NKHANI YOPHUNZILA 15
NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa
“Kuyandikila kwa Mulungu Ndi Cinthu Cabwino” kwa Ife!
“Kwa ine, kuyandikila kwa Mulungu ndi cinthu cabwino.”—SAL. 73:28.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Zimene tingacite kuti tiyandikile Yehova, komanso mapindu amene timapeza tikatelo.
1-2. (a) Kodi munthu afunika kucita ciyani kuti akhale pa ubwenzi wathithithi ndi wina? (b) Tikambilane ciyani m’nkhani ino?
KODI muli ndi bwenzi la ponda apa nane m’pondepo? N’ciyani cinacititsa kuti mukhale mabwenzi? N’kutheka kuti munali kuceza naye, munadziwa mavuto omwe anali kukumana nawo, ndipo munadziwanso zomwe anali kukonda ndi zimene anali kudana nazo. Ndipo munazindikila kuti anali ndi makhalidwe osililika amene mungakonde kutengelako. Munafika polikonda kwambili bwenzilo.
2 Kukhala pa ubwenzi wathithithi ndi wina kumalila nthawi ndi khama. Mofananamo, timafunikilanso nthawi ndi khama kuti tikhale pa ubale wathithithi ndi Yehova Mulungu. M’nkhani ino, tikambilana zimene tingacite kuti tiyandikile Mulungu wathu, komanso mapindu amene timapeza tikatelo. Koma coyamba tiyeni tikambilane cifukwa cake n’kwabwino kuyandikila Bwenzi lathu lapamtima, Yehova.
3. N’cifukwa ciyani tiyenela kusinkhasinkha za mapindu amene amabwela cifukwa coyandikila Yehova? Fotokozani citsanzo.
3 Mosakaikila, mumadziwa kuti kuyandikila Yehova n’cinthu cabwino. Koma kusinkhasinkha kuti n’kwabwino motani makamaka n’kumene kungatilimbikitse kupitiliza kumuyandikila kwambili. (Sal. 63:6-8) Mwacitsanzo, timadziwa kuti kudya cakudya copatsa thanzi, kucita masewela olimbitsa thupi, kugona mokwanila, komanso kumwa madzi okwanila n’zinthu zabwino kwa tonsefe. Ngakhale n’telo, ambili saganizilapo kwenikweni pa zinthuzi, conco samasamala thanzi lawo. Komabe, tikamaganizila kwambili za mapindu a zinthu zomwe tachulazi, tidzalimbikitsika kumazicita. Mofananamo, tingadziwe kuti kuyandikila Yehova monga Bwenzi lathu n’kwabwino kwa ife. Koma kusinkhasinkha pa mapindu amene amabwela tikamacita zimenezo kungatilimbikitse kupitiliza kumuyandikila.—Sal. 119:27-30.
4. Malinga ndi Salimo 73:28, kodi wamasalimo anati ciyani?
4 Welengani Salimo 73:28. Wolemba Salimo 73 anali Mlevi amene anaikidwa kuti azitumikila monga woimba pa kacisi wa Yehova. Zioneka kuti anali atatumikila Yehova mokhulupilika kwa kanthawi ndithu. Komabe, iye limodzi ndi ena anafunika kukumbutsidwa kuti “kuyandikila kwa Mulungu” kunali cinthu cabwino kwa iwo. Kodi ndi mapindu ena ati omwe amabwela kaamba kocita zimenezo?
“KUYANDIKILA KWA MULUNGU” KUMABWELETSA CIMWEMWE
5. (a) Kodi kuyandikila Yehova kumatibweletsela cimwemwe motani? (b) Kodi nzelu zimene Yehova amakupatsani zimakuthandizani komanso kukutetezani motani? (Miyambo 2:6-16)
5 Tikamamuyandikila kwambili Yehova, tidzawonjezela cimwemwe cathu. (Sal. 65:4) Zili telo pa zifukwa zambili. Coyamba n’cakuti tikagwilitsa nchito nzelu zothandiza zopezeka m’Mawu ake Baibulo, timapindula. Nzelu za m’Baibulo zimatiteteza ku makhalidwe oipa, komanso zimatithandiza kuti tisapange zolakwa zazikulu. (Welengani Miyambo 2:6-16.) M’pake kuti Baibulo limati: “Wosangalala ndi munthu amene amapeza nzelu, ndiponso munthu amene amaphunzila zinthu zimene zingamuthandize kukhala wozindikila.”—Miy. 3:13.
6. N’ciyani cinapangitsa wamasalimo kutaya cimwemwe?
6 Komabe, ngakhale mabwenzi a Yehova amakhala acisoni nthawi zina. Wolemba Salimo 73 anataya cimwemwe cake pamene anayamba kuganizila zinthu zimene anaona kuti ndi zopanda cilungamo. Anakhumudwa ndipo anacita nsanje cifukwa anali kuganiza kuti anthu oipa amene sanali kusamala za Mulungu, kapena amene sanali kuyendela mfundo zake, zinthu zinali kuwayendela bwino. Molakwika, iye anali kuganiza kuti anthu aciwawa ndi odzitukumula nthawi zonse anali kukhala olemela, athanzi labwino, komanso sanali kukumana ndi mavuto. (Sal. 73:3-7, 12) Wamasalimoyu anavutika maganizo kwambili, moti pa nthawi ina anaganiza kuti khama lonse limene anacita potumikila Yehova linapita pacabe. Mwacisoni iye anakamba kuti: “Ndithudi, ndayeletsa mtima wanga pacabe, ndipo ndasamba mʼmanja mwanga pacabe posonyeza kuti ndine wosalakwa.”—Sal. 73:13.
7. Tingacite ciyani tikakhala ndi cisoni? (Onaninso pacikuto.)
7 Wamasalimoyu sanalole cisoni cake kumufooketsa. M’malomwake, anacitapo kanthu. Analowa “mʼmalo opatulika aulemelelo a Mulungu.” Ndipo ali mmenemo, Yehova anawongolela kaganizidwe kake. (Sal. 73:17-19) Bwenzi lathu lapamtima, Yehova, amadziwa tikakhala ndi cisoni. Tikamapemphela kuti atitsogolele, komanso kulandila thandizo limene amapeleka kudzela m’Mawu ake komanso mu mpingo, tidzalandila mphamvu zimene zidzatithandiza kupilila cisoni cimene tingakhale naco. Ngakhale pamene nkhawa zaticulukila, Yehova amatitonthoza ndi kutipangitsa kumva bwino.—Sal. 94:19.a
Mlevi amene analemba Salimo 73 waimilila “mʼmalo opatulika aulemelelo a Mulungu” (Onani ndime 7)
“KUYANDIKILA KWA MULUNGU” KUMATIPATSA UMOYO WABWINO KOMANSO CIYEMBEKEZO
8. Kodi kuyandikila kwa Mulungu n’kwabwino kwa ife m’njila zina zofunika ziti?
8 Kuyandikila kwa Mulungu n’kwabwino kwa ife m’njila zina ziwili zofunika. Coyamba, kumatipatsa umoyo wabwino palipano. Caciwili, kumatipatsa ciyembekezo codalilika. (Yer. 29:11) Tiyeni tizikambilane mfundo ziwilizi mozamilapo.
9. Kodi kuyandikila Yehova kumatipatsa umoyo wabwino m’njila yotani?
9 Kuyandikila Yehova kumatipatsa umoyo wabwino palipano. Ambili lelolino amakana zakuti Mulungu aliko, moti amaganiza kuti moyo ulibe phindu, ndi kuti kutsogolo mtundu wonse wa anthu udzathelatu. Komabe, pamene tinaphunzila Mawu a Mulungu, tinakhala otsimikiza kuti Mulungu “alikodi ndipo amapeleka mphoto kwa anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheb. 11:6) Ngakhale masiku ano, timakhala ndi umoyo wacimwemwe cifukwa timacita zimene Atate wathu wakumwamba, Yehova, anatilengela kuti tizicita, zomwe ndi kumutumikila.—Deut. 10:12, 13.
10. Malinga ndi Salimo 37:29, kodi Yehova waalonjeza ciyani anthu amene amamudalila?
10 Anthu ambili alibe ciyembekezo ceniceni. Cimene amangocita ndi kupita ku nchito, kukhala ndi banja, komanso kusunga ndalama zimene zidzawathandize akadzapuma pa nchito. Iwo saganizilapo za Mulungu. Mosiyana ndi anthu otelewa, atumiki a Yehova amaika ciyembekezo cawo mwa iye. (Sal. 25:3-5; 1 Tim. 6:17) Timamudalila Mulungu wathu amenenso ndi Bwenzi lathu. Ndipo timakhulupililanso zimene anatilonjeza. Cimodzi mwa zinthu zimene watilonjeza ndi kudzamulambila kwamuyaya m’Paradaiso.—Welengani Salimo 37:29.
11. Kodi kuyandikila kwa Mulungu kumatikhudza bwanji? Nanga kodi Mulungu kumamukhudza motani?
11 Kuyandikila Mulungu n’kwabwino pa zifukwa zinanso zambili. Mwacitsanzo, Yehova anatilonjeza kutikhululukila macimo athu tikalapa. (Yes. 1: 18) Pa cifukwa cimeneci, sitiyenela kukhala ndi cikumbumtima covutitsidwa cifukwa ca macimo amene tinacita kumbuyoku. (Sal. 32:1-5) Phindu lina n’lakuti timakhala ndi cimwemwe podziwa kuti tikusangalatsa Yehova. (Miy. 23:15) Zoonadi, pali madalitso ena ambili obwela cifukwa cokhala bwenzi la Mulungu. Ndiye mungatani kuti mupitilize kumuyandikila Mulungu?
ZOMWE TINGACITE KUTI TIPITILIZE “KUYANDIKILA KWA MULUNGU”
12. Kodi mwacita ciyani kuti mumuyandikile kwambili Mulungu?
12 Ngati ndinu Mkhristu wobatizika, ndiye kuti munayamba kale kumuyandikila Yehova. Munadziwa coonadi conena za Mulungu ndi Yesu Khristu, munalapa macimo anu, munakhala ndi cikhulupililo colimba mwa Mulungu, ndipo munayesetsa kucita zinthu mogwilizana ndi cifunilo cake. Komabe, kuti timuyandikile kwambili Mulungu, tiyenela kupitiliza kucita zimenezi.—Akol. 2:6.
13. Ndi zinthu zitatu ziti zimene zingatithandize kupitiliza kumuyandikila kwambili Yehova?
13 Kodi tingatani kuti tipitilize kumuyandikila kwambili Yehova? (1) Tiyenela kupitiliza kuwelenga ndi kuliphunzila Baibulo. Pocita zimenezo, colinga cathu siciyenela kungophunzila mfundo zoyambilila zokhudza Mulungu ayi. M’malomwake, tiyenela kuyesetsa kuzindikila cifunilo ca Mulungu kwa ife ndi kupitiliza kugwilitsa nchito mfundo zimene watiikila m’Mawu ake. (Aef. 5:15-17) (2) Tiyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa kusinkhasinkha njila zimene iye waonetsela cikondi cake pa ife. (3) Tiyenela kupitiliza kudana ndi zinthu zimene zimamukhumudwitsa Yehova, komanso kupewa kuyanjana ndi anthu amene amacita zinthuzo.—Sal. 1:1; 101:3.
14. Malinga ndi 1 Akorinto 10:31, ndi zinthu ziti zimene tingacite tsiku lililonse kuti tizikondweletsa Yehova? (Onaninso zithunzi.)
14 Welengani 1 Akorinto 10:31. Cofunika kwa ife ndi kucita zinthu zimene zimakondweletsa Yehova. Ndipo tiyenela kucita zina kuposa pa kungolalikila komanso kusonkhana. Zocita zathu za tsiku ndi tsiku ziyenela kukondweletsa Yehova. Mwacitsanzo, tikamakhala oona mtima m’zinthu zonse, komanso tikamagawana zinthu ndi ena, timakondweletsa Yehova. (2 Akor. 8:21; 9:7) Iye amafunanso kuti tizilemekeza kwambili mphatso ya moyo. Timamuyandikila Mpatsi wa moyo mwa kupewa kudya ndi kumwa kwambili, komanso mwa kucita zinthu zimene zingatithandize kukhala ndi thanzi labwino. Zonse zimene timayesetsa kucita kuti tikondweletse Yehova ngakhale m’zinthu zing’onozing’ono, zidzacititsa kuti iye azitikonda kwambili.—Luka 16:10.
Njila zina zimene tingakondweletsele Yehova ndi kuyendetsa galimoto mosamala, kudzisamalila mwa kucita masewela olimbitsa thupi, kudya zakudya zopatsa thanzi, komanso kukhala oceleza (Onani ndime 14)
15. Kodi Yehova amafuna kuti tizicita nawo motani anthu ena?
15 Yehova ndi wabwino kwa olungama ndi osalungama omwe. (Mat. 5:45) Iye amafuna kuti ifenso tiziganizila ena potengela citsanzo cake. Mwacitsanzo, tiyenela kupewa ‘kunenela zoipa munthu aliyense ndiponso kukonda kukangana. Koma . . . tizikhala ofatsa kwa anthu onse.’ (Tito 3:2) Conco, ngakhale kuti anthu ena sakhulupilila mwa Yehova, sitidziona kuti ndife apamwamba kuposa iwo. (2 Tim. 2:23-25) Timamuyandikila kwambili Yehova ngati nthawi zonse timakhala oganizila ena komanso okoma mtima kwa onse.
MUNGAYANDIKILEBE KWA MULUNGU NGAKHALE PAMENE MWALAKWITSA ZINTHU
16. Kodi mlembi wa Salimo 73 anayamba kumva bwanji atatumikila Yehova kwa kanthawi?
16 Nanga bwanji ngati pa nthawi ina mwayamba kumva kuti sindinu woyenelela cikondi ca Yehova? Monga mmene taonela, izi n’zofanana ndi zimene zinacitikila wolemba Salimo 73. Iye anati: “Mapazi anga anangotsala pangʼono kusocela, mapazi anga anangotsala pangʼono kuteleleka.” (Sal. 73:2) Iyemwini anakamba kuti mtima wake ‘unamupweteka’ ndiponso kuti anali “wopanda nzelu” “ngati nyama yosaganiza pamaso” pa Yehova. (Sal. 73:21, 22) Kodi anaganiza kuti ndi wotaikilatu komanso wosayenela kukondedwa ndi Yehova cifukwa ca zolakwa zake?
17. (a) Kodi wamasalimo anacita ciyani ngakhale pamene anali wofooka kwambili? (b) Nanga tingaphunzilepo ciyani pa zimene zinamucitikila? (Onaninso zithunzi.)
17 Ngati wamasalimoyu anamva kuti wakanidwa ndi Yehova, ndiye kuti anangomva conco kwa kanthawi. Zikuoneka kuti atafooka kwambili, m’pamene anazindikila kufunika koyandikila Mulungu malinga ndi zimene anakamba kuti: “Koma tsopano ine ndili ndi inu [Yehova] nthawi zonse. Mwandigwila dzanja langa lamanja. Mumanditsogolela ndi malangizo anu, ndipo pambuyo pake mudzandipatsa ulemelelo.” (Sal. 73:23, 24) Ifenso tiyenela kupempha Yehova kuti atipatse mphamvu tikafooka kapena tikalefuka ndi zofooka zathu. (Sal. 73:26; 94:18) Ngakhale titalakwitsa zinthu zazikulu, tingabwelele kwa Yehova tili ndi cidalilo cakuti iye ndi “wokonzeka kukhululuka.” (Sal. 86:5) Pamene takhala ofooka zedi, tiyenela kumuyandikila Mulungu wathu.—Sal. 103:13, 14.
Tikafooka kuuzimu, timuyandikile kwambili Yehova pocita zinthu zauzimu mokwanila (Onani ndime 17)
“KUYANDIKILA KWA MULUNGU” KWAMUYAYA
18. N’cifukwa ciyani kuyandikila Yehova sikutha?
18 Kuyandikila Yehova sikutha, ndipo tidzapitilizabe kuphunzila zatsopano zokhudza iye. Baibulo limati njila za Yehova, nzelu zake, komanso cidziwitso cake, ndi zosasanthulika.—Aroma 11:33.
19. Kodi Masalimo amatitsimikizila za ciyani?
19 Salimo 79:13 limati: “Ife anthu anu komanso nkhosa zimene mukuweta, tidzakuyamikani mpaka kalekale. Ndipo tidzalengeza kuti inu ndi woyenela kutamandidwa ku mibadwomibadwo.” Mukapitiliza kumuyandikila Mulungu, simudzakaikila zakuti mudzalandila madalitso amuyaya, ndipo mudzatha kunena kuti: “Mulungu ndi thanthwe la mtima wanga ndiponso colowa canga mpaka kalekale.”—Sal. 73:26.
NYIMBO 32 Ima ku Mbali ya Yehova
a Ena amene akhala akugwebana ndi nkhawa kapena cisoni kwa nthawi yaitali, angafunikile thandizo la dokotala. Kuti mudziwe zambili, onani Nsanja ya Mlonda Na. 1 2023.