LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 June masa. 14-18
  • Yehova Anamva Mapemphelo Anga

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Anamva Mapemphelo Anga
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ALENDO AMENE ANASINTHA UMOYO WATHU
  • MMENE UMOYO UNALILI PA NTHAWI YA NKHONDO
  • KUKULA KUUZIMU
  • UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE
  • KUTETEZA UFULU WATHU WA KULAMBILA
  • UFULU WA KULAMBILA UPELEKEDWA KU CUBA
  • KUTHANDIZA ABALE ATHU KU RWANDA
  • KUFUNITSITSA KUKHALABE WOKHULUPILIKA
  • Nakhala Nikusangalala Kuphunzila za Yehova na Kuphunzitsako Ena
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 June masa. 14-18
M’bale Marcel Gillet ali mu ofesi yake pa Beteli ya ku Belgium.

MBILI YANGA

Yehova Anamva Mapemphelo Anga

WOSIMBA NI: MARCEL GILLET

USIKU wina n’nayang’ana kumwamba na kuona nyenyezi zowala bwino. Nthawi yomweyo n’nagwada pansi na kuyamba kupemphela, apo n’kuti nili na zaka 10. N’nali n’tangophunzila za Yehova, koma n’namukhutulila nkhawa zanga zonse. Pemphelo limenelo linali ciyambi ca ubwenzi wanga na Yehova, Mulungu “wakumva pemphelo.” (Sal. 65:2) Lekani nikufotokozeleni cifukwa cake n’napemphela kwa Mulungu amene n’nali n’tangomudziŵa kumene.

ALENDO AMENE ANASINTHA UMOYO WATHU

N’nabadwa pa December 22, 1929, m’mudzi waung’ono wa Noville. Mudziwo unali na mafamu 9, ndipo unali pafupi na tauni ya Bastogne, mu nkhalango yochedwa Belgian Ardennes. Nikumbukila zinthu zambili zosangalatsa zimene n’nali kucita nili mwana pamodzi na makolo anga pa famu yathu. Ine na mng’ono wanga Raymond, tinali kusenga mkaka wa ng’ombe zathu tsiku lililonse, ndiponso tinali kuthandizila pa nchito zaulimi. Tinali ogwilizana m’mudzi wathu waung’ono, ndipo tinali kuthandizana wina na mnzake.

Ine na banja lathu tikuseŵenza pa famu

Makolo athu, atate a Emile komanso amayi a Alice, anali Akatolika odzipeleka. Anali kupita ku Misa Sondo iliyonse. Komabe, ca m’ma 1939, apainiya ocokela ku England anabwela m’mudzi mwathu ndipo anapatsako atate magazini ochedwa Consolation (amene tsopano timati Galamuka!). Nthawi yomweyo, atate anazindikila kuti apeza coonadi, ndipo anayamba kuŵelenga Baibo. Ataleka kucita Misa, maneba athu amene poyamba anali aubwenzi, anayamba kuwatsutsa mwamphamvu. Anali kuwakakamiza kuti asacokemo m’cipembedzo cacikatolika, ndipo izi zinapangitsa kuti ayambe kukangana kwambili.

Cinali kuniŵaŵa ngako kuona atate akuvutitsidwa mwanjila imeneyi. Izi n’zimene zinanisonkhezela kupempha thandizo kwa Mulungu, mwa kupeleka pemphelo locokela pansi pa mtima limene nachula kumayambililo kwa nkhani ino. N’nakondwela ngako maneba athu ataleka kuwatsutsa atate. N’natsimikiza kuti Yehova ni “wakumva pemphelo.”

MMENE UMOYO UNALILI PA NTHAWI YA NKHONDO

Cipani ca Nazi ku Germany cinaukila dziko la Belgium pa May 10, 1940. Izi zinapangitsa anthu ambili m’dzikolo kuthaŵila ku maiko ena. Banja lathu linathaŵila kum’mwela kwa dziko la France. Tili pa ulendowo, nthawi zina miyoyo yathu inali kukhala pa ciwopsezo, cifukwa mosadziŵa tinali kupezeka kuti tili pakati pa magulu a asilikali a Germany komanso a France akumenyana koopsa.

Titabwelela kumudzi kwathu, tinapeza kuti katundu wathu wambili anabedwa. Tinangopezako cabe galu wathu Bobbie. Zimenezi zinanipangitsa kudzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciyani padzikoli pali nkhondo na mavuto ambili-mbili?’

Marcel ali wacinyamata.

Nili wacinyamata ninalimbitsa ubale wanga na Yehova

Pa nthawi imeneyo tinalimbikitsidwa zedi pamene M’bale Emile Schrantz,a amene anali mkulu komanso mpainiya wokhulupilika, anaticezela. Iye anafotokoza momveka bwino poseŵenzetsa Baibo cifukwa cake timakumana na mavuto, ndipo anayankha mafunso ena amene n’nali nawo okhudza moyo. N’nakhala pa ubale wolimba na Yehova, ndipo n’nakhulupilila kuti iye ni Mulungu wacikondi.

Ngakhale nkhondo isanathe, banja lathu linapitilizabe kucitila zinthu pamodzi na Mboni. Mu August 1943, M’bale José-Nicolas Minet anabwela kumudzi kwathu kudzakamba nkhani. Anafunsa kuti, “Kodi n’ndani amene afuna kubatizika?” Ine na Atate, tinakweza manja. Ndipo tonse aŵili tinabatizika mu mtsinje waung’ono pafupi na famu yathu.

Mu December 1944 gulu la nkhondo la Germany linacita nkhondo yake yothela komanso yaikulu kumadzulo kwa Europe. Nkhondoyo imadziŵika kuti Nkhondo ya Bulge. Tinali kukhala kufupi na kumene nkhondoyo inali kucitikila, ndipo pafupi-fupi kwa mwezi wathunthu, tinali kubisala m’cipinda ca pansi ca nyumba yathu. Tsiku lina n’tatuluka panja kuti nikadyetsele ziŵeto, mabomba anaponyedwa m’famu yathu, ndipo anawononga mtenje wa khola lathu. Msilikali wa gulu lankhondo la America amene anali m’kholalo ananiuza mokuwa kuti, “Gona pansi!” N’nathamanga na kukagona pansi pafupi naye, ndipo ananiveka cisoti cake codzitetezela kuti aniteteze.

KUKULA KUUZIMU

Pa tsiku la ukwati wathu

Nkhondo itatha, tinakwanitsa kumasonkhana mokhazikika na mpingo wa mu mzinda wa Liège, womwe unali pa mtunda wa makilomita 90 ca kumpoto kwa mudzi wathu. M’kupita kwa nthawi, tinakwanitsa kuyambitsa kagulu kakang’ono ku Bastogne. N’nayamba nchito mu dipatimenti yokhometsa misonkho, ndipo n’nakhala na mwayi wocita maphunzilo a uloya. Pambuyo pake, n’nayamba kuseŵenzela ku khanso. Mu 1951 tinacita msonkhano wa dela waung’ono ku Bastogne. Pa msonkhanowo, panapezeka anthu pafupifupi 100, kuphatikizapo mlongo amenenso anali mpainiya wokangalika, dzina lake Elly Reuter. Anachova njinga pa mtunda wa makilomita 50 kuti apezekepo. Posakhalitsa, tinagwa m’cikondi, ndipo tinatomelana. Pa nthawiyo, Elly anali ataitanidwa kuti akaloŵe Sukulu ya Giliyadi ku America. Analembela ku likulu lathu na kuwafotokozela cifukwa cake anakana ciitano cimeneco. M’bale Knorr, amene anali kutsogolela anthu a Mulungu pa nthawiyo anayankha kalatayo mokoma mtima mwa kunena kuti mwina tsiku lina iwe na mwamuna wako mungakaloŵele pamodzi Sukulu ya Giliyadi. Tinakwatilana mu February 1953.

Mkazi wanga Elly, na mwana wathu Serge

M’caka cimeneco, ine na Elly tinapezeka pa msonkhano wa dela wa mutu wakuti, Anthu a m’Dziko Latsopano, womwe unacitikila mu bwalo la Yankee Stadium, ku New York. Tili pa msonkhanowo, n’nakumana na m’bale wina amene ananipatsa mwayi wa nchito ya malipilo abwino, na kuniuza kuti tisamukile ku America. Pambuyo poipemphelela nkhaniyo, ine na mkazi wanga tinakana mwayi umenewo, ndipo tinabwelela ku Belgium kuti tikathandizile kagulu kakang’ono ka ofalitsa 10 ku Bastogne. Caka cotsatila, tinadalitsidwa na mwana wa mwamuna dzina lake Serge. N’zomvetsa cisoni kuti patangopita miyezi 7, Serge anadwala ndipo anamwalila. Tinapemphela kwa Yehova, kum’fotokozela za cisoni cacikulu cimene tinali naco. Ndipo tinalimbikitsidwa na ciyembekezo cotsimikizika ca ciukitso.

UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE

Mu October 1961, n’napeza nchito ya masiku ocepa pa mlungu. Izi zinapangitsa kuti zikhale zotheka kuyamba upainiya. Komabe, pa tsiku lomwelo n’nalandila foni yocokela kwa mtumiki wa nthambi ya ku Belgium. Ananifunsa ngati ningakonde kuyamba kutumikila ngati mtumiki wa dela (amene masiku ano timati woyang’anila dela). N’namufunsa kuti, “Kodi sitingayambe tatumikilako monga apainiya tisanalandile utumikiwu?” Anavomela pempho langa. Titatumikila monga apainiya kwa miyezi 8, tinayamba utumiki wa m’dela mu September 1962.

Titatumikila mu dela kwa zaka ziŵili, tinaitanidwa kuti tikatumikile ku Beteli ya ku Brussels. Tinayamba kutumikila pa Beteli mu October 1964. Utumiki watsopanowu unatibweletsela madalitso ambili. Patapita masiku ocepa M’bale Knorr atayendela Ofesi yathu ya Nthambi mu 1965, n’nadabwa kuti n’naikidwa kukhala mtumiki wa nthambi. Patapita nthawi, ine na Elly tinaitanidwa kuti tikaloŵe Sukulu ya Giliyadi mu kalasi ya namba 41. Mawu amene M’bale Knorr anakamba zaka 13 m’mbuyomo, anakwanilitsika! Titamaliza maphunzilo a Giliyadi, tinabwelela ku Beteli ya ku Belgium.

KUTETEZA UFULU WATHU WA KULAMBILA

Kwa zaka zambili, n’nali na mwayi woseŵenzetsa maphunzilo anga a uloya pothandizila kuteteza ufulu wathu wa kulambila ku Europe na kumadela ena. (Afil. 1:7) Izi zinacititsa kuti nikumane na akulu-akulu a boma ambili m’maiko oposa 55 kumene nchito yathu inali yoletsedwa. M’malo mowauza kuti ndine katswili wa za malamulo, n’nali kuwauza kuti ndine “munthu wa Mulungu.” Nthawi zonse n’nali kudalila citsogozo ca Yehova podziŵa kuti “mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi mʼdzanja la Yehova. Amaupititsa kulikonse kumene iye akufuna.”—Miy. 21:1.

Cocitika cimodzi cimene sinidzaiŵala ni makambilano amene n’nakhala nawo na membala wina wa Nyumba ya Malamulo ku Europe. N’namupempha maulendo angapo kuti nikambilane naye, koma sanali kuvomela. Koma pothela pake anavomela. Ananiuza kuti, “Ningokupatsa mphindi 5 basi.” N’naŵelama na kuyamba kupemphela. Munthuyo ataona izi, mwamantha ananifunsa kuti, “Ukucita ciyani?” N’naŵelamutsa mutu na kumuuza kuti, “N’nali kuyamikila Mulungu cifukwa ndinu mmodzi wa atumiki ake.” Ananifunsa kuti, “Utanthauza ciyani?” N’namuŵelengela Aroma 13:4. Popeza kuti anali m’Pulotesitanti, vesiyi inam’cititsa cidwi. Zotsatila zake n’zakuti tinakambilana kwa mphindi 30, ndipo makambilano athu anayenda bwino. Anafika ngakhale ponena kuti amalemekeza nchito yathu.

Kwa zaka zambili, anthu a Yehova akhala akumenyela ufulu wawo ku Europe pa nkhani za kusatengako mbali m’zandale, ufulu wolela ana, kupeleka msonkho, na nkhani zina zotelo. Unali mwayi wapadela kwa ine kutengako mbali posamalila nkhani zimenezi, na kudzionela mmene Yehova anatithandizila kupambana. Mboni za Yehova zapambana milandu yoposa 140 m’Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya!

UFULU WA KULAMBILA UPELEKEDWA KU CUBA

Ca m’ma 1990 n’naseŵenzela pamodzi na M’bale Philip Brumley, wa ku likulu lathu, komanso M’bale Valter Farneti, wa ku Italy, kuti tithandize abale athu ku Cuba kukhala na ufulu wolambila Yehova, cifukwa nchito yathu inali yoletsedwa kumeneko. N’nalemba kalata ku ofesi ya kazembe wa ku Cuba m’dziko la Belgium, na kukumana na nduna ya boma imene inasankhidwa kuti isamalile pempho lathu. Pa kukumana kwathu koyamba sitinathe kuthetsa nkhani zimene zinacititsa kuti boma iletse nchito yathu kumeneko.

Ine na M’bale Philip Brumley komanso M’bale Valter Farneti pa umodzi wa maulendo amene tinakacezela dziko la Cuba ca m’ma 1990

Pambuyo popempha citsogozo ca Yehova, tinapempha cilolezo cakuti titumize ma Baibo 5,000 ku Cuba, ndipo anatilola. Ma Baibo amenewo anafika bwino-bwino ndipo anagaŵilidwa kwa abale na alongo. Izi zinatitsimikizila kuti Yehova akudalitsa khama lathu. Kenako tinapemphanso cilolezo cakuti titumize ma Baibo ena 27,500. Apanso tinaloledwa. Kuthandiza abale na alongo athu ku Cuba kuti akhale na Baibo kunanipatsa cimwemwe cacikulu.

N’napita ku Cuba maulendo ambili-mbili kukathandiza kumenyela ufulu abale athu pa nchito yolalikila. Maulendo amenewa anacititsa kuti nikhale pa ubwenzi wabwino na akulu-akulu a boma a kumeneko.

KUTHANDIZA ABALE ATHU KU RWANDA

Mu 1994 anthu opitilila 800,000 anaphedwa mwankhanza ku Rwanda pa nkhondo ya pa ciweniweni. N’zacisoni kuti ena mwa abale na alongo athu nawonso anaphedwa. Posakhalitsa kagulu ka abale kanapemphedwa kuti kakapeleke thandizo kwa abale na alongo m’dzikolo.

Gulu lathu litafika ku Kigali, womwe ni mzinda waukulu m’dzikolo, tinapeza kuti ofesi yomasulila mabuku, komanso mosungila mabuku zinali zitawonongeka na zipolopolo za mfuti. Tinamva nkhani zambili zomvetsa cisoni za abale na alongo amene anaphedwa mwankhanza na zikwanje. Koma tinamvanso nkhani zokhudza mmene abale na alongo anali kuonetselana cikondi ca Cikhristu. Mwa citsanzo, tinakumana na m’bale wa Citutsi amene anabisala m’dzenje kwa masiku 28, ndipo anali kusamalidwa na banja la Mboni la Cihutu. Pa miting’i imene tinakhala nayo ku Kigali, tinapeleka citonthozo cauzimu kwa abale na alongo opitilila 900.

Zithunzi: 1. Buku limene mbali yake ina ni yowonongeka. 2. M’bale Marcel ali na abale ena aŵili pomwe anali kupeleka thandizo pa nthawi ya tsoka.

Kumanzele: Buku lowombeledwa mfuti pa ofesi yathu yomasulila mabuku

Kenako, tinapita ku Zaire (yomwe tsopano imadziŵika kuti Democratic Republic of the Congo) kukafufuza Mboni za ku Rwanda zomwe zinathaŵila mu msasa wa othaŵa kwawo, pafupi na mzinda wa Goma. Koma sitinawapeze. Conco tinapemphela kwa Yehova kuti atitsogolele kwa iwo. Ndiyeno tinaona mwamuna wina akubwela kwa ife, ndipo tinamufunsa ngati anali kudziŵako wa Mboni za Yehova aliyense. Anayankha kuti, “Inde, inenso ndine Mboni. Ningakupelekezeni kumene kuli komiti yothandiza anthu pakagwa tsoka.” Pambuyo pocita miting’i yolimbikitsa na komiti imeneyo, tinakumana na anthu othaŵa kwawo okwana 1,600 kuti tiwatonthoze kuuzimu na kuwalimbikitsa. Tinaŵaŵelengelanso kalata yocokela ku Bungwe Lolamulila. Abale na alongo analimbikitsidwa ngako atamva mawu akuti: “Timakupemphelelani nthawi zonse. Tidziŵa kuti Yehova sadzakusiyani.” Mawu ocokela ku Bungwe Lolamulila amenewa analidi oona. Tsopano Mboni zopitilila 30,000 ku Rwanda zikutumikila Yehova pamodzi mosangalala!

KUFUNITSITSA KUKHALABE WOKHULUPILIKA

Pambuyo pokhala m’cikwati kwa zaka pafupifupi 58, mkazi wanga wokondeka Elly anamwalila mu 2011. N’nafotokozela Yehova m’pemphelo kukula kwa cisoni cimene n’nali naco, ndipo ananitonthoza. N’napezanso citonthozo polalikila ena uthenga wabwino wa Ufumu.

Ngakhale kuti nili na zaka za m’ma 90, nimatengako mbali m’nchito yolalikila mlungu uliwonse. Ndine wosangalala zedi kuti nimathandizila m’Dipatimenti Yoona za Malamulo pa ofesi ya nthambi ku Belgium. Nimakhalanso wosangalala kufotokozelako ena zimene nakumana nazo, komanso kucita maulendo aubusa kwa abale na alongo acinyamata pa ofesi ya nthambi.

Zaka 84 m’mbuyomo n’napeleka pemphelo langa loyamba kwa Yehova. Cinali ciyambi ca ulendo wosangalatsa umene wanithandiza kumuyandikila. Ndine wosangalala ngako kuti pa umoyo wanga wonse, Yehova wakhala akumvetsela mapemphelo anga.—Sal. 66:19.b

a Mbili ya M’bale Schrantz inafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1973, masamba 570-574.

b M’bale Marcel Gillet anamwalila pa February 4, 2023 pomwe nkhaniyi inali kulembedwa.

Kulamanja: Kugwila nchito yothandiza pakagwa tsoka

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani