LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 June masa. 14-19
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • SITIDZIWA KUTI MAPETO ADZAFIKA LITI
  • SITIDZIWA MMENE YEHOVA ANGACITILE ZINTHU
  • SITIDZIWA ZA MAWA
  • SITINGAMVETSE MOFIKAPO MMENE YEHOVA AMATIDZIWILA
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Muzikumbukila Kuti Yehova ni “Mulungu Wamoyo”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Kodi Tidziŵapo Ciyani za Mmene Yehova Adzaweluzile Anthu M’tsogolo?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zimene Tiphunzilapo pa Mawu Othela Omwe Amuna Okhulupilika Anakamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 June masa. 14-19

NKHANI YOPHUNZILA 26

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa

“Wamphamvuyonse sitingathe kumumvetsa.”​—YOBU 37:23.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Tingathe kupilila mavuto tikavomeleza kuti pali zimene sitidziwa, tikaika maganizo athu pa zimene tidziwa, ndiponso tikaika cidalilo cathu mwa Yehova.

1. Kodi Yehova anatipatsa luso lotani potilenga? Nanga n’cifukwa ciyani?

YEHOVA anatilenga ndi luso lakuti tizitha kuganiza, kuphunzila zinthu, kumvetsa zinthu, komanso kugwilitsa nchito zinthu zimene taphunzila. N’cifukwa ciyani anatilenga mwa njila imeneyi? Mulungu amafuna kuti tim’dziwe ndi kum’tumikila pogwilitsa nchito luso la kuganiza.​—Miy. 2:​1-5; Aroma 12:1.

2. (a) Kodi tiyenela kudziwa ciyani? (Yobu 37:​23, 24) (Onaninso cithunzi.) (b) Timapindula motani tikavomeleza modzicepetsa kuti sitidziwa zonse?

2 Ngakhale kuti Yehova anatilenga ndi luso lokwanitsa kuphunzila zinthu, pali zinthu zambili zimene sitidziwa. (Welengani Yobu 37:​23, 24.) Tiyeni tikambilane zinacitikila Yobu. Yehova anafunsa Yobu mafunso ambili amene anam’thandiza kuzindikila kuti panali zambili zimene sanali kudziwa. Zimenezi zinam’thandiza kukhala wodzicepetsa komanso kuti awongolele kaganizidwe kake. (Yobu 42:​3-6) Nafenso timapindula tikazindikila kuti sitidziwa zonse. lzi zidzatithandiza kukhulupilila kuti Yehova adzatiululila zimene tikufunikiladi kudziwa kuti tipange zisankho zanzelu.​—Miy. 2:6.

Kuwala kocokela m’mitambo kukuonekela pa Yobu pamene Yehova akulankhula naye. Elihu ndi amuna otonthoza abodza atatu akupenyelela zocitikazo ali capafupi.

Monga zinalili ndi Yobu, nafenso tingapindule tikavomeleza kuti pali zimene sitidziwa (Onani ndime 2)


3. Kodi tikambilana ciyani m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tikambilana zina mwa zinthu zimene sitidziwa, komanso vuto limene lingakhalepo cifukwa ca kusadziwako. Tionanso ubwino umene umakhalapo ngati sitidziwa zinthu zina. Kukambilana zimenezi kudzalimbitsa cidalilo cathu cakuti Yehova, “amene amadziwa ciliconse,” amatiuza zimene tikufunikiladi kudziwa.​—Yobu 37:16.

SITIDZIWA KUTI MAPETO ADZAFIKA LITI

4. Malinga ndi Mateyo 24:​36, kodi n’ciyani cimene sitidziwa?

4 Welengani Mateyo 24:36. Sitidziwa kuti mapeto a dongosolo lino la zinthu adzafika liti. Ngakhale Yesu ali padziko lapansi, sanali kulidziwa “tsiku limenelo ndi ola lake.”a Ndipo pa nthawi ina, iye anauza atumwi kuti Yehova ndiye amasankha nthawi ya zocitika zinazake. (Mac. 1:​6, 7) Yehova anaika kale nthawi pomwe mapeto a dongosolo lino la zinthu adzafika. Koma si kwa ife kudziwa tsikulo.

5. Kodi tingakhudzidwe motani cifukwa cosadziwa nthawi pomwe mapeto adzafika?

5 Malinga n’zimene Yesu anakamba, sitidziwa utali umene watsalako kuti mapeto afike. Kusadziwa zimenezi kungacititse kuti tiyambe kuona kuti tsikulo likucedwa, kapena tingalefuke. Izi zingakhale telo makamaka ngati takhala tikuyembekezela tsiku la Yehova kwa nthawi yaitali. N’kutheka kuti cifukwa ca ici, zingakhale zovuta kwa ife kupilila pamene a m’banja lathu kapena anthu ena akutinyoza. (2 Pet. 3:​3, 4) Tingayambe kuganiza kuti zikanakhala zosavuta kuliyembekezela tsikulo moleza mtima, komanso kupilila manyozo mosavuta zikanakhala kuti tinali kulidziwa tsikulo.

6. Kodi kusadziwa tsiku pomwe mapeto adzafika kuli ndi ubwino wanji?

6 Posatiululila tsiku pomwe mapeto adzafika, Yehova amatipatsa mwayi woonetsa kuti timam’tumikila cifukwa comukonda, komanso kuti timam’khulupilila. Sitiika kwambili maganizo athu pa tsiku lomwe Yehova adzabweletse mapeto. Kucita izi kungakhale ngati kuika deti ya ekisipaya pa cikhulupililo cathu. M’malo moika kwambili maganizo athu pomwe “tsiku la Yehova” lidzafika, tingacite bwino kuika maganizo athu pa zimene zidzacitika tsikulo likadzafika. Tikatelo, tingawonjezele cangu cathu cotumikila Mulungu ndi kucita zonse zimene tingathe kuti tim’kondweletse.​—2 Pet. 3:​11, 12.

7. Kodi n’ciyani cimene tidziwa?

7 Tingacite bwino kuika maganizo athu pa zimene tidziwa. Mwacitsanzo, timadziwa kuti masiku otsiliza anayamba mu 1914. Kudzela m’Baibo, Yehova watipatsa maulosi amene amatitsimikizila kuti masiku otsiliza anayamba mu 1914. Iye anatiuzanso mmene zinthu zidzakhalile pa dziko lapansi kuyambila m’caka cimeneco kupita m’tsogolo. Conco, ndife otsimikiza kuti “tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.” (Zef. 1:14) Tidziwanso nchito imene Yehova amafuna kuti ticite, yomwe ndi kuuza anthu ambili mmene tingathele za “uthenga wabwino . . . wa Ufumu.” (Mat. 24:14) Uthengawu ukulalikidwa m’maiko pafupifupi 240, m’zinenelo zoposa 1,000. Sitifunikila kucita kudziwa “tsiku limenelo ndi ola lake” kuti tikhale acangu poigwila nchito yofunika imeneyi.

SITIDZIWA MMENE YEHOVA ANGACITILE ZINTHU

8. Kodi mawu akuti “nchito ya Mulungu woona” atanthauza ciyani? (Mlaliki 11:5)

8 Si nthawi zonse pomwe tingadziwe “nchito ya Mulungu woona.” (Welengani Mlaliki 11:5.) Mawu akuti “nchito ya Mulungu woona” pa lembali atanthauza zimene Yehova amapangitsa kuti zicitike, kapena zimene Mulungu amalola kuti zicitike pofuna kukwanilitsa colinga cake. Sitingadziwe mwatsimitsimi cifukwa cake iye walola zinazake kucitika kapena zimene iye adzacita kuti atithandize. (Sal. 37:5) Baibo imati kusamvetsa “nchito ya Mulungu woona” kuli ngati kusamvetsa mmene mwana amakulila m’mimba mwa mayi ake. Ngakhale asayansi mpaka pano samvetsa bwinobwino mmene mwana amakulila m’mimba mwa amayi ake. Mofananamo, nafenso sitidziwa mofikapo mmene Yehova adzacitila zinthu.

9. Posadziwa mmene Mulungu amacitila zinthu, kodi n’ciyani cingacitike kwa ife?

9 Kusadziwa mmene Yehova adzatithandizila kungapangitse kuti tizengeleze kupanga zisankho zinazake. Tingazengeleze kudzimana zinthu zinazake kuti tiwonjezele utumiki. Mwacitsanzo, tingalephele kukhala umoyo wosalila zambili, kapena tingalephele kupita kumalo osowa. Nthawi zina tingaganize kuti Mulungu sakondwela nafe tikalephela kukwanilitsa zolinga zathu zauzimu. Izi zingacitikenso ngati sitikuona zotulukapo zabwino pambuyo pogwila nchito molimbika mu utumiki, komanso ngati tikukumana ndi zopinga pogwila nchito zina za gulu.

10. Kodi kusadziwa mmene Yehova adzacitila zinthu kumatithandiza kukulitsa makhalidwe ati ofunika?

10 Kusadziwa mmene Mulungu adzacitila zinthu kumatithandiza kukulitsa makhalidwe ofunika monga kudzicepetsa. Izi zimatipangitsa kufika pozindikila kuti maganizo ndi njila za Yehova n’zapamwamba kuposa zathu. (Yes. 55:​8, 9) Timaphunzilanso kudalila Yehova kwathunthu podziwa kuti zonse adzaziyendetsa bwino. Tikakhala ndi zotulukapo zabwino mu utumiki kapena pa nchito zina za gulu, timapeleka citamando conse kwa Yehova. (Sal. 127:1; 1 Akor. 3:7) Ngati zinthu sizinayende mmene tinali kuyembekezela, tiyenela kukumbukila kuti Yehova ndiye adziwa zonse. (Yes. 26:12) Timacita zimene tingathe podziwa kuti Yehova adzatithandiza. Timakhala n’cidalilo cakuti iye adzatipatsa citsogozo cimene tikufunikila, ngakhale kuti sangacite zimenezo mozizwitsa monga anali kucitila nthawi zakumbuyo.​—Mac. 16:​6-10.

11. N’zinthu zotani zimene tidziwa zimene zingatithandize?

11 Tidziwa kuti Yehova nthawi zonse amacita zinthu mwacikondi, mwacilungamo, komanso mwanzelu. Tidziwanso kuti iye amayamikila kwambili zimene timamucitila komanso zimene timacitila alambili anzathu. Cina, tidziwanso kuti Yehova nthawi zonse amafupa awo amene ndi okhulupilika kwa iye.​—Aheb. 11:6.

SITIDZIWA ZA MAWA

12. Malinga ndi Yakobo 4:​13, 14, n’ciyani cimene sitidziwa?

12 Welengani Yakobo 4:​13, 14. Mfundo yosatsutsika ndi yakuti sitidziwa mmene zinthu zidzakhalile mawa. M’dongosolo lino la zinthu, “nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezeleka” zimatigwela. (Mlal. 9:11) Conco, sitingadziwe ngati zolinga zathu zidzakwanilitsidwa kapena ngati tidzakhala ndi moyo kuti tizikwanilitse.

13. Kodi kusadziwa za mawa kungatikhudze bwanji?

13 Cingakhale covuta kwa ife kupilila posadziwa zimene zidzacitike mawa. Cifukwa ciyani? Tingamade nkhawa kwambili pa zimene zingacitike, ndipo zimenezo zingatilande cimwemwe. Matsoka osayembekezeleka angacititse kuti tikhale ndi cisoni cacikulu komanso okhumudwa. Ndipo ngati zimene tinali kuyembekezela sizinacitike, tingakhumudwe ndi kulefuka.​—Miy. 13:12.

14. Kodi cimwemwe cathu cimadalila ciyani? (Onaninso zithunzi.)

14 Tikamapilila zovuta, timaonetsa kuti kaya mawa kubwela zotani, timatumikila Yehova cifukwa comukonda, osati cifukwa ca dyela. Nkhani za m’Baibo zimaonetsa kuti sitiyenela kuyembekezela kuti Yehova adzatichinjiliza ku mavuto onse, komanso kuti sanakonzeletu zocitika za mu umoyo wathu. Iye amadziwa kuti cimwemwe cathu sicidalila kudziwa za mawa. M’malomwake, cimwemwe cathu cimadalila pa kutsatila citsogozo cake ndi kumumvela. (Yer. 10:23) Tikamayang’ana kwa iye popanga zisankho, zimakhala ngati tikunena kuti: “Yehova akalola, tikhala ndi moyo ndipo ticita zakutizakuti.”​—Yak. 4:15.

Zithunzi: 1. Tate ndi mwana wake ali ndi cola conyamula pothawa kucitila zakugwa mwadzidzidzi. Akuikamo Baibo komanso zina zothandiza. 2. Tateyo, mayi, ndi mwanayo ali m’tenti pomwe mvula ikugwa, ndipo akugwilitsa nchito zinthu zomwe analongeza m’cola.

Kutsatila citsogozo ca Yehova ndi kumumvela kumatiteteza (Onani ndime 14-15)b


15. Kodi tidziwa ciyani ponena za kutsogolo?

15 Ngakhale kuti sitidziwa za mawa, tidziwa kuti Yehova watilonjeza moyo wosatha m’tsogolo. Ena akakhala kumwamba, ndipo ena pano padziko lapansi. Ndipo tidziwa kuti sanganame komanso kuti palibe ciliconse cingamulepheletse kukwanilitsa malonjezo ake onse. (Tito 1:2) Iye yekha ndiye amene ‘amanenelatu zimene zidzacitike, ndipo kale kwambili ananenelatu zinthu zimene zidzacitike m’tsogolo.’ Umu ndi mmene zinalili kumbuyoku ndipo zidzakhalanso conco m’tsogolo. (Yes. 46:10) Sitikayika konse kuti palibe cimene cingalepheletse Yehova kutikonda. (Aroma 8:​35-39) Adzatipatsa nzelu, citonthozo, komanso mphamvu zimene tikufunikila kuti tipilile zilizonse zimene zingatigwele. Ndife otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza ndi kutidalitsa.​—Yer. 17:​7, 8.

SITINGAMVETSE MOFIKAPO MMENE YEHOVA AMATIDZIWILA

16. Malinga ndi Salimo 139:​1-6, kodi Yehova amadziwa ciyani cimene sitingathe kumvetsa mofikapo?

16 Welengani Salimo 139:​1-6. Mlengi wathu amadziwa mmene tinapangidwila, ndipo amadziwa maonekedwe athu, mmene timamvela, komanso mmene timaganizila. Cidwi cake pa ife sicitha. Iye amadziwa zimene timakamba komanso colinga cake. Amadziwanso zonse zimene timacita komanso cifukwa cake. Monga anakambila Mfumu Davide, Yehova amatisamalila ndipo nthawi zonse ndi wokonzeka kutithandiza. N’zosangalatsa kwambili kuti Ambuye Wamkulu Koposa wa cilengedwe conse, Mulungu wamphamvuyonse amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, ali ndi cidwi cotelo pa ife! Davide anakamba kuti: “Zinthu zimenezi ndi zodabwitsa kwambili kwa ine. Ndi zapamwamba kwambili moti sindingathe kuzifikila.”​—Sal. 139:​6, mawu a m’munsi.

17. N’ciyani cingacititse kuti zikhale zovuta kuvomeleza kuti Yehova amatidziwa bwino?

17 Mwina cifukwa ca mmene banja lathu lilili, cikhalidwe cathu, kapena zimene tinali kukhulupilila kumbuyoku, zingakhale zotivuta kuona Yehova monga Tate wacikondi amene ali ndi cidwi pa ife. Mwina tingaganize kuti zimene tinalakwitsa kumbuyoku zinali zoipa kwambili moti Yehova sakafunanso kukhala nafe pa ubwenzi, ndipo anatalikilana nafe. Ngakhale Davide anamvapo conco nthawi zina. (Sal. 38:​18, 21) Mwinanso munthu amene akuyesetsa kusintha umoyo wake kuti azitsatila mfundo za Mulungu zolungama angadzifunse kuti, ‘Ngati Mulungu amandimvetsa, n’cifukwa ciyani angayembekezele kuti ndileke macitidwe amene aoneka acibadwa kwa ine?’

18. Timapindula motani tikavomeleza kuti Yehova amatidziwa bwino kuposa mmene timadzidziwila? (Onaninso zithunzi.)

18 M’kupita kwa nthawi tingayambe kuvomeleza kuti Yehova amatidziwa bwino kuposa mmene timadzidziwila ndi kuti amaona zabwino mwa ife zimene sitingaone. Iye amatikondabe ngakhale kuti amaona zophophonya zathu. Amamvetsanso cifukwa cake timamva mwa njila inayake, komanso cifukwa cake timacita zinazake, ndipo mwacikondi amafuna kutithandiza. (Aroma 7:15) Tikamvetsa mozamilapo kuti Yehova amaona kuti tingathe kucita zabwino, tingakulitse cidalilo cotithandiza kum’tumikila mokhulupilika komanso mwacimwemwe.

Zithunzi: 1. M’bale wolefuka akuyang’ana pa windo pomwe kwacita mdima komanso kukugwa mvula. 2. M’baleyo ali m’Paradaiso ndipo apita kokayenda ndi anzake. Iwo akusangalala kuona malo okongola.

Yehova amatithandiza kuyang’anizana ndi zinthu zosayembekezeleka za moyo uno mwa kulimbitsa cidalilo cathu cokhudza nthawi yosangalatsa imene tikuiyembekezela m’dziko latsopano (Onani ndime 18-19)c


19. Kodi timadziwa mfundo ziti zosatsutsika ponena za Yehova?

19 Timadziwa kuti Yehova ndiye cikondi. Ndipo mfundoyi ndi yosatsutsika. (1 Yoh. 4:8) Tidziwa kuti mfundo zake zolungama zimaonetsa cikondi cake pa ife komanso kuti nthawi zonse amatifunila zabwino. Tidziwa kuti Yehova amafuna kuti tikapeze moyo wosatha. Anapeleka dipo kuti zimenezi zitheke. Mphatso ya dipo imatitsimikizila kuti tingathe kumukondweletsa Yehova ngakhale kuti ndife ocimwa. (Aroma 7:​24, 25) Tidziwanso kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yoh. 3:​19, 20) Yehova amadziwa zilizonse zimene timacita, ndipo ali ndi cidalilo cakuti tingakwanitse kucita cifunilo cake.

20. N’ciyani cidzatithandiza kupewa nkhawa zosafunikila?

20 Yehova sanatibisile mfundo iliyonse imene tikufunikiladi kuidziwa. Tikavomeleza mfundoyi, timapewa kukhala ndi nkhawa pa zinthu zimene sitingasinthe. M’malomwake, timaika maganizo athu pa zinthu zimene ndi zofunikiladi. Mwa kutelo, timaonetsa kuti cidalilo cathu conse cili mwa Yehova, “amene amadziwa ciliconse.” (Yobu 36:4) Ngakhale kuti sitingathe kumvetsa zonse palipano, tikuyembekezela kudzakhala ndi moyo wamuyaya pamene tidzaphunzila zinthu zatsopano zocokela kwa Mulungu wathu wamkulu zokhudza iye.​—Mlal. 3:11.

TIMAPINDULA MOTANl TIKAVOMELEZA KUTI SITIDZIWA . . .

  • pamene mapeto adzafika?

  • zimene zidzacitika mawa?

  • mmene Yehova amatidziwila?

NYIMBO 104 Mphatso ya Mzimu Woyela

a Yesu ndiye adzakhala patsogolo pa nkhondo yolimbana ndi dziko la Satana loipali. Conco m’pomveka kukhulupilila kuti iye tsopano akudziwa nthawi ya Aramagedo komanso pamene ‘adzapambana pa nkhondo yolimbana’ ndi adani ake.​—Chiv. 6:2; 19:​11-16.

b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Tate ndi mwana wake wamwamuna akulongeza katundu m’cola conyamula pothawa kucitila zakugwa mwadzidzidzi.

c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’bale amene akukumana ndi mavuto akuganizila za cimwemwe cimene adzakhala naco m’dziko latsopano.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani