Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila
Wokondedwa Bwenzi la Yehova:
Yesu anati: “Mudzadziŵa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Mau amenewa ndi olimbikitsa kwambili. Inde, n’zotheka ‘m’masiku otsiliza’ ano ovuta, kudziŵa coonadi ngakhale kuti mabodza afala. (2 Timoteyo 3:1) Kodi mukumbukila mmene munamvelela pamene munazindikila coonadi ca Mau a Mulungu? Mwacionekele munasangalala kwambili!
Kukhala ndi cidziŵitso colongosoka ca coonadi ndi kulalikila coonadi cimeneco mokhazikika n’kofunika. Komabe, tifunikanso kukhala ndi moyo mogwilizana ndi coonadi. Kuti ticite zimenezo, tiyenela kukhalabe m’cikondi ca Mulungu. Kodi zimenezi zimaphatikizapo kucita ciani? Mau amene Yesu anakamba pa usiku wake womaliza asanaphedwe amayankha funso limeneli. Iye anauza atumwi ake okhulupilika kuti: “Mukasunga malamulo anga, mudzakhalabe m’cikondi canga, monga mmene ine ndasungila malamulo a Atate ndi kukhalabe m’cikondi cake.”—Yohane 15:10.
Apa taona kuti Yesu anakhalabe m’cikondi ca Mulungu cifukwa anasunga malamulo a Atate wake. Ifenso tiyenela kucita cimodzimodzi masiku ano. Kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, tifunika kutsatila coonadi paumoyo wathu tsiku ndi tsiku. Pa usiku wake womaliza, Yesu anakambanso kuti: “Ngati zimenezi mukuzidziŵa, ndinu odala mukamazicita.”—Yohane 13:17.
Sitikaikila kuti buku lino lidzakuthandizani kupitiliza kutsatila coonadi paumoyo wanu, kuti mukhalebe ‘m’cikondi ca Mulungu . . . ndi kuti mukalandile moyo wosatha.’—Yuda 21.
Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova