Malifalensi nga Nkhani za Unganu wa Umoyu Widu Ndipuso Uteŵeti
© 2022 Christian Congregation of Jehovah’s Witnesses
JANUARY 2-8
CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | 2 MAFUMU 22-23
“Ntchifukwa Wuli Tikhumbika Kuja Akujiyuyuwa?”
w00-CN 9/15 29-30
Yosiya Wodzichepetsayo Anayanjidwa Ndi Yehova
Kuchokera m’mamaŵa, okonza kachisi ameneŵa akugwira ntchito mwakhama. Ndithudi Yosiya akuthokoza Yehova kuti ogwira ntchito akukonza mbali za nyumba ya Mulungu zimene makolo ake ena oipa anawononga. Ntchito ili m’kati, Safani akubwera kudzamuuza zina zake. Nanga chimene wanyamulacho n’chiyani? Wanyamula mpukutu! Akufotokoza kuti Hilikiya Mkulu wa Ansembe wapeza “buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.” (2 Mbiri 34:12-18) Limene anapezalo mosakayikira linali buku lenileni la Chilamulo!
Yosiya akufunitsitsa kumva mawu onse a bukulo. Pamene Safani akuŵerenga, mfumuyo ikuyesetsa kuona mmene lamulo lililonse likugwirira ntchito kwa iye ndi kwa anthu ake. Makamaka akukondwera ndi mmene bukulo likufotokozera kwambiri za kulambira koona ndi kuneneratu za miliri ndi kuchotsedwa m’dziko zimene zingadze ngati anthu adziloŵetsa m’chipembedzo chonyenga. Podziŵa tsopano kuti malamulo ena a Mulungu sanatsatiridwe, Yosiya akung’amba chovala chake nalamula Hilikiya, Safani, ndi ena kuti: ‘Funsirani kwa Yehova za mawu a buku ili; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvera mawu a buku ili.’—2 Mafumu 22:11-13; 2 Mbiri 34:19-21.
w00-CN 9/15 30 ¶2
Yosiya Wodzichepetsayo Anayanjidwa Ndi Yehova
Amithenga a Yosiya apita kwa Hulida mneneri wamkazi ku Yerusalemu ndipo abwerako ndi mawu. Hulida wawauza mawu a Yehova, kunena kuti masoka amene analembedwa m’buku limene langopezedwa kumenelo adzagweradi mtundu wopandukawo. Komabe, chifukwa cha kudzichepetsa kwake pamaso pa Yehova Mulungu, Yosiya sadzaona masokawo. Adzam’sonkhanitsa kukhala ndi makolo ake ndipo adzatengedwa aloŵe m’manda mwake mwamtendere.—2 Mafumu 22:14-20; 2 Mbiri 34:22-28.
Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu
w01 4/15 26 ¶3-4
Mungachite Moyenera Ngakhale Sanakulereni Bwino
Ngakhale kuti panachitika zoipa panthaŵi ya ubwana wake, Yosiya anachita zoyenera pamaso pa Yehova. Ulamuliro wake unali wopambana ndipo Baibulo limati: “Asanabadwe iye panalibe mfumu [y]olingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu yake yonse, monga mwa chilamulo chonse cha Mose; atafa iyeyu sanaukanso wina wolingana naye.”—2 Mafumu 23:19-25.
Zimene Yosiya anachita n’chitsanzo cholimbikitsa kwa amene anakumana ndi zoipa paubwana wawo. Kodi chitsanzo chimenechi chingatiphunzitse chiyani? N’chiyani chinathandiza Yosiya kusankha njira yoyenera ndi kupitirizabe kuitsatira?
JANUARY 9-15
CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | 2 MAFUMU 24-25
“Muŵengi Masu Ndipu Muziŵengi Nyengu yo Tilimu”
w01-CN 2/15 12 ¶2
Tsiku la Yehova Lopereka Chiŵeruzo Layandikira!
Mosakayikira, kulosera kwa Zefaniya kunachititsa Yosiya wachinyamatayo kuzindikira kwambiri za kufunika kochotsa kulambira konyansa m’dziko la Yuda. Komabe, zimene mfumu inachita poyesetsa kufafaniza chipembedzo chonyenga m’dzikolo sizinathetse kuipa konse pakati pa anthuwo kapena kufafaniza machimo a agogo ake aamuna, Mfumu Manase, amene “anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosachimwa.” (2 Mafumu 24:3, 4; 2 Mbiri 34:3) Chotero, tsiku la Yehova lopereka chiŵeruzo linali kudzafika ndithu.
w07-CN 3/15 11 ¶10
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yeremiya
Chaka cha 607 B.C.E., chinali chaka cha 11 mu ulamuliro wa mfumu Zedekiya. Ndipo mfumu ya ku Babulo, Nebukadinezara inali itazinga Yerusalemu kwa miyezi 18 tsopano. Patsiku la 7 la mwezi wachisanu, m’chaka cha 19 cha ulamuliro wa Nebukadinezara, mkulu wa asilikali oteteza mfumu dzina lake Nebuzaradani, “anadza,” kapena kuti anafika ku Yerusalemu. (2 Mafumu 25:8) Mwina Nebuzaradani ankachokera ku misasa imene anamanga kunja kwa mpanda wa Yerusalemu, n’kumakazonda mzindawo kuti adziwe mmene angaugonjetsere. Patangopita masiku atatu okha, patsiku la khumi la mweziwu, Nebuzaradani “anadza,” kapena kuti analowa mu Yerusalemu, ndipo anatentha mzindawu ndi moto.—Yeremiya 52:12, 13.
Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu
w05 8/1 12 ¶1
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yeremiya
24:3, 4. Chifukwa choti Manase anali ndi mlandu wopha anthu, Yehova “sanafuna kukhululukira” Yuda. Mulungu amaona kuti mwazi wa anthu osalakwa n’ngofunika. Tisamakayikire m’pang’ono pomwe kuti Yehova adzabwezera anthu okhetsa mwazi wosalakwa powawononga.—Salimo 37:9-11; 145:20.
JANUARY 16-22
CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | 1 MBIRI 1-3
“Bayibolu ndi Buku lo Likamba Uneneska, Nthanu Cha”
w09-CN 9/1 14 ¶1
Kodi Adamu ndi Hava Anali Anthu Enieni?
Mwachitsanzo, onani ndandanda ya makolo achiyuda otchulidwa m’Baibulo m’buku la 1 Mbiri chaputala 1 mpaka 9, ndiponso Uthenga Wabwino wa Luka chaputala 3. Buku la 1 Mbiri limatchula mwatsatanetsatane makolo a mibadwo 48 ndipo Luka amatchula makolo a mibadwo 75. Buku la Luka limatchula m’badwo wa makolo a Yesu Khristu, pomwe buku la 1 Mbiri limatchula mibadwo ya ansembe a mtundu wa Isiraeli. Mabuku onsewa amatchula maina a anthu odziwika bwino monga Solomo, Davide, Yakobo, Isake, Abulahamu ndi Nowa ndipo pomalizira pake amatchula Adamu. Maina onse a m’mabuku amenewa ndi a anthu enieni, ndipo Adamu anali munthu weniweni pa m’ndandanda uliwonse.
w08-CN 6/1 3 ¶4
Chigumula cha Nowa Chinachitikadi Kapena Ndi Nthano?
Nkhani ziwiri za m’Baibulo zotchula mzera wobadwira wa anthu, zimasonyeza kuti Nowa anali munthu weniweni. (1 Mbiri 1:4; Luka 3:36) Ezara ndi Luka, amene analemba nkhani zimenezi anali anthu odziwa kufufuza bwino nkhani. Luka anafufuza ndi kupeza kuti Nowa anali m’gulu la makolo a Yesu Khristu.
w09-CN 9/1 14-15
Kodi Adamu ndi Hava Anali Anthu Enieni?
Mwachitsanzo, taonani nkhani ya m’Baibulo yokhudza dipo imene anthu ambiri opemphera amaona kuti ndi yofunika kwambiri. Mawu akuti dipo amatanthauza kuti Yesu Khristu anapereka moyo wake wangwiro monga nsembe yopulumutsa anthu ku uchimo. (Mat. 20:28; Yohane 3:16) Monga tikudziwira, dipo ndi mtengo wokwanira kuwombolera kapena kugulanso chinthu chomwe chinatayika kapena kuwonongedwa. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Yesu ndi ‘dipo lolingana.’ (1 Tim. 2:6) Koma tingafunse kuti, kodi ndi dipo lolingana ndi chiyani? Baibulo limayankha kuti: “Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akorinto 15:22) Moyo wangwiro umene Yesu anapereka kuti awombole anthu omvera unali wolingana ndi moyo wangwiro umene Adamu anataya pamene anachimwa m’munda wa Edene. (Aroma 5:12) Ndithudi, ngati Adamu sanali munthu weniweni, ndiye kuti nsembe ya dipo imene Khristu anapereka ikanakhala yopanda tanthauzo.
Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu
it-1 911 ¶3-4
Mkoka
Mazina nga Anthukazi. Nyengu zinyaki mazina nga anthukazi ngalembekanga mumabuku nga mkoka asani vo munthukazi yo wanguchita vakukhumbika ukongwa pa mbiri ya ŵanthu aku Chiuta. Sarayi (Sara) wazumbulika pa Genezesi 11:29, 30, chifukwa chakuti Yehova wangukamba kuti Mbewu yakulayizgika yazamutuliya mwaku iyu, mwa munthukazi munyaki cha. Milika nayu wazumbulika mu nkhani yeniyi chifukwa wenga ambuyaki aku Rabeka, muwoli waku Isaki. Venivi vilongo kuti Rabeka wenga mubali waku Aburahamu chifukwa Isaki wakhumbikanga cha kuto munthukazi kutuwa ku mitundu yinyaki. (Ge 22:20-23; 24:2-4) Lemba la Genezesi 25:1, lizumbuwa zaku Ketura kuti ndiyu wenga munthukazi yo Aburahamu wanguto kachiŵi. Venivi vilongo kuti Aburahamu wanguto so munthukazi munyaki Sara wati wafwa. Aburahamu wenga weche ndi nthazi zakubaliya pati pajumpha vyaka 40 kutuliya po Yehova wangumupaskiya nthazi zakubaliya mwakuziziswa. (Ar 4:19; Ge 24:67; 25:20). Kweniso fundu yakuti Aburahamu wanguto Ketura yilongo ubali wo wengapu pakati pa Ayisirayeli ndi Amidiyani ndipuso mitundu yinyaki ya ku Arabia.
Leya, Rakelu ndipuso mbilika zaku Yakobe ndi ŵana wo angubala, nawuso azumbulika. (Ge 35:21-26) Vifukwa vo vakambika pachanya yapa ndivu vinguchitiska kuti mazina nga anthukazi anyaki ngasanilikengi mu mabuku nga mkoka. Mazina nga anthukazi ngalembekanga so asani chihara cha pabanja lawu chipaskikengi kwaku yiwu. (Nu 26:33) Tamara, Rahabi ndi Ruti nawu azumbulika mu Bayibolu. Anthukazi yaŵa azumbulika chifukwa chakuti ŵenga apapi aku Mesiya, yo ndi Yesu Khristu. (Ge 38; Ru 1:3-5; 4:13-15; Mt 1:1-5) Malemba nganyaki ngo ngazumbuwa anthukazi wo akulembeka mu mabuku nga mkoka ndi 1 Mbiri 2:35, 48, 49; 3:1-3, 5.
JANUARY 23-29
CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | 1 MBIRI 4-6
“Kumbi Mapempheru Ngangu Ngalongo Kuti nde Munthu Wamtundu Wuli?”
w10-CN 10/1 23 ¶3-7
“Wakumva Pemphero”
Yabezi anali munthu wokonda kupemphera. Iye anayamba pemphero lake ndi kupempha madalitso kwa Mulungu. Kenako anapempha zinthu zitatu zimene zikusonyeza kuti iye anali ndi chikhulupiriro cholimba.
Poyamba, Yabezi anapempha Mulungu kuti: ‘Mukulitse dziko langa.’ (Vesi 10) Munthu wolemekezekayu sankalanda malo a anthu kapena kusirira zinthu za eni. N’kutheka kuti iye ankaganizira za anthu osati malo. Mwina ankapempha kuti dera lake likule mwamtendere n’cholinga choti mukhale anthu ambiri olambira Mulungu woona.
Chachiwiri, Yabezi anapempha kuti “dzanja” la Mulungu likhale naye. Mawu ophiphiritsa akuti dzanja la Mulungu amatanthauza mphamvu zimene Mulungu amagwiritsa ntchito pothandiza anthu amene amamulambira. (1 Mbiri 29:12) Kuti alandire zimene anapempha kuchokera pansi pa mtima, Yabezi anadalira Mulungu yemwe dzanja lake silifupika kwa anthu amene amamukhulupirira.—Yesaya 59:1.
Chachitatu, Yabezi anapemphera kuti: ‘Munditeteze ku tsoka, kuti lisandivulaze.’ Mawu akuti, ‘kuti lisandivulaze’ akusonyeza kuti Yabezi sanapemphe kuti asakumane ndi tsoka koma kuti asade nkhawa kwambiri ndi tsokalo kapena kugonja pokumana ndi zoipa.
Pemphero la Yabezi limasonyeza kuti iye ankaganizira kwambiri za kulambira koona ndipo ankakhulupirira ndi kudalira Wakumva pemphero. Kodi Yehova anamuyankha bwanji? Nkhani yachiduleyi imatha ndi mawu akuti: “Choncho Mulungu anakwaniritsa zimene iye anapempha.”
Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu
w05-CN 10/1 9 ¶7
Mfundo Zazikulu za M’buku Loyamba la Mbiri
5:10, 18-22. M’masiku a Mfumu Sauli, mafuko amene anali kum’mawa kwa Yordano anagonjetsa Ahagiri ngakhale kuti chiwerengero cha Ahagiri chinali chochuluka kuwirikiza kawiri pochiyerekeza ndi cha mafukowa. Izi zinali choncho chifukwa chakuti amuna amphamvu a mafuko amenewa anadalira Yehova kuwathandiza. Tiyeni tidalire Yehova ndi mtima wonse pamene tikupitiriza kumenya nkhondo yauzimu ndi adani omwe ali ochuluka kutiposa.—Aefeso 6:10-17.
JANUARY 30–FEBRUARY 5
CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | 1 MBIRI 7-9
“Yehova Wangakuwovyani Kuti Mufiski Kuchita Uteŵeti Wakusuzga”
w05-CN 10/1 9 ¶8
Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku Loyamba la Mbiri
9:26, 27. Alevi oyang’anira zipata anali ndi udindo wofunika kwambiri. Iwo anapatsidwa makiyi otsegulira malo opatulika osiyanasiyana a pakachisi. Anali okhulupirika potsegula zipata tsiku lililonse. Tapatsidwa udindo wofikira anthu m’gawo lathu ndi kuwathandiza kuyamba kupembedza Yehova. Kodi sitiyenera kukhala odalirika ndi okhulupirika monga mmene Alevi oyang’anira zipata anachitira?
w11-CN 9/15 32 ¶7
Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi?
Pinihasi anali ndi udindo waukulu mu Isiraeli wakale koma anathana ndi mavuto bwinobwino chifukwa cha kulimba mtima, kumvetsa zinthu ndiponso kudalira Mulungu. Komanso zimene Pinihasi anachita posamalira mpingo wa Mulungu zinasangalatsa kwambiri Yehova. Patapita zaka 1,000, Ezara anauziridwa kulemba kuti: “Pinihasi mwana wa Eleazara ndiye anali mtsogoleri wawo kalekale, ndipo Yehova anali naye.” (1 Mbiri 9:20) Mawu amenewa ayeneranso kugwira ntchito kwa amene amatsogolera anthu a Mulungu masiku ano komanso Akhristu onse amene amatumikira Mulungu mokhulupirika.
Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu
w10-CN 12/15 21 ¶6
Imbirani Yehova
Kudzera mwa aneneri ake, Yehova analamula kuti anthu amene amamulambira azimutamanda ndi nyimbo. Anthu oimba nyimbo ochokera m’fuko la ansembe sankaloledwa kugwira ntchito zina zimene Alevi ena ankagwira n’cholinga choti akhale ndi nthawi yokwanira yokonza nyimbo n’kuyesa kuziimba.—1 Mbiri 9:33.
FEBRUARY 6-12
CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | 1 MBIRI 10-12
“Nyengu Zosi Muŵengi ndi Mtima Wakuchita vo Chiuta Wakhumba”
w12-CN 11/15 6 ¶12-13
“Ndiphunzitseni Kuchita Chifuniro Chanu”
Davide anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yofunitsitsa kutsatira mfundo za m’Chilamulo. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika Davide atanena kuti ankafunitsitsa kumwa “madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu.” Asilikali atatu a Davide anakalowa mwamphamvu mumzindawo, womwe pa nthawiyo unali utalandidwa ndi Afilisiti. Iwo anakatunga madzi m’chitsimecho n’kubwera nawo. Koma “Davide anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.” N’chifukwa chiyani sanamwe? Iye anafotokoza kuti: “Sindingachite zimenezo chifukwa ndimalemekeza Mulungu wanga. Kodi ndimwe magazi a anthuwa omwe anaika moyo wawo pachiswe? Iwowa akanataya moyo wawo pokatunga madziwa.”—1 Mbiri 11:15-19.
Davide anadziwa kuti Chilamulo chimanena kuti magazi sayenera kudyedwa koma kuperekedwa kwa Yehova. Iye ankadziwa kuti “moyo wa nyama [kapena munthu] uli m’magazi.” Komatu Davide anakana madzi osati magazi. Ndiye anakaniranji? Iye anakana chifukwa ankadziwa mfundo ya m’lamulolo. Davide ankaona kuti madziwo anali amtengo wapatali ngati magazi a amuna atatuwa. Choncho ankaona kuti n’kulakwa kwambiri kumwa madziwo. Chotero sanamwe koma anawathira pansi.—Lev. 17:11; Doto. 12:23, 24.
Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu
it-1 1058 ¶5-6
Mtima
Kujipereka ndi “Mtima Wosi.” Mtima ukhumbika kuja wamphumphu kuti ugwiri ntchitu umampha, kweni mtima wakuyeruzgiya ungagaŵikana. Davidi wangupemphera kuti: “Ndipaskeni mtima wamphumphu kuti ndiwopengi zina linu.” Venivi vilongo kuti mtima wa munthu ungagaŵikana chifukwa cha vo watanja pamwenga vo watopa. (Sl 86:11) Munthu waviyo waja wa “mtima wa paŵipaŵi”—wakuluputuka pakuteŵete Chiuta. (Sl 119:113; Chv 3:16) Munthu wangaŵa so ndi “mtima wachinyengu” (Mazu ngaki chayingu, ndi mtima ndi mtima), wangateŵete mabwana ngaŵi, wangakamba vinthu vinyaki penipo mu mtima waŵanaŵana vinyaki. (1Mb 12:33; Sl 12:2, mazu ngamumphata) Yesu wangukamba kuti ŵanthu a mtima wa paŵipaŵi ŵenaŵa mbachinyengu.—Mt 15:7, 8.
Munthu yo wakhumba kukondwesa Chiuta wakhumbika kuja ndi mtima wa paŵipaŵi cha pamwenga wachinyengu kweni wakhumbika kumuteŵete ndi mtima wosi. (1Mb 28:9) Iyu wakhumbika kufwiyapu kuti wateŵete Yehova ndi mtima wosi chifukwa chakuti mtima ngwakunyenga kweniso uŵanaŵana vinthu viheni. (Yer 17:9, 10; Ge 8:21) Munthu wangateŵete Chiuta ndi mtima wosi asani: wapemphera kutuliya pasi pa mtima (Sl 119:145; Chj 3:41), wasambira Mazu ngaku Chiuta nyengu zosi (Ezr 7:10; Nth 15:28), wapharazga uthenga wamampha mwaphamphu (yeruzgiyani ndi Yer 20:9), ndipuso wacheza ndi ŵanthu wo ateŵete Yehova ndi mtima wosi.—Yeruzgiyani ndi 2Mf 10:15, 16.
FEBRUARY 13-19
CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | 1 MBIRI 13-16
“Kulondo Ulongozgi Kutovya Kuti Vinthu Vitiyendiyengi Umampha”
w03-CN 5/1 10-11
Kodi Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”
Likasa la chipangano litabwerera ku Israyeli ndipo litakhala zaka zambiri ku Kiriyati-Yearimu, Mfumu Davide inafuna kusamutsira Likasalo ku Yerusalemu. Anakambirana ndi akulu amene anali kutsogolera anthu ndipo anawauza kuti Likasa lisamutsidwa ‘chikakomera iwo, ndipo chikachokera kwa Yehova.’ Koma sanafufuze mokwanira kuti adziŵe maganizo a Yehova pankhaniyi. Akanakhala kuti anachita zimenezo, sibwenzi atanyamulira Likasalo pa galeta. Alevi Achikohati ndi amene akananyamula pa mapeŵa pawo, monga momwe Mulungu analangizira momveka bwino. Ngakhale kuti Davide nthaŵi zonse ankafunsira kwa Yehova, analephera kuchita zimenezo moyenera panthaŵi imeneyi. Zotsatira zake zinali zomvetsa chisoni zedi. Patapita nthaŵi Davide anavomereza kuti: “Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinam’funafuna Iye monga mwa chiweruzo.”—1 Mbiri 13:1-3; 15:11-13; Numeri 4:4-6, 15; 7:1-9.
w03-CN 5/1 11 ¶13
Kodi Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”
Tsopano Alevi atasamutsa Likasa ku Obedi-Edomu kupita nalo ku Yerusalemu, anthu anaimba nyimbo imene Davide analemba. Ena mwa mawu a m’nyimboyo anali mawu ochokera pansi pamtima owakumbutsa, akuti: “Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yake; funani nkhope yake nthaŵi zonse. Kumbukirani zodabwiza zake adazichita, zizindikiro zake, ndi maweruzo a pakamwa pake.”—1 Mbiri 16:11, 12.
Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu
w14 1/1 10 ¶14
Sopani Yehova, Karonga Wamuyaya
Davidi wanguza ndi bokosi la phanganu lakupaturika ku Yerusalemu. Pa nyengu yalikondwa yeniyi, Alevi angumba sumu yakuthamika Chiuta yo ye ndi mazu ngakuzirwa ngo nge pa 1 Mikoka 16:31 ngakuti: “Anene mukati mu mitundu kuti ‘Ambuya [ayamba, NW] kuwusa.’” Panyaki mungazizwa kuti, ‘Yehova ndi Karonga wamuyaya, nanga wangwamba wuli kuwusa pa nyengu yo?’ Iyu waja Karonga asani wagwiriskiya nchitu mazaza ngaki pamwenga asani wasankha munthu kuti wamumiyi. Kuziŵa mo Yehova wajaliya Karonga nkhwakukhumbika ukongwa. Davidi wechendafwi, Yehova wangumulayizga kuti ufumu waki wazamumala cha. Ndipu wanguti: “Nkhasoskanga mphapu yaku pavuli paku, yo wakatuliyanga mu liŵavu laku, ndipu ndikakhozganga ufumu waki.” (2 Sam. 7:12, 13) Layizgu lenili lingufiskika po “mphapu” yaku Davidi yinguziŵaku pati pajumpha vyaka pafupifupi 1,000. Kumbi mphapu yeniyi yenga yani, nanga yinguzija Fumu zukwanji?
FEBRUARY 20-26
CHUMA CHAKUTULIYA MU MAZU NGAKU CHIUTA | 1 MBIRI 17-19
“Lutirizgani Kukondwa Chinanga Kuti Mukumana ndi Vinthu Vakugongowesa”
w06-CN 7/15 19 ¶1
Ganizirani za Ubwino wa Gulu la Yehova
DAVIDE wa ku Israyeli wakale ndi mmodzi mwa anthu odziwika kwambiri ofotokozedwa m’Malemba Achihebri. Munthuyu yemwe anali mbusa, woimba, mneneri ndi mfumu, ankakhulupirira kwambiri Yehova Mulungu. Ubwenzi wolimba umene Davide anali nawo ndi Yehova unam’limbikitsa kukhala ndi chikhumbo chofuna kumangira Mulungu nyumba. Nyumba kapena kachisi ameneyu anadzakhala likulu la kulambira koona m’Israyeli. Davide ankadziwa kuti kachisi ndiponso ntchito yomwe inkachitika pakachisipo idzabweretsa chimwemwe ndi madalitso kwa anthu a Mulungu. Motero, Davide anaimba kuti: “Wodala munthuyo [amene inu Yehova] mum’sankha, ndi kum’yandikizitsa, akhale m’mabwalo anu: Tidzakhuta nazo zokoma za m’nyumba yanu, za m’malo oyera a Kachisi wanu.”—Salimo 65:4.
Fundu Zakuzirwa za mu Bayibolu
w05-CN 10/1 11 ¶6
Mfundo Zazikulu za M’buku Loyamba la Mbiri
21:13-15. Yehova analamula mngelo kuletsa mliri chifukwa chakuti Iye amakhudzidwa kwambiri anthu Ake akamavutika. Ndithudi, “zifundo zake zichulukadi.”