LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 11/1 tsa. 5
  • Kodi Mboni za Yehova zimakhulupilila ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mboni za Yehova zimakhulupilila ciani?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Zofanana
  • N’cifukwa ciani timalalikila?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani?
    Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani?
  • Kuyelekezela Zinthu Kopindulitsa Kwambili
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 11/1 tsa. 5
Banja la Mboni za Yehova likuphunzila Baibulo ndi ana ao

Kodi Mboni za Yehova zimakhulupilila ciani?

Mboni za Yehova zimakhulupilila kuti “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Timoteyo 3:16) Baibulo limatithandiza kudziŵa zambili zokhudza Mlengi komanso kuti tikhale ndi umoyo wabwino.

Baibulo limati: “Kuti anthu adziŵe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulila dziko lonse lapansi.” (Salimo 83:18) Conco, timalambila Yehova Mulungu yekha ndipo monga Mboni zake, timauzako ena za dzina lake.—Yesaya 43:10-12.

Monga Akristu, timakhulupilila kuti Yesu, “Mwana wa Mulungu”a anabwela padziko lapansi n’kukhala Mesiya. (Yohane 1:34, 41; 4:25, 26) Yesu ataphedwa, anaukitsidwa n’kupita kumwamba. (1 Akorinto 15:3, 4) Patapita nthawi anakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 11:15) Ufumu umenewo ndi boma lenileni limene lidzabwezeletsa Paradaiso padziko lapansi. (Danieli 2:44) Baibulo limati: “Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, Ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Salimo 37:11, 29.

“Akamaŵelenga Baibulo amakhulupilila kuti Mulungu akulankhula nao. Akakumana ndi mavuto amafufuza m’Mau a Mulungu kuti apeze njila yothetsela mavutowo. . . . Kwa io Mau a Mulungu ndi amphamvu.”—Anatelo Benjamin Cherayath, Papa wa chalichi ca katolika m’nyuzipepala ya Münsterländische Volkszeitung ya ku Germany

Mboni za Yehova zimakhulupilila kuti mfundo za m’Baibulo n’zopindulitsa. (Yesaya 48:17, 18) Conco, timatsatila kwambili mfundo zimenezo. Mwacitsanzo, Baibulo limaticenjeza pa zinthu zimene zingaononge maganizo ndi matupi athu. Conco, timapewa kukoka fodya kapena kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo. (2 Akorinto 7:1) Timapewanso zinthu zimene Baibulo limaletsa, monga kuledzela, ciwelewele, ndi kuba.—1 Akorinto 6:9-11.

a Baibulo limacha Yesu kuti “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu” cifukwa analengedwa mwacindunji ndi Yehova.—Yohane 3:18; Akolose 1:13-15.

Makolo akumwetulila pamene mwana wao akutsegula mphatso

Kuti mudziŵe zimene timakhulupilila, cifukwa cake sitikondwelela maholide, ndi cifukwa cimene sitilolela kuikidwa magazi, pitani pa www.jw.org polemba kuti ZOKHUDZA IFE > MAFUNSO OFUNSIDWA KAŴILIKAŴILI.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani