NKHANI YOPHUNZILA 49
N’zotheka Kudzakhala na Moyo Kwamuyaya
“Moyo wosatha adzaupeza.”—YOH. 17:3.
NYIMBO 147 Lonjezo la Moyo Wamuyaya
ZIMENE TIKAMBILANEa
1. Kodi timapindula bwanji tikamasinkhasinkha lonjezo la Yehova la moyo wosatha?
YEHOVA analonjeza kuti anthu amene amamumvela adzalandila “moyo wosatha.” (Aroma 6: 23) Tikamasinkhasinkha lonjezo la Yehova limeneli, cikondi cathu pa iye cimalimbilako. Ganizilani izi: Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambili, moti anatilonjeza mphatso ya moyo wosatha, kotelo kuti tisakalekane naye kwamuyaya.
2. Kodi lonjezo la moyo wosatha limatithandiza bwanji?
2 Lonjezo la Mulungu la moyo wosatha, limatithandiza kupilila mayeso amene tikupitamo palipano. Ngakhale adani athu atiwopseze kuti atipha, sitileka kutumikila Yehova. Cifukwa ciyani? Cifukwa cimodzi n’cakuti tikafa tili okhulupilika kwa Yehova, iye adzatiukitsa tikudziŵa kuti sitidzafanso. (Yoh. 5:28, 29; 1 Akor. 15:55-58; Aheb. 2:15) N’cifukwa ciyani tingakhale otsimikiza kuti n’zotheka kukhala na moyo kwamuyaya? Onani zifukwa izi.
YEHOVA NI WAMUYAYA
3. N’cifukwa ciyani sitikayikila kuti Yehova ni wokhoza kutipangitsa kukhalapobe na moyo kwamuyaya? (Salimo 102:12, 24, 27)
3 Tidziŵa kuti Yehova ni wokhoza kutipangitsa kukhalapobe na moyo kwamuyaya, cifukwa iye ni Gwelo la moyo, ndipo adzakhalapo kwamuyaya. (Sal. 36:9) Tiyeni tione mavesi ena m’Baibo amene atsimikizila kuti Yehova wakhalapo nthawi zonse, komanso kuti iye adzakhalapobe. Salimo 90:2 imakamba kuti Yehova wakhalapo “kuyambila kalekale mpaka kalekale.” Nayonso Salimo 102 imakambanso cimodzimodzi. (Ŵelengani Salimo 102:12, 24, 27.) Ndipo ponena za Atate wathu wakumwamba, mneneli Habakuku analemba kuti: “Inu Yehova, inutu mwakhalapo kuyambila kalekale. Inu Mulungu wanga, Mulungu wanga Woyela, inu simufa.”—Hab. 1:12.
4. Kodi tiyenela kuvutika maganizo ngati sitimvetsa kuti Yehova wakhalapo kuyambila kalekale? Fotokozani.
4 Kodi mumavutika kumvetsa kuti Yehova wakhalapo “mpaka kalekale”? (Yes. 40:28) Ngati mumaona conco, si inu nokha. Ponena za Mulungu, Elihu anati: “Zaka zake n’zosaŵelengeka.” (Yobu 36:26) Ngati sitinamvetsetse zinazake, sizitanthauza kuti zinthu zimenezo n’zabodza. Mwacitsanzo, ngakhale kuti sitimvetsa zonse zokhudza mmene magetsi amaseŵenzela, kodi zitanthauza kuti magetsiwo kulibe? Ayi! Mofananamo, mfundo yakuti Yehova wakhala alipo kucokela muyaya ndipo adzakhalapobe mpaka muyaya, ife anthu sitingaimvetse. Koma kusamvetsa kumeneku sikutanthauza kuti mfundo imeneyi si yoona. Kudziŵa zoona ponena za Mlengi wathu sikudalila zimene timamvetsa zokhudza iye, kapena zimene sitingamvetse. (Aroma 11:33-36) Iye analipo kale zolengedwa zonse zisanakhaleko, kuphatikizapo dzuŵa na nyenyezi. Yehova amatitsimikizila kuti iye ni amene “anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake.” Inde, iye anakhalako ‘asanayale kumwamba.’ (Yer. 51:15; Mac. 17:24) N’cifukwa cina citi cimene tingakhalile otsimikiza kuti n’zotheka kudzakhala na moyo kwamuyaya?
TINALENGEDWA KUTI TIKHALE NA MOYO KWAMUYAYA
5. Kodi banja loyamba linali na ciyembekezo cotani?
5 Pa zamoyo zonse zimene Yehova analenga padziko lapansi, ni anthu okha amene anawalenga kuti akhale na moyo kwamuyaya. Komabe, Yehova anacenjeza Adamu kuti: “Usadye zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa. Cifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Gen. 2:17) Adamu na Hava akanamvela Yehova sakanafa. Conco, m’pomveka kunena kuti m’kupita kwanthawi, Yehova akanawalola kudya cipatso ca “mtengo wa moyo.” Izi zikanawatsimikila kuti iwo adzakhala na “moyo mpaka kalekale.”b—Gen. 3:22.
6-7. (a) N’ciyani cina cimene cionetsa kuti anthu analengedwa kuti asamafe? (b) Ni zinthu ziti zimene muyembekezela kukacita m’dziko latsopano? (Onani zithunzi.)
6 N’zocititsa cidwi kuti asayansi ena apeza umboni woonetsa kuti ubongo wathu ulinako kuthekela kosunga zinthu zoculuka kuposa zimene timaphunzila pa zaka zimene timakhala na moyo pali pano. Mu 2010, magazini yakuti Scientific American Mind inati ubongo wathu ungasunge zinthu zoculuka mofanana na mapulogilamu a pa TV, amene angajambulidwe kwa maola 3 miliyoni (kapena kwa zaka zoposa 300). Ciŵelengelo cimeneci n’congoyelekezela cabe. Apa mfundo yake ni yakuti Yehova anapanga ubongo wathu kuti uzikwanitsa kusunga zinthu zoculuka kuposa zimene tingaphunzile pa zaka 70 kapena 80.—Sal. 90:10.
7 Yehova anatilenganso na cifuno copitiliza kukhalabe na moyo. Ponena za anthufe, Baibo imati Mulungu “anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Mlal. 3:11) Ici n’cifukwa cimodzi cimene timaonela imfa kukhala mdani. (1 Akor. 15:26) Tikadwala mwakayakaya, kodi timangoyembekezela kumwalila osacitapo kalikonse? Ayi. Nthawi zambili timapita ku cipatala, kukalandila cithandizo ca mankhwala kuti matenda athuwo athe. Timacita zonse zotheka kuti tisamwalile. Ndipo munthu amene timakonda akamwalila, kaya munthuyo ni wacicepele kapena wamkulu, timakhala na cisoni kwa nthawi yaitali. (Yoh. 11:32, 33) Kukamba zoona, ngati Mlengi wathu analibe colinga cakuti anthu akhale na moyo kosatha, sakanatipatsa cikhumbo komanso kuthekela kokhala na moyo kwamuyaya. Koma palinso zifukwa zina zotipangitsa kukhulupilila kuti n’zotheka kudzakhala na moyo kwamuyaya. Tsopano, tiyeni tikambilane zimene Yehova anacita kalelo, komanso zimene akucita palipano, zoonetsa kuti sanasinthe colinga cake ca poyamba.
Timasangalala kuona m’maganizo mwathu zinthu zimene tifuna kudzacita m’dziko latsopano (Onani ndime 7)c
COLINGA CA YEHOVA SICINASINTHE
8. Kodi Yesaya 55:11 imatitsimikizila ciyani za colinga ca Yehova pa anthu?
8 Ngakhale kuti Adamu na Hava anacimwa, komanso kubweletsa imfa kwa ana awo, Yehova sanasinthe maganizo ake pa colinga cake. (Ŵelengani Yesaya 55:11.) Colinga cake cikali cakuti anthu okhulupilika adzakhale na moyo kwamuyaya. Timadziŵa izi cifukwa ca zimene anakamba na kucita kuti akwanilitse colinga cakeco.
9. Kodi Mulungu analonjeza ciyani? (Danieli 12:2, 13)
9 Yehova analonjeza kuti adzaukitsa akufa, na kuwapatsa mwayi wodzakhala na moyo kwamuyaya. (Mac. 24:15; Tito 1:1, 2) Munthu wokhulupilika Yobu anali wotsimikiza kuti Yehova ni wofunitsitsa kuukitsa akufa. (Yobu 14:14, 15) Nayenso mneneli Danieli anali kudziŵa kuti anthu ali na ciyembekezo codzaukitsidwa n’kupatsidwa mwayi wodzakhala na moyo kwamuyaya. (Sal. 37:29; ŵelengani Danieli 12:2, 13.) Cinanso, Ayuda m’nthawi ya Yesu anali kudziŵa kuti Yehova adzapatsa atumiki ake okhulupilika “moyo wosatha.” (Luka 10:25; 18:18) Yesu anakamba za lonjezo limeneli mobweleza-bweleza, ndipo iye mwini anaukitsidwa na Atate ŵake.—Mat. 19:29; 22:31, 32; Luka 18:30; Yoh. 11:25.
Kodi ciukitso cimene Eliya anacita cimakutsimikizilani za ciyani? (Onani ndime 10)
10. Kodi ziukitso zakumbuyoku zionetsa ciyani? (Onani cithunzi.)
10 Yehova ni Mpatsi wa moyo, ndipo ali na mphamvu zoukitsa akufa. Iye anapatsa mphamvu mneneli Eliya zoukitsa mwana wa mkazi wamasiye wa ku Zarefati. (1 Maf. 17:21-23) Patapita nthawi, mothandizidwa na Mulungu, mneneli Elisa anaukitsa mwana wa mzimayi wina wacisunemu. (2 Maf. 4:18-20, 34-37) Ziukitso zimenezi komanso zina, zionetsa kuti Yehova ali na mphamvu zoukitsa anthu akufa. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anaonetsa kuti Atate wake anam’patsa mphamvu zimenezi. (Yoh. 11:23-25, 43, 44) Yesu lomba ali kumwamba, ndipo anapatsidwa “ulamulilo wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” Conco, iye adzakwanilitsa lonjezo lakuti “onse ali m’manda acikumbutso” aukitsidwe ali na ciyembekezo cokhala na moyo kwamuyaya.—Mat. 28:18; Yoh. 5:25-29.
11. Kodi dipo linapangitsa bwanji kuti zikhale zotheka kukalandila moyo wamuyaya?
11 N’cifukwa ciyani Yehova analola Mwana mwake wokondeka kufa imfa yoŵaŵa? Yesu anafotokoza cifukwa cake pamene anati: “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Popeleka Mwana wake dipo lotiwombola ku macimo athu, Mulungu anapangitsa kuti zikhale zotheka kukalandila moyo wosatha. (Mat. 20:28) Pofotokoza mbali yofunika yokhudza colinga ca Mulungu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Popeza imfa inafika kudzela mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzela mwa munthu mmodzi. Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.”—1 Akor. 15:21, 22.
12. Kodi Ufumu wa Mesiya udzakwanilitsa bwanji colinga ca Yehova pa anthu?
12 Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kupemphelela Ufumu wa Mulungu kuti ubwele, komanso kuti cifunilo ca Mulungu cicitike padziko lapansi. (Mat. 6:9, 10) Cimodzi mwa zolinga za Mulungu n’cakuti anthu akakhale na moyo kwamuyaya padziko lapansi. Kuti akwanilitse colinga cake cimeneci, Yehova anaika Mwana wake kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. Ndipo Mulungu wakhala akusonkhanitsa anthu okwana 144,000 padziko lapansi, amene adzagwila nchito pamodzi na Yesu pokwanilitsa colinga cake.—Chiv. 5:9, 10.
13. Kodi palipano Yehova akucita ciyani? Nanga ifeyo tiyenela kucita ciyani?
13 Yehova palipano akusonkhanitsa a “khamu lalikulu” la anthu, na kuwaphunzitsa kukhala nzika za Ufumu wake. (Chiv. 7:9, 10; Yak. 2:8) Ngakhale kuti anthu ambili m’dzikoli ni ogaŵikana cifukwa ca cidani komanso nkhondo, a khamu lalikulu amayesetsa kucotsa maganizo alionse a cidani mu mtima mwawo. Iwo mophiphilitsa anayamba kale kusula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo. (Mika 4:3) M’malo mocita nawo nkhondo zimene zimapha anthu ambili, iwo amathandiza anthu kupeza “moyo weniweniwo” mwa kuwaphunzitsa za Mulungu woona, komanso colinga cake. (1 Tim. 6:19) Iwo angamatsutsidwe na acibale awo kapena angasoŵe ndalama cifukwa cokhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu. Koma Yehova amaonetsetsa kuti akuwapatsa zonse zofunikila pa umoyo wawo. (Mat. 6:25, 30-33; Luka 18:29, 30) Mfundo zonsezi zimatitsimikizila kuti Ufumu wa Mulungu ni weniweni, komanso kuti udzapitiliza kukwanilitsa colinga ca Yehova.
MOYO WABWINO KOPOSA M’TSOGOLO
14-15. Kodi lonjezo la Yehova lakuti adzacotsapo imfa kwamuyaya lidzakwanilitsidwa bwanji?
14 Pano tikamba, Yesu ali kumwamba, ndipo adzakwanilitsa malonjezo onse a Yehova. (2 Akor. 1:20) Ciyambile 1914, Yesu wakhala akugonjetsa adani ake. (Sal. 110:1, 2) Posacedwa, iye pamodzi na olamulila anzake adzapambana, ndipo adzawononga anthu oipa.—Chiv. 6:2.
15 Mu Ulamulilo wa Yesu wa Zaka 1,000, akufa adzaukitsidwa, ndipo anthu omvela adzakhala angwilo. Pambuyo pa mayeso omaliza, anthu amene Yehova adzawaweluze kuti ni olungama “adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:10, 11, 29) Cokondweletsa kwambili, imfa “mdani womalizila, idzawonongedwa.”—1 Akor. 15:26.
16. Kodi cifukwa cacikulu com’tumikila Yehova ciyenela kukhala ciyani?
16 Monga taonela, ciyembekezo cathu codzakhala na moyo kwamuyaya n’cozikika kwambili m’Mawu a Mulungu. Ciyembekezo cimeneci cingatithandize kukhalabe okhulupilika m’masiku otsiliza ano ovuta kucita nawo. Koma kuti tim’kondweletse Yehova, sitiyenela kukhala cabe na cifuno codzakhala na moyo kwamuyaya. Cifukwa cacikulu cokhalilabe okhulupilika kwa Yehova na Yesu, n’cakuti timawakonda ngako. (2 Akor. 5:14, 15) Cikondico cimatilimbikitsa kutengela citsanzo cawo, na kuuzako ena za ciyembekezo cathu. (Aroma 10:13-15) Ndipo tikamaphunzila kukhala anthu osadzikonda komanso owoloŵa manja, timakhala mtundu wa anthu amene Yehova amafuna kukhala mabwenzi ake kwamuyaya.—Aheb. 13:16.
17. Kodi aliyense pacake ali na udindo wanji? (Mateyu 7:13, 14)
17 Kodi tidzakhala pa gulu la anthu amene adzalandila moyo wosatha? Yehova anatitsegulila khomo limeneli. Cili kwa ife tsopano kuyendabe pamsewu umenewo kapena ayi. (Ŵelengani Mateyu 7:13, 14.) Kodi zinthu zidzakhala bwanji tikadzakhala na moyo kwamuyaya? Funso limeneli tidzaliyankha m’nkhani yotsatila.
NYIMBO 141 Moyo ni Cozizwitsa
a Kodi mukuyembekezela kudzakhala na moyo kwamuyaya? Yehova anatilonjeza kuti m’tsogolo tidzakhala na moyo popanda kudelanso nkhawa kuti tsiku lina tidzafa. M’nkhani ino, tikambilane zifukwa zimene tingakhalile na cidalilo conse kuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake.
b Onani bokosi lakuti, “Tanthauzo la Mawu Akuti ‘Mpaka Muyaya’ m’Baibo.”
c MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wokalamba akuona m’maganizo mwake zina mwa zinthu zimene adzacite m’dziko latsopano.