LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 2
  • Munda Wokongola

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Munda Wokongola
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mulungu Anapanga Kumwamba na Dziko Lapansi
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Mmene Anataila Malo Ao Okhalako
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Mwamuna Ndi Mkazi Oyamba
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2011
Onaninso Zina
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 2

Nkhani 2

Munda Wokongola

ONA cabe mmene dziko lapansi lionekela pacithunzi-thunzi apa! Ciliconse cioneka bwino kwambili! Ona maudzu, mitengo, maluŵa ndi zinyama zonse. Kodi ungazisonthe njovu ndi mikango?

Kodi munda wokongola umenewu unakhalako bwanji? Cabwino, tiye tione mmene Mulungu anatikonzela dziko lapansi.

Coyamba, Mulungu anapanga maudzu obiliŵila kuti azimela padziko lonse lapansi. Ndiyeno anapanga zomela zing’ono-zing’ono zamitundu-mitundu, zitsamba ndi mitengo. Zomela zimenezi zimapangitsa dziko lapansi kuoneka lokongola kwambili. Koma zimatithandiza pambali zina. Zomela zambili zimatipatsanso vakudya vabwino kwambili.

Pambuyo pake, Mulungu anapanga nsomba kuti zizikhala m’madzi ndi mbalame kuti ziziuluka mu mlenga-lenga. Anapanga agalu, apusi ndi mahaci kapena kuti mahosi; zinyama zikulu na zing’ono. Kodi n’zinyama zabwanji zimene zimapezeka kufupi ndi kumene ukhala? Kodi sitiyenela kuyamikila Mulungu poona kuti anatipangila zinthu zonse zimenezi?

Potsilizila, Mulungu anapanga mbali ina ya dziko lapansi kukhala malo apadela kwambili. Malo amenewa anawacha kuti munda wa Edeni. Anali malo abwino kwambili. Vinthu vonse vimene vinalimo vinali vokongola. Ndipo Mulungu anali kufuna kuti dziko lonse lapansi likhale monga munda wokongola umenewu.

Koma yang’ananso pacinthuzi-thunzi ca munda wokongola ici. Kodi udziŵa cimene Mulungu anaona kuti palibe apa? Tiye tione.

Genesis 1:11-25; 2:8,9.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani