NKHANI YOPUNZILA 46
Yehova Akutitsimikizila za Lonjezo la Paradaiso-Motani?
“Aliyense wofuna kudalitsidwa padziko lapansi adzadalitsidwa ndi Mulungu wokhulupilika.”—YES. 65:16.
NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu
ZIMENE TIKAMBILANEa
1. Kodi uthenga wa mneneli Yesaya kwa Aisiraeli anzake unali wotani?
MNENELI Yesaya ananena kuti Yehova ni “Mulungu wokhulupilika.” Liwu lomasulidwa kuti “wokhulupilika” limatanthauza kuti ‘ameni.’ (Yes. 65:16) Liwu lakuti ‘Ameni’ limatanthauza kuti “zikhale mmenemo,” kapena “ndithudi.” Mawu akuti ‘ameni’ akagwilitsidwa nchito m’Baibo ponena za Yehova kapena Yesu, amatsimikizila kuti zinthu zina zake ni zenizeni. Conco, uthenga wa Yesaya kwa Aisiraeli anzake unali womveka bwino. Uthengawo unali wakuti, zilizonse zimene Yehova walosela, zimadzacitikadi. Yehova watsimikizila mfundo imeneyi mwa kukwanilitsa malonjezo ake onse.
2. N’cifukwa ciyani tiyenela kudalila malonjezo a Yehova onena za tsogolo lathu? Kodi tikambilane mafunso ati?
2 Kodi tingakhalenso otsimikiza kuti malonjezo a Yehova onena za tsogolo lathu adzakwanilitsikadi? Patapita zaka 800 kucokela m’nthawi ya Yesaya, mtumwi Paulo anafotokoza cifukwa cake malonjezo a Yehova nthawi zonse amakhala odalilika. Iye anati: “N’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Aheb. 6:18) Monga mmene kasupe wa madzi sangatulutse madzi abwino komanso oipa panthawi imodzi, nayenso Yehova amene ni Kasupe wa coonadi, sanganene mabodza. Conco, tingakhale na cidalilo conse kuti zonse zimene Yehova amanena, kuphatikizapo malonjezo ake okhudza tsogolo lathu, zidzakwanilitsidwa. M’nkhani ino tikambilane mafunso otsatilawa: Kodi Yehova walonjeza kuti adzaticitila ciyani m’tsogolo? Kodi wapeleka citsimikizo cotani coonetsa kuti malonjezo ake onse adzakwanilitsidwa?
KODI YEHOVA WATILONJEZA CIYANI?
3. (a) Ni lonjezo liti la mtengo wapatali kwa atumiki a Mulungu? (Chivumbulutso 21:3, 4) (b) Kodi ena amayankha bwanji tikaŵauzako za lonjezo limeneli?
3 Lonjezo limene tikambilane ni lamtengo wapatali kwa atumiki a Mulungu kuzungulila dziko lonse lapansi. (Ŵelengani Chivumbulutso 21:3, 4.) Yehova akutilonjeza nthawi pamene “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” Ambili a ife timaseŵenzetsa lonjezo la m’Baibo logwila mtima limeneli pamene tikulalikila ena, powafotokozela mmene umoyo udzakhalile m’Paradaiso. Kodi anthu ena amayankha bwanji tikaŵauzako za lonjezo limeneli? Ena amanena kuti, “Malonjezowa akumveka bwino ngako, koma nikaikila ngati angacitikedi.”
4. (a) Kodi Yehova anaonelatu ciyani zokhudza lonjezo lake la Paradaiso? (b) Kuwonjezela pa kupanga lonjezo, kodi Yehova anacitanso ciyani?
4 Pamene Yehova anauzila mtumwi Yohane kulemba lonjezo lokhudza umoyo m’Paradaiso, anadziŵa kuti masiku ano tiziuzako ena za lonjezo limeneli polalikila. Yehova anadziŵanso kuti zidzakhala zovuta kwa anthu ambili kukhulupilila lonjezo la “zinthu zatsopano” zimenezi. (Yes. 42:9; 60:2; 2 Akor. 4:3, 4) Ndiye kodi tingakhale bwanji otsimikiza—na kutsimikizilanso anthu ena—kuti madalitso ochulidwa pa Chivumbulutso 21:3, 4 adzabweladi? Yehova sanangotipatsa lonjezo labwino limeneli, anatipatsanso zifukwa zomveka zolikhulupilila. Kodi anatipatsa zifukwa ziti?
MMENE YEHOVA AMATSIMIKIZILA MALONJEZO AKE
5. Tili na zifukwa ziti zokhulupilila lonjezo la Mulungu la Paradaiso? Ndipo zifukwazo timazipeza pati?
5 Zifukwa zodalila lonjezo la Yehova la Paradaiso timazipeza m’mavesi 5 na 6. Pamenepo timaŵelenga kuti: “Ndipo wokhala pampando wacifumu anati: ‘Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.’ Ananenanso kuti: ‘Lemba, pakuti mawu awa ndi odalilika ndi oona.’ Anandiuzanso kuti: ‘Zakwanilitsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega, ciyambi ndi mapeto.’”—Chiv. 21:5, 6a.
6. N’cifukwa ciyani citsimikizo copezeka pa Chivumbulutso 21:5, 6 cimalimbitsa cidalilo cathu pa lonjezo a Mulungu?
6 N’cifukwa ciyani mavesiwa amalimbikitsa cidalilo cathu mu lonjezo la Mulungu? Ponena za mavesi amenewa buku la Mapeto a Chivumbulutso limati: “Zimenezi zili ngati kuti Yehova akusainila yekha cikalata cotsimikizila kuti anthu okhulupilika adzalandila madalitso am’tsogolo.”b Lonjezo la Mulungu limapezeka pa Chivumbulutso 21:3, 4. Koma mu vesi 5 na 6, timapezamo sigineca ya Yehova, titelo kunena kwake, lotitsimikizila kuti lonjezo limeneli lidzakwanilitsidwa. Tiyeni tikambilane mofatsa bwino mawu amene Yehova anagwilitsa nchito potitsimikizila.
7. Kodi mawu oyamba a citsimikizo ca Mulungu anakambidwa na ndani? Ndipo n’cifukwa ciyani n’kofunika kudziŵa zimenezi?
7 Mulungu potitsimikizila anayamba na mawu akuti: “Ndipo wokhala pampando wacifumu anati.” (Chiv. 21:5a) Aka kanali koyamba pa maulendo atatu pamene Yehova iye mwini analankhula m’masomphenya m’buku la Chivumbulutso. Citsimikizo cimeneci, cinapelekedwa na Yehova mwini wakeyo, osati na mngelo wamphamvu winawake, kapena Yesu woukitsidwayo ayi! Zimenezi zionetsa kudalilika kwa mawu otsatilapo. N’cifukwa ciyani? Cifukwa Yehova “sanganame.” (Tito 1:2) Mawu amenewo atitsimikizila kuti zimene timaŵelenga pa Chivumbulutso 21:5, 6 n’zodalilikadi.
“TAONANI! ZINTHU ZONSE ZIMENE NDIKUPANGA N’ZATSOPANO”
8. Kodi Yehova anatitsimikizila bwanji kuti adzakwanilitsa lonjezo lake? (Yesaya 46:10)
8 Cotsatila, tiyeni tikambilane liwu lakuti “Taonani!” (Chiv. 21:5) Liwu la Cigiriki limene anamasulila kuti “taonani!” analiseŵenzetsa mobweleza-bweleza m’buku la Chivumbulutso. Buku lina linanena kuti liwu la mfuulilo limeneli analigwilitsa nchito “pofuna kukopela cidwi omvetsela ku mawu otsatilapo.” Kodi Mulungu ananena ciyani pambuyo pa mfuulilo umenewu? Iye anati: “Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” N’zoona kuti Yehova anali kunena za masinthidwe a m’tsogolo, koma iye anali wotsimikiza kuti zidzacitikadi, moti ananena ngati zikucitika.—Ŵelengani Yesaya 46:10.
9. (a) Kodi mawu akuti “zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano” akusonya ku zinthu ziŵili ziti zimene Yehova adzacita? (b) N’ciyani cidzacitikile “kumwamba” kumene kulipo komanso “dziko lapansi”?
9 Lomba tiyeni tikambilane mawu otsatila, opezeka pa Chivumbulutso 21:5 akuti: “Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” M’caputala ici ca m’Baibo, mawuwa akuloza ku zinthu ziŵili zimene Yehova adzacita—kucotsapo zinthu zakale na kubweletsapo zatsopano. Coyamba, kodi Yehova adzacotsa zinthu ziti? Pa Chivumbulutso 21:1 timaŵelenga kuti: “Kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitacoka.” “Kumwamba kwakale” kuimila maboma andale omwe ali pansi pa ulamulilo wa Satana na ziŵanda zake. (Mat. 4:8, 9; 1 Yoh. 5:19) Monga imaonetsela Baibo, mawu akuti “dziko lapansi” angatanthauze anthu okhala pa dziko lapansi. (Gen. 11:1; Sal. 96:1) Conco, “dziko lapansi lakale” limatanthauza anthu oipa omwe alipo masiku ano. Sikuti Yehova adzangokonzanso “kumwamba” na “dziko lapansi” ayi; koma adzazicotselatu na kubweletsapo zatsopano. Adzalenga “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano”—kutanthauza boma latsopano lolamulila anthu olungama.
10. Kodi Yehova adzapanga zinthu ziti kukhala zatsopano?
10 Cotsatila mfuulilo wa pa Chivumbulutso 21:5 (NWT-E), timaŵelenga za zinthu zimene Yehova adzapanga kukhala zatsopano. Yehova sananene kuti, “Ndikupanga zinthu zonse zatsopano.” M’malo mwake anati: “Ndikupanga zinthu zonse kukhala zatsopano.” Conco, Yehova adzapanga dziko kukhala latsopano komanso anthu mwa kubwezeletsa ungwilo. Monga Yesaya ananenela, Yehova adzapanga dziko lonse lapansi kukhala Paradaiso wokongola. Ifenso tidzapangidwa kukhala atsopano, aliyense payekha-payekha. Anthu aulemali, osakhoza kuona kapena kumva adzacilitsidwa. Ngakhale akufa adzaukitsidwa.—Yes. 25:8; 35:1-7.
“MAWU AWA NDI ODALILIKA NDI OONA . . . . ZAKWANILITSIDWA!”
11. Kodi Yehova analamula Yohane kucita ciyani? Ndipo n’cifukwa ciyani?
11 N’ciyaninso cimene Yehova ananena m’citsimikizo cake? Iye anauza Yohane kuti: “Lemba, pakuti mawu awa ndi odalilika ndi oona.” (Chiv. 21:5) Yehova sanagomulamula kuti “alembe.” Anam’patsanso cifukwa ponena kuti: “Pakuti mawu awa ndi odalilika ndi oona.” Ndife oyamikila kuti Yohane anamvela lamulo lakuti “lemba.” Mwa ici, timaŵelenga za lonjezo la Mulungu la Paradaiso komanso kusinkhasinkha madalitso amene tikuwayembekezela.
12. N’cifukwa ciyani m’pake kuti Yehova anati: “Zakwanilitsidwa!”
12 N’ciyani cotsatila cimene Mulungu ananena? Anati, “zakwanilitsidwa!” (Chiv. 21:6) Apa, Yehova akunena ngati kuti zinthu zonse zokhudza lonjezo la Paradaiso zacitika kale. Ndipo m’pake kutelo cifukwa palibe ciliconse cingamulepheletse kukwanilitsa colinga cake. Yehova akutipatsanso mbali ina yofunika kwambili ya citsimikizo cake. Kodi anati ciyani?
“INE NDINE ALEFA NDI OMEGA”
13. N’cifukwa ciyani Yehova ananena kuti “Ine ndine Alefa ndi Omega”?
13 Monga tafotokozela kale, Yehova iye mwini analakhula maulendo atatu m’masomphenya kwa Yohane. (Chiv. 1:8; 21:5, 6; 22:13) Pa maulendo onse atatu, Yehova akuchula ciganizo cimodzimodzi cakuti: “Ine ndine Alefa ndi Omega.” Cilembo ca Alefa n’coyamba mu alifabeti ya Cigiliki, pamene cilembo ca Omega n’cothela. Podzifotokoza kuti iye ni “Alefa komanso Omega,” Yehova akumveketsa mfundo yakuti akayamba kucita cinacake amapitilizabe mpaka atacimalizitsa.
Yehova akayamba kucita cinacake amacipitiliza mpaka atacikwanilitsa (Onani ndime 14, 17)
14. (a) Pelekani citsanzo coonetsa pamene Yehova ananena kuti “Alefa” komanso nthawi imene adzanena kuti “Omega.” (b) Kodi pa Genesis 2:1-3 timapezapo citsimikizo cotani?
14 Yehova atalenga Adamu na Hava, anafotokoza za colinga cake ca poyamba cokhudza mtundu wa anthu komanso dziko lapansi. Baibo imati, “Mulungu anawadalitsa n’kuwauza kuti: ‘Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile.’” (Gen. 1:28) Pa nthawi imeneyo, zinali ngati Yehova akunena kuti “Alefa.” Anafotokoza colinga cake momveka bwino. Nthawi inali kudzafika pamene ana angwilo komanso omvela a Adamu na Hava anali kudzadzaza dziko lapansi na kulisandutsa kukhala Paradaiso. Pa nthawi yam’tsogolo imeneyo, tinganene kuti Yehova adzati “Omega.” Atamaliza kulenga “kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse za mmenemo,” Yehova anapeleka citsimikizo cimene cipezeka pa lemba la Genesis 2:1-3. (Ŵelengani.) Yehova anapatula tsiku la 7 kukhala lopatulika kwa iye. Kodi izi zitanthauza ciyani? Yehova anatsimikizila kuti adzakwanilitsa colinga cake kwa mtundu wa anthu komanso dziko lapansi. Colinga cake cinali kudzakwanilitsidwa kumapeto kwa tsiku la 7.
15. N’cifukwa ciyani zinaoneka ngati Satana walepheletsa colinga ca Mulungu pa mtundu wa anthu?
15 Adamu na Hava atapanduka, anakhala ocimwa, ndipo anapatsila ucimo na imfa kwa ana awo. (Aroma 5:12) Conco, zinaoneka ngati kuti Satana wakwanitsa kulepheletsa colinga ca Mulungu codzaza dziko lapansi na anthu angwilo komanso omvela. Zinaoneka ngati kuti Satana walepheletsa Yehova kunena kuti “Omega.” Mwina Satana anaganiza kuti Yehova wasoŵelatu cocita. Iye anaganiza kuti Mulungu adzangowononga Adamu na Hava na kulenganso banja lina latsopano kuti akwanilitse colinga cake. Koma Mulungu akanacita zimenezo, Mdyelekezi akanakamba kuti ni wabodza. Cifukwa ciyani? Zili conco cifukwa malinga na Genesis 1:28, Yehova anali atauza Adamu na Hava kuti ana awo azadzaza dziko lonse lapansi.
16. N’ciyani cikanapangitsa Satana kuganiza kuti Mulungu ni wolephela?
16 Ni njila ina iti imene Satana ayenela kuti anaganizila kuti Mulungu angaseŵenzetsa pokwanilitsa colinga cake? Mwina Satana anaganiza kuti Yehova adzalola Adamu na Hava kukhala na ana omwe sizinali zotheka kukhala angwilo. (Mlal. 7:20; Aroma 3:23) Zikanakhala telo, mosakaikila Mdyelekezi akanati Yehova ni wolephela. Cifukwa ciyani? Cifukwa njila imeneyi siikanakwanilitsa colinga ca Mulungu, cakuti dziko lapansi la Paradaiso lidzaze na ana angwilo komanso omvela a Adamu na Hava.
17. Kodi Yehova anathetsa bwanji cipanduko ca Satana komanso anthu oyambilila? Nanga mapeto ake adzakhala otani? (Onaninso cithunzi.)
17 Yehova anathetsa cipanduko ca Satana na anthu oyambilila m’njila imene inasoŵetsa Satana conena. (Sal. 92:5) M’malo mokhala wabodza, Yehova anaonetsa kuti ni wokhulupilika polola Adamu na Hava kukhala na ana. Ndipo m’malo mokhala wolephela, Yehova anaonetsa kuti ni wopambana. Anaonetsetsa kuti colinga cake cikupita patsogolo popeleka “mbewu” imene inali kudzapulumutsa ana omvela a Adamu na Hava. (Gen. 3:15; 22:18) Satana ayenela kuti anasoŵa conena cifukwa ca makonzedwe a Yehova a dipo. Cifukwa ciyani? Cifukwa ni makonzedwe ozikika pa cikondi copanda dyela. (Mat. 20:28; Yoh. 3:16) Satana alibe khalidwe limeneli cifukwa ni wodzikonda. Ndiye, n’ciyani cidzacitike cifukwa ca makonzedwe a dipo amenewa? Kumapeto kwa zaka 1000, mbadwa za Adamu na Hava zomwe zidzakhale zomvela, komanso zangwilo zidzakhala m’paradaiso padziko lapansi—mmene Yehova anafunila paciyambi. Zikadzatelo, zidzakhala ngati Yehova wanena kuti, “Omega.”
MMENE TINGALIMBIKITSILE CIDALILO CATHU MWA YEHOVA PA LONJEZO LAKE LA PARADAISO
18. Kodi ni zitsimikizo zitatu ziti zimene Yehova watipatsa? (Onaninso danga lakuti “Zifukwa Zitatu Zodalila Malonjezo a Yehova.”)
18 Malinga n’zimene takambitsilana, kodi ni zitsimikizo ziti zimene tingauzeko aja amene amakaikila zakuti lonjezo la Mulungu la Paradaiso lidzakwanilitsidwa? Coyamba, Yehova iye mwini ndiye anapeleka lonjezolo. Buku la Chivumbulutso limati: “Wokhala pampando wacifumu anati: ‘Taonani! Ndikupanga zinthu zonse kukhala zatsopano.’” Iye ali na nzelu, mphamvu, komanso cifuno cokwanilitsa lonjezo lake limeneli. Caciŵili, kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli ni kodalilika, moti malinga na kaonedwe ka Yehova, kwa iye zili ngati zakwanilitsika kale. Ndiye cifukwa cake anati: “Mawu awa ndi odalilika ndi oona. . . . Zakwanilitsidwa!” Cacitatu, Yehova akayamba kucita cina cake, amacicitabe mpaka atacikwanilitsa, ndiye cifukwa cake anati: “Ine ndine Alefa ndi Omega.” Yehova adzaonetsa poyela kuti Satana ni wabodza komanso wolephela.
19. Mungacite ciyani ngati anthu akukaikila za lonjezo la Mulungu la Paradaiso?
19 Kumbukilani kuti, nthawi zonse mukamauzako ena za citsimikizo ca Mulungu mu utumiki, mumalimbikitsa cidalilo canu m’malonjezo a Yehova. Kodi mudzacita ciyani ulendo wina mukadzaŵelengela munthu wina lonjezo la Paradaiso la pa Chivumbulutso 21:4, koma munthuyo n’kunena kuti, “N’zosatheka kucitika”? Mungaŵelenge na kumufotokozela vesi 5 na 6. Muonetseni mmene Yehova watsimikizila lonjezo lake limeneli mwa kulisainila iye mwini, titelo kunena kwake.—Yes. 65:16.
NYIMBO 145 Mulungu Analonjeza Paradaiso
a M’nkhani ino tiona citsimikizo cimene Yehova wapeleka cakuti adzakwanilitsadi lonjezo lake la Paradaiso. Nthawi zonse tikamauzako ena za citsimikizo cimeneci timalimbikitsanso cidalilo cathu pa malonjezo a Yehova.