LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 11/1 tsa. 4
  • Kodi Mboni za Yehova ndi anthu otani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mboni za Yehova ndi anthu otani?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Zofanana
  • N’cifukwa ciani timalalikila?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tanthauzo Lake la Kusakhalila Mbali
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 11/1 tsa. 4
Mboni za Yehova za mitundu yosiyanasiyana zikupatsana moni m’Nyumba ya Ufumu

Kodi Mboni za Yehova ndi anthu otani?

Ndife gulu lapadziko lonse ndipo sitigwilizana ndi magulu aliwonse a zipembedzo. Ngakhale kuti likulu lathu lili ku United States, Mboni za Yehova zambili zimakhala m’maiko ena. Mboni zoposa 8 miliyoni m’maiko oposa 230 zimaphunzitsa anthu Baibulo. Timacita zimenezi pokwanilitsa mau a Yesu akuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.”​—Mateyu 24:14.

Mosasamala kanthu za kumene timakhala, timamvela malamulo ndipo sitiloŵelela m’ndale za dziko. Timacita zimenezi cifukwa timamvela mau a Yesu akuti Akristu ‘sayenela kukhala mbali ya dziko.’ Conco sitiloŵelela m’ndale za dziko ndi m’zocitika zina zocilikiza nkhondo. (Yohane 15:19; 17:16) Pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, Mboni za Yehova zinaikidwa m’ndende, kuzunzidwa ndi kuphedwa cifukwa cokana kuloŵelela m’ndale za dziko. Bishopu wina wa ku Germany analemba kuti: “Iwo ayeneladi kunena kuti cipembedzo cao cokha n’cimene cinakanitsitsa kumenya nao nkhondo mu ulamulilo wa Hitler.”

“[Mboni za Yehova] zili ndi makhalidwe abwino kwambili. Timalakalaka kugwilitsila nchito anthu amenewa pa nkhani za ndale, koma sizingatheke. . . . Zimalemekeza maboma olamulila koma zimakhulupilila kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ukhoza kuthetsa mavuto onse a mtundu wa anthu.”—Anatelo Nová Svoboda, wofalitsa nkhani ku Czech Republic.

Ngakhale n’conco, sitidzipatula pa anzathu. Yesu anapemphelela ophunzila ake kuti: “Sindikupempha kuti muwacotse m’dziko, koma kuti muwayang’anile kuopela woipayo.” (Yohane 17:15) Mwina mumationa tikugwila nchito, tikupita kusukulu, ndi kugula zinthu m’dela limene timakhala.

MAIKO AMENE KULI MBONI ZAMBILI

  • United States 1,190,000

  • Mexico 800,000

  • Brazil 770,000

  • Nigeria 330,000

  • Italy 250,000

  • Japan 220,000

Isiraeli wa makono

Onelelani vidiyo yamutu wakuti, Special Convention in Israel pa webusaiti yathu ya www.jw.org, ndipo onani mmene Mboni za m’dziko la Israeli ndi Palestine zapewela kusankhana mitundu. (Pitani pa ZOKHUDZA IFE > MISONKHANO)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani