ZIMENE MUNGACITE PA PHUNZILO LA INU MWINI
Anthu Auzimu Amapanga Zisankho Zanzelu
Ŵelengani Genesis 25:29-34 kuti muone ngati Esau na Yakobo anapanga zisankho zanzelu.
Kumbani mozamilapo kuti mumvetse nkhani yonse. Kodi zinthu zinali bwanji izi zisanacitike? (Gen. 25:20-28) Nanga n’ciyani cinacitika pambuyo pake?—Gen. 27:1-46.
Kumbani mozamilapo kuti mumvetse mmene zinthu zinali kucitikila pa nthawiyo. Ni mwayi wapadela uti, komanso ni maudindo ati amene mwana woyamba kubadwa anali kukhala nawo?—Gen. 18:18, 19; w10 5/1 13.
Kodi munthu anayenela kukhala woyamba kubadwa kuti akhale mu mzele wobadwila Mesiya? (w17.12 14-15)
Pezani maphunzilo amene alipo na kuwaseŵenzetsa. N’cifukwa ciyani Yakobo anaona mwayi wokhala woyamba kubadwa kuti ni wamtengo wapatali kuposa mmene Esau anauonela? (Aheb. 12:16, 17; w03 10/15 28-29) Kodi Yehova anali kuwaona bwanji anthu aŵili a pacibale amenewa? Ndipo n’cifukwa ciyani? (Mal. 1:2, 3) Kodi Esau akanawongolela pati kuti apange zisankho zanzelu?
Dzifunseni kuti, ‘Kodi ningaonetse bwanji kuti nimayamikila zinthu zauzimu m’zocita zanga mlungu uliwonse?’ Mwa citsanzo, ‘kodi nimapatula tsiku komanso nthawi yokwanila yocita kulambila kwa pabanja?’