LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w22 April tsa. 15
  • Mabisiketi a Tiagalu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mabisiketi a Tiagalu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Tumasitandi twa Ulaliki Tothandiza Pocitila “Umboni ku Mitundu Yonse”
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Kodi Mudziŵa?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
w22 April tsa. 15
Munthu akuyenda na tuagalu twake tuŵili. Iye akupitila pamalo amene banja likucita ulaliki wa pa kasitandi.

Mabisiketi a Tiagalu

NICK, amene akhala mu mzinda wa Oregon ku America, analemba kuti: “Kumayambililo kwa 2014, n’nayamba kupita kokayenda na tiagalu tanga tuŵili m’tauni ya kwathu. Nthawi zonse Mboni za Yehova zinali kulalikila m’tauni imeneyi pa tumasitandi twa ulaliki. Iwo anali kuvala bwino, ndipo anali kumwetulila aliyense amene wadutsa.

“Mbonizo zinali zokoma mtima kwa ine, komanso kwa tiagalu tanga. Tsiku lina, Elaine, amene anali pa kasitandi ka ulaliki, anapatsa tiagalu tanga mabisiketi. Kucokela pa tsikuli, nikangopitila pa kasitandi kawo ka ulaliki, tiagalu tanga tinali kunikokela kwa Mbonizo kuti tukatenge ‘cakudya cawo.’

“Izi zinapitiliza kwa miyezi yambili, ndipo tiagalu tanga tunali kusangalala na mabisiketi awo. Inenso n’nali kupindula na makambilano acidule na Mbonizo. Koma sin’nali kufuna kukambilana nawo kwa nthawi yaitali. N’nali na zaka pafupifupi 70, ndipo sin’nali kudziŵa zimene Mboni za Yehova zimakhulupilila. Cifukwa cogwilitsidwa mwala na zipembedzo zambili zacikhristu, n’naganiza zoyamba kuphunzila Baibo panekha.

“Panthawiyo, n’nali kuonanso a Mboni ena akulalikila pa kasitandi ka ulaliki m’madela osiyana-siyana. Iwonso anali aubwenzi. Anali kuyankha mafunso anga pogwilitsila nchito Baibo, ndipo izi zinapangitsa kuti niyambe kuwakhulupilila kwambili.

“Tsiku lina, Elaine ananifunsa kuti, ‘Kodi m’makhulupilila kuti nyama ni mphatso yocokela kwa Mulungu?’ N’nayankha kuti, ‘Inde!’ Ndiyeno ananiŵelengela Yesaya 11:6-9. Apa m’pamene zinthu zinasinthila. Koma sin’nali kufuna kutengako mabuku a Mboni.

“Kucokela tsiku limenelo, tinayamba kukhala na makambilano acidule koma opindulitsa na Elaine, komanso mwamuna wake Brent. Iwo ananilimbikitsa kuti nikaŵelenge Baibo kuyambila pa Mateyu mpaka Macitidwe kuti nikamvetse tanthauzo lokhala Mkhristu. N’nacita zimenezo. Posakhalitsa, n’navomela kuphunzila Baibo na banjali. Umu munali mu 2016.

“Mlungu ulionse n’nali kuyembekezela mwacidwi kuphunzila Baibo, komanso kupita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. N’naona kuti ni dalitso, komanso n’nali wokondwa kuphunzila zimene Baibo imakamba. Patapita caka na miyezi, n’nabatizika. Tsopano nili na zaka 79, ndipo ndine woyamikila kwambili kuti n’napeza cipembedzo coona. Yehova wanidalitsa ponilola kukhala m’banja la atumiki ake odzipatulila.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani