LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp21 na. 1 masa. 3-4
  • Zimene Anthu Amakamba Pankhani ya Kupemphela

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Anthu Amakamba Pankhani ya Kupemphela
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Athu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
wp21 na. 1 masa. 3-4
Anthu a mitundu yosiyana-siyana pa dziko lapansi akupemphela na kufuna-funa citsogozo ca Mulungu.

Zimene Anthu Amakamba Pankhani ya Kupemphela

“Pamene nipemphela, nimamvela monga Mulungu ali pambali panga, wanigwila dzanja ndipo akunitsogolela pamene niona monga nasocela.”—MARÍA.

“Mkazi wanga anamwalila pambuyo povutika na matenda a khansa kwa zaka 13. Nikumbukila kuti n’nali kupemphela kwa Mulungu nthawi zonse, ndipo n’nali kuona kuti anali kunimvetseladi panthawi yovutayo. Izi zinanithandiza kukhala na mtendele wa maganizo.”—RAÚL.

“Pemphelo ni mphatso yabwino ngako imene Mulungu anapatsa anthu.”—ARNE.

María, Raúl, Arne, na ena ambili amaona kuti pemphelo ni mphatso yapadela. Amaona kuti kupitila m’pemphelo, angakambe na Mulungu, kumuyamikila, na kum’pempha thandizo. Amakhulupilila na mtima wonse mawu olimbikitsa amene Baibo imakamba ponena za pemphelo. Imati: “Ifetu timamudalila kuti ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.”—1 Yohane 5:14.

Komabe, anthu ambili sakhulupilila zimene Baibo imakamba ponena za pemphelo. Steve anafotokoza mmene anali kulionela pemphelo kale. Anati: “N’tafika zaka 17, anzanga atatu anafa pangozi. Mmodzi anafa pangozi ya motoka, ndipo ena aŵili anamila panyanja.” Kodi Steve anacita ciani? Iye anati: “N’napemphela kwa Mulungu kuti anithandize kumvetsetsa cifukwa cake zimenezi zinacitika, koma sananiyankhe. Conco, mumtima n’nadzifunsa kuti, ‘Kodi kupemphela kulidi na phindu?’” Anthu ambili amaona kuti kupemphela kulibe phindu cifukwa coona ngati mapemphelo awo sayankhidwa.

Palinso zifukwa zina zimene anthu ena amaonela kuti kupemphela kulibe phindu. Ena amakamba kuti popeza Mulungu amadziŵa zonse, ndiye kuti adziŵa kale zosoŵa zathu kapena mavuto athu, ndipo palibe cifukwa comuuzila zinthu zimene azidziŵa kale.

Enanso amakhulupilila kuti Mulungu amakana kumvetsela mapemphelo awo cifukwa ca zolakwa zimene anacita kumbuyoko. Jenny anati: “Vuto langa lalikulu n’lakuti nimadziona ngati wosafunika. Kumbuyoko n’nacitako zinthu zimene nimadziimba nazo mlandu. Conco, nimadziona kuti ndine wocimwa kwambili cakuti n’kosayenela Mulungu kumvetsela mapemphelo anga.”

Mayi akupemphela m’chechi atayang’ana kumwamba pamene ena akupemphela atazyolika.

Kodi imwe kupemphela mumakuona bwanji? Ngati na imwe mumakhala na nkhawa kapena zikayikilo ngati zimenezi pa nkhani ya pemphelo, musataye mtima cifukwa Baibo ili na mayankho okhutilitsa. Zimene Baibo imakamba pa nkhani ya pemphelo n’zodalilika,a ndipo ingakuthandizeni kupeza mayankho pa mafunso monga akuti:

  • Kodi Mulungu amamvetseladi mapemphelo athu?

  • N’cifukwa ciani iye sayankha mapemphelo ena?

  • Mungapemphele bwanji kuti Mulungu azimvetsela mapemphelo anu?

  • Kodi mapemphelo angakuthandizeni bwanji?

a M’Baibo muli mapemphelo a atumiki ambili a Mulungu, kuphatikizapo a Yesu Khristu. M’Malemba Aciheberi, amenenso nthawi zambili amachedwa Cipangano Cakale, muli mapemphelo oposa 150.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani