LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • fg phunzilo 15 Mafunso. 1-4
  • N’cifukwa Ciani Muyenela Kupitilizabe Kuphunzila za Yehova?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Muyenela Kupitilizabe Kuphunzila za Yehova?
  • Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mungamuyandikile Bwanji Mulungu?
    Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
  • “Kuyandikila kwa Mulungu Ndi Cinthu Cabwino” kwa Ife!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Khalani Pafupi Ndi Yehova
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • N’ciyani Cingakuthandizeni Kuti Musaleke Kuphunzila Baibo?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
fg phunzilo 15 Mafunso. 1-4

PHUNZILO 15

N’cifukwa Ciani Muyenela Kupitilizabe Kuphunzila za Yehova?

1. Kodi mudzapindula bwanji mukapitiliza kuphunzila Baibo?

Akazi aŵili aphunzila Baibo panthawi yopuma kunchito

Mosakaikila, ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo zimene mwaphunzila zalimbitsa cikondi canu pa Yehova. Tifunikila kupitiliza kulimbitsa cikondi cimeneci. (1 Petulo 2:2) Kuti mukakhale ndi moyo wosatha mufunika kupitiliza kuyandikila kwa Mulungu mwa kuphunzila Mau ake.​—Ŵelengani Yohane 17:3; Yuda 21.

Mukamudziŵa bwino kwambili Mulungu, cikhulupililo canu cidzakhala colimba ndipo cidzakuthandizani kumukondweletsa. (Aheberi 11:1, 6) Cidzakulimbikitsani kulapa ndi kusintha zinthu pa umoyo wanu.​—Ŵelengani Machitidwe 3:19.

2. Kodi kudziŵa kwanu Mulungu kungathandize bwanji ena?

Mkazi apemphela kwa Mulungu

Mungakhale ndi ubwenzi wapadela ndi Yehova

Mwacibadwa, mudzafuna kuuzako ena zimene mwaphunzila. Tonse timakondwela tikamalalikila uthenga wabwino. Pamene mupitiliza kuphunzila Baibo, mudzaphunzila mmene mungaigwilitsile nchito pofotokoza cikhulupililo canu mwa Yehova. Ndipo mudzaphunzilanso mmene mungaigwilitsile nchito pofotokoza uthenga wabwino.​—Ŵelengani Aroma 10:13-15.

Anthu ambili amayamba kuuzako mabwenzi kapena acibanja ao uthenga wabwino. Koma muzikhala osamala pocita zimenezi. M’malo moŵauza kuti zimene amakhulupilila n’zabodza, muziŵauza za malonjezo a Mulungu. Ndiponso, muzikumbukila kuti nthawi zambili anthu amacita cidwi ndi khalidwe lanu kuposa zimene mumakamba.​—Ŵelengani 2 Timoteyo 2:24, 25.

3. Kodi ndi ubwenzi wanji umene mungakhale nao ndi Mulungu?

Kuphunzila Mau a Mulungu kudzakuthandizani kuti mukule kuuzimu. Posapita nthawi, mungakhale paubwenzi wapadela ndi Yehova. Mungakhalenso m’banja lake.​—Ŵelengani 2 Akorinto 6:18.

4. Kodi mufunika kucita ciani kuti mupitilize kukula kuuzimu?

Mungakule kuuzimu mwa kupitiliza kuphunzila Mau a Mulungu. (Aheberi 5:13, 14) Pemphani mmodzi wa Mboni za Yehova kuti ayambe kuphunzila nanu Baibo m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni. Mukaphunzila zambili ponena za Mau a Mulungu, m’pamene umoyo wanu udzakhala waphindu.​—Ŵelengani Salimo 1:1-3; 73:27, 28.

Mboni za Yehova ziyambitsa phunzilo la Baibo

Uthenga wabwino umacokela kwa Yehova, amene ndi Mulungu wacimwemwe. Mungamuyandikile Mulungu mwa kuyandikila anthu ake. (Aheberi 10:24, 25) Mukamapitiliza mwakhama kukondweletsa Yehova, ndiye kuti mukuyesa-yesa kuti mukapeze moyo weni-weni umene ndi moyo wosatha. Kuyandikila Mulungu ndi cinthu cabwino kwambili cimene mungacite.​—Ŵelengani 1 Timoteyo 1:11; 6:19.

Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 18 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani