Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa December 29, 2014.
Kodi lamulo la pa Deuteronomo 14:1 loletsa kudzicekaceka pa nthawi yolila malilo timaliona bwanji? [Nov. 3, w04 9/15 tsa. 27 ndime 5]
N’cifukwa ciani Mulungu analamula mafumu Aciisiraeli kuti azikopela buku la Cilamulo ca Mulungu ndi ‘kuliŵelenga masiku onse a moyo wao’? (Deut. 17:18-20) [Nov. 3, w02 6/15 tsa. 12 ndime 4]
N’cifukwa ciani Baibulo limanena kuti “usamange ng’ombe ndi bulu kuti uzilimitse pamodzi,” ndipo Akristu angatsatile bwanji lamulo limeneli? (Deut. 22:10) [Nov. 10, w03 10/15 tsa. 32]
N’cifukwa ciani Mulungu anali kuletsa munthu kulanda mnzake “mphelo kapena mwala wopelela monga cikole”? (Deut. 24:6) [Nov. 17, w04 9/15 tsa. 26 ndime 3]
Kodi Aisiraeli anafunika kumvela Mulungu motani, nanga n’ciani cifunika kutilimbikitsa kutumikila Yehova? (Deut. 28:47) [Nov. 24, w10 9/15 tsa. 8 ndime 4]
Kodi lemba la Deuteronomo 30:19, 20 limachula mfundo zitatu ziti zofunika kwambili kuti munthu akhalebe ndi moyo? [Nov. 24, w10 2/15 tsa. 28 ndime 17]
Kodi tifunika kuchula mokweza mau onse a m’Baibulo kuyambila Genesis mpaka Chivumbulutso tikamaŵelenga? Fotokozani. (Yos. 1:8) [Dec. 8, w13 4/15 tsa. 7 ndime 4]
Kodi “kalonga wa gulu lankhondo la Yehova” wochulidwa pa Yoswa 5:14, 15 ndani? Nanga nkhani imeneyi imatilimbikitsa bwanji? [Dec. 8, w04 12/1 tsa. 9 ndime 2]
N’ciani cinacititsa kuti Akani acimwe? Nanga ife tingaphunzilepo ciani pa citsanzo cake coipa? (Yos. 7:20, 21) [Dec. 15, w10 4/15 tsa. 20-21 ndime 2, 5]
Kodi citsanzo ca Kalebe cimatilimbikitsa bwanji masiku ano? (Yos. 14:10-13) [Dec. 29, w04 12/1 tsa. 12 ndime 2]