NKHANI YOPHUNZILA 43
NYIMBO 90 Tilimbikitsane Wina na Mnzake
Mmene Tingathetsele Zikaiko Zathu
“Tsimikizilani zinthu zonse.”—1 ATES. 5:21.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Mmene tingathetsele zikaiko zimene zingatilefule pamene tikutumikila Yehova.
1-2. (a) Ni mafunso ati amene atumiki a Yehova angakhale nawo? (b) Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?
ANTHU a misinkhu yonse amakhala na zikaikoa nthawi zina. Mwacitsanzo, ganizilani za wacicepele wa Mboni amene akukaika ngati Yehova amasamaladi za iye. Iye angamadodome kuti abatizike. Kapena ganizilani za m’bale wacikulile tsopano, amene pacinyamata cake anapanga cisankho coika za Ufumu patsogolo m’malo mofuna nchito yapamwamba m’dzikoli. Koma tsopano popeza n’zovutilapo kupeza ndalama zokwanila kusamalila banja lake, akukaikila ngati anapanga cisankho canzelu. Ganizilaninso za mlongo wacikalambile amene alibenso nyonga ngati kale. Angalefuke posakwanitsanso zimene anali kucita bwino kale. Kodi munadzifunsapo mafunso akuti: ‘Kodi Yehova amaniŵelengeladi? Kodi kudzimana konse kumene nacita cifukwa ca Yehova n’konipinduliladi? Kodi ineyo nikali wofunikadi kwa Yehova?’
2 Ngati sitipeza mayankho okhutilitsa pa mafunso amenewa, tingalefuke kapenanso kuleka kutumikila Yehova. M’nkhani ino, tikambilane mmene mfundo za m’Baibo zingatithandizile ngati tili na zikaiko izi: (1) Kodi Yehova amasamaladi za ine? (2) Kodi zisankho zimene n’napanga kumbuyoku zinalidi zanzelu? Kapena (3) kodi ineyo nikali wofunikadi kwa Yehova?
MMENE MUNGATHETSELE ZIKAIKO ZANU
3. Tingacite ciyani kuti tithetse zikaiko zathu?
3 Njila imodzi imene tingathetsele zikaiko zathu ni kuŵelenga Mawu a Mulungu. Tikatelo, tidzakhala pa ubwenzi wolimba na Yehova, ndipo tidzakhala na “cikhulupililo colimba.”—1 Akor. 16:13.
4. Kodi tingacite ciyani kuti ‘tizitsimikizila zinthu zonse’? (1 Atesalonika 5:21)
4 Ŵelengani 1 Atesalonika 5:21. Baibo imatilimbikitsa kuti: “Tsimikizilani zinthu zonse.” Tingacite bwanji zimenezi? Ngati si ndife otsimikiza pa nkhani inayake onani zimene Baibo imakambapo pa nkhaniyo. Mwacitsanzo, ganizilani za wacinyamata amene amakaikila ngati Mulungu amamuona kuti ni wofunika. Kodi iye ayenela kuganiza kuti Yehova samuona kuti ni wofunika, cabe cifukwa ali na maganizo amenewa? Ayi. M’malomwake, ayenela kufufuza na ‘kutsimikizila zinthu zonse’ mwa kuŵelenga Baibo kuti adziŵe maganizo a Yehova pa nkhaniyo.
5. Tingawapeze bwanji mayankho ocokela kwa Yehova a mafunso athu?
5 Tikamaŵelenga Mawu a Mulungu, zimakhala ngati Yehova akukamba nafe. Koma timafunika kucita zambili kuwonjezela pa kuŵelenga Baibo kuti tidziŵe maganizo a Yehova pa mafunso athu. Tiyenela kufufuza na kuŵelenga Malemba amene angatithandize kupeza mayankho a mafunso athu. Pocita izi, tingaseŵenzetse zida zofufuzila zimene Yehova wapeleka. (Miy. 2:3-6) Tiyenela kupempha Yehova kuti atithandize kupeza yankho locokela kwa iye la funso lathu. Kenako tingapeze mfundo za m’Baibo zimene zingakhale zothandiza. Tingapindulenso tikamaŵelenga nkhani za anthu a m’Baibo amene analipo na maganizo monga athu.
6. Kodi misonkhano ingatithandize bwanji kuthetsa zikaiko zathu?
6 Yehova amalankhulanso nafe kudzela m’misonkhano imene timakhala nayo. Tikamasonkhana nthawi zonse, tingamve nkhani kapena ndemanga imene ingatithandize kuthetsa zikaiko zathu. (Miy. 27:17) Tsopano tiyeni tikambilane zimene zingatithandize kuthetsa zikaiko zina zimene tingakhale nazo.
MUKAMAKAIKILA NGATI YEHOVA AMASAMALADI ZA INU
7. Kodi anthu ena angadzifunse funso liti?
7 Kodi munadzifunsapo kuti, ‘Kodi Yehova amaniŵelengeladi?’ Mukamadziona kuti ndinu wosafunika, mungaone kuti n’zosatheka kukhala pa ubwenzi na Mlengi wacilengedwe conse. N’kutheka kuti Mfumu Davide anaganizapo mwa njila imeneyi. Iye anadabwa kuti Yehova amasamala za anthu, conco anafunsa kuti: “Inu Yehova, munthu ndi ndani kuti muzimuganizila? Kodi mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimuŵelengela?” (Sal. 144:3) Kodi yankho la funso limeneli mungalipeze kuti?
8. Malinga na 1 Samueli 16:6, 7, 10-12, kodi Yehova amaona ciyani mwa anthu?
8 Baibo imaphunzitsa kuti Yehova amaŵelengela anthu amene amaoneka osafunika kwa ena. Mwacitsanzo, Yehova anatuma Samueli kupita kunyumba ya Jese kukadzoza mmodzi mwa ana ake aamuna kuti adzakhale mfumu ya m’tsogolo ya Isiraeli. Ngakhale kuti Jese anali na ana 8, iye anangoitana ana ake 7 kuti adzaonane na Samueli. Koma anasiya Davide amene anali wamng’ono kwambili.b Ngakhale n’telo, Yehova anasankha Davide. (Ŵelengani 1 Samueli 16:6, 7, 10-12.) Yehova anaona mmene Davide analili. Anaona kuti mnyamatayu anali kukonda zinthu zauzimu.
9. N’ciyani cingakutsimikizileni kuti Yehova amakuonani kuti ndinu ofunika? (Onaninso cithunzi.)
9 Ganizilani mmene Yehova waonetsela kale kuti amakuonani kuti ndinu ofunika. Iye amakupatsani malangizo abwino koposa ogwilizana na zimene mukukumana nazo. (Sal. 32:8) Amakwanitsa kucita zimenezi cifukwa amakudziŵani bwino. (Sal. 139:1) Mukamaseŵenzetsa malangizo a Yehova, na kuona mmene malangizowo akukuthandizilani, mudzakhala otsimikiza kuti Yehova amakuonani kuti ndinu ofunika. (1 Mbiri 28:9; Mac. 17:26, 27) Yehova amaona zonse zimene mumacita pomutumikila. Iye amaona makhalidwe anu abwino ndipo amafuna kuti mukhale bwenzi lake. (Yer. 17:10) Ndipo iye amasangalala inunso mukafuna kukhala bwenzi lake.—1 Yoh. 4:19.
“Ukamufunafuna [Yehova], adzalola kuti umupeze.”—1 Mbiri 28:9 (Onani ndime 9)c
MUKAMAKAIKILA NGATI ZISANKHO ZIMENE MUNAPANGA KUMBUYOKU ZINALI ZANZELU
10. Kodi tingakhale na mafunso ati tikaganizila zisankho zimene tinapanga kumbuyoku?
10 Nthawi zina, ena angamaganizile zisankho zimene anapanga kumbuyoku, n’kumadzifunsa ngati anasankhadi zinthu mwanzelu. Mwina anasiya nchito ya malipilo abwino, kapena anasiya bizinesi yapamwamba kuti acite zambili potumikila Yehova. Koma tsopano papita nthawi yaitali kucokela pamene anapanga zisankhozo. Ndipo angamaone kuti anzawo amene anapanga zisankho zosiyanako na zawo ali na ndalama zambili, ndiponso kuti zinthu zikuwayendela bwino. Conco angayambe kudzifunsa kuti: ‘Kodi cinalidi canzelu kudzimana zinthu zambili kuti nitumikile Yehova? Kapena kodi cisankho cangaci cinanitayitsa mwayi wopanga ndalama zambili?’
11. Kodi wolemba Salimo 73 anali na maganizo ati olefula?
11 Ngati inunso mumadzifunsa mafunso ngati amenewa, onani mmene munthu yemwe analemba Salimo 73 anamvela. Iye anaona kuti anthu amene sanali kutumikila Yehova anali kuoneka athanzi, acuma, komanso opanda nkhawa. (Sal. 73:3-5, 12) Ataona kuti zinthu zikuwayendela bwino anthu amenewa, iye anayamba kuona kuti kutumikila Yehova kulibe phindu lililonse. Maganizo olefula amenewa anali “kumuvutitsa tsiku lonse.” (Sal. 73:13, 14) N’ciyani cinamuthandiza kugonjetsa maganizo olefula amenewa?
12. Malinga na Salimo 73:16-18, n’ciyani cinathandiza wolemba salimoli kuthetsa maganizo ake olefula?
12 Ŵelengani Salimo 73:16-18. Wolemba salimoyu anapita ku malo opatulika a Yehova komwe anapeza mtendele. Ali kumeneko, iye anatha kuiganizila mozama nkhaniyo. Ndipo anamvetsa kuti ngakhale kuti anthuwo anali kukhala umoyo wa wofuwofu, analibe tsogolo. Zimenezi zinamubweletsela mtendele wa mumtima podziŵa kuti cisankho cimene anapanga cotumikila Yehova, cinali cabwino koposa. Izi zinamuthandiza kutsimikiza mtima kuti apitilize kutumikila Yehova.—Sal. 73:23-28.
13. Mungapeze bwanji mtendele wa mumtima mukamakaikila ngati zisankho zimene munapanga kumbuyoku zinalidi zanzelu? (Onaninso cithunzi.)
13 Monga anacitila wamasalimo, inunso mungathe kuwagonjetsa maganizo olefula. Mungacite bwanji zimenezi? Muziganizila zinthu zabwino zimene muli nazo, komanso mmene Yehova wakudalitsilani. Ndipo muzikumbukila kuti anthu amene satumikila Yehova, salandila thandizo lake. Iwo amangodalila zinthu zakuthupi zimene ali nazo cifukwa alibe ciyembekezo ca za m’tsogolo. Koma ife, Yehova watilonjeza kuti tidzasangalala na zinthu zabwino kwambili m’tsogolo. (Sal. 145:16) Kunena zoona, simunganene motsimikiza mmene umoyo wanu ukanakhalila mukanasankha zinthu mosiyanako na mmene munacitila. Koma cinthu cimodzi cotsimikizika n’cakuti: Mukasankha kucita zina zake cifukwa cokonda Mulungu komanso anthu, simudzasoŵa ciliconse cabwino.
Muziganizila madalitso a za m’tsogolo amene Yehova wakulonjezani (Onani ndime 13)d
MUKAMAKAIKILA NGATI MUKALI WOFUNIKA KWA YEHOVA
14. Kodi ena akukumana na zovuta zotani? Nanga angamadzifunse funso liti?
14 Atumiki ena a Yehova amalephela kucita zambili cifukwa ca ukalamba, vuto la thanzi, kapenanso cifukwa ca ulemali. Izi zingawapangitse kuyamba kukaikila ngati akali ofunika m’maso mwa Yehova. Angamadzifunse kuti, ‘Kodi nikali wofunika kwa Yehova?’
15. Kodi wolemba Salimo 71 anali wotsimikiza za ciyani?
15 Wolemba Salimo 71 nayenso anali na nkhawa yofanana na imeneyi. Iye anauza Yehova kuti: “Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zatha.” (Sal. 71:9, 18) Ngakhale kuti anali na nkhawa imeneyi, wamasalimoyo anadziŵa kuti ngati watumikila Mulungu mokhulupilika, Mulunguyo adzamuthandiza. Iye anadziŵa kuti Yehova amakondwela na anthu amene amacita zonse zimene angathe pomutumikila ngakhale kuti ali na vuto la thanzi.—Sal. 37:23-25.
16. Kodi Yehova angaŵasewenzetse bwanji okalamba? (Salimo 92:12-15)
16 Ngati ndinu okalamba, muzidziona mmene Yehova amakuonelani. Angakuthandizeni kuti mupitilize kumutumikila mwacimwemwe ngakhale kuti muli na thanzi lofooka. (Ŵelengani Salimo 92:12-15.) M’malo moganizila zimene simungakwanitse kucita, muziganizila kwambili zimene mungakwanitse. Mwacitsanzo, mungalimbikitse ena mwa kukhalabe okhulupilika komanso mwa kuwaonetsa cidwi. Mungawafotokozeleko mmene Yehova wakhala akukusamalilani kwa zaka zambili, na kuwauzako za ciyembekezo cimene muli naco cakuti malonjezo a za m’tsogolo adzakwanilitsidwa. Ndipo musamaiŵale kuti mukamapemphelela ena mocokela pansi pa mtima, Mulungu amamva. (1 Pet. 3:12) Mulimonse mmene zinthu zilili kwa ife, tonsefe tili na cina cake cimene tingapatse Yehova komanso anthu ena.
17. N’cifukwa ciani tiyenela kupewa kudziyelekezela na ena?
17 Ngati mumakhumudwa cifukwa cakuti simungacite zambili potumikila Yehova, dziŵani kuti iye amayamikila zilizonse zimene mungakwanitse kum’patsa. Nthawi zina mungafune kuyelekezela zimene mumakwanitsa kucita na zimene ena amacita. Koma musacite zimenezo. Cifukwa ciyani? Cifukwa Yehova satiyelekezela na munthu wina aliyense. (Agal. 6:4) Mwacitsanzo, Mariya anapatsa Yesu mphatso ya mafuta odula komanso onunkhila kwambili. (Yoh. 12:3-5) Koma mosiyanako na zimenezi, mkazi wina wamasiye wosauka anacita copeleka pa kacisi ca tumakobili tuŵili tocepa mphamvu kwambili. (Luka 21:1-4) Koma Yesu sanayelekezele mphatso za azimayi aŵiliwa. M’malomwake, anaona kuti azimayi onsewa anali na cikhulupililo. Yesu amatengela citsanzo ca Atate wake, Yehova. Conco sitikaikila kuti Yehova amayamikila kwambili zilizonse zimene timamucitila cifukwa ca kudzipeleka kwathu, komanso cikondi cathu pa iye ngakhale zioneke zazing’ono kwa ife.
18. N’ciyani cingatithandize kuthetsa zikaiko zathu? (Onaninso danga lakuti “Mawu a Yehova Angatithandize Kuthetsa Zikaiko Zathu”)
18 Tonsefe nthawi zina tingakhale na zikaiko. Koma monga mmene taonela, Mawu a Mulungu odalilika a coonadi, angatithandize kuthetsa zikaiko zimene tingakhale nazo. Conco citani zonse zotheka kuti muthetse zikaiko zanu. Mukatelo, mudzalimbikitsidwa ndipo simudzakhala na nkhawa. Mosakaikila, Yehova amakudziŵani bwino inuyo panokha. Amayamikila kuti munasankha kumuika patsogolo mu umoyo wanu ndipo adzakudalitsani. Khalani otsimikiza mtima kuti Yehova amakonda atumiki ake onse okhulupilika ndipo amawasamalila.
NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe
a KUFOTOKOZELA MAWU ENA: M’nkhani ino, tikambilane zikaiko zimene tingakhale nazo zakuti kodi Yehova amationadi kukhala ofunika, kapena kodi zisankho zomwe tinapanga kumbuyoku zinalidi zanzelu. Apa sitikunena zikaiko zimene Baibo imakambapo zobwela cifukwa copanda cikhulupililo mwa Yehova komanso pa malonjezo ake ayi.
b Ngakhale kuti Baibo sitiuza kuti Davide anali na zaka zingati pamene Yehova anamusankha, zikuoneka kuti iye anali wacinyamata pa nthawiyo.—Onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 2011, tsamba 29, ndime 2.
c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mlongo wacitsikana akufufuza m’Malemba kuti adziŵe maganizo a Yehova pa nkhani inayake.
d MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Pamene m’bale akugwila nchito kuti apeze ndalama zosamalila banja lake, akudziona m’maganizo mwake kuti ali m’Paradaiso.