PEZANI THANDIZO PA NKHAWA ZANU
N’zotheka Kukhala na Umoyo Wopanda Nkhawa
Nzelu zopezeka m’Baibo zingatithandize kupewa nkhawa zambili zosafunikila. Pa ife tekha sitingakwanitse kuthetsa zinthu zonse zimene zimatibweletsela nkhawa mu umoyo wathu. Koma Mlengi wathu angakwanitse. Iye anasankha munthu wina kuti atithandize. Munthuyo ni Yesu Khristu. Posacedwa, iye adzacita zinthu zambili zabwino pa dziko lonse la pansi, kuposa zimene anacita pamene anali pa dziko monga munthu. Mwacitsanzo:
YESU ADZACILITSA ODWALA MONGA MMENE ANACITILA ALI PA DZIKO LAPANSI.
“Anthu anamubweletsela onse amene sanali kumva bwino m’thupi, amene anali kuvutika ndi matenda . . . , ndipo iye anawacilitsa.”—MATEYU 4:24.
YESU ADZATHANDIZA ANTHU ONSE KUKHALA NA NYUMBA KOMANSO CAKUDYA.
“Iwo [olamulilidwa na Khristu] adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya.”—YESAYA 65:21, 22.
ULAMULILO WA YESU UDZABWELETSA MTENDELE NA CITETEZO PA DZIKO LONSE.
“M’masiku ake, wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendele woculuka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo. Ndipo adzakhala ndi anthu omugonjela kucokela kunyanja kukafika kunyanja, komanso kucokela ku Mtsinje kukafika kumalekezelo a dziko lapansi. . . . Ndipo adani ake adzabwila fumbi.”—SALIMO 72:7-9.
YESU ADZATHETSA KUPANDA CILUNGAMO.
“Adzamvela cisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzawombola miyoyo yawo ku cipsinjo ndi ciwawa.”—SALIMO 72:13, 14.
YESU ADZATHETSA MAVUTO NA IMFA.
“Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—CHIVUMBULUTSO 21:4.