LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 June tsa. 32
  • Kodi Muli na Cikhulupililo?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Muli na Cikhulupililo?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Nkhani Zofanana
  • Khalani na Cikhulupililo m’Malonjezo a Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Cikhulupililo Khalidwe Limene Limatithandiza Kukhala Olimba Mwauzimu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • “Tionjezeleni Cikhulupililo”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 June tsa. 32

MAWU A M’BAIBO

Kodi Muli na Cikhulupililo?

Kuti tikondweletse Yehova tiyenela kukhala na cikhulupililo. Koma Baibo imati “si anthu onse amene ali ndi cikhulupililo.” (2 Ates. 3:2) Ponena mawu amenewa, mtumwi Paulo anali kunena za “anthu oipa kwambili” amene anali kumuzunza, ndipo anali kufuna kuti apulumutsidwe kwa iwo. Koma mfundo imene anakamba pa nkhani ya cikhulupililo ingagwilenso nchito kwa anthu onse. Anthu ena amanyalanyaza umboni wosatsutsika wakuti kuli Mulungu amene ni Mlengi wa zinthu zonse. (Aroma 1:20) Anthu ena anganene kuti ali na cikhulupililo cifukwa amakhulupilila cinthu cina cake, kapena munthu wina wake wamphamvu zapadela. Koma ici si cikhulupililo ceniceni.

Sitiyenela kukayikila kuti Yehova alikodi, komanso kuti amapeleka mphoto kwa anthu amene ali na cikhulupililo colimba mwa iye. (Aheb. 11:6) Cikhulupililo ni cimodzi mwa zipatso zimene mzimu wake woyela umabala. Kupemphela kwa Yehova kungatithandize kuti tilandile mzimu woyela. (Luka 11:​9, 10, 13) Njila ina yapadela imene tingalandilile mzimu woyela ni kuŵelenga Mawu ake ouzilidwa. Ndiyeno tizisinkhasinkha zimene taŵelenga na kuzigwilitsa nchito. Tikatelo, mzimu wa Yehova udzatithandiza kukhala na cikhulupililo cimene cimam’kondweletsa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani