NKHANI YOPHUNZILA 25
NYIMBO 96 Buku Lake la Mulungu ni Cuma
Maphunzilo Omwe Tikutengapo pa Malailano a Yakobo Olosela Zam’tsogolo—Mbali 2
“Aliyense anam’patsa madalitso omuyenelela.”—GEN. 49:28.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Maphunzilo amene tikutengapo pa malailano a Yakobo olosela zam’tsogolo kwa ana ake 8.
1. Kodi tikambilana ciyani m’nkhani ino?
ANA a Yakobo anasonkhana momuzungulila kuti amvetsele pamene atate awo anali kuwadalitsa. Monga tinaonela m’nkhani yapita, mawu a Yakobo kwa Rubeni, Simiyoni, Levi, ndi Yuda anawacititsa cidwi ana akewo, mwinanso ngakhale kuwadabwitsa kumene. Conco, iwo ayenela kuti anali kuganizila zimene Yakobo anafuna kunena kwa ana 8 enawo. Tiyeni tione zimene tingaphunzilepo pa mawu ake kwa Zebuloni, lsakara, Dani, Gadi, Aseri, Nafitali, Yosefe, ndi Benjamini.a
ZEBULONI
2. Kodi Yakobo anati ciyani kwa Zebuloni? Nanga mawu akewo anakwanilitsika motani? (Genesis 49:13) (Onaninso bokosi.)
2 Welengani Genesis 49:13. Yakobo analosela kuti mbadwa za Zebuloni zidzakhala m’mbali mwa nyanja cakumpoto kwa Dziko Lolonjezedwa. Patapita zaka zoposa 200, mbadwa za Zebuloni zinapatsidwa malo. Malowo anali pakati pa Nyanja ya Galileya ndi Nyanja ya Mediterranean. Ponena za fukolo, Mose analosela kuti: “Kondwela Zebuloni iwe, pa maulendo ako.” (Deut. 33:18) Ulosiwu uyenela kuti unatanthauza kuti zamalonda zidzawayendela bwino a fuko la Zebuloni pokhala kuti dela lawo linali pakati pa nyanja ziwili. Mulimonsemo, mbadwa za Zebuloni zinali ndi cifukwa cokhalila zosangalala.
3. N’ciyani cingatithandize kukhala okhutila?
3 Kodi tiphunzilapo ciyani? Tingakhalebe acimwemwe mosasamala kanthu kuti timakhala kuti kapena zinthu zili motani kwa ife. Kuti tikhalebe acimwemwe, tiyenela kukhala okhutila n’zimene tili nazo. (Sal. 16:6; 24:5) Nthawi zina, cimakhala capafupi kuganizila zinthu zomwe tilibe m’malo moganizila zinthu zomwe tili nazo. Conco, muziika maganizo anu pa zinthu zabwino zimene muli nazo pa umoyo.—Agal. 6:4.
ISAKARA
4. Kodi Yakobo anati ciyani kwa Isakara? Nanga mawu akewo anakwanilitsika motani? (Genesis 49:14, 15) (Onaninso bokosi.)
4 Welengani Genesis 49:14, 15. Yakobo anayamikila Isakara cifukwa cogwila nchito molimbika. Anamuyelekezela ndi bulu wa mafupa olimba. Nyamayi imanyamula katundu wolemela. Yakobo analoselanso kuti Isakara adzakhala ndi nthaka yaconde. Malinga ndi mawu a Yakobo, mbadwa za Isakara zinalandila malo aconde m’mbali mwa Mtsinje wa Yorodano. (Yos. 19:22) Mosakaikila, iwo anacita khama posamalila malo awo. Anacitanso khama pothandiza anthu ena. (1 Maf. 4:7, 17) Mwacitsanzo, pamene woweluza Baraki ndi mneneli wamkazi Debora anapempha Aisiraeli kuti awathandize kumenyana ndi Sisera, fuko la Isakara linali limodzi mwa mafuko amene anadzipeleka. Anacita cimodzimodzi pa nthawi zinanso.—Ower. 5:15.
5. N’cifukwa ciyani tiyenela kugwila nchito mwakhama?
5 Kodi tiphunzilapo ciyani? Yehova amatiyamikila cifukwa ca khama limene timaonetsa pom’tumikila, monga anacitila ndi fuko la Isakara. (Mlal. 2:24) Mwacitsanzo, ganizilani za abale amene amacita khama posamalila mpingo. (1 Tim. 3:1) Abalewa sayenela kumenya nkhondo zenizeni. Koma ayenela kudzipeleka poteteza anthu a Mulungu ku zinthu zimene zingawaononge ku uzimu. (1 Akor. 5:1, 5; Yuda 17-23) Amacitanso khama pokonzekela ndi kukamba nkhani zolimbikitsa mpingo.—1 Tim. 5:17.
DANI
6. Kodi a fuko la Dani anapatsidwa utumiki wotani? (Genesis 49:17, 18) (Onaninso bokosi.)
6 Welengani Genesis 49:17, 18. Yakobo anayelekezela Dani ndi njoka imene imatha kuluma adani aakulu kwambili kuiposa monga hachi ya nkhondo ndi wokwelapo wake. Fuko la Dani linali lolimba mtima komanso lokonzeka kukantha adani a mtundu wa Isiraeli. Pa ulendo wawo wopita ku Dziko Lolonjezedwa, fuko la Dani linali kuteteza mtundu wa Isiraeli mwa ‘kuwalondela kumbuyo.’ (Num. 10:25) Utumikiwu unali wofunika kwambili ngakhale kuti pamene iwo anali kuucita, sanali kuonekela kwa Aisiraeli onse.
7. Kodi tiyenela kukumbukila ciyani pa utumiki uliwonse umene tacita?
7 Kodi tiphunzilapo ciyani? Kodi munacitapo utumiki winawake ndipo munaona kuti ena sanaone nchito imene munagwila? N’kutheka munathandizapo kuyeletsa kapena kukonza Nyumba za Ufumu, kudzipeleka kugwilako nchito pa msonkhano wadela kapena wacigawo, kapenanso kugwilako nchito zina. Ngati munatelo, tikukuyamikilani kwambili. Muzikumbukila nthawi zonse kuti Yehova amaona ndi kuyamikila zonse zimene mumacita pom’tumikila. Iye amayamikila ngako ngati mukum’tumikila, osati n’colinga cakuti ena akutamandeni, koma poonetsa kuti mumam’konda mocokela pansi pa mtima.—Mat. 6:1-4.
GADI
8. N’cifukwa ciyani zinali zosavuta adani a Aisiraeli kuukila a fuko la Gadi? (Genesis 49:19) (Onaninso bokosi.)
8 Welengani Genesis 49:19. Yakobo ananenelatu kuti gulu la acifwamba lidzaukila Gadi. Patapita zaka zopitilila 200, fuko la Gadi linakakhala kum’mawa kwa Mtsinje wa Yorodano, kumalile ndi mitundu ya adani. Izi zinacititsa kuti cikhale capafupi adani kuwaukila. Ngakhale n’telo, fuko la Gadi linafuna kukhala kumeneko cifukwa kunali msipu wabwino wodyetselako ziweto zawo. (Num. 32:1, 5) Ngakhale kuti anthu a fuko la Gadi anali olimba mtima, iwo anadalila kwambili Yehova kuti adzawathandiza kugonjetsa adani awo ndi kuteteza dziko limene Mulungu anawapatsa. Kwa zaka, iwo anali kutumiza magulu awo a nkhondo kukathandiza mafuko ena kugonjetsa mbali yotsala ya Dziko Lolonjezedwa lomwe linali kumadzulo kwa Mtsinje wa Yorodano. (Num. 32:16-19) Iwo anali ndi cidalilo cakuti Yehova adzateteza akazi awo ndi ana awo pomwe amuna anali ku nkhondo. Yehova anawadalitsa cifukwa ca kulimba mtima ndi kudzimana kwawo.—Yos. 22:1-4.
9. Ngati timadalila Yehova, kodi tidzapanga zisankho zotani?
9 Kodi tiphunzilapo ciyani? Tisaleke kudalila Yehova kuti tipitilize kum’tumikila tikakumana ndi mavuto. (Sal. 37:3) Ambili masiku ano amaonetsa kuti amadalila Yehova podzimana zinazake kuti athandizeko pa nchito zomangamanga za gulu, kupitako kumalo osowa, kapena kucitako mautumiki ena. Amatelo cifukwa amakhala ndi cidalilo cakuti Yehova adzawasamalila.—Sal. 23:1.
ASERI
10. Kodi fuko la Aseri linalephela kucita ciyani? (Genesis 49:20) (Onaninso bokosi.)
10 Welengani Genesis 49:20. Yakobo analosela kuti fuko la Aseri lidzakhala lotukuka, ndipo izi n’zimene zinacitikadi. Gawo limene fuko la Aseri linapatsidwa linaphatikizapo malo amene anali aconde kwambili mu Isiraeli yense. (Deut. 33:24) Delali linali m’mphepete mwa Nyanja ya Mediterranean ndipo linaphatikizapo gombe la Sidoni, kumene anthu ambili anali kucitilako malonda. Komabe, fuko la Aseri linalephela kuthamangitsa Akanani omwe anali m’delalo. (Ower. 1:31, 32) N’kutheka kuti cisonkhezelo coipa ca Akanani ndi kutukuka kwa fuko la Aseri, n’zimene zinacepetsa cangu cawo pa kulambila koyela. Pamene woweluza Baraki anali kufunafuna anthu oti akamenyane ndi Akanani, fuko la Aseri silinacitepo kanthu. Izi zinacititsa kuti fuko la Aseri lisatengepo gawo pa cipambano cozizwitsa cimene cinacitika “pafupi ndi madzi a ku Megido.” (Ower. 5:19-21) Fuko la Aseri liyenela kuti linacita manyazi litamva Baraki ndi Debora akuimba nyimbo yacipambano youzilidwa. Ena mwa mawu a m’nyimboyo anali akuti: “Aseri anangokhala phee m’mbali mwa nyanja.”—Ower. 5:17.
11. N’cifukwa ciyani sitiyenela kuona ndalama kukhala cinthu cofunika koposa pa umoyo wathu?
11 Kodi tiphunzilapo ciyani? Timafuna kupatsa Yehova zinthu zabwino koposa. Koma kuti tikwanitse kutelo, tiyenela kupewa kaganizidwe ka dziko pa ndalama komanso pa zinthu zakuthupi. (Miy. 18:11) Timayesetsa kuona ndalama moyenela. (Mlal. 7:12; Aheb. 13:5) Sitimalola kuti zinthu zakuthupi zosafunikila kwenikweni zitilepheletse kutumikila Mulungu. M’malomwake, timayesetsa kupatsa Yehova nthawi ndi mphamvu zathu palipano, tikudziwa kuti moyo wawofuwofu komanso wotetezeka ukutiyembekezela m’dziko latsopano.—Sal. 4:8.
NAFITALI
12. Kodi mawu a Yakobo kwa Nafitali ayenela kuti anakwanilitsika motani? (Genesis 49:21) (Onaninso bokosi.)
12 Welengani Genesis 49:21. Yakobo ananena kuti Nafitali adzakamba “mawu osangalatsa.” Mawu a Yakobo amenewa angakhale kuti anali kuloza mmene Yesu anali kulankhulila pa utumiki wake. Yesu amene anali kudziwika cifukwa ca kaphunzitsidwe kake kogwila mtima, pa nthawi ina anayamba kukhala mu mzinda wa Kaperenao umene unali m’dela la Nafitali. (Mat. 4:13; 9:1; Yoh. 7:46) Ponena za Yesu, Yesaya ananenelatu kuti anthu a ku Zebuloni ndi a ku Nafitali adzaona “kuwala kwakukulu.” (Yes. 9:1, 2) Kudzela m’zimene anali kuphunzitsa, Yesu anali “kuwala kwenikweni kumene kumaunikila anthu osiyanasiyana.”—Yoh. 1:9.
13. Kodi tingatani kuti zokamba zathu zizikondweletsa Yehova?
13 Kodi tiphunzilapo ciyani? Zimene timakamba komanso mmene timazikambila ndi nkhani yaikulu kwa Yehova. Tingacite ciyani kuti tilankhule “mawu osangalatsa” amene amakondweletsa Yehova? Tiyenela kukamba zoona. (Sal. 15:1, 2) Cina, tingalimbikitse ena m’zokamba zathu powayamikila akacita zabwino, ndi kupewa kuwapeza zifukwa kapena kukhala odandaula. (Aef. 4:29) Cinanso, tingadziikile colinga cokhala aluso poyambitsa makambilano amene angatsogolele ku ulaliki.
YOSEFE
14. Kodi mawu a Yakobo kwa Yosefe anakwanilitsika motani? (Genesis 49:22, 26) (Onaninso bokosi)
14 Welengani Genesis 49:22, 26. Yakobo ayenela kuti anali kumunyadila mwana wake Yosefe. Yosefe anali “wosankhidwa pakati pa abale ake.” Ndipo Yehova anamugwilitsa nchito m’njila yapadela. Yakobo anamucha “mphukila ya mtengo wobala zipatso.” Yakobo ndiye anali mtengowo, ndipo Yosefe ndiye anali mphukila. Yosefe ndiye anali mwana woyamba kubadwa wa Yakobo kwa mkazi wake wokondedwa Rakele. Yakobo anaonetsa kuti Yosefe adzalandila colowa ca Rubeni amene anali mwana wake woyamba kubadwa kwa mkazi wake Leya. (Gen. 48:5, 6; 1 Mbiri 5:1, 2) Pokwanilitsa ulosiwo, ana awili a Yosefe, Efuraimu ndi Manase, anakhala mafuko awili ndipo onse awili analandila colowa aliyense payekha.—Gen. 49:25; Yos. 14:4.
15. Kodi Yosefe anacita ciyani atacitidwa zopanda cilungamo?
15 Yakobo ananenanso za anthu oponya mivi ndi uta amene sanaleke “kumuzunza, kumulasa ndi kumusungila cidani [Yosefe].” (Gen. 49:23) Anthuwo anali abale ake omwe poyamba anali kumucitila nsanje, ndipo anapangitsa kuti acitidwe zinthu zambili zopanda cilungamo. Ngakhale n’telo, Yosefe sanadane nawo abale ake kapena kuimba Yehova mlandu pa zimene zinamucitikila. Zinali monga Yakobo anakambila kuti: “Uta [wa Yosefe] unakhalabe pa malo ake ndipo manja ake anakhalabe amphamvu ndi ocenjela.” (Gen. 49:24) Yosefe anadalila Yehova pamene anali kukumana ndi mavuto. Ndipo kuwonjezela pa kukhululukila abale ake, anacitanso nawo mokoma mtima. (Gen. 47:11, 12) Yosefe analola mavuto amene anakumana nawo kuti amuyenge. (Sal. 105:17-19) Zotsatilapo zake zinali zakuti Yehova anamugwilitsa nchito m’njila yapadela.
16. Tingatengele bwanji citsanzo ca Yosefe tikakumana ndi ziyeso?
16 Kodi tiphunzilapo ciyani? Tisalole kuti ziyeso zitilekanitse ndi Yehova kapena ndi alambili anzathu. Tizikumbukila kuti Yehova angalole kuti tikumane ndi zinthu zoyesa cikhulupililo cathu pofuna kutiphunzitsa zinazake. (Aheb. 12:7) Tikalola kuphunzitsidwa mwa njila imeneyi, tingakulitse makhalidwe abwino acikhristu monga cifundo komanso kukhululuka. (Aheb. 12:11) Ngati tipilila, Yehova adzatidalitsa monga anacitila ndi Yosefe.
BENJAMINI
17. Kodi mawu a Yakobo kwa Benjamini anakwanilitsika motani? (Genesis 49:27) (Onaninso bokosi.)
17 Welengani Genesis 49:27. Yakobo analosela kuti ana a Benjamini adzakhala ndi luso lomenya nkhondo ngati m’mbulu. (Ower. 20:15, 16; 1 Mbiri 12:2) Ulosiwu unakwanilitsika m’lingalilo lakuti mfumu yoyamba ya Isiraeli, Sauli, anali wa fuko la Benjamini. Iye anaonetsa kuti anali msilikali wamphamvu komanso wopanda mantha pomenyana ndi Afilisiti. (1 Sam. 9:15-17, 21) Ndipo patapita zaka zambili, Mfumukazi Esitere ndi Moredekai a fuko la Benjamini anapulumutsa Aisiraeli kuti asawonongedwe mu ulamulilo wa Perisiya.—Esitere 2:5-7; 8:3; 10:3.
18. Tingatengele motani citsanzo ca fuko la Benjamini cokhalabe okhulupilika pa makonzedwe a Yehova?
18 Kodi tiphunzilapo ciyani? N’zosacita kufunsa kuti fuko la Benjamini linanyadila kwambili kuona munthu wa fuko lawo akukhala mfumu pokwanilitsa ulosi wa Yakobo. Komabe Yehova atasintha kuti ufumu upite kwa Davide wa fuko la Yuda, a fuko la Benjamini sanatsutse masinthidwewo. (2 Sam. 3:17-19) Patapita zaka, mafuko 10 atapanduka ndi kupanga ufumu wawo, fuko la Benjamini linakhalabe lokhulupilika ku fuko la Yuda komanso ku banja lacifumu la Davide limene Yehova anali atasankha. (1 Maf. 11:31, 32; 12:19, 21) Nafenso tiyeni tipitilize kukhalabe okhulupilika kwa awo amene Yehova wasankha kuti azitsogolela anthu ake masiku ano.—1 Ates. 5:12.
19. Timapindula motani ndi mawu a malailano olosela a Yakobo?
19 Taona mmene malailano olosela a Yakobo angatipindulile. Kuona kukwanilitsika kwa mawuwo kumalimbitsa cidalilo cathu m’malonjezo a Yehova kuti adzakwanilitsika. Ndipo kuona madalitso amene ana a Yakobo anapeza kumatithandiza kumvetsa zimene tingacite kuti tikondweletse Yehova.
NYIMBO 128 Pilila Mpaka Mapeto
a Podalitsa Rubeni, Simiyoni, Levi, ndi Yuda, Yakobo anayambila ndi wamkulu n’kutsilizila ndi wamng’ono. Koma podalitsa ana ake 8 othela aamuna, sanatsate ndondomeko yobadwila.