LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 7
  • Munthu Wopanda Mantha

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Munthu Wopanda Mantha
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • ‘Mulungu Anakondwela Naye’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Kucokela pa Cilengedwe Kufika pa Cigumula
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 7

Nkhani 7

Munthu Wopanda Mantha

PAMENE anthu anayamba kuculuka padziko lapansi, ambili anali kucita vinthu voipa monga Kaini. Koma panali munthu wina amene anali wosiyana ndi ena. Munthu ameneyu dzina lake anali Inoki. Inoki anali munthu wopanda mantha. Anthu onse panthawi imeneyo anali kucita vinthu voipa kwambili, koma iye anapitiliza kutumikila Mulungu.

Kodi udziŵa cifukwa cake anthu akale amenewo anali kucitila vinthu voipa? Cabwino, ngati ungaganize, ndani amene anapangitsa Adamu ndi Hava kupandukila Mulungu mwa kudya cipatso cimene Iye anaŵaletsa? Inde, anali mngelo woipa. Baibo imati mngelo ameneyo ni Satana. Ndipo amafuna kupangitsa anthu onse kuti akhale oipa.

Tsiku lina Yehova Mulungu anatuma Inoki kuti auze anthu uthenga umene io sanafune kumva. Uthengawu unali wakuti: ‘Tsiku lina Mulungu adzaononga anthu oipa onse.’ Anthu amenewo ayenela kuti anakalipa kwambili pamene anamva zimenezi. Mwina anafuna ngakhale kumupha Inoki. Conco, Inoki anafunikila kukhala wopanda mantha kuti auze anthu zimene Mulungu anali kufuna kucita.

Mulungu sanalole kuti Inoki akhale kwa nthawi yaitali pakati pa anthu oipa amenewo. Conco Inoki anakhala ndi moyo kwa zaka 365 cabe. N’cifukwa ciani takamba kuti “zaka 365” cabe? Cifukwa anthu m’masiku amenewo anali olimba kuposa masiku ano, ndipo anali kukhala zaka zambili. Mwacitsanzo, Metusela mwana wa Inoki anakhala zaka 969!

Pamene Inoki anafa, anthu anapitiliza kukhala oipa kwambili. Baibo imakamba kuti ‘zonse zimene anali kuganiza zinali zoipa nthawi zonse,’ ndi kuti dziko lapansi ‘linadzala ndi ciwawa.’

Kodi udziŵa cifukwa cake padziko lapansi panali kucitika vinthu voipa kwambili m’masiku amenewo? N’cifukwa cakuti Satana anapeza njila yatsopano yopangitsa anthu kucita vinthu voipa. M’nkhani yotsatila tidzaphunzila za njila imeneyo.

Genesis 5:21-24, 27; 6:5; Aheberi 11:5; Yuda 14, 15.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani