LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • jl phunzilo 13
  • Kodi Mpainiya Ndani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mpainiya Ndani?
  • Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Nkhani Zofanana
  • Upainiya Umalimbitsa Unansi Wathu Ndi Mulungu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
jl phunzilo 13

PHUNZILO 13

Kodi Mpainiya Ndani?

Mlaliki wa nthawi zonse ali mu utumiki

Ku Canada

Alelengezi a nthawi zonse ali mu ulaliki

Alalikila nyumba ndi nyumba

Alaliki amene ndi apainiya akucititsa phunzilo la Baibo

Phunzilo la Baibo

Mpainiya aphunzila Baibo

Phunzilo laumwini

Kaŵili-kaŵili mau akuti “mpainiya” amakamba za munthu amene amatulukila malo atsopano ndi kutsegulila ena njila kuti atsatile. Yesu anali ngati mpainiya cifukwa anatumidwa padziko lapansi kudzagwila nchito yopatsa moyo ndi kutsegula njila ya cipulumutso. (Mateyu 20:28) Masiku ano, otsatila ake amatengela citsanzo cake mwa kuthela nthawi yao yambili pa nchito yopanga ophunzila. (Mateyu 28:19, 20) Ena amagwila nchito imene ife Mboni timaicha kuti utumiki wa upainiya.

Mpainiya ni munthu amene nchito yake ni kulalikila. Mboni za Yehova zonse zimalalikila uthenga wabwino. Koma zina zasintha zinthu pa umoyo wao kuti zikhale apainiya a nthawi zonse, ndipo zimathela maola 70 mwezi uliwonse pa nchito yolalikila. Kuti zikwanitse zimenezi, zambili zimapeza nchito ya maola ocepa. Mboni zina zimasankhidwa kukhala apainiya apadela kuti akatumikile kumalo osoŵa. Iwo amathela maola 130 kapena kuposapo mwezi uliwonse pa nchito yolalikila. Apainiya amakhutila ndi umoyo wosafuna zambili, ndipo amadalila Yehova kuti adzawapatsa zosoŵa zao. (Mateyu 6:31-33; 1 Timoteyo 6:6-8) Amene sangakwanitse kucita upainiya wa nthawi zonse angakhale apainiya othandiza ngati angakwanitse. Amenewa amaonjezela nchito yao yolalikila kuti akwanitse maola 30 kapena 50 pa mwezi.

Mpainiya amakonda Mulungu ndi anthu. Mofanana ndi Yesu, timazindikila kuti anthu ambili lelolino ali ndi njala yauzimu. (Maliko 6:34) Koma ife tili ndi uthenga umene ungawathandize pa nthawi ino ndi kuwapatsa ciyembekezo colimba ca mtsogolo. Mpainiya amathela nthawi yake ndi mphamvu zake zonse pa kuthandiza ena mwauzimu cifukwa ca cikondi. (Mateyu 22:39; 1 Atesalonika 2:8) Zotsatilapo zake n’zakuti cikhulupililo ca mpainiya cimalimba mwakuti amayandikila Mulungu, ndipo amakhala ndi cimwemwe cacikulu.—Machitidwe 20:35.

  • Kodi mungakambe kuti mpainiya ndani?

  • Kodi n’cifukwa ciani ena amacita upainiya wa nthawi zonse?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani