ndinafunika kukamba mokweza mau pophunzila. Izi zinacititsa kuti anthu onse azimva zimene tinali kuphunzila.
Vuto laciŵili linali lakuti, Kingsley anali kuŵelenga movutikila ndi kugwila zinthu zocepa kwambili. Conco kuti phunzilo likhale lopindulitsa, anali kukonzekela mwakhama. Iye anali kuŵelenga mobwelezabweleza nkhani imene tidzaphunzila ndipo anali kuŵelenganso Malemba m’Baibulo lake la zilembo za akhungu. Akatelo anali kupezelatu mayankho a mafunso ndipo njila imeneyi inathandiza kwambili. Pophunzila anali kukhala pansi mopinda miyendo yake, ndipo mokweza mau anali kufotokoza zimene waphunzila. Posapita nthawi, tinayamba kuphunzila kaŵili pa mlungu ndipo phunzilo lililonse linali kutenga maola aŵili.
KUYAMBA KUSONKHANA NDI KUTENGAMO MBALI
Kingsley ndi Paul
Kingsley anali kufunitsitsa kupezeka pamisonkhano, koma zinali zovuta kwambili. Iye anali kufunika kuthandizidwa kuti akhale pa njinga ya olemala, kukhala m’galimoto ndiponso mu Nyumba ya Ufumu. Zosangalatsa ndi zakuti abale ndi alongo ambili anadzipeleka kumuthandiza ndipo nchito imeneyi anaiona kukhala mwai wa utumiki. Pamisonkhano, Kingsley anali kukhala pafupi kwambili ndi zokuzila mau ndi kumvetsela mosamalitsa ndiponso kutengamo mbali mwa kuyankha.
Ataphunzila kwa kanthawi, Kingsley analembetsa m’Sukulu ya Ulaliki. Patatsala milungu iŵili kuti akakambe nkhani yake yoyamba, ndinamufunsa ngati anali kuyeseza. Iye anayankha motsimikiza kuti: “Inde M’bale, ndakhala ndikuyeseza kwa maulendo 30.” Ndinamuyamikila kwambili kaamba ka khama lake ndipo ndinam’pempha kuti ndimve mmene akuŵelengela. Iye anatsegula Baibulo lake la zilembo za akhungu ndi kuyamba kuŵelenga. Ndinadabwa kuona kuti poŵelenga sanali kugwila pa Baibulo lake monga mmene anali kucitila poyamba. Iye anali ataloŵeza nkhani yake yonse pamtima.
Ndinakhudzika mtima kwambili cakuti misozi inagwa m’maso mwanga. Ndinamufunsa kuti ndidziŵe zimene zinamuthandiza kuŵelenga bwino motele atangoyeseza nthawi 30 cabe. Kingsley anayankha kuti: “Iyai, ndakhala ndikuyeseza maulendo 30 tsiku lililonse.” Pafupifupi mwezi wonse, iye anali kukhala pansi kuŵelenga mobwelezabweleza kufikila ataloŵeza nkhani yonse pamtima.
Tsiku linafika lakuti Kingsley akambe nkhani mu Nyumba ya Ufumu. Pamene anamaliza nkhani yake, abale ndi alongo anaomba m’manja mokhudzidwa mtima kwa nthawi yaitali, ndipo ena anagwetsa misozi poona khama la mwana wa sukulu watsopano ameneyu. Mlongo wina amene analeka kukamba nkhani m’sukulu cifukwa ca mantha anapempha kuti ayambenso. N’cifukwa ciani? Mlongoyu anati: “Ngati Kingsley wakwanitsa inenso ndingakwanitse.”
Pambuyo pophunzila Baibulo kwa zaka zitatu, Kingsley anadzipeleka kwa Yehova ndi kubatizidwa pa September 6, 2008. Anamwalila ali wokhulupilika pa May 13, 2014. Kingsley anali ndi cikhulupililo cakuti adzapitilizabe utumiki wake ali ndi mphamvu ndiponso thanzi labwino m’Paladaiso padziko lapansi. (Yes. 35:5, 6)—Yosimbidwa ndi Paul McManus
a Lofalitsidwa m’caka ca 1995 koma tsopano silisindikizidwanso.